Kodi Kuphunzira Baibulo Kuli Ndi Phindu Lililonse M’moyo Wanu?
Kodi Kuphunzira Baibulo Kuli Ndi Phindu Lililonse M’moyo Wanu?
“MUSALIŴERENGE popanda wansembe.” Limeneli ndi chenjezo lomwe lili koyambirira kwa mabaibulo ena a Akatolika. Mayi wina wotchedwa Kay Murdy wa pa sukulu ya Catholic Bible Institute ku Los Angeles, ananena kuti: “Ife Akatolika, takhala tilibe mwayi wokhala ndi Baibulo, koma zimenezi zikusintha tsopano.” Iye anawonjezera kuti, Akatolika amati akadziŵa mmene Malemba Opatulika angakhudzire moyo wawo, “amalifunitsitsa kwambiri Baibulo.”
Pankhani ya kusintha kumeneku, magazini yotchedwa U.S. Catholic inagwira mawu a wamkulu wamaphunziro achipembedzo yemwe ananena kuti, Akatolika amene amaphunzira Baibulo m’kalasi amaona kuti “anali kumanidwa zambiri ndipo amazindikira kuti m’Baibulo muli chuma chambiri chauzimu. Iwo amafuna atapeza chuma chauzimu chomwe anali kumanidwacho.”
Mulimonse mmene zilili, kodi wophunzira Baibulo angapeze “chuma” chotani chauzimu? Talingalirani izi: Kodi mungakonde kudziŵa mmene mungathetsere nkhaŵa za tsiku ndi tsiku? Kodi mtendere m’banja mungausungebe motani? N’chifukwa chiyani mwano ndi kupanda khalidwe zachuluka chonchi? Kodi chimachititsa achinyamata amasiku ano kukhala achiwawa n’chiyani? Mayankho odalirika a mafunso ameneŵa ndiponso ena owiritsa mutu angapezeke m’Mawu a Mulungu, Baibulo, ndipo angakhaledi “chuma” chenicheni osati kwa Akatolika kapena a Pulotesitanti okha komanso kwa Abuda, Ahindu, Asilamu, Ashinto, ngakhalenso kwa okana Mulungu ndi okhulupirira kuti Mulungu n’ngosadziŵika. Monga wamasalmo ananenera, ‘mawu a Mulungu ndiwo anali nyali ya kumapazi ake, ndi kuunika kwa panjira pake.’ Zingakhalenso chimodzimodzi kwa inuyo.—Salmo 119:105.