Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalanibe Osasunthika Ngati Oona Wosaonekayo!

Khalanibe Osasunthika Ngati Oona Wosaonekayo!

Khalanibe Osasunthika Ngati Oona Wosaonekayo!

“[Mose] anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo.”​—AHEBRI 11:27.

1. Kodi ndi mawu osaiŵalika ati onena za Mulungu omwe Yesu anatchula mu Ulaliki wa pa Phiri?

YEHOVA ndi Mulungu wosaoneka. Mose atapempha kuti aone ulemerero Wake, Yehova anayankha kuti: “Sungathe kuona nkhope yanga; pakuti palibe munthu adzandiona ine ndi kukhala ndi moyo.” (Eksodo 33:20) Ndipo mtumwi Yohane analemba kuti: “Kulibe munthu anaona Mulungu nthaŵi zonse.” (Yohane 1:18) Ngakhalenso Yesu Kristu ali padziko lino lapansi monga munthu, sanathe kuona Mulungu. Komabe, mu Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu anati: “Odala ali oyera mtima; chifukwa adzaona Mulungu.” (Mateyu 5:8) Kodi Yesu anatanthauzanji?

2. N’chifukwa chiyani sititha kuona Mulungu ndi maso athu enieniwa?

2 Malemba amasonyeza kuti Yehova ndi Mzimu wosaoneka. (Yohane 4:24; Akolose 1:15; 1 Timoteo 1:17) Choncho,Yesu sanatanthauze kuti anthufe tingaone Yehova ndi maso athu enieniwa ayi. N’zoona kuti Akristu odzozedwa adzaona Yehova Mulungu kumwamba ataukitsidwa ndi matupi auzimu. Koma anthu “oyera mtima” omwenso ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi kosatha amathanso ‘kumuona’ Mulungu. Kodi zimenezi zimatheka bwanji?

3. Kodi anthu angazindikire motani ina mwa mikhalidwe ya Mulungu?

3 Timaphunzira zambiri zokhudza Yehova mwa kupenda mosamalitsa zinthu zimene analenga. Tikatero timachita chidwi ndi mphamvu zake ndipo timasonkhezereka kum’zindikira monga Mulungu ndi Mlengi. (Ahebri 11:3; Chivumbulutso 4:11) Pambali imeneyi, mtumwi Paulo analemba kuti: “Chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka [za Mulungu] ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake.” (Aroma 1:20) Chotero mawu a Yesu onena za kuona Mulungu akuphatikizapo kutha kuzindikira ina ya mikhalidwe ya Yehova. Kuona kumeneku n’kozikidwa pa chidziŵitso cholondola ndipo timaona mwauzimu ndi “maso a mitima.” (Aefeso 1:18) Mawu ndi zochita za Yesu zimasonyezanso zambiri zokhudza Mulungu. N’chifukwa chake Yesu anati: “Iye amene wandiona Ine waona Atate.” (Yohane 14:9) Yesu anasonyeza umunthu wonse wa Yehova. Chotero, kudziŵa moyo wa Yesu ndi ziphunzitso zake kungatithandize kuona, kapena kuti kuzindikira, ina mwa mikhalidwe ya Mulungu.

Uzimu Ndi Wofunika

4. Kodi ambiri amasonyeza motani kupereŵera kwa uzimu lerolino?

4 Lerolino, chikhulupiriro ndi uzimu weniweni n’zochepa kwambiri. “Si onse ali nacho chikhulupiriro,” anatero Paulo. (2 Atesalonika 3:2) Ambiri ngotanganidwa kwambiri ndi ntchito zaumwini ndipo alibe chikhulupiriro mwa Mulungu. Mikhalidwe yawo yauchimo ndi kusoŵa kwawo mkhalidwe wauzimu zimawalepheretsa kumuona ndi maso a kuzindikira, pakuti mtumwi Paulo analemba kuti: “Iye wakuchita choipa sanamuona Mulungu.” (3 Yohane 11) Popeza kuti anthu otereŵa saona Mulungu ndi maso enieni, amachita zinthu ngati kuti iye sangaone zimene akuchitazo. (Ezekieli 9:9) Amapeputsa zinthu zauzimu, chotero sangathe “kum’dziŵadi Mulungu.” (Miyambo 2:5) Moyenerera, Paulo analemba kuti: “Munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu; pakuti aziyesa zopusa; ndipo sakhoza kuzizindikira, chifukwa ziyesedwa mwauzimu.”​—1 Akorinto 2:14.

