Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kumanga Banja Lolimba Mwauzimu

Kumanga Banja Lolimba Mwauzimu

Kumanga Banja Lolimba Mwauzimu

“Komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” ​—AEFESO 6:4.

1. Kodi Mulungu anali n’cholinga chotani chokhudza banja, koma mmalo mwake chinachitika n’chiyani?

“MUBALANE, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.” (Genesis 1:28) Mwa kuuza Adamu ndi Hava mawu amenewo, Yehova Mulungu anayambitsa banja. (Aefeso 3:14, 15) Poyang’ana m’tsogolo, banja loyambali linkaona m’maganizo awo dziko lapansi litadzaza ndi mbadwa zawo​—banja lapachibale la anthu angwiro, akukhala m’dziko lapansi la paradaiso mosangalala ndi kulambira Mlengi wawo Wamkulu mogwirizana. Koma Adamu ndi Hava anachimwa, ndipo dziko lapansi silinadzaze anthu olungama, anthu oopa Mulungu. (Aroma 5:12) Mmalo mwake, moyo wabanja unaipa mofulumira, ndipo udani, chiwawa, ndi kusoŵa kwa “chikondi chachibadwidwe” zafala kwambiri, makamaka “masiku otsiriza” ano.​—2 Timoteo 3:1-5; Genesis 4:8, 23; 6:5, 11, 12.

2. Kodi mbadwa za Adamu zinkatha kuchitanji, koma anafunikira chiyani kuti amange banja lolimba mwauzimu?

2 Adamu ndi Hava anawalenga m’chifanizo cha Mulungu. Ngakhale kuti tsopano anali wochimwa, Yehova anam’lolabe Adamu kubala ana. (Genesis 1:27; 5:1-4) Mofanana ndi atate awo, mbadwa za Adamu zinkadziŵa zinthu zofunika kuchita ndipo zinaphunzira kusiyanitsa chabwino ndi choipa. Ankalandira malangizo a mmene angalambirire Mlengi wawo ndi kufunika komukonda ndi mtima wawo wonse, moyo wawo, nzeru zawo, ndi mphamvu zawo zonse. (Marko 12:30; Yohane 4:24; Yakobo 1:27) Komanso, akanatha kuphunzira ‘kuchita cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu.’ (Mika 6:8) Koma monga anthu ochimwa, anafunikira khama lowonjezereka kuti amange banja lolimba mwauzimu.

Patulani Nthaŵi

3. Kodi makolo ‘angapatule motani nthaŵi’ kuti alere ana achikristu?

3 M’nthaŵi zovuta ndi zoŵaŵitsa zino, mpofunika kuchita khama kwambiri kuti ana akhale “okonda Yehova” ndi “odana nacho choipa” moona mtima. (Salmo 97:10) Makolo anzeru ‘amapatula nthaŵi’ kuti akwaniritse ntchito yovutayi. (Aefeso 5:15-17) Ngati ndinu kholo, kodi mungachite motani zimenezi? Choyamba, sankhani zinthu zofunika kuchita moyambirira, kusamalira “zinthu zofunika kwambiri,” kuphatikizapo kuphunzitsa ana ndi kuwasonyeza mmene angachitire zinthu. (Afilipi 1:10, 11, NW) Chachiŵiri, feŵetsani zinthu m’moyo wanu. Mungafunikire kuleka kuchita zinthu zomwe n’zosafunika kwenikweni. Kapena mungafunikire kuchotsa katundu wina wosafunika kwenikweni amene amangotha nthaŵi pomukonzetsa. Monga kholo lachikristu, simudzadandaula chifukwa chakuti mwachita zonse zimene mungathe kuti mulere ana oopa Mulungu.​—Miyambo 29:15, 17.

4. Kodi tingatani kuti banja likhale logwirizana?

4 Kuthera nthaŵi mukucheza ndi ana anu, makamaka ngati nkhani zake zili zauzimu, nkopindulitsa kwambiri ndipo ndi imodzi mwa njira zabwino koposa zogwirizanitsira banja. Koma osachita zimenezi popanda dongosolo lenileni. Sankhani nthaŵi yabwino yoti muzikhala chapamodzi. Zimenezi sizikutanthauza kungokhala m’nyumba imodzi, aliyense n’kumachita zofuna zake ayi. Ana amakula bwino ngati mumacheza nawo tsiku ndi tsiku. Muyenera kuwasonyeza chikondi ndi kuwadera nkhaŵa mokoma mtima. Ngakhale asanaganize zokhala ndi ana, okwatirana ayenera kulingalira mozama za udindo wofunika umenewu. (Luka 14:28) Akatero sadzaona kulera ana ngati chintchito cholemetsa. Mmalo mwake, adzakuona ngati mwayi wamtengo wapatali.​—Genesis 33:5; Salmo 127:3.

