Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Khalidwe Lobisika Lowononga Thanzi”

“Khalidwe Lobisika Lowononga Thanzi”

“Khalidwe Lobisika Lowononga Thanzi”

KAFUKUFUKU wina waposachedwapa wokhudza za kugonana kwa pa Intaneti wasonyeza kuti anthu achikulire oposa 200,000 amene amagwiritsa ntchito Intaneti ku United States, anatsegulapo malo oonetsa za kugonana. Anthu ambiri masiku ano sakuthanso kuletsa chilakolako chawo chofuna kuonera zithunzi zogonana za pa Intaneti. “Limeneli ndi khalidwe lobisika lowononga thanzi lomwe, mwa zina, lafala chifukwa choti ndi anthu ochepa amene akuzindikira kapena kuganizirapo mozama za kuopsa kwake,” anatero katswiri wazamaganizo Dr. Al Cooper yemwe anachita kafukufuku tam’tchulayu.

Kodi ndani kwenikweni amene amakopeka msanga ndi zithunzi zogonana za pa Intaneti? Dr. Cooper ananena kuti, ndi “anthu ogwiritsa ntchito Intaneti amene sankakonda zogonana ndiponso amene adzisunga moyo wawo wonse” koma amene “mwadzidzidzi apeza mwayi woonerera zogonana nthaŵi zonse” pa Intaneti.

Komabe, ambiri amene kaŵirikaŵiri amatsegula malo oonetsa zogonanawa, amaona ngati khalidwe limeneli n’losavulaza. Kodi zimenezi n’zoona? Mofanana ndi munthu wokonda mankhwala osokoneza bongo amene amakhala atazoloŵera kumwa mankhwala omwe amakondawo, ambiri amenenso amakonda kuonerera kugonana kwa pa Intaneti amangofuna ataonereranso kuti akhutiritse zilakolako zawo. Ndithudi, iwo angachotsedwe ntchito kapena kusokoneza unansi wawo ndi wokwatirana naye.

Komabe, amene amafuna kukondweretsa Mulungu ali ndi chifukwa china chopeŵera kuonerera zithunzi zogonana za pa Intaneti. Mawu a Mulungu amalangiza kuti: “Chifukwa chake fetsani ziŵalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso cha manyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano; chifukwa cha izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera.” (Akolose 3:5, 6) Kuti ‘afetse ziŵalo’ pankhani ya chilakolako chonyansa cha kugonana, munthu ayenera kukonda Yehova Mulungu kwambiri. (Salmo 97:10) Ngati ataona kuti akukopeka ndi khalidwe lowononga thanzi la kuonerera kugonana kwa pa Intaneti, iye ayenera kulimbitsa chikondi chake kwa Yehova mwa kuphunzira Mawu a Mulungu Baibulo. Kusonkhana ndi Mboni za Yehova ku Nyumba ya Ufumu ya m’deralo kungathandize kwabasi kuti munthu akhale wotsimikiza kwambiri kukondweretsa Mulungu.