Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Taonani Wochita Zinthu Zodabwitsa!

Taonani Wochita Zinthu Zodabwitsa!

Taonani Wochita Zinthu Zodabwitsa!

“Taimani, mulingirire zodabwitsa za Mulungu.”​—YOBU 37:14.

1, 2. Kodi n’chozizwitsa chotani chomwe anapeza m’chaka cha 1922, nanga anamva bwanji atachipeza?

KWA zaka zambiri, katswiri wofukula m’mabwinja komanso wochokera m’banja lolemekezeka ku England anagwirizana ndi ena m’ntchito yofufuza chuma. Pamapeto pake, pa November 26, 1922, katswiri wofukula za m’mabwinja Howard Carter limodzi ndi Lord Carnarvon, anapeza mphoto ya kufufuza kwawo. Mphotoyo anaipeza ku manda a afarao ku Igupto m’Chigwa chotchuka cha Mafumu​—anali manda a Farao Tutankhamen. Atafika pakhomo lotseka, anaboola penapake. Carter analoŵetsapo kandulo ndi kusuzumira m’katimo.

2 Patapita nthaŵi Carter anasimba kuti: “Lord Carnarvon atalephera kuugwira mtima, anafunsa kuti, ‘kodi ukuonamo china chilichonse?’ ndinasoŵa chonena, komabe ndinangoti, ‘Inde, zinthu zodabwitsa.’” Chimodzi mwa chuma chochuluka chomwe chinali m’mandamo chinali bokosi la golide. Mwinamwake munaonapo zina mwa “zinthu zodabwitsa” zimenezo m’zithunzi kapena m’malo oonetsera zinthu zamakedzana. Komabe, kaya zinthuzo n’zodabwitsa chotani, koma n’zodziŵikiratu kuti sizikukhudzana ndi moyo wanu. Choncho pano tiyeni tikambe za zinthu zodabwitsa zomwe n’zokhudzana ndi moyo wanu komanso zamtengo wapatali kwa inu.

3. Kodi n’kuti kumene tikupeza nkhani zokhudza zinthu zodabwitsa zimene zingakhale zopindulitsa kwa ife?

3 Mwachitsanzo, lingalirani za munthu wina amene anakhalako zaka mazana ambiri zapitazo, munthu wotchuka kwambiri kuposa wina aliyense wa m’mafilimu, katswiri wa zamaseŵera, kapena aliyense wa m’banja lachifumu. Ankatchedwa wamkulu kuposa anthu onse a Kum’maŵa. Dzina lake mukulidziŵa bwino​—Yobu. Buku lathunthu m’Baibulo likusimba za iyeyu. Komabe, m’modzi wa anzake a Yobu wachinyamata wotchedwa Elihu, anaona kuti kunali kofunika kuti amulangize. M’mawu ake, Elihu anati Yobu anali kudziganizira mopambanitsa komanso kuganizira kwambiri za anthu amene anali kukhala nawo. Pa Yobu chaputala 37, tikupezapo malangizo ena ake achindunji komanso anzeru omwe angakhale aphindu kwabasi kwa aliyense wa ife.​—Yobu 1:1-3; 32:1–33:12.

4. Kodi n’chiyani chomwe chinam’chititsa Elihu kupereka langizo lomwe likupezeka pa Yobu 37:14?

4 Anthu atatu omwe Yobu ankaganiza kuti anali anzake anathera nthaŵi yaitali akulankhula za mbali zimene iwo ankakhulupirira kuti Yobu anachimwa poganiza kapena pochita zinthu. (Yobu 15:1-6, 16; 22:5-10) Elihu anadikira moleza mtima kufikira atamaliza kukambiranako. Atatha, iye analankhula mozindikira komanso mwanzeru. Anatchula mfundo zambiri zogwira mtima, koma tamvani mfundo yofunika iyi: “Tamverani ichi, Yobu, taimani, mulingirire zodabwitsa za Mulungu.”​—Yobu 37:14.

