Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuthetsa Mnyozo pa Dzina la Mulungu

Kuthetsa Mnyozo pa Dzina la Mulungu

Olengeza Ufumu Akusimba

Kuthetsa Mnyozo pa Dzina la Mulungu

MAWU a Mulungu, Baibulo, limati: “Mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, mmene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m’tsiku la kuyang’anira.” (1 Petro 2:12) Choncho, Akristu oona amayesetsa kukhalabe ndi khalidwe labwino kuti apeŵe kunyozetsa dzina la Yehova.

M’tauni ina yotchedwa Senanga m’dera lakumidzi m’dziko la Zambia, mphunzitsi wa pa sukulu ina anamubera wailesi m’nyumba yake. Popeza kuti Mboni za Yehova zinali kulalikira m’deralo, iye anaziimba mlandu wa kuba wailesiyo. Iye anakanena nkhaniyi ku polisi. Kumeneko, anatulutsa thirakiti lomwe analipeza m’nyumba yake monga umboni wosonyeza kuti Mbonizo zinafika panyumbayo. Komabe, apolisiwo sanam’khulupirire. Iwo anam’langiza kuti akafufuzenso bwinobwino nkhaniyi.

Bungwe la akulu linauza Mboni zimene patsikulo zinkalalikira m’deralo kuti zikakambirane ndi mphunzitsiyo nkhaniyi. Abale ena anapita kukakambirana naye. Anam’fotokozera kuti iwo akufuna kuthetsa mnyozo pa dzina la Yehova. M’kukambirana kwawo, Mbonizo zinauza mphunzitsiyo kuti zinakumana ndi mnyamata wina panyumba yakeyo ndipo zinam’patsa thirakiti. Iye anam’zindikira munthuyo malinga ndi mmene Mbonizo zinalongosolera kaonekedwe kake. Ndiponso munthuyo anali watchalitchi chimodzi ndi mphunzitsiyo. Iye anakam’funsa mnyamatayo zankhaniyi koma anakana. Mphunzitsiyo anakambirana nkhaniyi ndi makolo a mnyamatayo ndipo anabwerera kunyumba. Lisanathe ndi ola limodzi lomwe, mayi a mnyamatayo anabweretsa wailesi yobedwayo.

Atachita manyazi, mphunzitsiyo anapita kwa akulu kukapepesa chifukwa chonamizira Mboni mlanduwo. Akuluwo anavomera kupepesa kwakeko koma anam’pempha kuti zomwe zachitikazo azifalitse kuti aliyense adziŵe kuti Mboni sizinalakwe. Nkhaniyi anailengeza pasukulu ndipo inathetsa mnyozo pa dzina la Yehova. Mboni za Yehova zikupitirizabe kulalikira momasuka m’deralo.

[Mapu/​Chithunzi patsamba 19]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

AFRICA

Zambia

[Mawu a Chithunzi]

Mountain High Maps® Copyright © 1997 Digital Wisdom, Inc.