Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nthaŵi Yomwe Mulungu Walola Anthu Kuvutika Ili Pafupi Kutha

Nthaŵi Yomwe Mulungu Walola Anthu Kuvutika Ili Pafupi Kutha

Nthaŵi Yomwe Mulungu Walola Anthu Kuvutika Ili Pafupi Kutha

KULIKONSE anthu akuvutika. Ena chifukwa cha zochita zawo. Iwo anadzitengera matenda opatsirana pochita chiwerewere. Ena akuvutika ndi zotsatira za kumwa mankhwala osokoneza bongo, uchidakwa, komanso kusuta fodya. Enanso angadwale chifukwa cha kudya mosayenera. Komabe, mavuto ambiri amachitika chifukwa cha zinthu zomwe munthu wamba sangathe kuziletsa monga: nkhondo, ziwawa zapachiŵeniŵeni, kuswa malamulo, umphaŵi, chilala, ndi matenda. Chinanso chomwe anthu sangathe kuchiletsa ndicho kuvutika kokhudzana ndi ukalamba ndiponso imfa.

Baibulo limatitsimikizira kuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Koma nanga n’chifukwa chiyani Mulungu wachikondiyo walola anthu kuvutika kwa zaka mazana ambiri chonchi? Kodi adzathetsa liti mavuto ameneŵa? Kuti tiyankhe mafunso ameneŵa, tiyenera kupeza cholinga cha Mulungu ponena za anthu. Zimenezi zitithandiza kumvetsa chifukwa chomwe Mulungu walolera anthu kuvutika ndiponso zomwe adzachite ndi vutoli.

Mphatso ya Ufulu Wakudzisankhira

Mulungu atalenga munthu woyamba, sanangom’panga ndi thupi lokhala ndi ubongo wokha koma anawonjezera zinthu zina. Komanso, Mulungu sanalenge Adamu ndi Hava kukhala maloboti osaganiza. Anawapatsa ufulu wakudzisankhira. Ndipotu imeneyo inali mphatso yabwino kwambiri chifukwa “anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu.” (Genesis 1:31) Inde, “ntchito yake ndi yangwiro.” (Deuteronomo 32:4) Tonsefe timayamikira kwambiri mphatso imeneyi ya ufulu wakudzisankhira chifukwa sitifuna kuti zokhumba ndi zochita zathu zonse azichita kutiuza osakhala ndi mwayi wodzisankhira chilichonse.

Komabe, kodi mphatso yabwinoyi ya ufulu wakudzisankhira inayenera kugwiritsidwa ntchito popanda malire? Malangizo a Mawu a Mulungu omwe Akristu oyambirira analandira, akuyankha kuti: “Monga mfulu, koma osakhala nawo ufulu monga chobisira choipa, koma ngati akapolo a Mulungu.” (1 Petro 2:16) Panayenera kukhala malire kuti anthu apindule ndi mphatsoyi. Choncho, ufulu wakudzisankhira unayenera kugwiritsidwa ntchito motsatira lamulo. Apo ayi, zotsatira zake zinali chisokonezo.

Lamulo la Yani?

Kodi ndi lamulo la yani linayenera kuika malire oyenera a ufulu umenewu? Yankho la funso limeneli ndilo chifukwa chachikulu chomwe Mulungu walolera anthu kuvutika. Popeza kuti Mulungu ndiye analenga anthu, iye amadziŵa bwino kwambiri malamulo omwe anthuwo ayenera kutsata kuti apindule ndiponso kupindulitsa ena. Baibulo limanena kuti: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.”​—Yesaya 48:17.

Mwachionekere, mfundo yaikulu n’njakuti: Anthu sanawalenge kuti adzilamulire okha popanda Mulungu. Anawapanga mwanjira yakuti kupambana ndi chimwemwe chawo zimadalira kumvera kwawo malamulo ake olungama. Mneneri wa Mulungu Yeremiya ananena kuti: “Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.”​—Yeremiya 10:23.

Mulungu anapanga anthu kuti azitsatira malamulo a zinthu zomwe iye analenga, monga lamulo la mphamvu yokoka ya dziko. Mofananamo, anapanga anthu kuti azitsatira malamulo a makhalidwe omwe anawapanga n’cholinga choti anthu onse akhale ogwirizana. N’chifukwa chake Mawu a Mulungu amalangiza kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako.”​—Miyambo 3:5.

Choncho, anthu sangathe kudzilamulira bwinobwino popanda ulamuliro wa Mulungu. Poyesa kukhala odzilamulira okha, anthu akhala ndi makhalidwe, chuma, magulu a ndale ndi zipembedzo zomwe zimatsutsana ndipo “wina apweteka mnzake pom’lamulira.”​—Mlaliki 8:9.

Kodi Chinalakwika N’chiyani?

Mulungu anapatsa makolo athu oyambirirawo, Adamu ndi Hava chiyambi cha moyo wangwiro. Anali ndi matupi ndi maganizo angwiro ndiponso munda wa paradaiso wokhalamo. Akanamvera lamulo la Mulungu, akanakhalabe angwiro ndi osangalala. M’kupita kwanthaŵi, akanakhala makolo a banja lonse la anthu olungama achimwemwe okhala padziko lapansi la paradaiso. Chimenecho ndicho chinali cholinga cha Mulungu kwa anthu.​—Genesis 1:27-29; 2:15.