Yemwe Anachita Zodabwitsazo

5. Kodi “zodabwitsa za Mulungu” zimene Elihu ananena zikuphatikizapo chiyani?

5 Onani kuti Elihu sanauze Yobu kuti adzilingalire yekha, alingalire za Elihuyo, kapena kuti alingalire za anthu ena. Mwanzeru Elihu anapempha Yobu​—komanso ifeyo​—kulingalira zodabwitsa za Yehova Mulungu. Kodi mukuganiza kuti mawu akuti “zodabwitsa za Mulungu” akunena zinthu monga chiyani? Komanso, mwina muli nayo kale nkhaŵa yokhudza umoyo wanu, nkhani zachuma, tsogolo lanu, banja lanu, anzanu akuntchito, ndi anansi anu, n’chifukwa chiyaninso mungafunike kulingalira zodabwitsa za Mulungu? Mosakayikira, zodabwitsa za Yehova Mulungu zikuphatikizapo nzeru zake ndi ulamuliro wake pa zolengedwa zonse zotizinga. (Nehemiya 9:6; Salmo 24:1; 104:24; 136:5, 6) Kuti timvetse bwino zimenezi, taonani mfundo imene ili m’buku la Yoswa.

6, 7. (a) Kodi n’zinthu ziti zodabwitsa zimene Yehova anachita m’masiku a Mose ndi Yoswa? (b) Mukanakhala kuti inuyo munaonerera chimodzi mwa zozizwitsa zimenezo m’nthaŵi ya Mose ndi m’nthaŵi ya Yoswa, mukanachita chiyani?

6 Yehova anadzetsa miliri pa Igupto wakale ndipo kenako analekanitsa madzi pa Nyanja Yofiira kuti Mose athe kutsogolera Aisrayeli ku mtendere. (Eksodo 7:1–14:31; Salmo 106:7, 21, 22) Zochitika zofananazo zafotokozedwa pa Yoswa chaputala 3. Yoswa, amene analoŵa m’malo mwa Mose, anayenera kutsogolera anthu a Mulungu kuwoloka mtsinje winanso ndi kukafika nawo m’Dziko Lolonjezedwa. Yoswa anati: “Mudzipatule, pakuti maŵa Yehova adzachita zodabwitsa pakati pa inu.” (Yoswa 3:5) Zodabwitsa zake zotani?

7 Eya, nkhaniyo ikusonyeza kuti Yehova analekanitsanso madzi a Mtsinje wa Yordano, kotero kuti anthu masauzande ambiri, amuna, akazi, ndi ana anadutsa pamchenga pouma. (Yoswa 3:7-17) Ngati panthaŵi imeneyo tikanakhala komweko n’kumaonerera mtsinje ukugaŵika ndiyeno anthu onsewo n’kumadutsa popanda vuto lililonse, tikanachitatu chidwi zedi ndi kuzizwitsa kwa chochitika chimenechi! Chinasonyeza mphamvu zimene Mulungu ali nazo pa chilengedwe. Komanso, pakali pano​—m’nthaŵi yathu ino​—palinso zinthu zina zofanana ndi zimenezo kuzizwitsa kwake. Kuti tione zina mwa zinthu zimenezo komanso chifukwa chake tiyenera kuzilingalira, tiyeni tione Yobu 37:5-7.

8, 9. Kodi Yobu 37:5-7 akutchula zodabwitsa ziti, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuzilingalira?

8 Elihu anati: “Mulungu agunda modabwitsa ndi mawu ake, achita zazikulu osazidziŵa ife.” Kodi Elihu anali kulingalira za chiyani zimene anaona kuti Mulungu amachita zinthu “modabwitsa”? Eya, iye akutchula za chipale chofeŵa ndi kuvumba kwa mvula. Zimenezi zingaimitse mlimi amene akugwira ntchito m’munda wake, kum’patsa mpata ndi chifukwa chabwino cholingalira ntchito zodabwitsa za Mulungu. Mwina ife sindife alimi, koma mvula ndi chipale chofeŵa zingatikhudze tonsefe. Malinga ndi kumene tikukhala, chipale chofeŵa kapena mvula zingatilepheretse ifenso kuchita zinthu zina. Kodi timafatsa n’kumadzifunsa kuti ndani amachita zozizwitsa zoterezi ndikuti zimatanthauzanji? Kodi munachitapo zimenezo?