Phunzitsani mwa Mawu ndi Chitsanzo

5. (a) Kodi kuphunzitsa ana kukonda Yehova kumayamba n’chiyani? (b) Kodi makolo apatsidwa malangizo otani pa Deuteronomo 6:5-7?

5 Kuphunzitsa ana anu kukonda Yehova kumayamba ndi chikondi chanu pa iye. Ngati Mulungu mukum’konda kwambiri mudzasonkhezereka kutsatira malangizo ake onse mokhulupirika. Zimenezi zikuphatikizapo kulera ana “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Mulungu akulangiza makolo kupereka chitsanzo chabwino kwa ana awo, kulankhula nawo, ndiponso kuwaphunzitsa. Deuteronomo 6:5-7 amati: “Ndipo muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse. Ndipo mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.” Mwa kuwalangiza mobwerezabwereza, mungathe kukhomereza malamulo a Mulungu m’mitima ya ana anu. Mwa kuchita zimenezi, ana anu angaone chikondi chomwe inuyo muli nacho kwa Yehova ndipo, nawonso angasonkhezereke kukulitsa ubwenzi wawo ndi iye.​—Miyambo 20:7.

6. Kodi makolo angapezerepo mwayi motani pamfundo yakuti ana amaphunzira kuchokera m’zitsanzo?

6 Ana amafunitsitsa kuphunzira. Amamvetsera mwatcheru ndi kuonerera mwachidwi zomwe inu mukuchita ndipo sachedwa kutengera chitsanzo chanu. Akaona kuti si ndinu wokondetsa zinthu zakuthupi, zimenezi zimawathandiza kuphunzira mmene angatsatirire malangizo a Yesu. M’mawaphunzitsa kukhala osadera nkhaŵa za zinthu zakuthupi koma ‘kufuna Ufumu wa Mulungu choyamba.’ (Mateyu 6:25-33) Mwa kukambirana nawo nkhani zolimbikitsa zokhudza choonadi cha Baibulo, mpingo wa Mulungu, ndi akulu oikidwa, mumaphunzitsa ana anu kulemekeza Yehova ndi kuona kufunika kwa zogawira zake zauzimu. Popeza kuti ana amaona mwamsanga kusemphana kwa zinthu, pamene mukuwalangiza muyeneranso kuonetsa makhalidwe ndi malingaliro osonyeza kuyamikira kwanu zinthu zauzimu. Zimakhalatu zolimbikitsa kwambiri makolo akaona kuti chitsanzo chawo chabwino chathandiza ana awo kukonda Yehova ndi mtima wonse!​—Miyambo 23:24, 25.

7, 8. N’chitsanzo chiti chomwe chikusonyeza kufunika kophunzitsa ana adakali aang’ono, nanga ndani ayenera kutamandidwa chifukwa cha zotsatira zabwino?

7 Ubwino wophunzitsa ana adakali aang’ono tingauone m’chitsanzo china kuchokera ku Venezuela. (2 Timoteo 3:15) Chikukhudza achinyamata ena okwatirana, Félix ndi Mayerlín. Ameneŵa akuchita utumiki wa upainiya. Mwana wawo wamwamuna Felito atabadwa, anali ofunitsitsa kuchita chilichonse chomwe angathe kuti amulere monga wolambira Yehova moona. Mayerlín anayamba kumuŵerengera Felito mokweza buku lotchedwa Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Adakali wamng’ono, Felito anaoneka kuti akutha kum’zindikira Mose ndi anthu ena otchulidwa m’buku limeneli.

