Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kondwerani Nthaŵi Zonse Potumikira Yehova

Kondwerani Nthaŵi Zonse Potumikira Yehova

Kondwerani Nthaŵi Zonse Potumikira Yehova

“Kondwerani mwa Ambuye nthaŵi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.”​—AFILIPI 4:4.

1, 2. Kodi mbale wina ndi banja lake anatha bwanji kukhalabe achimwemwe katundu wawo yense amene anali naye atawonongeka?

JAMES, Mkristu wa zaka 70 wa ku Sierra Leone, anagwira ntchito mwakhama moyo wake wonse. Tangoganizani chimwemwe chimene anali nacho atakwanitsa kusunga ndalama zokwanira kugula nyumba yooneka bwino yazipinda zinayi! Koma patapita nthaŵi James ndi banja lake atasamukira m’nyumba imeneyo, m’dzikomo munabuka nkhondo yapachiŵeniŵeni, ndipo nyumba yawoyo inawonongedwa. Nyumba inathera pomwepo, koma chimwemwe chawo sichinathe. Chifukwa chiyani?

2 James ndi banja lake sanaike mtima kwambiri pa zowonongekazo koma analingalira kwambiri zotsala. James anafotokoza kuti: “Ngakhale m’nthaŵi yoopsayo, tinkachitabe misonkhano, kuŵerenga Baibulo, kupemphera limodzi, ndi kugaŵira ena zochepa zomwe tinali nazo. Tinakhalabe achimwemwe chifukwa chakuti tinalingalira za ubwenzi wamtengo wapatali umene tili nawo ndi Yehova.” Akristu okhulupirika ameneŵa anapitirizabe ‘kukondwera’ chifukwa chakuti analingalira zinthu zabwino zomwe anali nazo. Chachikulu mwa zinthu zimenezi ndicho kukhala bwenzi lenileni la Yehova. (2 Akorinto 13:11) Komatu kupirira zochitika zodetsa nkhaŵa zimenezo sikunali kwapafupi. Komabe sanaleke kukondwera mwa Yehova.

3. Kodi Akristu ena oyambirira anatha bwanji kukhalabe achimwemwe?

3 Akristu oyambirira anakumana ndi mayesero ofanana ndi amene anagwera James ndi banja lake. N’chifukwa chake mtumwi Paulo analembera Akristu a Chihebri mawu aŵa: “[Inu] mudalola mokondwera kulandidwa kwa chuma chanu.” Kenako Paulo anafotokoza gwero la kukondwera kwawoko kuti: “Pozindikira kuti muli nacho nokha chuma choposa chachikhalire.” (Ahebri 10:34) Inde, Akristu a m’zaka za zana loyamba amenewo anali ndi chiyembekezo champhamvu. Anayembekezera ndi mtima wonse kulandira chinthu chomwe wina aliyense sangawalande​—“korona wa moyo” mu Ufumu wakumwamba wa Mulungu. (Chivumbulutso 2:10) Lerolino, chiyembekezo chathu chachikristu​—kaya ndi chakumwamba kapena cha pansi pompano​—chingatithandize kukhalabe achimwemwe ngakhale titakumana ndi masoka.

“Kondwerani M’chiyembekezo”

4, 5. (a) N’chifukwa chiyani malangizo a Paulo akuti “kondwerani m’chiyembekezo” anali apanthaŵi yake kwa Aroma? (b) Kodi n’chiyani chomwe chingapangitse kuti Mkristu asaone kufunika kwa chiyembekezo chake?

4 Mtumwi Paulo analimbikitsa okhulupirira anzake ku Roma kuti ‘akondwere m’chiyembekezo’ cha moyo wosatha. (Aroma 12:12) Amenewo anali malangizo apanthaŵi yake kwa Aromawo. Zaka khumi zisanathe Paulo atangowalembera mawuwa, anazunzidwa mwankhanza, ndipo ena anawazunza mpaka kuwapha mwalamulo la Mfumu Nero. Chikhulupiriro chawo chakuti Mulungu adzawapatsa korona wamoyo yemwe anawalonjeza, mosakayika chinawalimbitsa m’masautso awo. Nanga bwanji ifeyo lerolino?

