Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tamandani Yehova Chifukwa cha Ntchito Zake Zazikulu!

Tamandani Yehova Chifukwa cha Ntchito Zake Zazikulu!

Tamandani Yehova Chifukwa cha Ntchito Zake Zazikulu!

“Moyo wanga ulemekeza Ambuye . . . Chifukwa Iye Wamphamvuyo anandichitira ine zazikulu.”​—LUKA 1:46-49.

1. Kodi Yehova timam’tamanda moyenerera chifukwa cha ntchito zazikulu ziti?

YEHOVA ngoyeneradi kutamandidwa chifukwa cha ntchito zake zazikulu. Mneneri Mose atasimba za kuwomboledwa kwa Aisrayeli kuchoka ku Igupto, anati: “Maso anu anapenya ntchito yonse yaikulu ya Yehova anaichita.” (Deuteronomo 11:1-7) Mofananamo, mngelo Gabrieli atalengeza kuti Yesu adzabadwa mwa namwali Mariya, namwaliyu anati: “Moyo wanga ulemekeza Ambuye . . . chifukwa Iye Wamphamvuyo anandichitira ine zazikulu.” (Luka 1:46-49) Monga Mboni za Yehova, timam’tamanda chifukwa cha ntchito zake zazikulu monga kumasula Aisrayeli kuukapolo wa Aigupto ndi kubadwa kozizwitsa kwa Mwana wake wokondedwa.

2. (a) Kodi “chifuno chosatha” cha Mulungu kwa anthu omvera n’chotani? (b) Kodi Yohane anaona zotani pachisumbu cha Patmo?

2 Ntchito zazikulu zambiri zimene Yehova amachita n’zogwirizana ndi “chifuno [chake] chosatha” chodalitsa anthu kupyolera mwa Mesiya ndi ulamuliro wake wa Ufumu. (Aefeso 3:8-13, NW) Chifuno chimenecho chinali kukula pang’onopang’ono atalola mtumwi wokalambayo Yohane, kusuzumira pakhomo lotsegula lakumwamba m’masomphenya. Anamva mawu ngati lipenga akunena kuti: “Kwera kuno, ndipo ndidzakuonetsa zimene ziyenera kuchitika m’tsogolomo.” (Chivumbulutso 4:1) Boma la Roma litam’pitikitsa Yohane ndi kukam’ponya pa chisumbu cha Patmo, “chifukwa cha mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu,” Yohane analandira “chivumbulutso cha Yesu Kristu.” Zomwe mtumwiyo anaona ndi kuzimva zinavumbula zochuluka zokhudza chifuno chosatha cha Mulungu, motero zinaunikira mwauzimu ndi kupereka chilimbikitso chapanthaŵi yake kwa Akristu onse oona.​—Chivumbulutso 1:1, 9, 10.

3. Kodi akulu 24 omwe Yohane anawaona m’masomphenya akuimira yani?

3 Pakhomo lotsegula lakumwambalo, Yohane anaona akulu 24, atakhala m’mipando yachifumu ndiponso atavala akorona monga mafumu. Anagwa pansi pamaso pa Mulungu ndi kunena kuti: “Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.” (Chivumbulutso 4:11) Akulu amenewo akuimira Akristu onse odzozedwa omwe anaukitsidwa ndipo ali m’malo okwezeka omwe Mulungu anawalonjeza. Akusonkhezereka kutamanda Yehova chifukwa cha ntchito zake zazikulu zokhudza chilengedwe. Nafenso timazizwa ndi umboni womwe timaona wa ‘mphamvu yosatha ya Yehova ndi umulungu wake.’ (Aroma 1:20) Ndipotu tikamaphunzira zochuluka zokhudza Yehova, m’pamenenso timapeza zifukwa zambiri zomutamandira chifukwa cha ntchito zake zazikulu.

Lengezani Ntchito Zotamandika za Yehova!

4, 5. Perekani zitsanzo za mmene Davide anatamandira Yehova.

4 Wamasalmo Davide anatamanda Mulungu chifukwa cha ntchito Zake zazikulu. Mwachitsanzo, Davide anaimba kuti: “Imbirani zoyamika Yehova, wokhala ku Ziyoni; lalikirani mwa anthu ntchito zake. Ndichitireni chifundo, Yehova; penyani kuzunzika kwanga kumene andichitira ondidawo, Inu wondinyamula kundichotsa ku zipata za imfa; kuti ndibukitse lemekezo lanu lonse [ntchito zanu zonse zotamandika, NW]; pa bwalo la mwana wamkazi wa Ziyoni.” (Salmo 9:11, 13, 14) Atapereka pulani ya kachisi kwa mwana wake Solomo, Davide analemekeza ndi kutamanda Mulungu nati: “Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi kulakika, ndi chifumu ndi zanu, Yehova . . . ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse. . . . Motero tsono, Mulungu wathu, tikuyamikani ndi kulemekeza dzina lanu lokoma.”​—1 Mbiri 29:10-13.