8 Felito anayamba kulalikira payekha adakali wamng’ono ndithu. Anakwaniritsa cholinga chake chofuna kukhala wofalitsa Ufumu, ndipo pambuyo pake anabatizidwa. Mkupita kwa nthaŵi, Felito anakhala mpainiya wokhazikika. Pothirira ndemanga makolo ake anati: “Tikamaona mwana wathu akupita patsogolo, tinkadziŵa kuti zatheka chifukwa cha Yehova ndi malangizo ake.”

Thandizani Ana Kukula Mwauzimu

9. N’chifukwa chiyani tiyenera kuthokoza chifukwa cha malangizo auzimu omwe timalandira kudzera m’gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru?

9 Kuli magazini, mabuku, ndi malo a pa Intaneti masauzande osaneneka opereka malangizo a kaleredwe ka ana. Mkonzi wina wa magazini yapadera pankhani za ana ya Newsweek anati, kaŵirikaŵiri “nkhani zopezeka m’zinthu zimenezi zimatsutsana. Zimakhumudwitsa kwambiri makamaka pamene nkhani inayake yomwe umaganiza kuti njothandiza yadziŵika kuti ndi bodza lamkunkhuniza.” Tikuthokozatu kwambiri kuti Yehova watipatsa malangizo mooloŵa manja ndiponso kuthandiza mabanja kukula mwauzimu! Kodi mukugwiritsa ntchito mokwanira zonse zimene zikuperekedwa kudzera m’gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru?​—Mateyu 24:45-47.

10. Kodi phunziro la Baibulo labanja n’lopindulitsa motani kwa makolo komanso kwa ana?

10 China chofunika kwambiri ndicho kuchita phunziro la Baibulo la banja mokhazikika nthaŵi zonse. Kuti likhale lothandiza, losangalatsa, ndi lolimbikitsa, mpofunika kukonzekera mokwanira. Mwa kupatsa mpata ana awo kuti nawonso alankhule, makolo angadziŵe zomwe zili m’mitima ndi m’malingaliro awo. Njira imodzi yodziŵira ngati phunziro labanja likuthandiza ndiyo kuona ngati onse m’banjamo amaliyembekezera mwachidwi.

11. (a) Kodi makolo angathandize ana awo kupanga zolinga zotani? (b) Kodi panali zotsatira zotani mtsikana wina wa ku Japan atatsatira cholinga chake?

11 Mofananamo, zolinga zauzimu zimathandiza kuti banja likhale lolimba mwauzimu, ndipo makolo ayenera kuthandiza ana awo kupanga zolinga zimenezi. Zolinga zoyenera zingaphatikizepo kuŵerenga Baibulo tsiku lililonse, kukhala wofalitsa uthenga wabwino wanthaŵi zonse, ndiponso kupita patsogolo mwa kudzipatulira komanso kubatizidwa. Zolinga zina zingaphatikizepo kuchita utumiki wa nthaŵi zonse monga mpainiya, pa Beteli, kapena monga mmishonale. Ali ku sukulu yapulaimale, mtsikana wina wa ku Japan wotchedwa Ayumi anapanga cholinga cholalikira kwa aliyense m’kalasi mwake. Kuti achititse chidwi aphunzitsi ake ndi anzake m’kalasimo, iye anapempha chilolezo kuti aike zofalitsa zingapo zofotokoza Baibulo m’laibulale. Zotsatira zake zinali zakuti Ayumi anachititsa maphunziro a Baibulo 13 m’zaka zisanu ndi chimodzi zomwe anali pasukulu yapulaimaleyo. Mmodzi mwa ophunzira Baibulo amenewo komanso ena a m’banja la wophunzirayo anakhala Akristu obatizidwa.

