Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tiyenera Kukhulupirira Mizimu Pofuna Zinthu Zauzimu Zenizeni?

Kodi Tiyenera Kukhulupirira Mizimu Pofuna Zinthu Zauzimu Zenizeni?

Kodi Tiyenera Kukhulupirira Mizimu Pofuna Zinthu Zauzimu Zenizeni?

TONSEFE timafuna zinthu zauzimu komanso zofunika pa moyo wathu. N’chifukwa chake ambiri amafunsa kuti, Kodi cholinga cha moyo n’chiyani? Ndipo n’chifukwa chiyani timavutika? Nanga tikamwalira chimatichitikira n’chiyani? Anthu oona mtima ambiri amafunafuna mayankho a mafunso ameneŵa ndi enanso ofanana nawo pamisonkhano yomwe amafunsira kwa oombeza, pofuna kulankhula ndi mizimu ya akufa. Kumeneku ndiko kukhulupirira mizimu.

Anthu okhulupirira mizimu amapezeka m’mayiko ambiri ndipo amasonkhana m’mipingo ndi m’matchalitchi. Mwachitsanzo, ku Brazil, amizimu pafupifupi 4,000,000 amatsatira ziphunzitso zomwe analemba Hyppolyte Léon Denizard Rivail, mphunzitsi wachifalansa ndi wafilosofi wa m’zaka za m’ma 1800. Iye analemba ziphunzitsozo m’dzina lakuti Allan Kardec. Kardec anayamba kuchita chidwi ndi zamizimu mu 1854. Kenako anafunsa oombeza m’malo ambiri ndipo analemba mayankho awo m’buku lotchedwa The Book of Spirits (Buku la Mizimu) lomwe linafalitsidwa mu 1857. Iye analembanso mabuku ena aŵiri akuti The Mediums’ Book (Buku la Oombeza) ndi The Gospel According to Spiritism (Uthenga Wabwino wa Okhulupirira Mizimu).

Kukhulupirira mizimu n’kogwirizana kwambiri ndi miyambo yachipembedzo monga vudu, ufiti, matsenga, kapena kulambira Satana. Koma anthu amene amakhulupirira ziphunzitso za Allan Kardec amanena kuti zikhulupiriro zawo n’zosiyana ndi zimenezi. Mabuku awo nthaŵi zambiri amagwira mawu m’Baibulo ndipo amati Yesu ndiye “mtsogoleri komanso chitsanzo cha anthu onse.” Iwo amanena kuti zomwe Yesu anaphunzitsa ndizo “chilamulo choyeretsetsa cha Mulungu.” Allan Kardec ankaona mabuku a zamizimu monga vumbulutso lachitatu la chilamulo cha Mulungu kwa anthu. Loyamba ndi lachiŵiri linali zomwe Mose ndi Yesu anaphunzitsa.

Kukhulupirira mizimu kumakopa anthu ambiri chifukwa chakuti kumagogomeza mfundo ya kukonda anansi ndiponso kuchita ntchito zachifundo. Zina zimene amizimu amakhulupirira n’zakuti: “Popanda ntchito zachifundo munthu sangapulumuke.” Amizimu ambiri akujijirika pantchito yothandiza anthu, kumanga zipatala, sukulu, ndi kuchirikiza mabungwe ena. Zimene akuchitazo n’zabwino ndithu. Koma kodi zomwe amakhulupirira zikugwirizana motani ndi zomwe Yesu anaphunzitsa monga zalembedwera m’Baibulo? Tiyeni tione mbali ziŵiri izi: chiyembekezo cha anthu akufa ndiponso chifukwa chomwe anthu akuvutikira.

Kodi Akufa Ali ndi Chiyembekezo Chotani?

