Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Poti Yehova ali wofunitsitsa kukhululukira machimo kudzera mu nsembe ya dipo, n’chifukwa chiyani kuli kofunika kwa Akristu kuulula machimo awo kwa akulu mu mpingo?

Nkhani ya Davide ndi Bateseba ikusonyeza kuti ngakhale tchimo la Davide linali loopsa, Yehova anam’khululukira chifukwa chakuti Davideyo analapadi moona mtima. Pamene mneneri Natani anam’funsa za nkhaniyo, Davide anavomereza kuti: “Ndinachimwira Yehova.”​—2 Samueli 12:13.

Ngakhale kuti Yehova amavomereza kulapa ndi mtima wonse ndipo amakhululuka, amakonzanso njira yothandiza wochimwayo kuchira mwauzimu. Kwa Davide, thandizolo linadzera mwa mneneri Natani. Masiku ano, m’mipingo yachikristu muli amuna achikulire okhwima mwauzimu, kapena akulu. Wophunzira Yakobo anati: “Pali wina kodi adwala [mwauzimu] mwa inu? Adziitanire akulu a mpingo, ndipo apemphere pa iye, atam’dzoza ndi mafuta m’dzina la Ambuye: ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye.”​—Yakobo 5:14, 15.

Akulu aluso angathandize kwambiri kuthetsa kupwetekedwa mtima kwa wochimwa wolapa. Amayesetsa kutsanzira Yehova pothandiza wochimwa. Safuna kuchita mwankhanza ngakhale pamene uphungu wamphamvu ukufunika. Koma mwachifundo, amaona zomwe munthuyo akufunikira panthaŵiyo. Amayesetsa kukonza maganizo a wolakwayo modekha pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu. (Agalatiya 6:1) Ngakhale pamene munthu sanakaulule yekha tchimo lake, angasonkhezereke kulapa pamene akulu akamba naye, monga anachitira Davide pamene Natani anam’lankhula za tchimo lake. Choncho, thandizo la akulu limathandiza wolakwayo kupeŵa kulibwereza tchimolo ndi kuzoloŵera kulichita.​—Ahebri 10:26-31.

Kuulula machimo ochititsa manyazi kwa ena ndi kupempha kukhululukidwa n’kovuta. Kumafuna kulimba mtima. Taganizani pang’ono za mbali inayo. Mwamuna wina yemwe analephera kuulula tchimo lake loopsa kwa akulu kumpingo anati: “Nthaŵi zonse ndinkamva kupweteka mumtima. Ndinalimbikira kulalikira, koma sindinamvebe bwino.” Anaganiza kuti kuulula machimo kwa Mulungu m’pemphero n’kokwanira, koma zinaoneka kuti sikokwanira chifukwa ankamva monga anamvera Mfumu Davide. (Salmo 51:8, 11) Ndi bwinotu kwambiri kuvomereza thandizo lachikondi lomwe Yehova amapereka kudzera mwa akulu!