5 Monga Akristu, nafenso timayembekezera mazunzo. (2 Timoteo 3:12) Komanso tikudziŵa kuti nthaŵi ndi zochitika mwadzidzidzi zimagwera aliyense wa ife. (Mlaliki 9:11) Winawake amene timam’konda angafe pangozi. Kholo kapena bwenzi lathu lapamtima lingamwalire litadwala mwakayakaya. Ngati sitikulingalira mozama za chiyembekezo chathu cha Ufumu, tingakhale pangozi yauzimu masoka otereŵa atabuka. Moyenera, tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ‘ndimakondwera m’chiyembekezo’? Kodi ndi kangati pamene ndimafatsa kusinkhasinkha za chiyembekezocho? Kodi Paradaiso amene akudzayo ndi weniweni kwa ine? Kodi ndimayerekezera n’tafikamo kale? Kodi ndikufunitsitsa mapeto a dongosolo lazinthu lilipoli atafika monga momwe ndinkafunira nditangophunzira kumene choonadi?’ Funso lotsirizali n’lofunika kulilingalira mozama. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti ngati tili ndi thanzi labwino, ndife achuma, ndipo tikukhala m’dziko lomwe mulibe nkhondo, kupereŵera kwa chakudya, kapena masoka achilengedwe​—m’kanthaŵi kameneka​—sitingathe kuona kufunika koti dziko latsopano la Mulungu libwere mwamsanga.

6. (a) Kodi Paulo ndi Sila analingalira kwambiri za chiyani pamene anali kuzunzidwa? (b) Kodi chitsanzo cha Paulo ndi Sila chingatilimbikitse motani ifeyo lerolino?

6 Paulo anapitiriza kulangiza Aromawo kuti ‘apirire m’masautso.’ (Aroma 12:12) Masautso sanali achilendo kwa Paulo. Nthaŵi inayake, m’masomphenya anaona munthu amene anam’pempha ‘kuwolokera ku Makedoniya’ kuti akathandize anthu kumeneko kuphunzira za Yehova. (Machitidwe 16:9) Atamva izi, Paulo, Luka, Sila, komanso Timoteo, anapita ku Ulaya. Kodi n’chiyani chomwe chinali kuyembekezera amishonale achangu ameneŵa? Chisautso! Atatsiriza kulalikira mumzinda wa Filipi ku Makedoniya, Paulo ndi Sila anakwapulidwa ndi kuponyedwa m’ndende. Mwachionekere, nzika zina za ku Filipi sizinkadana chabe ndi uthenga wa Ufumuwo komanso zinkautsutsa mwamphamvu. Kodi masautso otereŵa anachotsa chimwemwe cha amishonale achanguwo? Ayi. Atawakwapula ndi kuwaponya m’ndende, “pakati pa usiku, Paulo ndi Sila analinkupemphera, nayimbira Mulungu nyimbo.” (Machitidwe 16:25, 26) N’zoona kuti ululu umene Paulo ndi Sila anamva powakwapula sunawasangalatse, komabe amishonale aŵiriwo sanaike mtima kwambiri pa zimenezo. Analingalira kwambiri za Yehova komanso njira zomwe anali kuwadalitsira. Mwa ‘kupirira masautso’ mokondwera, Paulo ndi Sila anapereka chitsanzo chabwino kwa abale awo ku Filipi komanso kwina kulikonse.

7. N’chifukwa chiyani tiyenera kutchula mawu othokoza m’mapemphero athu?

7 Paulo analemba kuti: “Limbikani chilimbikire m’kupemphera.” (Aroma 12:12) Kodi mumapemphera pamene muli ndi nkhaŵa? Kodi pemphero lanu limakhudza chiyani? Mwachionekere mumatchula vuto lanu mosapita m’mbali ndi kupempha Yehova kuti akuthandizeni. Koma mungathenso kutchula mawu othokoza chifukwa cha zabwino zomwe mulinazo. M’nthaŵi ya mavuto, kulingalira zinthu zabwino zimene Yehova akutichitira kumatithandiza ‘kukondwera m’chiyembekezo.’ Davide, amene anakumana ndi mavuto osaneneka m’moyo wake, analemba kuti: “Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita n’zambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziŵerenga.” (Salmo 40:5) Ngati ife, mofanana ndi Davide, tilingalira nthaŵi zonse za madalitso omwe tikulandira kuchokera kwa Yehova, mosakayika tidzakhala okondwa nthaŵi zonse.