Amizimu ambiri amakhulupirira kuti munthu amabadwanso akamwalira. Buku lawo lina limanena kuti: “N’chiphunzitso chokhachi cha kubadwanso kwa munthu akamwalira chomwe chimagwirizana ndi zomwe timadziŵa pa zachilungamo cha Mulungu, n’chiphunzitso chokhachi chomwe chingalongosole za m’tsogolo ndi kulimbitsa chiyembekezo chathu.” Iwo amanena kuti munthu akamwalira, mzimu wake, kapena kuti “mzukwa,” umatuluka m’thupi lake monga amachitira gulugufe kutuluka m’kathumba komwe amabadwiramo. Amakhulupirira kuti mizimu imeneyi imabadwanso monga anthu n’cholinga chotaya machimo amene munthuyo anawachita m’moyo wake woyamba. Ndipo sakumbukira machimo akalewo. “Mulungu anaona kuti n’kwabwino kuiŵala machimo amene munthu anawachita m’moyo woyamba,” limatero buku lakuti The Gospel According to Spiritism.

Allan Kardec analemba kuti: “Ngati wina atakana kuti munthu sabadwanso akamwalira ndiye kuti akukana mawu a Kristu.” Koma Yesu sanatchulepo mawu akuti “munthu akamwalira amabadwanso,” ndipo sanatchulepo n’komwe chiphunzitso choterocho. (Onani mutu wakuti “Kodi Baibulo Limaphunzitsa za Kubadwanso Munthu Akamwalira?” patsamba 22.) M’malo mwake, Yesu anaphunzitsa za kuuka kwa akufa. Pautumiki wake wa padziko lapansi, anaukitsa anthu atatu​—mwana wamwanuna wa mkazi wamasiye wa ku Naini, mwana wamkazi wa mkulu wa sunagoge, ndiponso bwenzi lake lapamtima Lazaro. (Marko 5:22-24, 35-43; Luka 7:11-15; Yohane 11:1-44) Tiyeni tipende chimodzi mwa zochitika zochititsa chidwi zimenezo kuti tione zomwe Yesu anatanthauza pa mawu akuti “kuuka.”

Kuuka kwa Lazaro

Yesu anamva kuti bwenzi lake Lazaro akudwala. Patapita masiku aŵiri, anauza ophunzira ake kuti: “Lazaro bwenzi lathu ali m’tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take.” Ophunzira akewo sanamvetse zomwe Yesu anatanthauza, choncho iye anawauza mosapita m’mbali kuti: “Lazaro wamwalira.” Pomwe Yesu amafika kumanda a Lazaro n’kuti iye ali wakufa masiku anayi. Komabe, Yesu analamula kuti mwala womwe anatsekera mandawo auchotse. Kenako anafuula kuti: “Lazaro tuluka!” Atatero, panachitika zodabwitsa. “Womwalirayo anatuluka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za kumanda; ndi nkhope yake inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nawo, M’masuleni iye, ndipo m’lekeni amuke.”​—Yohane 11:5, 6, 11-14, 43, 44.

Mwachionekere, kumeneko sikunali kubadwanso. Yesu ananena kuti Lazaro womwalirayo anali mtulo, wosadziŵa kanthu. Monga momwe Baibulo limanenera, ‘zotsimikiza mtima zake zinatayika.’ ‘Sanadziŵe kanthu bi.’ (Salmo 146:4; Mlaliki 9:5) Lazaro anaukayo sanali munthu wina wokhala ndi mzimu wobadwanso. Anali munthu wakale yemweyo, wazaka zakubadwa zomwezo ndiponso chikumbumtima chake chomwecho. Anayambiranso moyo wake pomwe anaulekeza ndipo anabwerera kwa okondedwa omwe analira maliro ake.​—Yohane 12:1, 2.

Kenako, Lazaro anamwaliranso. Ndiye kodi cholinga cha kuuka kwake chinali chiyani? Kuuka kwake komanso kwa anthu ena omwe Yesu anawaukitsa kumalimbikitsa chikhulupiriro chathu m’malonjezo a Mulungu akuti atumiki Ake okhulupirika adzauka panthaŵi Yake yoikika. Zozizwitsa zomwe Yesu anachitazo zimasonyezadi mphamvu ya mawu ake akuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo.”​—Yohane 11:25.

