Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Sitinali Tokha Pamene Chikhulupiriro Chathu Chinali Kuyesedwa

Sitinali Tokha Pamene Chikhulupiriro Chathu Chinali Kuyesedwa

Sitinali Tokha Pamene Chikhulupiriro Chathu Chinali Kuyesedwa

Vicky ali wakhanda anali mwana wamkazi wosangalatsa, wathanzi, wokongola, ndi wamphamvu. Inde, tinasangalala kwambiri mwanayu atabadwa m’nyengo yachilimwe mu 1993. Tinkakhala m’tauni ina yaing’ono kummwera kwa dziko la Sweden ndipo zinthu zinali kutiyendera bwino kwabasi.

KOMA pamene Vicky anali ndi chaka chimodzi ndi theka, zinthu zinayamba kusokonekera. Kwakanthaŵi ndithu iye sanali kupeza bwino moti tinam’tengera kuchipatala. Sitidzaiŵala nthaŵi yomwe dokotala anatiuza kuti mwana wathuyo akudwala kansa yotchedwa acute lymphoblastic leukemia yomwe imagwira maselo oyera amagazi, ana akadali aang’ono.

Zinali zovuta kumvetsa kuti mwana wathu wamng’onoyo akudwala matenda oopsaŵa. Iye anali atangoyamba kuzindikira zinthu koma tsopano anali kuyembekezera kufa. Pofuna kutilimbikitsa, dokotala anatiuza kuti mwanayo atha kuchira ngati atam’patsa mtundu winawake wa makemikolo omwe amafuna kuika magazi kangapo. Zimenezi zinatisokonezanso maganizo.

Chikhulupiriro Chathu Chinayesedwa

Tinkamukonda kwambiri mwana wathu ndipo tinkafuna kuti alandire chithandizo chamankhwala chabwino koposa. Komabe, sitikanalola m’pang’ono pomwe kuti amuike magazi. Timakhulupirira kwambiri Mawu a Mulungu, Baibulo, lomwe limanena mosapita m’mbali kuti Akristu ayenera ‘kusala mwazi.’ (Machitidwe 15:28, 29) Tinkadziŵanso kuti kuikidwa magazi kokhako n’koopsa. Anthu miyandamiyanda atenga matenda ndiponso kumwalira chifukwa choikidwa magazi. Njira yokhayo imene tikanasankha inali thandizo lililonse lamphamvu koma losafuna kuika magazi. Pamenepa, nkhondo yathu yomenyera chikhulupiriro inayamba.

Kodi tikanatani pamenepa? Tinalankhula ndi a ku Dipatimenti Yopereka Chidziŵitso cha Zachipatala ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya ku Sweden kuti atithandize. * Mwamsanga, anatumiza uthenga m’zipatala zosiyanasiyana za ku Ulaya kutifunira chipatala ndiponso dokotala amene angakonde kupereka thandizo pogwiritsa ntchito makemikolowo popanda kuika magazi. Zinali zolimbikitsa kwambiri kuona changu ndiponso chikondi chomwe abale athu achikristu anasonyeza poyesa kutithandiza. Sanatisiye tokha pankhondo yathu yomenyera chikhulupiriro.

M’maola ochepa chabe, chipatala ndiponso dokotala anapezeka ku Homburg/​Saar, Germany. Ulendo unakonzedwa woti tinyamuke pa ndege m’mawa mwake kuti Vicky akamuyese. Titafika, abale athu achikristu amumpingo wa Mboni za Yehova wa m’deralo ku Homburg, pamodzi ndi achibale athu ena anali kutiyembekezera. Ndipo woimira Komiti Yolankhulana ndi Chipatala ya m’deralo anatilandira bwino kwambiri. Iye anatiperekeza ku chipatala ndipo anatichirikiza mmene akanathera. Tinalimbikitsidwa kwambiri kuona kuti ngakhale m’dziko lachilendo limenelo abale athu auzimu anali kutichirikiza.

Tinalimbikitsidwanso titaonana ndi Dr. Graf pa chipatalacho. Iye anali dokotala womvetsa ndipo anatitsimikizira kuti ayesetsa mmene angathere kuthandiza Vicky popanda kumuika magazi. Ananenetsa kuti ngakhale magazi ake atachepa kwambiri kufika pa 5g/​dl, adzapitirizabe kum’patsa mankhwala popanda kumuika magazi. Iye ananenanso kuti pali mwayi woti Vicky atha kuchira popeza kuti matendawo anawazindikira msanga ndiponso kuti sanazengereze kum’tengera kuchipatalacho. Ndipo ananeneratunso kuti aka kakhala koyamba kuti iye apereke thandizo pogwiritsa ntchito makemikolo kwa wodwala matenda ngati a Vicky popanda kuika magazi. Tinam’thokoza kwambiri ndiponso kum’tayira kamtengo Dr. Graf chifukwa cholimba mtima komanso kutsimikiza kuti atithandiza.