Khalani Odekha M’maganizo

8. Kodi n’chiyani chomwe chimathandiza Mkristu kukhala wachimwemwe pamene akukumana ndi chizunzo?

8 Yesu analimbikitsa otsatira ake kukhala odekha m’maganizo pokumana ndi mayesero osiyanasiyana. Iye anati: “Odala muli inu mmene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha Ine.” (Mateyu 5:11) Kodi tili n’chifukwa chotani chokhalira achimwemwe m’mikhalidwe yotereyi? Kukhoza kwathu kupirira chitsutso uli umboni wakuti mzimu wa Yehova uli pa ife. Mtumwi Petro anauza Akristu anzake m’nthaŵi yake kuti: “Mukatonzedwa pa dzina la Kristu, odala inu; pakuti mzimu wa ulemerero, ndi mzimu wa Mulungu apuma pa inu.” (1 Petro 4:13, 14) Mwa mzimu wake, Yehova adzatithandiza kupirira mwakuti, tidzakondwera nthaŵi zonse.

9. Kodi n’chiyani chinathandiza abale ena kupeza zifukwa zokhalira achimwemwe ataikidwa m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chawo?

9 Ngakhale titakumana ndi mavuto osaneneka, tingapezebe zifukwa zosangalalira. Mkristu wina wotchedwa Adolf anatsimikiza kuti zimenezi n’zoona. Iye akukhala m’dziko lomwe ntchito ya Mboni za Yehova inali yoletsedwa kwa zaka zambiri. Adolf ndi anzake ambiri anamangidwa ndi kuwalamula kugwira ukaidi kwanthaŵi yaitali chifukwa chakuti anakana kusiya zikhulupiriro zawo zochokera m’Baibulo. Moyo wam’ndende unali wovuta zedi, koma monga Paulo ndi Sila, Adolf ndi anzakewo anapeza zifukwa zothokozera Mulungu. Iwo anati, moyo wawo wam’ndende unawathandiza kulimbitsa chikhulupiriro chawo ndi kukulitsa mikhalidwe yamtengo wapatali yachikristu, monga kuwolowa manja, chifundo, ndi chikondi chaubale. Mwachitsanzo, wina m’ndendemo akalandira phukusi kuchokera kunyumba, ankagaŵana zomwe zili m’katimo ndi okhulupirira anzake, amene ankaona zinthu zapadera zimenezo monga zochokera kwa Yehova, Wopatsa wamkulu wa ‘mphatso iliyonse yabwino ndi chopereka chilichonse changwiro.’ Kuchita mwachifundo koteroko kunadzetsa chimwemwe kwa wogaŵira anzakeyo komanso kwa olandirawo. Choncho kuikidwa m’ndende kumeneku, komwe cholinga chake chinali kuwawonongera chikhulupiriro, kwenikweni kunawalimbitsa mwauzimu!​—Yakobo 1:17; Machitidwe 20:35.

10, 11. Kodi mlongo wina anatani atam’panikiza ndi mafunso ndipo kenako n’kumulamula kukhala m’ndende nthaŵi yaitali?

10 Ella, amenenso akukhala m’dziko limene analetsa ntchito ya Ufumu, anamangidwa chifukwa chouza ena za chiyembekezo chake chachikristu. Kwa miyezi isanu ndi itatu, mlongoyo anam’panikiza ndi mafunso. Poweruza mlandu wake, anamulamula kukhala m’ndende zaka khumi, momwe munalibe olambira ena a Yehova. Panthaŵiyo n’kuti Ella ali ndi zaka 24 zokha.