Pankhani ya kuuka kwa m’tsogolo, Yesu anati: “Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu [anga], nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza.” (Yohane 5:28, 29) Monga zinalili kwa Lazaro, kumeneko kudzakhala kuuka kwa anthu akufa. Sikudzakhala kugwirizananso kwa mizimu yamoyo ndi matupi oukitsidwa amene anaola ndipo mwinanso kukhala mbali ya zinthu zina zamoyo. Mphamvu ya kuukitsa akufa ili m’manja mwa Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi, amene ali ndi nzeru ndi mphamvu zosatha.

Kodi simukuvomereza kuti chiphunzitso cha chiukiriro chomwe Yesu Kristu anaphunzitsa chimavumbula chikondi chachikulu cha Mulungu kwa munthu aliyense? Koma bwanji nanga za funso lachiŵiri lomwe tafunsa poyamba lija?

N’chifukwa Chiyani Anthu Akuvutika?

Mavuto ambiri a anthu amabwera chifukwa cha zinthu zomwe anthu opanda nzeru, osadziŵa zambiri, ndiponso oipa amachita. Koma bwanji nanga za masoka amene sitinganene mwachindunji kuti akuwachititsa ndi anthu? Mwachitsanzo, n’chifukwa chiyani pali ngozi ndi masoka achilengedwe? N’chifukwa chiyani ana ena amabadwa ali olumala? Allan Kardec ankaona zinthu ngati zimenezi monga chilango. Iye analemba kuti: “Ngati tikulangidwa ndiye kuti tinalakwa chinachake. Ndipo ngati cholakwacho sitinachichite pa moyo uno ndiye kuti tinachichita pa moyo wam’mbuyomo.” Okhulupirira mizimu amawaphunzitsa kupemphera kuti: “Ambuye, Inu ndinu wachilungamo chonse. Matenda amene mwasankha kunditumizira ayenera kuti ali ondiyenera . . . Ndawalandira monga chitetezo cha machimo anga a m’mbuyomu ndiponso monga umboni wa chikhulupiriro changa ndi kumvera kwanga chifuniro Chanu chodalitsika.”​—The Gospel According to Spiritism.

Kodi Yesu anaphunzitsa zinthu zoterezi? Ayi. Yesu ankadziŵa bwino kwambiri mawu a m’Baibulo akuti: “Yense angoona zom’gwera m’nthaŵi mwake.” (Mlaliki 9:11) Anadziŵa kuti nthaŵi zina zinthu zoipa zimangochitika. Zinthu zoipa zimenezo si chilango cha machimo.

Talingalirani izi zimene zinachitika pa moyo wa Yesu: “Popita, [Yesu] anaona munthu ali wosaona chibadwire. Ndipo akuphunzira ake anam’funsa Iye, nanena, Rabi, anachimwa ndani, ameneyo, kapena atate wake ndi amake, kuti anabadwa wosaona?” Yankho limene Yesu anapereka linali lomveka kwambiri. Iye anayankha kuti: “Sanachimwa ameneyo, kapena atate wake ndi amake; koma kuti ntchito za Mulungu zikaonetsedwe mwa iye. Pamene ananena izi, analavula pansi, nakanda thope ndi malovuwo, napaka thopelo m’maso, nati kwa iye, Muka, kasambe m’thamanda la Siloamu . . . Pamenepo anachoka, nasamba, nabwera alikuona.”​—Yohane 9:1-3, 6, 7.