Komabe, makolo athu oyambirirawo anagwiritsa ntchito molakwa ufulu wawo wakudzisankhira. Anaganiza molakwa kuti atha kukhala odziimira popanda Mulungu. Mwakufuna kwawo, anadumpha malire a malamulo a Mulungu. (Genesis, chaputala 3) Chifukwa chakuti anakana ulamuliro wa Mulungu, iye analibenso udindo wowachirikiza kukhalabe angwiro. ‘Anam’chitira zovunda, sanakhalebe ana ake, ndipo chirema n’chawo.’​—Deuteronomo 32:5.

Kuchokera pamene Adamu ndi Hava anakana kumvera Mulungu, thupi ndi maganizo awo zinayamba kufooka. Chitsime cha moyo chili ndi Yehova. (Salmo 36:9) Chifukwa chakuti mwamuna ndi mkazi oyambawo anasankha kupatukana ndi Yehova, anasanduka opanda ungwiro ndipo m’kupita kwanthaŵi anamwalira. (Genesis 3:19) Malinga ndi malamulo a majini, ana awo akanalandira zokhazo zomwe makolo awo anali nazo. Kodi anali ndi chiyani? Analitu ndi kupanda ungwiro ndi imfa. N’chifukwa chake mtumwi Paulo analemba kuti: “Monga uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, [Adamu] ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.”​—Aroma 5:12.

Nkhani Yaikulu Inali Ufulu Wakulamulira

Adamu ndi Hava atapanduka anakana ulamuliro wa Mulungu kapena kuti ufulu wake wa kulamulira. Yehova akanatha kuwawononga ndi kuyambiranso kupanga mwamuna ndi mkazi wina. Koma zimenezo sizikanathetsa nkhani yakuti kodi ndi ulamuliro wayani umene uli wabwino kwambiri kwa anthu. Mwa kuwapatsa mpata woti apange maboma malinga ndi maganizo awo, anthu mosakayika akanasonyeza ngati ulamuliro wodziimira popanda Mulungu uli wopambana.

Kodi mbiri ya anthu kwa zaka masauzande ambiri yavumbula chiyani? Kwa zaka mazana ambiri, anthu ayesa mitundu yambiri ya maboma, mfundo zachuma, ndale ndiponso zipembedzo. Komabe, kuipa ndi kuvutika zapitirizabe. Ndiponsotu ‘anthu oipa aipa chiipire,’ makamaka nthaŵi zathu zino.​—2 Timoteo 3:13.

Sayansi ndiponso ntchito za mafakitale zapita patsogolo kwambiri m’zaka za m’ma 1900. Komabe, panthaŵi imodzimodziyo anthu anavutika kwambiri kuposa zaka zina zonse m’mbiri ya anthu. Ndipo ngakhale atapita patsogolo motani pa zamankhwala, lamulo la Mulungu lidzakhalabe loona kuti: Anthu opatukana ndi Mulungu, amene ali chitsime chamoyo, amadwala, kukalamba, ndi kufa. Zaonekeratu kuti anthu ‘sangalongosole mapazi awo.’

Ulamuliro wa Mulungu Ukwezeka

Kwanthaŵi yonseyi, mavuto adzaoneni amene anthu akumana nawo chifukwa cha kudzilamulira popanda Mulungu asonyeza kuti ulamuliro wawo popanda iye sungapambane. Ndi ulamuliro wa Mulungu wokha umene ungabweretse chimwemwe, mgwirizano, thanzi labwino, ndi moyo. Komanso, Mawu osalephera a Yehova Mulungu, Baibulo Lopatulika, amasonyeza kuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ a ulamuliro wa anthu wodziimira popanda Mulungu. (2 Timoteo 3:1-5) Nthaŵi yomwe Yehova walola kuipa ndi kuvutika ili pafupi kutha.

Posachedwapa Mulungu alowerera m’zochita za anthu. Malemba amatiuza kuti: “Masiku a mafumu aja [maulamuliro a anthu amene alipoŵa] Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu [kumwamba] woti sudzawonongeka kunthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, [anthu sadzalamuliranso dziko lapansi] koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [maulamuliro alipoŵa], nudzakhala chikhalire.”​—Danieli 2:44.

Kutsimikizika kwa ulamuliro wa Yehova Mulungu kudzera mu Ufumu wakumwamba ndiyo mfundo yaikulu ya Baibulo. Ufumu wakumwamba ndiwo unali chiphunzitso chachikulu cha Yesu. Iye anati: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”​—Mateyu 24:14.

Pamene ulamuliro wa Mulungu ukuloŵa m’malo ulamuliro wa anthu, kodi adzapulumuka ndani ndipo sadzapulumuka ndani? Pa Miyambo 2:21, 22, pamatitsimikizira kuti: “Oongoka mtima [amene amachirikiza ulamuliro wa Mulungu] adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa [amene sachirikiza ulamuliro wa Mulungu] adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.” Atauziridwa ndi Mulungu, wamasalmo anaimba kuti: “Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka. Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”​—Salmo 37:10, 11, 29.