12. Kodi ana angapindule kwambiri motani ndi misonkhano yachikristu?

12 Chinanso chofunika kuti tikhale athanzi mwauzimu ndicho kupezeka pamisonkhano nthaŵi zonse. Mtumwi Paulo anachenjeza okhulupirira anzake kuti ‘asaleke kusonkhana kwawo pamodzi, monga amachita ena.’ Tisakhale n’chizoloŵezi chophonya misonkhano, chifukwa chakuti achinyamata ndi achikulire omwe amapindula kwambiri mwa kupezeka pamisonkhano yachikristu nthaŵi zonse. (Ahebri 10:24, 25; Deuteronomo 31:12) Ana muyenera kuwaphunzitsa kumvetsera mwatcheru. Kukonzekera misonkhano n’kofunikanso kwambiri chifukwa chakuti munthu amapindula kwambiri ngati atenga nawo mbali mwa kupereka ndemanga. Mwana wamng’ono angayambe mwa kutchula mawu ochepa kapena kuŵerenga kachigawo kochepa m’ndime, komabe n’zopindulitsa kwabasi ngati ana titawaphunzitsa kufufuza mayankho ndi kuwatchula m’mawu awoawo. Kodi inuyo makolo mumasonyeza chitsanzo chabwino mwa kupereka mayankho ogwira mtima nthaŵi zonse? Ndi bwinonso kuti aliyense m’banjamo akhale ndi Baibulo lakelake, buku la nyimbo, ndi chofalitsa chomwe tikugwiritsa ntchito pokambirana Malemba.

13, 14. (a) N’chifukwa chiyani makolo ayenera kupita muutumiki limodzi ndi ana awo? (b) N’chiyani chingathandize kuti utumiki wakumunda ukhale wopindulitsa ndi wosangalatsa kwa ana?

13 Makolo anzeru amalimbikitsa ana awo kuti agwiritse ntchito mphamvu zawo zaunyamata potumikira Yehova, kuwathandiza kupanga ntchito yolalikira mbali yofunika kwambiri ya moyo wawo. (Ahebri 13:15) Makolo angaonetsetse kuti ana awo akuphunziradi zonse zofunikira kuti akhale atumiki ‘opanda chifukwa cha kuchita manyazi, olunjika nawo bwino mawu a choonadi’ pokhapokha ngati makolowo akuyenda limodzi ndi anawo muutumiki. (2 Timoteo 2:15) Kodi inuyo m’machita zimenezo? Ngati ndinu kholo, kodi m’mathandiza ana anu kukonzekera utumiki wakumunda? Kuchita zimenezi kudzathandiza kuti utumiki ukhale wosangalatsa, watanthauzo, ndi wopindulitsa kwa iwo.

14 N’chifukwa chiyani n’kopindulitsa kuti makolo ndi ana awo azigwirira ntchito limodzi muutumiki? Mwa kuyendera nawo limodzi muutumiki, ana angaone ndi kutengera chitsanzo chabwino cha makolo awo. Panthaŵi imodzimodziyo, makolo angaone mtima, khalidwe, ndi luso la ana awo. Onetsetsani kuti nthaŵi zonse muli ndi ana anu pochita utumiki wamtundu uliwonse. Ngati n’kotheka, pezerani mwana aliyense chikwama chopitira kuulaliki, ndipo m’phunzitseni kuchisamalira kuti chikhale chooneka bwino. Mwa kusatopa kuwaphunzitsa ndi kuwalimbikitsa, mudzawathandiza kukhala ndi chidwi chenicheni ndi utumiki, ndipo anawo adzaona ntchito yolalikira monga njira yosonyezera chikondi chawo kwa Mulungu ndi kwa mnansi.​—Mateyu 22:37-39; 28:19, 20.

Khalanibe Athanzi Mwauzimu

15. Popeza kusunga banja lili lolimba mwauzimu n’kofunika kwambiri, kodi ndi njira zina ziti zochitira zimenezi?

15 Kusunga banja lili lolimba mwauzimu n’kofunika kwambiri. (Salmo 119:93) Njira imodzi yochitira zimenezi ndiyo kukambirana nkhani zauzimu ndi banja lanu pa mpata uliwonse. Kodi mumakambirana ndi banja lanu lemba la m’Baibulo latsikulo? Kodi m’makonda kuuzako ena “poyenda inu panjira” zomwe zakuchitikirani muutumiki wakumunda kapena mfundo zochokera m’magazini atsopano a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!? Kodi mumakumbukira kuthokoza Yehova m’pemphero “pogona inu pansi, ndi pouka inu” chifukwa chokusungani ndi moyo tsiku lililonse komanso chifukwa chokupatsani zinthu zosiyanasiyana mooloŵa manja? (Deuteronomo 6:6-9) Ana anu akamaona chikondi chanu pa Mulungu m’chilichonse chimene mukuchita, zimenezi zidzawathandiza kupanga choonadi kukhala chawochawo.