5 Malemba akutipempha mobwerezabwereza​—inde, kutichonderera​—kutamanda Mulungu, monga momwe Davide anachitira. M’buku la Masalmo muli mawu ochuluka kwabasi otamanda Mulungu, ndipo pafupifupi theka la nyimbo zimenezi n’za Davide. Iye anali kutamanda ndi kuthokoza Yehova nthaŵi zonse. (Salmo 69:30) Kuwonjezera apo, kuchokera m’nthaŵi yakaleyo, nyimbo za Davide limodzinso ndi za anthu ena, zomwe analemba mouziridwa zagwiritsidwa ntchito potamanda Yehova.

6. Kodi Masalmo ouziridwa n’ngofunika motani kwa ife?

6 Masalmo ngofunikatu kwambiri kwa onse olambira Yehova! Pamene tikufuna kuthokoza Mulungu chifukwa cha zabwino zonse zimene akutichitira, tingalingalire za mawu osangalatsa opezeka m’Masalmo. Mwachitsanzo, titangogalamuka ndi kuona tsiku latsopano, tingagwiritse ntchito mawu ofanana ndi aŵa: “N’kokoma kuyamika Yehova, ndi kuimbira nyimbo dzina lanu, Wam’mwambamwamba Inu: kuonetsera chifundo chanu m’mamaŵa, ndi chikhulupiriko chanu usiku uliwonse. . . . Popeza Inu, Yehova, munandikondweretsa ndi kuchita kwanu. Ndidzafuula mokondwera pa ntchito ya manja anu.” (Salmo 92:1-4) Titagonjetsa cholepheretsa kupita kwathu patsogolo mwauzimu, sitingachitire mwina, koma kusonyeza chimwemwe ndi kuthokoza kwathu m’pemphero, monga momwe wamasalmo anachitira pamene anaimba kuti: “Tiyeni tiyimbire Yehova mokondwera; tifuule kwa thanthwe la chipulumutso chathu. Tidze nacho chiyamiko pamaso pake, tim’fuulire Iye mokondwera ndi masalmo.”​—Salmo 95:1, 2.

7. (a) Kodi chochititsa chidwi n’chiyani ndi nyimbo zambiri zomwe Akristu timaimba? (b) Kodi pali chifukwa chiti chofikira mofulumira pa misonkhano ndi kukhalapobe mpaka pamapeto?

7 Nthaŵi zonse timaimba nyimbo zotamanda Yehova pa misonkhano yampingo, misonkhano ikuluikulu, ndi misonkhano yachigawo. Chochititsa chidwi n’chakuti zochuluka mwa nyimbo zimenezi n’zochokera m’malingaliro ouziridwa a m’buku la Masalmo. Ndifetu okondwa kwabasi kukhala ndi buku la nyimbo zamakono zokhudza mtima zotamanda Yehova! Kuimba nyimbo zotamanda Mulungu n’chifukwa chabwino kwabasi chofikira mofulumira pamisonkhano yathu ndi kukhalapobe kufikira kumapeto, mwakutero tikumatamanda Yehova m’nyimbo ndi pemphero limodzi ndi olambira anzathu.

“Tamandani Ya, Anthu Inu!”

8. Kodi mfundo yaikulu m’mawu akuti “Haleluya” n’njotani, nanga kodi amatanthauzanji?

8 Mfundo yaikulu m’mawu akuti “Haleluya,” ndiyo kutamanda Yehova. Mawu ameneŵa anatengedwa ku liwu lachihebri lomwe limatanthauza kuti “Tamandani Ya, anthu inu.” Mwachitsanzo pa Salmo 135:1-3, timapezapo pempho lachikondi koma lamphamvu lakuti: “Haleluya! Lemekezani dzina la Yehova; lemekezani inu atumiki a Yehova: inu akuimirira m’nyumba ya Yehova, m’mabwalo a nyumba ya Mulungu wathu. Lemekezani Yehova; pakuti Yehova ndiye wabwino; muimbire zolemekeza dzina lake; pakuti n’kokondweretsa kutero.”