Mawu a Yesu anasonyeza kuti si munthuyo kapena makolo ake amene anachititsa kuti iyeyo abadwe wosaona. Chotero Yesu sanachirikize mfundo yoti munthuyo anali kulangidwa chifukwa cha machimo amene anachita pa moyo wake wam’mbuyo. N’zoona kuti Yesu anadziŵa kuti anthu onse amalandira choloŵa cha uchimo. Koma iwo analandira uchimo wa Adamu osati kuti anachita machimowo asanabadwe. Chifukwa cha uchimo wa Adamu, anthu onse amabadwa opanda ungwiro, ndipo atha kudwala ndi kufa. (Yobu 14:4; Salmo 51:5; Aroma 5:12; 9:11) Ndipotu Yesu anam’tumiza kudzawombola anthu ku vuto limeneli. Yohane Mbatizi ananena kuti, Yesu anali “Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!”​—Yohane 1:29. *

Komanso onani kuti Yesu sananene kuti Mulungu anachitira dala kuti munthuyo abadwe wosaona n’cholinga choti Yesu adzabwera nthaŵi ina kudzam’chiritsa. Zimenezo zikanakhalatu nkhanza zadzaoneni! Kodi zoterozo zikanachititsa anthu kum’tamanda Mulungu? Kutalitali. Mosiyana ndi zimenezo, kuchira kozizwitsa kwa munthu wosaonayo ‘kunaonetsa ntchito za Mulungu.’ Mofanana ndi kuchiritsa anthu ena kumene Yesu anachita, kunasonyeza chikondi chenicheni chomwe Mulungu ali nacho kwa anthu ovutika ndiponso kudalirika kwa lonjezo Lake lodzathetseratu matenda ndi kuvutika konse panthaŵi Yake yoikika.​—Yesaya 33:24.

Kodi si zosangalatsa kudziŵa kuti m’malo mochititsa mavuto, Atate wathu wakumwamba amapereka “zinthu zabwino kwa iwo akum’pempha iye”? (Mateyu 7:11) Kudzakhalatu kutamanda Wam’mwambamwamba pamene maso a akhungu ndi makutu a ogontha adzatsegulidwe, ndiponso olumala adzayende, kudumpha, ndi kuthamanga!​—Yesaya 35:5, 6.

Kukwaniritsa Zofuna Zathu Zauzimu

Yesu ananena kuti: “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.” (Mateyu 4:4) Inde, timakwaniritsa zofuna zathu zauzimu pamene tiŵerenga Mawu a Mulungu, Baibulo, ndi kukhala ndi moyo mogwirizana ndi mawuwo. Kufunsira kwa oombeza sikukwaniritsa zofuna zathu zauzimu. Ndithudi, malemba omwe Allan Kardec anawatcha kuti vumbulutso loyamba la chilamulo cha Mulungu amaletseratu zimenezi.​—Deuteronomo 18:10-13.

Anthu ambiri kuphatikizapo amizimu amazindikira kuti Mulungu ndiye Wamphamvuyonse, wamuyaya, wangwiro, wachifundo, wabwino, ndiponso wachilungamo. Koma Baibulo limavumbulanso zina zambiri. Limanena kuti iye ali ndi dzina lake lenileni loti Yehova, limene tiyenera kulilemekeza monga anachitira Yesu. (Mateyu 6:9; Yohane 17:6) Limasonyezanso kuti Mulungu ndi munthu weniweni amene anthu atha kukhala naye paubwenzi. (Aroma 8:38, 39) Tikamaŵerenga Baibulo, timaphunzira kuti Mulungu ndi wachifundo ndiponso kuti ‘satichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu.’ (Salmo 103:10) Mwa Mawu ake olembedwa, Ambuye Mfumu Yehova amavumbula chikondi chake, ukulu wake, ndiponso kulolera kwake. Iye Ndiye amatsogolera ndi kuteteza anthu omvera. Kudziŵa Yehova ndi Mwana wake Yesu Kristu ndiko kudzatipezetsa “moyo wosatha.”​—Yohane 17:3.