11 Komatu Ella sanayembekezere kuthera nthaŵi yonse ya unyamata wake ali m’ndende. Koma poti sakanatha kuchitira mwina, anaganiza zosintha malingaliro ake. Choncho anayamba kuona ndendeyo ngati gawo lakelake lolalikiramo. Iye anati: “Ndinali ndi ntchito yochuluka yolalikira, mwakuti zaka zinkatha mofulumira kwabasi.” Patatha zaka zoposa zisanu, Ella anabwerezanso kumufunsa. Poona kuti ukaidiwo sunawononge chikhulupiriro cha mtsikanayu, omufunsawo anamuuza kuti: “Sitikutulutsa; chifukwa choti sunasinthe.” Molimba mtima Ella anayankha kuti: “Komatu ndasintha! Malingaliro anga ndi okhazikika tsopano kuposa momwe ndimaloŵa m’ndende, ndipo chikhulupiriro changa n’cholimba zedi kuposa kale!” Ndipo powonjezera iye anati: “Ngati simukufuna kunditulutsa, ndikhala momwemuno mpaka pamene Yehova adzandilanditse.” Kukhala m’ndende zaka zisanu ndi theka sikunachotse chimwemwe cha Ella! Anaphunzira kukhutira ndi chilichonse chimene chikum’chitikira. Kodi mwaphunzirapo chilichonse pa chitsanzo cha mlongoyu?​—Ahebri 13:5.

12. Kodi n’chiyani chingapatse Mkristu mtendere wamumtima panthaŵi yamavuto?

12 Musaganize kuti Ella anali ndi mphatso yapadera yomwe inam’thandiza kupirira mavuto ngati amenewo. Ponena za nthaŵi yomwe ankam’funsayo, miyezi ingapo asanam’lamule kukhala m’ndende, Ella akuvomereza kuti: “Ndikukumbukira kuti mano anga ankalumana chifukwa chonjenjemera ndi mantha, ndinadzimva ngati mpheta yomwe aiopseza.” Koma chikhulupiriro cha Ella mwa Yehova n’cholimba. Waphunzira kumukhulupirira. (Miyambo 3:5-7) Zotsatira zake n’zakuti watsimikizira kuposa kale kuti Mulungu ndi weniweni. Akufotokoza kuti: “Nthaŵi zonse ndikaloŵa m’kachipinda momwe ankandifunsiramo, ndinkaona kuti ndili pamtendere. . . . Zinthu zikavuta kwambiri m’pamenenso mtenderewo unkachuluka.” Yehova ndiye anali gwero la mtendere umenewo. Mtumwi Paulo anati: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.”​—Afilipi 4:6, 7.

13. Kodi n’chiyani chikutitsimikizira kuti ngati tikumana ndi masautso, tidzapeza mphamvu zokhoza kupirira?

13 Ella, tsopano anatuluka m’ndende, ndipo adakali wachimwemwe ngakhale kuti wavutika kwanthaŵi yaitali. Wapirira, osati m’mphamvu zake, koma m’mphamvu zomwe Yehova anam’patsa. Zinalinso choncho ndi mtumwi Paulo yemwe analemba kuti: “Chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m’maufoko anga, kuti mphamvu ya Kristu ikhale pa ine. . . . Pakuti pamene ndifoka, pamenepo ndili wamphamvu.”​—2 Akorinto 12:9, 10.

