Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwapindula poŵerenga makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Chabwino, yesani kuyankha mafunso otsatiraŵa:

N’chifukwa chiyani mtumwi Paulo pa Aroma 5:3-5, anatchula chiyembekezo kumapeto kwa m’ndandanda wa mawu enawo?

Paulo anatchula m’ndandanda wa zinthu zomwe Akristu amakumana nazo​—Masautso, chipiriro, chizoloŵezi [“chiyanjo,” NW], ndi chiyembekezo. Ichi si chiyembekezo choyamba chomwe munthu amapeza kuchokera m’Baibulo ayi, koma ndi chiyembekezo cholimbitsidwa, chozamitsidwa, ndiponso choŵalitsidwa chomwe Mkristu angachipeze m’kupita kwanthaŵi​—12/15, masamba 22-3.

N’chifukwa chiyani Mkristu lerolino angakhale ndi chidwi ndi mipikisano ya maseŵera othamanga yomwe inkachitika ku Girisi wakale?

Kuzindikira mtundu wamaseŵera komanso zomwe zinali kuchitika pa maseŵerawo kungathandize kumvetsa bwino mawu ena a mavesi a m’Baibulo. Ena mwa mawu ameneŵa ndi ‘kuyesana monga adapangana’ [‘kupikisana motsatira malamulo,’ NW] ‘kutaya cholemetsa chilichonse ndi kupenyerera chitsanzo cha Yesu,’ ‘kutsiriza njirayo,’ ndiponso kulandira korona kapena mfupo. (2 Timoteo 2:5; 4:7, 8; Ahebri 12:1, 2; 1 Akorinto 9:24, 25; 1 Petro 5:4)​—1/1, masamba 28-30.

Kodi ndi njira yatsopano iti yolengezera uthenga wabwino yomwe inakhazikitsidwa mu January 1914?

“Seŵero la Pakanema la Chilengedwe” linatulutsidwa panthaŵiyo. Seŵeroli linali la zigawo zinayi zokhala ndi zithunzi zoyenda komanso zithunzi zosayenda mazanamazana zokongola. Zambiri mwa zithunzi zimenezi zinkayendera limodzi ndi nkhani zojambulidwa pa galamafoni kapena mawu ofotokozera. Maseŵero okwana 20 amtunduwu anakonzedwa ndipo anagwiritsidwa ntchito mofala kwambiri kuphunzitsa anthu uthenga wa m’Baibulo.​—1/15, masamba 8-9.

Kodi Bungwe Lolamulira limasiyana motani ndi bungwe lalamulo?

Akuluakulu oyendetsa bungwe lalamulo amasankhidwa ndi mamembala a bungweli koma Bungwe Lolamulira silisankhidwa ndi munthu wina aliyense koma Yesu Kristu. Palibe chifukwa choti madailekitala a mabungwe alamulo osiyanasiyana omwe Mboni za Yehova zimagwiritsa ntchito azikhala mamembala a Bungwe Lolamulira. Pamsonkhano wapachaka waposachedwapa wa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, mamembala a Bungwe Lolamulira amene ankagwira ntchito monga madailekitala ndi maofesala anatula pansi maudindowo mwakufuna kwawo. Maudindowo anaperekedwa kwa abale oyenera a m’gulu la “nkhosa zina.” (Yohane 10:16) Chotero Bungwe Lolamulira lizikhala ndi nthaŵi yochuluka yokonza chakudya chauzimu ndiponso kusamalira zosoŵa zauzimu za abale padziko lonse.​—1/15, masamba 29, 31.

Kodi ndi zitsanzo ziŵiri ziti za m’Baibulo zomwe tingapende kuti tidziŵe mmene tingapiririre tikalefulidwa?

Chitsanzo choyamba ndi Hana, amake a Samueli. Iye akanatha kukhumudwa pamene Eli mkulu wa ansembe wa Aisrayeli anamuganizira molakwa. Mmalo mwake, iye moona mtima ndiponso mwaulemu anamuuza Eli zoona zake. Komanso, Hana sanasunge udani ndi Eli. Chitsanzo chachiŵiri ndi Marko, amene ayenera kuti anafooketsedwa kwambiri pamene mtumwi Paulo sanafune kuti iye apite nawo pa ulendo waumishonale. Mmalo mogwa ulesi chifukwa chom’mana mwayi ngati umenewu, iye anapitirizabe utumiki wake mwachangu, akumayenda ndi Barnaba.​—2/1, masamba 20-2.

N’chifukwa chiyani Akristu ayenera kusamala kwambiri pankhani yopereka kapena kulandira makope a mapulogalamu apakompyuta kuchokera kwa ena?

Mapulogalamu ambiri apakompyuta (kuphatikizapo maseŵera apakompyuta) amafuna laisensi yomwe malamulo ake amaneneratu kwa mwiniwake kapena amene akuwagwiritsa ntchito kuti pulogalamuyo iyenera kuikidwa m’kompyuta imodzi basi. Nthaŵi zambiri kukopera pulogalamu n’cholinga choti tipatse anzathu, ngakhale mwaulere, n’kulakwira lamulo loletsa kukopera zinthu. Akristu amafuna kumvera lamulo la ‘kupereka zake za Kaisara kwa Kaisara.’ (Marko 12:17)​—2/15, masamba 28-29.

Kodi Cyril ndi Methodius anali ayani, ndipo anathandiza motani pankhani yophunzira Baibulo?

Iwo anali pachibale ndipo anabadwira ku Tesalonika, Girisi, m’zaka za m’ma 800. Iwo anayambitsa zilembo za zinenero za anthu amtundu wa Asilavo komanso anatembenuza mbali yaikulu ya Baibulo kupita m’Chisilavo.​—3/1, masamba 28-29.

Kodi mawu akuti “chisamaliro cha mzimu” amatanthauzanji?​—Aroma 8:6.

Amatanthauza kulamulidwa, kutsogozedwa, ndi kusonkhezeredwa ndi mphamvu yogwira ntchito ya Yehova. Tingalole kuti mzimu wa Mulungu uzigwira ntchito pa ife mwa kuŵerenga ndi kuphunzira Baibulo, kumvera malamulo a Mulungu ndi mtima wonse, komanso kupempherera mzimu wa Mulungu.​—3/15, masamba 15.

Kodi tingatani ngati titaona kuti anthu sakutimvetsetsa?

Ndibwino kuyesetsa kuthetsa nkhaniyo mwachikondi. Ngati zimenezo sizikuthandiza, musade nkhaŵa. Pemphani chidziŵitso ndiponso chithandizo kwa Yehova amene ‘amayesa mitima.’ (Miyambo 21:2; 1 Samueli 16:7)​—4/1, masamba 21-3.