Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kusamalirana Muubale Wapadziko Lonse

Kusamalirana Muubale Wapadziko Lonse

Kusamalirana Muubale Wapadziko Lonse

KULIKONSE kukuoneka anthu okhaokha. Ambiri ndi okalamba, ena ndi olumala moti sangathe kuyenda bwinobwino. Palinso amayi oyembekezera komanso mabanja atsopano amene abereka ana aang’ono kumbuyo. Onseŵa ndi othaŵa kwawo​—amuna, akazi, ndi ana. Iwo athaŵa kwawo kudzabisala m’dziko loyandikana nalo chifukwa cha nkhondo, masoka achilengedwe, ndi mikhalidwe ina. Ena akhala akuthaŵa kwawo mobwerezabwereza. Akangoona chizindikiro cha nkhondo yapachiweniweni kapena tsoka lachilengedwe, iwo amasonkhanitsa katundu wina pang’ono ndi kutenga ana awo ulendo wothaŵira m’dziko lopanda nkhondo. Kenako, zinthu zikayambanso kuyenda bwino, ambiri amabwerera kwawo kukamanganso nyumba zawo ndi kuyambanso moyo watsopano.

Kwazaka zambiri ndithu, dziko la Central African Republic lakhala likulandira anthu othaŵa kwawo kuchokera m’mayiko angapo. Posachedwapa, anthu miyandamiyanda kuphatikizapo Mboni za Yehova, akakamizika kuthaŵa nkhondo m’dziko la Democratic Republic of Congo kupita m’dziko lopanda nkhondo la Central African Republic.

Abale Anathandiza Anthu Ovutikawo

Mboni za m’dziko la Central African Republic zinali zokondwa kugwira ntchito yokonza thandizo la anthu ovutikawo. Iwo anapeza nyumba zoti abale achikristu azifikiramo. Poyamba, malo ankapezeka m’nyumba za abale, koma chiŵerengero cha anthuŵa chitayamba kuwonjezeka, zinaonekeratu kuti pakufunika kuchitapo kanthu mwamsanga. Choncho, Nyumba zina za Ufumu zinasandutsidwa zipinda zogona. Mboni za m’deralo zinadzipereka ndi mtima wonse kugwira ntchito yoika magetsi ena owonjezera, kupatutsa mapaipi a madzi, ndiponso kuika simenti m’nyumbazo kuti abale azidzagona mwabwino. Othaŵa kwawo anagwira ntchito limodzi ndi abale a m’deralo kukonza nyumba zogona zimenezo. Pulogalamu yachikwanekwane ya misonkhano yachikristu inakonzedwa m’chinenero cha Lingala kuti abale obwerawo azilandira chakudya chauzimu chopatsa moyo. Mgwirizano wa Mboni za m’deralo ndi alendowo unasonyeza kuti ubale wapadziko lonse ulipodi.

Nthaŵi zambiri mabanja aanthu othaŵa kwawo ameneŵa sanali kufika onse nthaŵi imodzi. Nthaŵi zina, anthu a m’banja limodzi amene anasiyana pothaŵa anali kuyanjananso akafika. Maina a anthu amene afika bwinobwino anali kuwasunga pa Nyumba ya Ufumu iliyonse. Panali ntchito yofufuza anthu amene akusoŵabe. Ofesi ya nthambi yomwe imatsogolera ntchito ya Mboni za Yehova m’dzikolo inkatumiza magalimoto atatu patsiku kuti akathandize kunyamula Mboni zimene zinali zikadali m’njira komanso kufufuza amene asoŵa. Magalimotowo ankawazindikira chifukwa cha chizindikiro chachikulu cholembedwa kuti “WATCH TOWER​—Mboni za Yehova.”

Tangoganizani chisangalalo chimene ana asanu ndi aŵiri omwe anatayana ndi makolo awo anali nacho ataona galimoto ya Mboni za Yehova. Iwo nthaŵi yomweyo anathamangira ku galimotoyo n’kudzidziŵikitsa kuti anali a Mboni. Abalewo anakweza anawo m’galimotoyo n’kupita nawo ku Nyumba ya Ufumu kumene anayanjananso ndi mabanja awo.

Kodi chinawatheketsa Akristu oona mtima ameneŵa kupirira mavuto otereŵa, osati kamodzi kokha, koma mobwerezabwereza n’chiyani? Iwo ali otsimikiza kotheratu kuti tikukhala m’masiku otsiriza monga momwe Malemba Opatulika analoserera​—2 Timoteo 3:1-5; Chivumbulutso 6:3-8.

Choncho, iwo akudziŵa kuti Yehova Mulungu posachedwapa adzathetsa nkhondo, udani, chiwawa, ndi mikangano. Vuto lothaŵa m’dziko lakwanu lidzakhala chinthu chakale. Padakali pano, mogwirizana ndi malangizo a mtumwi Paulo opezeka pa 1 Akorinto 12:14-26, Mboni za Yehova zimayesetsa kusamalirana. Ngakhale kuti zimakhala m’madera osiyana, kulankhula zinenero zosiyana ndiponso kukhala m’mayiko otalikirana, Mboni zimaganizirana ndipo zimachitapo kanthu mwamsanga ngati wina akufuna thandizo.​—Yakobo 1:22-27.

[Mapu patsamba 30]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

AFRICA

Central African Republic

Democratic Republic of Congo

[Mawu a Chithunzi]

Mountain High Maps® Copyright © 1997 Digital Wisdom, Inc.

[Zithunzi patsamba 30]

Nyumba za Ufumu zitatu zinagwiritsidwa ntchito monga malo olandirira anthu othaŵa kwawo

[Chithunzi patsamba 31]

Makhichini anamangidwa mofulumira

[Chithunzi patsamba 31]

Anthu othaŵa kwawo anafika ambiri

[Zithunzi patsamba 31]

Ana ongobadwa kumene akhala kale othaŵa kwawo