5. Kodi anthu okonda zauzimu amadziŵa mfundo iti?

5 Komatu ngati timakonda zauzimu, tidzazindikira nthaŵi zonse kuti ngakhale kuti Yehova si Mulungu wofufuza zolakwa za anthu, amadziŵa ngati tikuchita zinthu motsatira malingaliro kapena zilakolako zathu zoipa. Ndithudi, “njira za munthu zili pamaso pa Yehova, asinkhasinkha za mayendedwe ake onse.” (Miyambo 5:21) Tikachita tchimo, timasonkhezereka kulapa ndi kupempha Yehova kuti atikhululukire chifukwa chakuti timam’konda ndipo sitifuna kumukhumudwitsa.​—Salmo 78:41; 130:3.

Kodi Chimatipangitsa Kukhalabe Osasunthika N’chiyani?

6. Kodi kukhalabe osasunthika n’kutani?

6 Ngakhale kuti Yehova sitingathe kumuona ndi maso athuŵa, nthaŵi zonse tizikumbukira kuti iyeyo amationa. Kudziŵa kuti alipo ndi kukhulupirira kuti ali pafupi ndi onse oitanira pa iye kudzatithandiza kukhalabe osasunthika​—amphumphu ndi osagwedera m’kukhulupirika kwathu. (Salmo 145:18) Tikatero tingakhale ngati Mose amene ponena za iye Paulo analemba kuti: “Ndi chikhulupiriro anasiya Aigupto, wosaopa mkwiyo wa mfumu; pakuti anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo.”​—Ahebri 11:27.

7, 8. Kodi chinam’limbitsa mtima Mose pamaso pa Farao n’chiyani?

7 Pogwira ntchito imene Mulungu anam’patsa yotsogolera Aisrayeli kuchoka kuukapolo ku Igupto, mobwerezabwereza Mose anaonekera kwa Farao wouma mtima uja m’bwalo lachifumu lokhala ndi akuluakulu achipembedzo ndi ankhondo ambiri. Mosakayika konse, m’makoma a nyumba yachifumuyo anapachikamo kapena kujambula mafano. Koma Yehova, ngakhale kuti ngosaoneka, anali weniweni kwa Mose, mosiyana ndi mafano onsewo oimira milungu yopanda moyo ya Igupto. N’chifukwa chaketu Mose sanachite naye mantha Farao!

8 N’chiyani chinam’limbitsa mtima Mose kukaonekera kwa Farao mobwerezabwereza? Malemba amatiuza kuti “Munthuyu Mose ndiye wofatsa woposa anthu onse a pa dziko lapansi.” (Numeri 12:3) Mwachionekere, uzimu wake wolimba ndi kutsimikiza kuti Mulungu anali naye zinapatsa Mose mphamvu zofunika kuti akaimire “Wosaonekayo” pamaso pa mfumu yopanda chifundo ya Igupto. Kodi amene ‘amaona’ Mulungu wosaonekayo amasonyeza chikhulupiriro chawo m’njira ziti lerolino?

9. Ndi njira imodzi iti yomwe tingakhalire osasunthika?

9 Njira imodzi yosonyezera chikhulupiriro ndiponso kukhalabe osasunthika ngati kuti tikuona Wosaonekayo ndiyo kulalikira molimba mtima ngakhale m’kati mwa chizunzo. Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti: “Anthu onse adzadana ndi inu chifukwa cha dzina langa.” (Luka 21:17) Iye anawauzanso kuti: “Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake. Ngati anandilondalonda Ine, adzakulondalondani inunso.” (Yohane 15:20) Monga momwe Yesu ananenera, mosakhalitsa pambuyo pa imfa yake, otsatira ake anazunzidwa mwa kuwaopseza, kuwamanga, ndi kuwamenya. (Machitidwe 4:1-3, 18-21; 5:17, 18, 40) Ngakhale kuti kunali chizunzo choterocho, atumwi a Yesu ndi ophunzira ena anapitirizabe kulalikira uthenga wabwino molimba mtima.​—Machitidwe 4:29-31.