9. N’chiyani chimatisonkhezera kutamanda Yehova?

9 Tikamalingalira ntchito zodabwitsa za Mulungu m’chilengedwe ndi zomwe akutichitira, kuyamikira kochokera pansi pamtima kumatisonkhezera kum’tamanda. Tikamaganiza mozama za zinthu zozizwitsa zimene Yehova anachitira anthu ake m’nthaŵi zam’mbuyomu, mitima yathu imatisonkhezera kumuyamika. Ndipo tikamasinkhasinkha za malonjezo a zinthu zodabwitsa zimene Yehova adzachite m’tsogolo, timafufuza njira zom’tamandira ndi kumuthokoza.

10, 11. Kodi kukhalapo kwathu kwenikweniko kumatipatsa motani chifukwa chotamandira Mulungu?

10 Kukhalapo kwathu kwenikweniku kumatipatsa chifukwa chokwanira chotamandira Ya. Davide anaimba kuti: “Ndikuyamikani [Yehova] chifukwa kuti chipangidwe changa n’choopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu n’zodabwitsa; moyo wanga uchidziŵa ichi bwino ndithu.” (Salmo 139:14) Inde, ‘tinapangidwa modabwitsa’ ndipo tili ndi mphatso zamtengo wapatali monga kutha kuona, kumva, ndi kuganiza mwaluso. Kodi si kwabwino kuchita zinthu m’moyo wathu m’njira yotamanda Mlengi wathu? Paulo anatchulanso mfundo yomweyo pamene analemba kuti: “Mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.”​—1 Akorinto 10:31.

11 Tidzachita chilichonse ku ulemerero wa Yehova ngati timamukondadi. Yesu anati lamulo loyamba n’lakuti: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse.” (Marko 12:30; Deuteronomo 6:5) Inde tiyeneradi kukonda Yehova ndi kumutamanda monga Mlengi wathu ndi Wopatsa “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro.” (Yakobo 1:17; Yesaya 51:13; Machitidwe 17:28) Tiyeneradi kutero, chifukwa chakuti luntha lathu la kulingalira, uzimu wathu, ndi mphamvu zathupi lathu​—mikhalidwe ndi maluso athu onse​—n’zochokera kwa Yehova. Monga Mlengi wathu, iye ndiyedi woyenerera chikondi ndi kutamanda kwathu.

12. Kodi m’mamva bwanji mukaganiza za ntchito zazikulu za Yehova ndi mawu a pa Salmo 40:5?

12 Ntchito zazikulu za Yehova zimatipatsa zifukwa zosaŵerengeka zomukondera ndi kumutamanda! Davide anaimba kuti: “Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita n’zambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziŵerenga.” (Salmo 40:5) Davide sanathe kuŵerenga zodabwitsa zonse za Yehova, ndipotu nafenso sitingathe kuziŵerenga. Koma tiyenera kutamanda Yehova nthaŵi zonse tikakumbukira iliyonse ya ntchito zake zazikulu.

Ntchito Zogwirizana ndi Chifuno Chosatha cha Mulungu

13. Kodi chiyembekezo chathu chikugwirizana motani ndi ntchito zazikulu za Mulungu?

13 Chiyembekezo chathu cha m’tsogolo n’chogwirizana kwambiri ndi ntchito zodabwitsa ndi zotamandika zogwirizana ndi chifuno chosatha cha Mulungu. Pambuyo pa kupanduka kwa anthu mu Edene, Yehova anapereka ulosi woyambirira wopatsa chiyembekezo. Popereka chiŵeruzo kwa njoka, Mulungu anati: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.” (Genesis 3:15) Anthu okhulupirika anapitirizabe kuyembekezera Mbewu ya mkazi yolonjezedwayo, pambuyo pakuti Yehova wachita zazikulu mwa kupulumutsa Nowa ndi banja lake pa Chigumula chadziko lonse chomwe chinawonongeratu anthu oipa. (2 Petro 2:5) Malonjezo aulosi operekedwa kwa amuna okhulupirika monga Abrahamu ndi Davide anapereka chidziŵitso chowonjezeka cha zomwe Yehova adzakwaniritse kudzera m’Mbewu imeneyo.​—Genesis 22:15-18; 2 Samueli 7:12.