Dziko Latsopano Labwino Kwambiri

Mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, anthu opulumuka chimaliziro cha dongosolo la zinthu lilipoli adzaloŵa m’dziko latsopano lopanda zoipa ndi mavuto. Anthu adzalandira malangizo ochokera kwa Mulungu ndipo m’kupita kwanthaŵi “dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.” (Yesaya 11:9) Malangizo abwino olimbikitsa ameneŵa adzachititsa kuti anthu akhale pamtendere weniweni, ndiponso ogwirizana. Choncho, kudzakhala kopanda nkhondo, kuphana, chiwawa, kugwirira chigololo, kuba, kapena zoipa zina zilizonse.

Zinthu zosangalatsa kwambiri zidzakhalapo kwa anthu omvera okhala m’dziko lapansi latsopanolo la Mulungu. Zotsatira zoŵaŵa za kupandukira ulamuliro wa Mulungu zidzachotsedwa. Kupanda ungwiro, matenda, ukalamba, ndi imfa zidzakhala zinthu zakale. Baibulo limatitsimikizira kuti: “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” Malemba amalonjezanso kuti: “Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba.” (Yesaya 33:24; 35:5, 6) Zidzakhalatu zosangalatsa kwabasi kukhala ndi thanzi labwino tsiku n’tsiku​—mpaka kalekale!

Motsatira malangizo achikondi a Mulungu, anthu okhala m’dziko latsopanolo adzagwiritsa ntchito mphamvu ndi luso lawo kumanga paradaiso wapadziko lonse. Umphaŵi, njala, kusoŵa nyumba, zidzatheratu chifukwa ulosi wa Yesaya umanena kuti: “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya.” (Yesaya 65:21, 22) Ndithudi, “adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsa.”​—Mika 4:4.

Dziko lapansi lidzasintha pamene Mulungu ndi anthu omvera adzalisamala bwino. Tili ndi mawu otsimikiza a m’Malemba akuti: “Chipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti se lidzasangalala ndi kuphuka ngati duŵa . . . m’chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m’dziko loti se.” (Yesaya 35:1, 6) “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.”​—Salmo 72:16.

Bwanji nanga za anthu miyandamiyanda amene anamwalira? Onse amene Mulungu akuwakumbukira adzawaukitsa chifukwa chakuti “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) Inde, akufa adzakhalanso ndi moyo. Adzawaphunzitsa choonadi chosangalatsa chokhudza ulamuliro wa Mulungu ndipo adzawapatsa mwayi wokhala m’Paradaiso kosatha.​—Yohane 5:28, 29.

Mwa njira zimenezi, Yehova Mulungu adzasintha kotheratu mkhalidwe woopsa wa kuvutika, matenda, ndi imfa zomwe anthu avutika nazo kwa zaka masauzande ambiri. Sikudzakhalanso matenda! Sikudzakhalanso zilema! Sikudzakhalanso imfa! Mulungu “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”​—Chivumbulutso 21:3, 4.

Ndi mmenetu Mulungu adzathetsere kuvutika. Adzawononga dziko lachinyengoli ndipo adzabweretsa dongosolo latsopano la zinthu ndipo ‘m’menemo mudzakhalitsa chilungamo.’ (2 Petro 3:13) Imeneyitu ndi nkhani yabwino kwabasi! Tikulakalaka dziko latsopano limenelo. Ndipo sitichita kuliyembekezera kwanthaŵi yaitali. Malinga ndi kukwaniritsidwa kwa maulosi a Baibulo timadziŵa kuti dziko latsopano lili pafupi kwambiri ndipo kuti nthaŵi yomwe Mulungu walola anthu kuvutika ili pafupi kutha.​—Mateyu 24:3-14.

[Bokosi patsamba 8]

Kulephera kwa Ulamuliro wa Anthu

Pokambapo za ulamuliro wa anthu, Nduna Yaikulu yakale ya ku Germany a Helmut Schmidt ananena kuti: “Anthufe . . . nthaŵi zonse timalamulira bwino dzikoli pang’ono chabe koma nthaŵi zambiri timalamulira moipa kwabasi. . . . Sitinalilamulirepo mwamtendere wokhawokha.” Buku lotchedwa Human Development Report 1999 linati: “Mayiko onse akusimba za kusokonezeka kwa makhalidwe komwe kwadzetsa mavuto aakulu achikhalidwe, kuswa malamulo koŵirikiza, ndiponso chiwawa chowonjezereka panyumba. . . . Mavutoŵa akuopseza dziko lonse mowonjezereka kwambiri kuposa mphamvu za mayiko komanso zomwe mayikowo akuchita pofuna kuwathetsa.”

[Zithunzi patsamba 8]

‘Iwo adzakondwera nawo mtendere wochuluka.’​—Salmo 37:11

[Mawu a Chithunzi patsamba 5]

Chithunzi chachitatu kuchokera pamwamba, mayi ndi mwana: FAO photo/​B. Imevbore; m’munsimu, kuphulika kwa mabomba: U.S. National Archives photo