16. Kodi kuthandiza ana kuchita okha kafukufuku n’kopindulitsa motani?

16 Nthaŵi zina, ana angafune malangizo kuti athane ndi mavuto kapena mikhalidwe yovuta yomwe ingabuke. Mmalo mongowauza zoti achite nthaŵi zonse, bwanji osawasonyeza mmene angapezere malingaliro a Mulungu pankhaniyo mwa kuwalimbikitsa kufufuza pawokha? Kuphunzitsa ana kugwiritsa ntchito bwino zipangizo zonse ndi zofalitsa zoperekedwa kudzera mwa ‘kapolo wokhulupirika’ kudzawathandiza kukhala mabwenzi enieni a Yehova. (1 Samueli 2:21b) Ndipo pamene auza ena m’banjamo za phindu lomwe apeza pochita kafukufuku m’Baibulo, banjalo lidzapitiriza kukula mwauzimu.

Dalirani Kwambiri Yehova

17. N’chifukwa chiyani makolo omwe alibe mnzawo wamuukwati sayenera kuda nkhaŵa pankhani yolera ana awo monga Akristu?

17 Bwanji nanga za mabanja a kholo limodzi? Ameneŵa amakumana ndi mavuto ochuluka pamene akulera ana. Koma makolo omwe mulibe mnzanu wamuukwati musataye mtima! Mukhoza kupambana, monga momwe makolo ambiri opanda mnzawo amene akhulupirira mwa Mulungu achitira. Atsatira malangizo ake mokhulupirika, ndipo alera ana azitsanzo zabwino, olimba mwauzimu. (Miyambo 22:6) Inde, Akristu omwe alibe mnzawo wamuukwati afunikira kudalira kwambiri Yehova. Ayenera kukhala n’chikhulupiriro kuti adzawathandiza.​—Salmo 121:1-3.

18. Kodi makolo ayenera kusamalira kwambiri zofunika za m’malingaliro ndi zakuthupi ziti za ana awo, koma kodi ayenera kuikira mtima kwambiri pa chiyani?

18 Makolo anzeru amazindikira kuti ‘pali nthaŵi yoseka, ndi nthaŵi yovina.’ (Mlaliki 3:1, 4) Nthaŵi yocheza ndiponso kusanguluka mosapambanitsa n’zofunika kuti malingaliro ndi matupi a ana akhale omasuka. Nyimbo zolimbikitsa, makamaka kuimba nyimbo zotamanda Mulungu kudzathandiza mwana kukulitsa malingaliro abwino othandiza kwambiri polimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova. (Akolose 3:16) Nthaŵi yaunyamata ndi nthaŵi yabwino kukonzekera kudzakhala wachikulire woopa Mulungu, ndi kuti mudzapitirize kusangalala ndi moyo kosatha padziko lapansi la paradaiso.​—Agalatiya 6:8.

19. N’chifukwa chiyani makolo ayenera kukhala otsimikiza kuti Yehova adzadalitsa khama lawo polera ana?

19 Yehova akufuna kuti mabanja onse achikristu akhalebe olimba mwauzimu ndi ogwirizana. Ngati Mulungu timamukondadi ndi mtima wonse ndi kuchita zonse zimene tingathe momvera Mawu ake, adzadalitsa khama lathu lonse ndipo adzatipatsa mphamvu zofunika kuti titsatire malangizo ake ouziridwa. (Yesaya 48:17; Afilipi 4:13) Kumbukirani kuti mwayi womwe muli nawo panopa wophunzitsa ndi kusonyeza ana anu mmene angachitire zinthu ndi wochepa ndipo ukadutsa sudzapezekanso. Chitani mmene mungathere kugwiritsa ntchito malangizo a m’Mawu a Mulungu, ndipo Yehova adzadalitsa khama lanu pomanga banja lolimba mwauzimu.

Kodi Taphunzira Chiyani?

• N’chifukwa chiyani kupatula nthaŵi kuli kofunika pamene tikuphunzitsa ana?

• N’chifukwa chiyani chitsanzo chabwino cha makolo chili chofunika?

• Ndi njira zina ziti zofunika pothandiza ana kukula mwauzimu?

• Kodi uzimu wa banja tingausungebe motani?

[Mafunso]

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

Mabanja olimba mwauzimu amaphunzira Mawu a Mulungu nthaŵi zonse, amapezeka m’misonkhano yachikristu, ndiponso amapitira limodzi muutumiki