14. Kodi n’chitsanzo chapamwamba chiti cha zodabwitsa zazikulu zomwe Yehova anachitira mtundu wa anthu?

14 Chionetsero chapamwamba cha Yehova monga wochitira mtundu wa anthu zinthu zazikulu chinachitika pamene anapereka Mwana wake wobadwa yekha​—Mbewu yolonjezedwayo, Yesu Kristu​—monga nsembe ya dipo. (Yohane 3:16; Machitidwe 2:29-36) Dipo linapereka maziko oyanjanira ndi Mulungu. (Mateyu 20:28; Aroma 5:11) Yehova anasonkhanitsa oyanjanitsidwa oyambirirawo mumpingo wachikristu, umene anaukhazikitsa pa Pentekoste mu 33 C.E. Ndi thandizo la mzimu woyera, analalikira uthenga wabwino m’madera ambiri, kusonyeza mmene imfa ya Yesu ndi kuuka kwake zinatsegulira njira kuti anthu okhulupirika akalandire madalitso osatha mu ulamuliro wa Ufumu wakumwamba wa Mulungu.

15. Kodi Yehova wachita motani zozizwitsa m’nthaŵi yathu ino?

15 M’tsiku lathu lino, Yehova wasonkhanitsa Akristu odzozedwa otsiriza modabwitsa zedi. Anaimitsa mphepo zachiwonongeko kufikira otsalira a 144,000, omwe adzalamulira limodzi ndi Kristu kumwamba atasindikizidwa chizindikiro. (Chivumbulutso 7:1-4; 20:6) Mulungu waonetsetsa kuti Akristu odzozedwa amasulidwa mu ukapolo wauzimu mu “Babulo Wamkulu,” ufumu wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga. (Chivumbulutso 17:1-5) Kodi kuwomboledwa kumeneko m’chaka cha 1919 limodzi ndi chitetezo cha Mulungu chomwe akulandira kuchokera m’nthaŵiyo zathandiza otsalira odzozedwawo kuchitanji? Zawathandiza kuwala popereka umboni wotsiriza, Yehova asanawononge dongosolo la zinthu la Satana loipali pa “chisautso chachikulu” chomwe chikuyandikira mofulumiracho.​—Mateyu 24:21; Danieli 12:3; Chivumbulutso 7:14.

16. Kodi chikuchitika n’chiyani monga zotsatira za ntchito yamakono yolalikira Ufumu padziko lonse?

16 Mboni zodzozedwa za Yehova zatsogolera mwachangu ntchito yapadziko lonse yolalikira za Ufumu. Zotsatira zake n’zakuti, chiŵerengero cha “nkhosa zina” zomwe zikulambira Yehova tsopano chikuwonjezeka. (Yohane 10:16) Tikukondwera kuti mwayi ulipobe wakuti odzichepetsa apadziko lapansi agwirizane nafe potamanda Yehova. Amene akuvomera kuitana koti “idzani” akuyembekezera kupulumuka pa chisautso chachikulu, ndiponso ali ndi chiyembekezo chodzatamanda Yehova kwamuyaya.​—Chivumbulutso 22:17.

Anthu Zikwizikwi Akukhamukira ku Kulambira Koona

17. (a) Kodi Yehova akuchita motani zodabwitsa kumbali ya ntchito yathu yolalikira? (b) Kodi Zekariya 8:23 akukwaniritsidwa motani?

17 Tsopano Yehova akuchita zinthu zazikulu ndi zotamandika zokhudzana ndi ntchito yathu yolalikira. (Marko 13:10) M’zaka zaposachedwapa, iye ‘watsegula makomo akuluakulu a kuntchito.’ (1 Akorinto 16:9) Zimenezi zachititsa kuti uthenga wabwino ulengezedwe m’magawo akuluakulu komwe poyamba adani a choonadi anali atatseka njira. Ambiri omwe poyamba anali mumdima wauzimu tsopano avomera kuitana ndi kudza kudzalambira Yehova. Akukwaniritsa mawu aulosi aŵa akuti: “Atero Yehova wa makamu: Kudzachitika masiku awo amuna khumi adzagwira, ndiwo a manenedwe onse a amitundu, inde adzagwira mkawo wa munthu ali Myuda, ndi kuti, Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.” (Zekariya 8:23) Amuna khumiwo akuuza Ayuda auzimu, otsalira a Akristu odzozedwa amakono kuti “tidzamuka nanu”. Popeza kuti khumi angaimire kukwanira kwa padziko lapansi, “amuna khumi” ameneŵa akuimira “khamu lalikulu” limene analigwirizanitsa ndi “Israyeli wa Mulungu,” kupanga “gulu limodzi.” (Chivumbulutso 7:9, 10; Agalatiya 6:16) Tikukondwera kwabasi kuona ochuluka otereŵa tsopano akuchitira limodzi utumiki wopatulika monga olambira a Yehova Mulungu!