9 Pamene tikuŵerenga Yobu chaputala 38, Yehova Mulungu mwiniyo alinso ndi malingaliro ofananawo, pamene akufunsa Yobu mafunso atanthauzo. Ngakhale kuti Mlengi wathuyo anafunsa Yobu mafunsoŵa, mwachionekere akukhudza mtima wathu, kukhalapo kwathu, ndi tsogolo lathu. Choncho tiyeni tione mafunso a Mulunguwo, ndi kulingalira mmene tingawagwiritsire ntchito, inde, tiyeni tichite zomwe Yobu 37:14 akutipempha kuchita.

10. Kodi Yobu chaputala 38 chiyenera kutikhudza motani, nanga chikupereka mafunso otani?

10 Chaputala 38 chikuyamba ndi mawu akuti: “Yehova anayankha Yobu m’kavumvulu, nati, ndani uyu adetsa uphungu, ndi mawu opanda nzeru? Udzimangire m’chuuno tsono ngati mwamuna; ndikufunsa, undidziŵitse.” (Yobu 38:1-3) Zimenezi n’zokhudza mtima zedi. Zinam’thandiza Yobu kusintha malingaliro ake podziŵa kuti waima pamaso pa Mlengi wachilengedwe chonse ndi kuti adzafunikira kuyankha mafunso ake. N’zofunikanso kuti ifeyo ndi anzathu tichite zomwezo. Kenako Mulungu anatchulanso zinthu zimene Elihu anali atatchula kale. “Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi? Fotokoza ngati udziŵa kuzindikira. Analemba malire ake ndani, popeza udziŵa? Anayesapo chingwe chake ndani? Maziko ake anakumbidwa pa chiyani? Kapena anaika ndani mwala wake wa pangondya.”​—Yobu 38:4-6.

11. Kodi Yobu 38:4-6 watithandiza kuzindikira chiyani?

11 Kodi Yobu anali kuti​—inde, aliyense wa ife anali kuti​—pamene amakhazikitsa dziko? Kodi ife ndife amisiri amene tinalinganiza pulani ya dziko lathuli ndiyeno, kuchokera pa pulani imeneyo, n’kuyeza bwinobwino ngati kuti tagwiritsa ntchito lula? Ndithudi ayi! Panthaŵiyo n’kuti anthu kulibe nkomwe. Poyerekezera dziko lathuli ndi nyumba, Mulungu anafunsa kuti: “Anaika ndani mwala wake wa pangondya?” Tikudziŵa kuti dziko lili pamtunda woyenera kuchokera pa dzuŵa kuti tikhale ndi moyo ndi kusangalala nawo. Ndipo kukula kwake n’nkoyenereranso. Ngati dziko likanakhala lalikulu kwambiri, mpweya wa hydrogen sukanatha kumachoka m’mlengalengamu ndipo dzikoli likanakhala lopanda chamoyo chilichonse. Mwachionekere, winawake ‘anaika mwala wake wa pangondya’ pamalo oyenerera. Kodi ndani ayenera kutamandidwa? Kodi ndi Yobu? Ifeyo? Kapena Yehova Mulungu?​—Miyambo 3:19; Yeremiya 10:12.

Munthu Wake Ndani Angapereke Mayankho?

12. Kodi funso la pa Yobu 38:6 likutichititsa kuganiza za chiyani?

12 Mulungu anafunsanso kuti: “Maziko ake anakumbidwa pa chiyani?” Kodi limenelo si funso loŵiritsa mutu? Ife tikudziŵa bwino mawu aŵa amene Yobu sankaŵadziŵa​—mphamvu yokoka. Ambirife tikudziŵa kuti mphamvu yokoka yochokera ku mphamvu zochuluka za dzuŵa imathandiza kuti dziko lathuli lisachoke m’malo ake, maziko ake anakumbidwa, kunena kwake titero. Komabe, ndani amamvetsetsa za mphamvu yokoka imeneyi?

13, 14. (a) Kodi tiyenera kuvomereza chiyani za mphamvu yokoka? (b) Kodi zomwe Yobu 38:6 akufotokoza tiyenera kuziona motani?

