Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Umasiye Unakhudzira Akazi Aŵiri

Mmene Umasiye Unakhudzira Akazi Aŵiri

Mmene Umasiye Unakhudzira Akazi Aŵiri

SANDRA ndi mkazi wamasiye amene akukhala m’dziko la Australia. Mwamuna wake atamwalira, Sandra anasokonezeka maganizo ndipo sanakhulupirire. “Kudziŵa kuti mwamuna wanga wokondedwa wamwalira mwadzidzidzi, kunandisokoneza maganizo kwambiri. Sindikukumbukira mmene ndinayendera kuchoka kuchipatala kufika kunyumba kapena zomwe ndinachita tsikulo. M’milungu ingapo yotsatira, mantha anga anayambitsa kupweteka m’thupi kosalekeza.”

Mnzake wa Sandra dzina lake Elaine nayenso wakhala wamasiye kwa zaka zisanu ndi chimodzi. Elaine anadwazika mwamuna wake, David, kwa miyezi isanu ndi umodzi mwamunayo asanamwalire ndi matenda a kansa. Iye anali ndi chisoni kwambiri moti mpaka anasiya kuona kwakanthaŵi ndithu. Patatha zaka ziŵiri, iye anakomoka pamaso pa anthu. Dokotala wake sanam’peze ndi matenda alionse. Komabe, dokotalayo anazindikira kuti Elaine wakhala akusunga chisoni m’mtima mwake. Choncho, anamuuza kuti apite kunyumba ndipo akadzikakamize kulira. “Zinanditengera nthaŵi yaitali ndithu kuti ndithetse chisoni changa,” anavomereza motero Elaine. Ndipo anawonjezera kuti, ndikasungulumwa “ndinkakonda kupita ku chipinda chogona n’kukafunda zovala za mwamuna wanga David.”

Inde, anthu angachite zinthu zosiyanasiyana mwamuna kapena mkazi wawo wapamtima akamwalira. Kwa akazi amasiye, imfa ya mwamuna imaphatikizapo zambiri kuposa kungokhala wopanda mwamuna. Mwachitsanzo, Sandra kwakanthaŵi ndithu, ankadziona kuti si mmene analili kale. Mofanana ndi akazi ambiri amene amuna awo amwalira posachedwapa, Sandra nayenso ankadziona kuti sali wotetezedwa. Iye anakumbukira kuti: “Popeza kuti mwamuna wanga ndiye anali kusankha zochita, kumwalira kwake kwadzidzidzi kunachititsa kuti ndizisankha ndekha zochita zoterozo. Ndinali kulephera kugona. Ndinali kutopa ndiponso kufooka. Ngakhale kudziŵa kokha zofunika kuchita kunali kovuta kwabasi.”

Nkhani zofanana ndi ya Sandra ndi Elaine zikuchitika tsiku n’tsiku padziko lonse. Matenda, ngozi, nkhondo zapachiweniweni, ndiponso ziwawa zikuthandiza kuwonjezera chiŵerengero cha akazi amasiye. * Ambiri mwa akazi ameneŵa amavutika ndi chisoni m’mtima mwawo. Sadziŵa kuti kaya agwira mtengo wanji. Kodi mabwenzi ndi achibale angatani kuti athandize akazi amasiye? Nkhani yotsatirayi ili ndi malangizo amene angathandize kwambiri.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Akazi ena ali ngati amasiye chifukwa chakuti amuna awo anawachokera. Ngakhale kuti kupatukana m’banja ndiponso kusudzulana kumabweretsa mavuto ena apadera, mfundo zina zomwe zili m’nkhani yotsatirayi zingathandizenso akazi otereŵa.