14. Fotokozani mmene Mkristu angakhalire ndi malingaliro oyenera m’nthaŵi yachiyeso komanso zotsatira zake.

14 Ziyeso zimene inuyo mukukumana nazo lerolino zingakhale zosiyanako ndi zomwe tafotokoza panozi. Komabe, mulimonse mmene zingafikire, ziyeso zimavuta kupirira. Mwachitsanzo, bwana wanu angamakunyozeni kwambiri, mwinanso mowirikiza kwambiri kuposa mmene anganyozere antchito anzanu omwe ali m’zipembedzo zina. Mwina simungathe kupeza ntchito ina. Kodi mungatani kuti mupitirizebe kukhala wachimwemwe? Kumbukirani Adolf ndi anzake aja amene, moyo wakundende unawaphunzitsa kukulitsa mikhalidwe yofunika kwambiri. Ngati mutayesetsa moona mtima kukhutiritsa bwana wanuyo​—ngakhale ali ‘waukali’​—mudzakulitsa mikhalidwe yachikristu monga kupirira ndi kuleza mtima. (1 Petro 2:18) Kuwonjezera pamenepo, mudzakhala wodalirika pantchito, zomwenso zingawonjeze mwayi wanu wopeza ntchito yodalirika m’tsogolo. Tsopano tiyeni tikambirane zina mwa njira zomwe zingatithandize kukhalabe achimwemwe potumikira Yehova.

Kufeŵetsa Zinthu Kumadzetsa Chimwemwe

15-17. Kodi banja lina linadziŵa kuti n’chiyani chingathetse kuvutika maganizo, ngakhale kuti gwero lake silingachokeretu?

15 Mwina mwake simungathe kumasinthasintha mtundu wantchito imene m’magwira kapena malo ogwirira ntchito, koma pangakhale mbali zina m’moyo wanu zimene mungaonetse kudziletsa. Lingalirani chochitika chotsatirachi.

16 Banja lina lachikristu linaitanira mkulu wina kunyumba kwawo kuti akadye naye limodzi. Nthaŵi yamadzulo, mbaleyo ndi mkazi wake anaulula kuti posachedwapa ayamba kumachita mantha ndi mavuto a m’moyo. Ngakhale kuti onseŵa analoŵa ntchito zotangwanitsa, amalephera kuyang’ana ntchito zina. Sankadziŵa kuti adzatha kuchita zoterezi kwa utali wotani.

17 Atapempha mkuluyo kuti awalangize, iye anati, “feŵetsani zinthu.” Motani? Mwamuna ndi mkazi wakeyu ankathera maola atatu tsiku lililonse popita ndi pobwera kuntchito. Mkuluyo, amene ankalidziŵa bwino banjalo, anati angachite bwino kulingalira zosamukira kufupi ndi kuntchito kwawoko, kuti athe kuchepetsa nthaŵi imene amawononga tsiku ndi tsiku popita ndi pobwera kuntchito. Nthaŵi imene angapulumutse angathe kuigwiritsa ntchito pa zinthu zina zofunika kapena kupumula. Ngati zovuta zina m’moyo zikuchotsa mbali ina ya chimwemwe chanu, bwanji osafufuza ngati kusintha zinthu zina kungathetse mavutowo?

18. N’chifukwa chiyani kulingalira mosamala kuli kofunika tisanachite chilichonse?

18 Njira ina yochepetsera mavuto ndiyo kulingalira mozama musanachite chilichonse. Mwachitsanzo, Mkristu wina analingalira zomanga nyumba. Anasankha pulani yovuta kwambiri ngakhale anali asanamangepo nyumba chiyambire. Tsopano wazindikira kuti akanatha kupeŵa mavuto ena akanati ‘asamale mayendedwe ake’ asanasankhe pulani ya nyumba yakeyo. (Miyambo 14:15) Mkristu wina anavomera kukachitira umboni wokhulupirira mnzake potenga ngongole. Malinga ndi pangano lawo, ngati wobwereka ndalamayo atalephera kupereka ngongoleyo, wochitira umboniyo anayenera kupereka. Poyamba, zonse zinkayenda bwino, koma patapita nthaŵi wobwereka ndalama uja anayamba utambwali. Wobwereketsa ndalama uja anatutumuka ndipo anakakamiza wochitira umboni uja kuti abweze ngongole yonseyo. Zimenezo zinaika m’mavuto wochitira umboniyo. Kodi sakanatha kupeŵa ngati akanalingalira mosamala kwambiri mbali zonse asanavomere kuchitira umboni ndi kutenga udindo wodzabweza ngongole?​—Miyambo 17:18.

