Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungakhulupirire Miyezo ya Ndani?

Kodi Mungakhulupirire Miyezo ya Ndani?

Kodi Mungakhulupirire Miyezo ya Ndani?

Mlendo wina atabwera ku Africa kwanthaŵi yake yoyamba anachita chidwi kuona munthu ali chilili m’mphepete mwa msewu. Mlendoyo anaona kuti m’mphindi zingapo zilizonse munthuyo anali kusendeza mapazi ake ndi kusuntha pang’ono koma ali chiimire. Zinam’tengera nthaŵi ndithu kuti azindikire chifukwa chomwe munthuyo ankasunthira chotero. Iye kwenikweni anali kulondola mthunzi wa mtengo wanthambo za telefoni. Mthunziwo unali kusuntha pang’onopang’ono dzuŵa likamasendera.

MOFANANA ndi mthunzi womwe umasuntha chifukwa cha dzuŵa, zochita za anthu ndi miyezo yawo zikusuntha komanso kusintha nthaŵi ndi nthaŵi. Mosiyana ndi zimenezo, Yehova Mulungu “Atate wa mauniko,” sasinthika. Wophunzira Yakobo analemba za iye kuti “amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.” (Yakobo 1:17) Mneneri wachihebri Malaki analemba mawu a Yehova weniweniyo akuti: “Ine Yehova sindisinthika.” (Malaki 3:6) Mulungu anauza mtundu wa Israyeli m’nthaŵi ya Yesaya kuti: “Ngakhale mpaka mudzakalamba Ine ndine, ndipo ngakhale mpaka tsitsi laimvi, Ine ndidzakusenzani inu; ndalenga.” (Yesaya 46:4) Choncho, kupita kwa nthaŵi sikusintha kudalira kwathu malonjezo a Wamphamvuyonse.

Kutengerapo Phunziro pa Chilamulo

Monga momwe malonjezo a Yehova alili odalirika ndi osasinthika momwemonso miyezo yake ya chabwino ndi choipa. Kodi mungakhulupirire munthu wamalonda amene akugwiritsa ntchito sikero ziŵiri zomwe imodzi yokha ndiyo yolondola? Ndithudi simungatero. Mofananamo, “muyeso wonyenga unyansa Yehova; koma mulingo wamphumphu um’sekeretsa.” (Miyambo 11:1; 20:10) Chilamulo chomwe Yehova anapatsa Aisrayeli, chinalinso ndi lamulo ili: “Musamachita chisalungamo poweruza mlandu, poyesa utali wake, kulemera kwake, kapena kuchuluka kwake. Mukhale nacho choyesera choona, miyeso yoona, efa woona, hini woona; ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m’dziko la Aigupto.”​—Levitiko 19:35, 36.

Kumvera lamulo limeneli kunachititsa Mulungu kuyanja Aisrayeli ndipo anapindula zinthu zambiri pa moyo wawo. Momwemonso, kutsatira miyezo yosasintha ya Yehova osati poyeza zinthu pokha komanso m’mbali zonse za moyo, kumabweretsa madalitso kwa wolambira amene amam’khulupirira. Mulungu ananena kuti: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.”​—Yesaya 48:17.

N’chifukwa Chiyani Miyezo Ikuchepa Mphamvu Masiku Ano?

Baibulo limatchula chifukwa chake miyezo ikuchepa mphamvu masiku ano. Buku lomalizira la Baibulo, Chivumbulutso, limafotokoza za nkhondo kumwamba, yomwe zotsatira zake zakhudza anthu onse mpaka lerolino. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Munali nkhondo m’mwamba. Mikayeli ndi angelo ake akuchita nkhondo ndi chinjoka, chinjokanso ndi angelo ake chinachita nkhondo; ndipo sichinalakika, ndipo sanapezekanso malo awo m’mwamba. Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.”​—Chivumbulutso 12:7-9.

Kodi zotsatira zanthaŵi yomweyo za nkhondoyo zinali zotani? Yohane akupitiriza kuti: “Chifukwa chake, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtundu ndi nyanja, chifukwa mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kam’tsalira kanthaŵi.”​—Chivumbulutso 12:12.

‘Tsoka la dziko’ linadza pamene nkhondo yoyamba ya padziko lonse inaulika mu 1914 ndi kuthetsa nyengo za miyezo yomwe inali yosiyana kwambiri ndi ya masiku ano. Wolemba mbiri wina wotchedwa Barbara Tuchman ananena kuti, “Nkhondo Yaikulu ya 1914-​18 inali ngati malire a nyengo yakale ndi yathu ino. Mwa kupha anthu ambiri amene akanathandiza pantchito m’zaka zotsatira, mwa kuwononga zikhulupiriro, kusintha malingaliro a anthu, ndiponso kusiya zilonda zosachiritsika za kukhumudwa, nkhondoyo inasintha kwambiri zinthu ndiponso maganizo omwe anthu anali nawo nkhondoyo isanachitike ndi pambuyo pake.” Wolemba mbiri winanso wotchedwa Eric Hobsbawm anavomereza kuti: “Kuyambira mu 1914, miyezo yomwe kale ankaiona monga yabwino m’mayiko otukuka yatha mphamvu kwambiri . . . N’kovuta kumvetsa mmene zinthu zasinthira mofulumira kwambiri kubwereranso ku miyezo yomwe makolo athu a m’zaka za m’ma 1800 ayenera kuti ankaiona kukhala yotsalira.”