Baibulo limatiuza zonse zomwe tingafune zokhudza zolinga za Mulungu ndiponso zomwe tiyenera kuchita ngati tikufuna kum’kondweretsa. Kuphunzira Baibulo mosamalitsa kumapereka mayankho oona ndiponso okhutiritsa a mafunso athu. Baibulo limatiuzanso zimene zili zabwino ndi zoipa ndipo limatipatsa chiyembekezo chodalirika. Limatitsimikizira kuti patsogolopa, Mulungu “adzawapukutira [anthu] misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo [zidzakhala] zitapita.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Yehova adzagwiritsa ntchito Yesu Kristu kumasula anthu ku choloŵa cha uchimo ndi kupanda ungwiro, ndipo anthu omvera adzalandira moyo wosatha m’dziko lapansi la paradaiso. Nthaŵiyo, zofuna zawo zakuthupi ndi zauzimu zidzakwaniritsidwa kotheratu.​—Salmo 37:10, 11, 29; Miyambo 2:21, 22; Mateyu 5:5.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 19 Kuti mudziŵe mmene uchimo ndi imfa zinayambira, onani mutu 6 m’buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi patsamba 22]

KODI BAIBULO LIMAPHUNZITSA ZA KUBADWANSO MUNTHU AKAMWALIRA?

Kodi pali malemba alionse m’Baibulo ochirikiza chiphunzitso cha kubadwanso munthu akamwalira? Talingalirani malemba ena omwe anthu okhulupirira zimenezi agwiritsa ntchito:

“Pakuti aneneri onse ndi chilamulo chinanenera kufikira pa Yohane . . . Uyu ndiye Eliya amene amati akudza.”​—Mateyu 11:13, 14.

Kodi Yohane Mbatizi anali Eliya wobadwanso? Atam’funsa kuti: “Ndiwe Eliya kodi?” Yohane anayankha momveka bwino kuti: “Sindine iye.” (Yohane 1:21) Komabe, ulosi unali utaneneratu kuti Yohane adzatsogolera Mesiya “ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya.” (Luka 1:17; Malaki 4:5, 6) Kunena kwina, Yohane Mbatizi anali Eliya m’lingaliro lakuti anachita ntchito yofanana ndi ya Eliya.

“Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu. Usadabwe chifukwa ndinati kwa iwe, Uyenera kubadwa mwatsopano.”​—Yohane 3:3, 7.

Pambuyo pake, mmodzi wa atumwi analemba kuti: “Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso [“tinabadwanso,” Revised Standard Version] ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Kristu.” (1 Petro 1:3, 4; Yohane 1:12, 13) Mwachionekere, kubadwanso kumene Yesu ananena, kunali kwauzimu ndipo kukachitika pamene otsatira ake anali amoyo osati kubadwanso m’tsogolo atamwalira ayi.

“Munthu akafa, amakhala ndi moyo kosatha: masiku a moyo wanga pa Dziko Lapansi akatha, ndidzayembekeza, podziŵa kuti ndidzabweranso.”​—Mmene “Baibulo lachigiriki” logwidwa mawu m’buku la The Gospel According to Spiritism limamasulira Yobu 14:14.

Pa vesi limeneli, Baibulo la Revised Standard Version limati: “Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi? Ndidzayembekeza masiku onse a ntchito yanga, kufikira n’tamasulidwa.” Mutapenda nkhani yonse ya vesili, mudzaona kuti akufa amayembekezera ‘kumasulidwa’ kwawo ali kumanda. (Vesi 13) Iwo amayembekezera ali akufa. “Munthu amene wamwalira watha basi; ndipo munthu akafa, sakhalakonso.”​—Yobu 14:10, Baibulo la Bagster lotchedwa Septuagint.

[Chithunzi patsamba 21]

Chiyembekezo cha chiukiriro chimavumbula chikondi chachikulu chomwe Mulungu ali nacho kwa munthu aliyense

[Zithunzi patsamba 23]

Mulungu adzathetsa mavuto onse a anthu