13 Buku limene langofalitsidwa posachedwapa lakuti The Universe Explained limavomereza kuti ‘mphamvu yokoka n’njodziŵika bwino kwambiri, komanso ndi yovuta kuimvetsa, mwa mphamvu zonse m’chilengedwe.’ Powonjezera limati: “Mphamvu yokoka ikuoneka kuti imadutsa mosadziŵika bwino komanso mofulumira kwambiri m’mlengalenga mopanda kanthu. Komabe, m’zaka zaposachedwapa, akatswiri asayansi ayamba kuganizira kuti mwina mphamvu yokoka imadutsa m’mafunde opangidwa ndi tinthu tating’onoting’ono totchedwa ma graviton . . . Komabe palibe amene akutsimikiza kuti tinthu timeneti tilikodi.” Talingalirani tanthauzo la zimenezo.

14 Sayansi yapita patsogolo kwambiri m’zaka 3,000 kuchokera pamene Yehova anafunsa Yobu mafunso amenewo. Komabe, ifeyo kapena akatswiri a sayansi sangafotokoze mokwanira za mphamvu yokoka, imene imathandiza kuti dziko lathuli lipitirizebe kuyenda m’kanjira kake koyenera, komanso pamalo oyenera kuti tithe kusangalala ndi moyo. (Yobu 26:7; Yesaya 45:18) Zimenezi sizikutanthauza kuti tonsefe tikufunikira kuphunzira mozama kuti tidziŵe zinsinsi zakuya za mphamvu yokoka ayi. Koma kuti kulingalira mozama ngakhale mbali imodzi yokhayi ya zodabwitsa za Mulungu kuyenera kusonkhezera mmene timamuonera. Kodi m’mazizwa ndi nzeru komanso chidziŵitso chake, nanga kodi mumayesa kulingalira chifukwa chake tifunikira kuphunzira zochuluka zokhudza chifuno chake?

15-17. (a) Kodi lemba la Yobu 38:8-11 likugogomeza za chiyani, nanga likubutsa mafunso otani? (b) Kodi tiyenera kuvomereza chiyani pankhani ya kudziŵa za nyanja zamchere ndi mmene zinakhalira mosiyana ndi zolengedwa zina padziko lapansi?

15 Mlengiyo anapitirizabe kufunsa kuti: “Anatseka nyanja ndani ndi zitseko, muja idakamula ngati kutuluka m’mimba, muja ndinayesa mtambo chovala chake, ndi mdima wa bii nsalu yake yokulunga, ndi kuilembera malire anga, ndi kuika mipikizo ndi zitseko, ndi kuti, ufike mpaka apa, osapitirirapo; apa adzaletseka mafunde ako odzikuza?”​—Yobu 38:8-11.

16 Kutseka nyanja kukukhudza nthaka, nyanja zamchere, ndi mafunde. Kodi munthu waona ndi kuphunzira zinthu zimenezi kwautali wotani? Kwa zaka masauzande ambiri​—ndipo achita izi moŵirikiza kwambiri m’zaka 100 zapitazi. Mwinamwake mungaganize kuti zochuluka zofunikira kuzidziŵa pa zinthu zimenezi zadziŵika kale. Komabe, m’chaka chino cha 2001, ngati mukanachita kafukufuku wa zinthu zimenezi m’malaibulale akuluakulu kapena kugwiritsa ntchito njira yamphamvu yofufuzira ya Intaneti kuti mupeze mfundo zina zaposachedwapa, kodi mukanapeza chiyani?

17 M’buku lina lamaumboni lodalirika kwa anthu ambiri, mungapezemo mfundo yakuti: “Kugaŵikana kwa mtunda ndi nyanja zamchere m’dzikoli komanso mmene zinthu zikuluzikulu zachilengedwe padziko lapansi zinakhalira mosiyanasiyana kwakhala chimodzi mwa zinthu zochititsa chidwi zomwe kwa zaka zambiri asayansi ayesa kufufuza ndi kuzifotokoza.” Itatha kufotokoza zimenezi, insaikulopediya yomwe tatengamo mawu ameneŵa inapereka mfundo zinayi zokhutiritsa komabe inati zimenezi ndi “zina mwa mfundo zambiri zongoganizira chabe.” Monga mukudziŵa, kungoganizira “kumatanthauza kuti palibe umboni wokwanira, chotero zimene munthu angafotokoze sizikhala zotsimikizika.”