18, 19. Kodi pali umboni wotani wakuti Yehova akudalitsa ntchito yolalikira?

18 Tikunyadira kuti masauzande, inde anthu zikwi mazanamazana akulandira kulambira koona m’mayiko omwe kale anali oumirira kwambiri chipembedzo chonyenga mwakuti zinkaoneka ngati kuti anthuwo sadzalandira uthenga wabwino. Tangotengani Yearbook of Jehovah’s Witnesses yatsopano, ndipo muŵerenge mayiko omwe akusonyeza chiŵerengero cha olengeza Ufumu kuyambira 100,000 mpaka pafupifupi 1,000,000. Ndi umbonitu wamphamvu umenewu wakuti Yehova akudalitsa ntchito yolengeza Ufumu.​—Miyambo 10:22.

19 Monga anthu a Yehova, tikutamanda ndi kuthokoza Atate wathu wakumwamba potipatsa chifuno chenicheni m’moyo, ntchito yopindulitsa muutumiki wake, ndi chiyembekezo chabwino cha m’tsogolo. Tikuyembekezera mwatcheru kukwaniritsidwa kwa malonjezo onse a Mulungu ndipo ndife otsimikiza mtima ‘kudzisunga tokha m’chikondi cha Mulungu, ndi kulindira kufikira moyo wosatha.’ (Yuda 20, 21) Tikukondwera kwabasi kuona khamu lalikulu lomwe likutamanda Yehova tsopano litakwana pafupifupi 6,000,000! Chifukwa cha madalitso oonekeratu a Yehova, otsalira odzozedwa limodzi ndi anzawo a nkhosa zina akusonkhana mogwirizana m’mipingo pafupifupi 91,000 m’mayiko 235. Tonsefe tikudya bwino zedi mwauzimu kupyolera m’khama losatopa la “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45) Gulu lateokalase lopita patsogololi, likuyang’anira mwachikondi, ndi kuyendetsa ntchito za Ufumu kudzera m’maofesi a nthambi a Mboni za Yehova okwana 110. Tikuthokoza kwambiri kuti Yehova wasonkhezera mitima ya anthu ake kuti ‘amulemekeze ndi chuma chawo.’ (Miyambo 3:9, 10) Padakali pano, ntchito yathu yolalikira yapadziko lonse ikupitirizabe, mwakuti nyumba zosindikizira mabuku, nyumba za Beteli ndi za a mishonale, Nyumba za Ufumu, ndi Nyumba za Misonkhano zikumangidwa komwe zikufunika.

20. Kodi kulingalira ntchito zazikulu ndi zotamandika za Yehova kuyenera kutikhudza motani?

20 Sitingathe kutchula mndandanda wonse wa zinthu zazikulu ndi zotamandika zomwe Atate wathu wakumwamba wachita. Koma kodi wowongoka mtima aliyense angangokhala duu osagwirizana ndi namtindi wa olambira a Yehova? Ndithudi ayi! Choncho, onse okonda Mulungu afuule mokondwera kuti: “Haleluya. Lemekezani Yehova kochokera kumwamba; mlemekezeni m’misanje. Mlemekezeni, angelo ake onse; . . . Anyamata ndiponso anamwali; okalamba pamodzi ndi ana: Alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka; ulemerero wake uli pamwamba pa dziko lapansi ndi thambo.” (Salmo 148:1, 2, 12, 13) Inde, tsopano lino ndi kunthaŵi zanthaŵi, tiyeni tonse titamande Yehova chifukwa cha ntchito zake zazikulu!

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi zina mwa ntchito zotamandika za Yehova ndi ziti?

• N’chifukwa chiyani mwasonkhezereka kutamanda Yehova?

• Kodi chiyembekezo chathu chikugwirizana motani ndi ntchito zodabwitsa za Mulungu?

• Kodi Yehova akuchita motani ntchito zotamandika mogwirizana ndi ntchito yolengeza Ufumu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi mumaimba nawo ndi mtima wonse nyimbo zotamanda Yehova?

[Zithunzi patsamba 13]

Tikunyadira kuti mwayi udakalipo wakuti ofatsa agwirizane nafe potamanda Yehova