Mavuto a Zachuma

Tsopano nkhani inagona pakuti, Kodi tidzalipira bwanji chithandizo chamankhwala a Vicky? Tinadzidzimuka kwambiri atatiuza kuti kwa zaka ziŵiri zomwe mwanayo akhale akulandira mankhwala, tiyenera kulipira ndalama za ku Germany pafupifupi 150,000 deutsche marks. Tinalibe m’pang’ono pomwe ndalama zochuluka chonchi ngakhale kuti Vicky anayenera kuyamba kulandira mankhwala nthaŵi yomweyo. Popeza kuti tinachoka ku Sweden kukapeza chithandizo ku Germany, tinalibe mwayi wogwiritsa ntchito inshuwalansi iliyonse ya zaumoyo ya m’dziko lakwathu. Zinthu zinafika pothina kwambiri, mwana wathu wamng’ono wodwalayo ali potero, dokotala woti atithandize wapezeka, koma ndalama zokwanira tilibe.

Achipatala anatikomera mtima ndipo anatiuza kuti mwanayo atha kuyamba kulandira mankhwala ngati titaperekako ndalama zokwana 20,000 marks ndi kusayina pangano loti tidzalipira zotsalazo. Tinalipira ndalamazo pogwiritsa ntchito kangachepe komwe tinasunga komanso chithandizo chomwe mabwenzi ndi achibale anatipatsa. Koma vuto linali lakuti nanga ndalama zotsalazo tidzazitenga kuti?

Kachiŵirinso, tinakumbutsidwa kuti sitinali tokha m’nkhondo yathu yomenyera chikhulupiriro. Mbale wathu wina wauzimu amene panthaŵiyo sitinali kum’dziŵa, anali wofunitsitsa kutilipirira ndalama zonse zotsalazo. Komabe, panalibe chifukwa chogwiritsira ntchito ndalama zomwe mbaleyo anapereka mowolowa manja popeza kuti tinali titapeza njira zina zopezera ndalamazo.

Madokotala Pantchito Yawo

Ntchito yopereka mankhwala inayamba. Masiku ndi milungu ingapo zinadutsa. Nthaŵi zina zinthu zinali zovuta zedi komanso zotangwanitsa kwa ife ndiponso kwa mwanayo. Komabe, tinkasangalala ndiponso kuthokoza nthaŵi zonse pamene akuonetsa kuti akupezako bwino. Iye anatenga miyezi isanu ndi itatu akulandira mankhwalawo. Nthaŵi yomwe magazi a Vicky anachepa kwambiri inali pomwe anafika 6g/​dl, ndipo Dr. Graf anasunga lonjezo lake.

Tsopano patha zaka zopitirira zisanu ndi chimodzi, ndipo kuyeza komaliza madzi a m’fupa la msana wake kukusonyeza kuti matenda a leukemia anatheratu. Iye tsopano ndi mtsikana wosangalala wopanda zizindikiro zilizonse za matenda. Inde, zikuoneka ngati kutulo kuti Vicky anachira kotheratu. Tikudziŵa kuti ana ambiri amene amadwala matendaŵa amamwalira ngakhale atalandira makemikolo komanso kuwaika magazi.

Nkhondo yathu yomenyera chikhulupiriro taipambana chifukwa cha chithandizo cha achibale, abale ndi alongo athu achikristu, komanso madokotala. Dipatimenti Yopereka Chidziŵitso cha Zachipatala inali kutichirikiza kwambiri maola onse 24 patsiku. Dr. Graf ndi anzake anagwiritsa ntchito maluso awo kuthandiza Vicky kuti achire. Chifukwa cha ntchito yaikulu yonseyi, tikuthokoza kuchokera pansi pa mtima.

Chikhulupiriro Chathu Chalimbitsidwa

Komabe, koposa zonse tikuthokoza kwambiri Mulungu wathu Yehova chifukwa chotisamalira mwachikondi komanso nyonga zomwe tinalandira kuchokera m’Mawu ake Baibulo. Tikayang’ana zomwe takumana nazo m’mbuyomu, timazindikira kuti taphunzira zochuluka ndiponso kuti chikhulupiriro chathu chalimbitsidwa kwambiri ndi mavuto omwe takumana nawo m’moyo.

Tsopano cholinga chathu chochokera pansi pa mtima ndicho kupitirizabe unansi wathu wabwino ndi Yehova Mulungu ndiponso kuphunzitsa mwana wathu wamkazi ameneyu ubwino wokhala ndi moyo mogwirizana ndi zomwe Mulungu amafuna. Inde, tikufuna kum’siyira choloŵa chabwino chauzimu cha moyo wosatha m’dziko likudzali la Paradaiso pano padziko lapansi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Dipatimenti Yopereka chidziŵitso cha Zachipatala imayang’anira ntchito ya padziko lonse ya Makomiti Olankhulana ndi Chipatala. Makomiti ameneŵa nawonso amakhala ndi Akristu odzipereka omwe anaphunzitsidwa kulimbikitsa mgwirizano pakati pa madokotala ndi Mboni zodwala. Pali Makomiti Olankhulana ndi Chipatala okwana 1,400 omwe akuthandiza odwala m’mayiko oposa 200.