18. Kodi Yobu 38:8-11 wakupangitsani kutsimikiza kuti chiyani?

18 Kodi zimenezo sizikutsimikiza kuti funso la pa Yobu 38:8-11 n’lapanthaŵi yake? Ndithudi si ife amene tingatamandidwe chifukwa cha kulinganiza zinthu zosiyanasiyana m’pulaneti lathu lino. Ife sitinakhazike mwezi pamalo oyenera kuti mphamvu yake yokoka izithandiza kuchepetsa mphamvu za mafunde kuti asamasefukire m’magombe kapena kumene ife timakhala. Inu mukum’dziŵa amene anachita zimenezo, ndiye Wochita zodabwitsa.​—Salmo 33:7; 89:9; Miyambo 8:29; Machitidwe 4:24; Chivumbulutso 14:7.

N’koyenera Kutamanda Yehova

19. Kodi mawu onga am’ndakatulo a pa Yobu 38:12-14 akutithandiza kulingalira zochitika zotani za chilengedwe?

19 Anthu sangatamandidwe chifukwa cha kuzungulira kwa dziko. Malinga n’kunena kwa Yobu 38:12-14, kuzungulira kumeneku ndiko kumachititsa kuti kukhale mbandakucha umene kaŵirikaŵiri umakhala wokongola kwabasi. Pamene dzuŵa likutuluka, zinthu zosiyanasiyana m’dzikoli zimaoneka bwino zedi, monga momwe chizindikiro cha m’chikombole chimaonekera pa njerwa. Ngati titapenda pang’ono chabe liŵiro la dziko, tingadabwe kuona kuti dziko silizungulira mofulumira kwambiri, zimene mwachionekere zingakhale zoopsa kwambiri. Komanso silizungulira pang’onopang’ono kwambiri mwakuti usana ndi usiku uzitalika kwambiri. Zikadatero ndiye kuti sikukanatheka kuti anthu akhale ndi moyo padziko lapansi chifukwa bwenzi kuli usana wotentha ndi usiku wozizira mopambanitsa. Kunena zoona, tiyenera kusangalala kuti Mulungu, osati gulu lililonse la anthu, ndi amene anakonza kuti dzikoli lizizungulira pa liŵiro loyenera.​—Salmo 148:1-5.

20. Kodi mafunso a pa Yobu 38:16, 18 mungawayankhe motani?

20 Tsopano, yerekezani kuti Mulungu akukufunsani mafunso ena aŵa: “Kodi unaloŵa magwero a nyanja? Kodi unayendayenda pozama penipeni?” Ngakhale katswiri wa za m’nyanja sangayankhe mokwanira! “Kodi unazindikira chitando cha dziko lapansi? Fotokozera, ngati uchidziŵa chonse.” (Yobu 38:16, 18) Kodi munayamba mwafika m’zigawo zonse zadziko lapansi, kapena zochuluka mwa zigawo zimenezi? Kodi kulingalira za malo okongola otereŵa ndi zozizwitsa za m’dziko lathu lino kungatitengere nthaŵi yaitali motani m’moyo wathu? Ndipotu imeneyo ingakhale nthaŵi yosangalatsa zedi!

21. (a) Kodi funso la pa Yobu 38:19 likubweretsa malingaliro ati a sayansi? (b) Kodi zochitika zokhuza kuŵala ziyenera kutisonkhezera kuchitanji?

