“Yehova Wandichitira Zabwino Zambiri!”
“Yehova Wandichitira Zabwino Zambiri!”
TSIKU lina madzulo m’March 1985, amuna ndi akazi a m’Dipatimenti Yolemba ku likulu la Mboni za Yehova ku New York, U.S.A., anakumbukira chinthu chapamwamba kwambiri. Anakumbukira kuti Karl F. Klein wakwanitsa zaka 60 mu utumiki wa nthaŵi zonse. Mosangalala, Mbale Klein anati: “Yehova wandichitira zabwino zambiri!” Iye anati amakonda lemba la m’Baibulo la Salmo 37:4. Kenako anasangalatsa anthu onse powaimbira gitala.
Zaka 15 kuchokera pamenepo, Mbale Klein anapitiriza kugwira ntchito m’Dipatimenti yolemba ndi m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Koma pa January 3, 2001, Karl Klein anamaliza moyo wake wa padziko lapansi mokhulupirika ali ndi zaka 95.
Karl anabadwira ku Germany. Banja lawo linasamukira ku Chicago m’chigawo cha Illinois m’dziko la United States komwe Karl anakulira. Karl ndi mng’ono wake Ted anachita chidwi kwambiri ndi Baibulo akali ang’onoang’ono. Karl anabatizidwa mu 1918, ndipo zochititsa chidwi zomwe anamva pamsonkhano wa Ophunzira Baibulo mu 1922 zinamusonkhezera kukonda kulalikira kwa moyo wake wonse. Sankafuna kuti sabata ithe osalalikira. Anachita zimenezi ngakhale m’masabata omalizira a moyo wake.
Karl anayamba kutumikira pa likululo mu 1925, ndipo anayamba ndi kugwira ntchito m’chipinda chosindikizira mabuku. Anali wokonda nyimbo kwambiri. Kwa zaka zingapo, ankaimba gitala m’gulu loimba nyimbo ndi zida zokhazokha zomwe ankaziulutsa pa wailesi yachikristu. Kenako, anagwira ntchito m’Dipatimenti ya Utumiki komwe ankasangalala kwambiri kucheza ndi woyang’anira dipatimentiyo T. J. Sullivan. Panthaŵiyo Ted anali atakwatira Doris ndipo anali amishonale ku Puerto Rico.
Kwa zaka pafupifupi 50, Karl Klein anagwira ntchito m’Dipatimenti Yolemba, komwe anathandiza kwambiri pakuti ankakonda kufufuza ndiponso ankalidziŵa bwino kwambiri Baibulo. Mu 1963, Karl anakwatira Margareta wa ku Germany yemwe anali mmishonale ku Bolivia. Mwachikondi, mkaziyu anamuthandiza kwambiri Karl makamaka pamene thanzi lake silinali bwino, moti anachita zambiri pa msinkhu womwe anthu ambiri sangathe kuchita kalikonse. Polankhula kuchokera pansi pa mtima ndiponso monga woimba, Karl anakamba nkhani zosaiŵalika m’mipingo ndi m’misonkhano. Chakumapeto kwa moyo wake, anali tcheyamani pokambirana lemba la tsiku m’maŵa m’banja lalikulu la Beteli ku New York lomwe linasangalatsa ndi kupindulitsa aliyense.
Ambiri omwe amaŵerenga Nsanja ya Olonda kaŵirikaŵiri, angakumbukire nkhani yosangalatsa yofotokoza moyo wake m’magazini ya October 1, 1984. Mudzasangalala kuŵerenga kapena kubwerezanso kuŵerenga nkhaniyo mukudziŵa kuti wolembayo anapitirizabe kukhala Mkristu wokhulupirika ndi wodzipereka kwa zaka zina 15.
Monga mmodzi wa odzozedwa wa Ambuye, Mbale Klein anafunitsitsa kulamulira ndi Kristu kumwamba ndi mtima wonse. Palibe chifukwa chokayikira kuti tsopano Yehova wakwaniritsa chilakolako chimenecho.—Luka 22:28-30.
[Chithunzi patsamba 31]
Karl ndi T. J. Sullivan mu 1943, komanso Ted ndi Doris
[Chithunzi patsamba 31]
Karl ndi Margareta, mu October 2000