M’buku lake lotchedwa Humanity​—A Moral History of the Twentieth Century, wolemba bukuli Jonathan Glover anati: “Chizindikiro china cha nthaŵi yathu ino ndicho kutha kwa malamulo amakhalidwe abwino.” Popeza kuti akukayikira kwambiri malamulo a makhalidwe abwino ochokera kwa anthu wamba, chifukwa cha kuloŵa pansi kwa chipembedzo ku mayiko a azungu, iye anachenjeza kuti: “Ife amene sitikhulupirira chipembedzo kutha kwa malamulo a makhalidwe abwino kuyenera kutidetsabe nkhaŵa.”

Kugwiritsidwa mwala kwamakono kaya m’zamalonda, ndale, chipembedzo, zaumwini, ndiponso za banja, komanso zotsatira zake zochititsa mantha, zili mbali ya cholinga cha Mdyerekezi chobweretsa tsoka kwa anthu okhala padziko lapansi. Satana ali wotsimikiza kwambiri kumenyabe nkhondo yake mpaka mapeto, kufunafuna onse amene akuyesetsa kutsatira miyezo ya Mulungu kuti akawonongeke naye limodzi.​—Chivumbulutso 12:17.

Kodi pali njira yothetsera kugwiritsidwa mwala kofalaku? Mtumwi Petro akuyankha kuti: “Monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13) Lonjezo limenelo tingalikhulupirire osati chifukwa chakuti Mulungu ali ndi mphamvu zokwaniritsira cholinga chake komanso kuti watsimikiza kuti zimenezi zidzachitikadi. Ponenapo za ‘mawu alionse otuluka m’kamwa mwake,’ Yehova anati: “Sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.” Lonjezo lodalirikatu kwambiri!​—Yesaya 55:11; Chivumbulutso 21:4, 5.

Kutsatira Miyezo ya Mulungu

M’dziko la miyezo yosinthasintha ndiponso yomacheperachepera mphamvu, Mboni za Yehova zimayesetsa kutsatira miyezo ya makhalidwe imene Baibulo limapereka. Zotsatira zake n’zakuti, iwo amakhala osiyana ndi anthu ambiri ndipo kaŵirikaŵiri zimenezi zimachititsa ena kuchita nawo chidwi komanso kudana nawo.

Pamsonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova ku London, mtolankhani wa wailesi yakanema ina anafunsa wolankhulira msonkhanowo ngati Mboni za Yehova zilidi Akristu. Iye anayankha kuti: “Inde, ndifedi Akristu chifukwa chakuti Yesu ndiye chitsanzo chathu. Dzikoli ladzala ndi kudzikonda, ndipo ife timaika maganizo kwambiri kwa Yesu Kristu monga njira, choonadi, ndi moyo. Timakhulupirira kuti iye ali Mwana wa Mulungu osati mbali ya Utatu. Choncho, Baibulo timalimva mosiyana ndi chipembedzo chilichonse chotchuka.”

Pamene nkhaniyi anali kuiulutsa pa wailesi yakanema ya BBC, mtolankhaniyo anamaliza pulogalamuyo mwa kunena kuti: “Ndaphunzira zambiri zokhudza chifukwa chimene Mboni za Yehova zimagogodera m’makomo mwathu. Ndipo sindinaonepo anthu ovala bwino okwana 25,000 ndiponso a khalidwe labwino atakhalira pamodzi, nthaŵi imodzi.” Umbonitu wabwino kwabasi kuchokera kwa munthu yemwe si Mboni wosonyeza kuti n’kwanzeru kutsatira miyezo yosasintha ya Mulungu!

Ngakhale kuti ena angagwe ulesi ndi mfundo yotsatira miyezo imene sanapange okha, tikukulimbikitsani kuŵerenga m’Baibulo lanu kuti mudziŵe miyezo ya Mulungu. Koma musakhutire ndi kungopenda chabe pamwamba. Tsatirani malangizo a mtumwi Paulo akuti: “Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Pitani ku Nyumba ya Ufumu yakwanuko ndipo kaonaneni ndi Mboni kumeneko. Mukadzionera nokha kuti iwo ndi anthu amene amakhulupirira malonjezo a m’Baibulo ndipo amasonyeza kudalira kwawo Mulungu mwa kuyesetsa kutsatira miyezo yake.

Kutsatirabe miyezo yosasintha ndiponso yodalirika ya Mulungu pa moyo wanu mosakayikira kudzakubweretserani madalitso. Labadirani mawu a Mulungu akuti: “Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.”​—Yesaya 48:18.

[Zithunzi patsamba 5]

Masiku ano anthu akugwiritsidwa mwala pa nkhani za malonda, ndale, zachipembedzo, ndiponso za m’banja