21 Onaninso mafunso ena ofunika kwambiri pa Yobu 38:19: “Ili kuti njira yomukira pokhala kuunika? Ndi mdima, pokhala pake pali kuti?” Mwina mukudziŵa kuti kwa nthaŵi yaitali, anthu ankalingalira kuti kuŵala kumayenda ngati mafunde, mizera imene tingaione pamwamba pa madzi. Kenako m’chaka cha 1905, Albert Einstein anafotokoza kuti kuŵala kumachita ngati kaphukusi kapena kagulu ka tinthu ting’onoting’ono tamphamvu. Kodi anthu amakhutira ndi zimenezi? Insaikulopediya yaposachedwapa inafunsa kuti: “Kodi kuŵala kuli ngati mizera ya mafunde kapena ndi tinthu ting’onoting’ono?” Poyankha inati: “Zikuoneka kuti [kuŵala] sikungakhale zonse ziŵirizo chifukwa chakuti zonsezi [mizera yangati mafunde komanso tinthu ting’onoting’ono] n’zosiyana kwambiri. Yankho lolondola ndi lakuti kuŵala sikuli chilichonse mwa ziŵirizo.” Komabe, [mwachindunji kapena m’njira zina] timamva kufunda chifukwa cha kuŵala kwa dzuŵa, ngakhale kuti anthu sakutha kufotokoza momveka ntchito zodabwitsa za Mulungu pambali imeneyi. Timasangalala ndi chakudya komanso mpweya wa oxygen zimene zimapangidwa ndi mbewu mothandizidwa ndi kuŵala kwa dzuŵa. Timatha kuŵerenga, kuona nkhope za okondedwa athu, kuonerera dzuŵa likamaloŵa, ndi zina zambiri. Tikamachita zimenezo, kodi sitiyamikira ntchito zodabwitsa za Mulungu?​—Salmo 104:1, 2; 145:5; Yesaya 45:7; Yeremiya 31:35.

22. Kodi Davide wakaleyo anatani poona ntchito zodabwitsa za Mulungu?

22 Kodi cholinga cha kulingalira ntchito zodabwitsa za Yehova n’chakuti tingochita nazo chidwi, kuopsedwa nazo kapena kusoŵa nazo chonena? Ayi sichoncho. Wamasalmo Davide anavomereza kuti n’zosatheka kumvetsa ndi kuthirira ndemanga pa ntchito zodabwitsa zonse za Mulungu. Davide analemba kuti: “Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita n’zambiri . . . Ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziŵerenga.” (Salmo 40:5) Komabe, iye kwenikweni sanatanthauze kuti adzangokhala chete osanena za ntchito zodabwitsa zimenezi. Davide anasonyeza zimenezi mwa mawu ake otsimikiza a pa Salmo 9:1 akuti: “Ndidzayamika Yehova ndi mtima wanga wonse; ndidzaŵerengera zodabwitsa zanu zonse.”

23. Kodi mumachitanji mukaona ntchito zodabwitsa za Mulungu, nanga ena mungawathandize motani?

23 Kodi sikoyenera kuti nafenso tisonkhezereke mofananamo? Kodi kudabwitsa kwa ntchito zazikulu za Mulungu sikuyenera kutisonkhezera kunena za iye, za zimene wachita, ndi zomwe adzachite m’tsogolo? Yankho lake n’lodziŵikiratu​—tiyenera ‘kufotokozera ulemerero wake mwa amitundu; zodabwitsa zake mwa mitundu yonse ya anthu.’ (Salmo 96:3-5) Inde, tingasonyeze kuyamikira kwathu ntchito zodabwitsa za Mulungu modzichepetsa mwa kuuza ena zomwe taphunzira ponena za iye. Ena anakulira m’mafuko amene sakhulupirira kuti kuli Mlengi. Komabe, titawafotokozera momveka komanso mogwira mtima zingawathandize kumudziŵa Mulungu. Kuwonjezera pamenepo, zingawasonkhezere kufuna kuphunzira ndi kutumikira yemwe ‘analenga zonse,’ Wochita ntchito zodabwitsa, Yehova.​—Chivumbulutso 4:11.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi langizo la pa Yobu 37:14 lakuthandizani kulingalira za ntchito ziti za Mulungu?

• Kodi ndi zinthu zina ziti zimene Yobu chaputala 37 ndi 38 akufotokoza zimene sayansi singafotokoze mokwanira?

• Kodi mumamva bwanji mukalingalira ntchito zodabwitsa za Mulungu, nanga zimakusonkhezerani kuchitanji?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 7]

Ndani anatseka nyanja, kuikhazika m’malo ake?

[Chithunzi patsamba 7]

Ndani amene anapita kukaona malo onse okongola padziko lapansi, omwe Mulungu analenga?