19. Kodi zina mwa njira zomwe tingachepetsere kuvutika maganizo m’moyo wathu ndi ziti?

19 Tikatopa, tisaganize kuti kutopa kwathuko kungachepe ndikuti chimwemwe chathu chingabwerere mwa kuchepetsa nthaŵi yochita phunziro la Baibulo laumwini, yopita muutumiki wakumunda, kapena kupezeka m’misonkhano. Sitiyenera kutero, chifukwa chakuti zimenezi ndi njira zofunika kwambiri zomwe tingalandirire mzimu woyera wa Yehova, umene chipatso chake ndi chimwemwe. (Agalatiya 5:22) Ntchito zachikristu n’zolimbikitsa nthaŵi zonse ndipo kaŵirikaŵiri sizikhala zotopetsa mopambanitsa. (Mateyu 11:28-30) N’kutheka kuti zochita zina zomwe si zauzimu, monga ntchito kapena kusangalala, n’zomwe zikutitopetsa kwambiri. Kuphunzira kugona nthaŵi yabwino kungatithandize kupeza mphamvu. Tingapindule kwambiri mwa kupatula kanthaŵi kena kapadera kuti tipumule. N. H. Knorr, yemwe anali wa Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova kufikira imfa yake, ankakonda kuuza amishonale kuti: “Ngati chinachake chakufooketsani, chinthu choyamba kuchita ndicho kupeza nthaŵi yokwanira yopumula. Mudzadabwa kuona kuti pafupifupi vuto lililonse n’losavuta kulithetsa ngati mutagona mokwanira usiku!”

20. (a) Fotokozani mwachidule zina mwa njira zimene zingatithandize kukhalabe achimwemwe. (b) Kodi mukuganizira zifukwa ziti zokhalira achimwemwe? (Onani bokosi patsamba 17.)

20 Akristu ali ndi mwayi wapadera wotumikira “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteo 1:11, NW) Monga momwe taonera, tingapitirizebe kukhala achimwemwe ngakhale titakumana ndi mavuto othetsa nzeru. Tiyeni tisungebe chiyembekezo chathu cha Ufumu, tisinthe malingaliro athu ngati n’koyenera kutero, ndiponso kufeŵetsa zinthu m’moyo wathu. Tikatero, kaya tidzakumana ndi zotani m’moyo, tidzatha kuchita monga mwa mawu a mtumwi Paulo akuti: “Kondwerani mwa Ambuye nthaŵi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.”​— Afilipi 4:4.

Lingalirani Mafunso Aŵa Mozama:

• N’chifukwa chiyani Akristu ayenera kulingalira za chiyembekezo cha Ufumu nthaŵi zonse?

• N’chiyani chimene chingatithandize kukhalabe achimwemwe tikakhala m’mavuto?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesa kufeŵetsa zinthu m’moyo wathu?

• Kodi ena afeŵetsa zinthu m’moyo wawo m’mbali ziti?

[Mafunso]

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 17]

Zifukwa Zowonjezera Zokhalira Achimwemwe

Monga Akristu, tili ndi zifukwa zambiri zokhalira okondwa. Lingalirani zotsatirazi:

1. Tikum’dziŵa Yehova.

2. Taphunzira choonadi cha Mawu a Mulungu.

3. Machimo athu angakhululukidwe mwa chikhulupiriro chathu m’nsembe ya Yesu.

4. Ufumu wa Mulungu ukulamulira​—posachedwapa dziko latsopano lifika!

5. Yehova watiloŵetsa m’paradaiso wauzimu.

6. Tikukondwera mu ubale wosangalatsa wachikristu.

7. Tili ndi mwayi wogwira nawo ntchito yolalikira.

8. Tili ndi moyo, ndipo tili ndi nyonga pamlingo winawake.

Kodi mungatchule zifukwa zina ziti zokhalira achimwemwe?

[Chithunzi patsamba 13]

Paulo ndi Sila anali achimwemwe ndi m’ndende momwe

[Zithunzi patsamba 15]

Kodi mukulingalira mozama za chiyembekezo chokondweretsa cha dziko latsopano la Mulungu?