10. Kodi kudalira kwathu Yehova kutiteteza ndi kutisamalira kumatithandiza motani muutumiki wathu?

10 Mofanana ndi Mose, otsatira Yesu oyambirirawo sanaope adani awo ambiri oonekawo. Ophunzira a Yesu anali n’chikhulupiriro mwa Mulungu, ndipo zotsatira zake zinali zakuti, anali okhoza kupirira chizunzo champhamvu chomwe anakumana nacho. Inde, anakhalabe osasunthika ngati kuti amaona Wosaonekayo. Lerolino, kuzindikira nthaŵi zonse kuti Yehova amatisamalira ndi kutiteteza kumatipatsa mphamvu, kutilimbitsa mtima ndi kutichotsa mantha m’ntchito yathu yolalikira Ufumu. Mawu a Mulungu amati “kuopa anthu kutchera msampha; koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka.” (Miyambo 29:25) Chotero, sitibwerera mmbuyo chifukwa choopa chizunzo; ndipo sitichita manyazi ndi utumiki wathu. Chikhulupiriro chathu chimatisonkhezera kuchitira umboni molimba mtima kwa anansi athu, anzathu akuntchito, anzathu akusukulu, ndi ena.​—Aroma 1:14-16.

Wosaonekayo Amatsogolera Anthu Ake

11. Malinga n’kunena kwa Petro ndi Yuda, kodi ena omwe anali mumpingo wachikristu anasonyeza motani kupanda uzimu?

11 Chikhulupiriro chimatithandiza kuona kuti Yehova ndi amene akutsogolera gulu lake lapadziko lapansi. Potero timapeŵa kukhala ndi mtima wotsutsana ndi amene ali ndi maudindo mumpingo. Mtumwi Petro komanso Yuda mbale wake wa Yesu, anachenjeza za ena omwe analibe mkhalidwe wauzimu kuti amalankhula monyoza amuna otsogolera pakati pa Akristu. (2 Petro 2:9-12; Yuda 8) Kodi ofufuza zolakwa za anzawo ameneŵa akanalankhula motero pamaso pa Yehova akanakhala kuti akumuona ndi maso awo? Ndithudi sakanatero! Koma chifukwa chakuti Mulungu ndi wosaoneka, anthu amenewo analephera kulingalira kuti ali ndi mlandu kwa iye.

12. Kodi ndi mtima wotani umene tiyera kuusonyeza kwa atsogoleri athu mumpingo?

12 Inde, mumpingo wachikristu muli anthu opanda ungwiro. Amene akutumikira monga akulu amatha kulakwitsa zinthu ndipo nthaŵi zina zimatikhudza. Komabe, Yehova akugwiritsa ntchito amuna amenewo monga oweta gulu lake. (1 Petro 5:1, 2) Amuna ndi akazi okonda zauzimu nthaŵi zonse amadziŵa kuti imeneyi ndi njira imene Yehova akutsogolera anthu ake. Chotero, monga Akristu, timapeŵa mzimu wotsutsa, ndi wong’ung’udza ndipo timalemekeza dongosolo la Mulungu lotsogolera anthu ake. Mwa kumvera atsogoleri athu, timasonyeza kuti tikuona Wosaonekayo.​—Ahebri 13:17.

Kuona Mulungu Monga Mlangizi Wathu Wamkulu

13, 14. Kodi kuona Yehova monga Mlangizi Wamkulu kumatanthauzanji kwa inu?

13 Pali mbali ina imene imafuna kuzindikira kwauzimu. Yesaya analosera kuti: “Maso anu adzakhala maso oona Mlangizi wanu Wamkulu.” (Yesaya 30:20, NW) Pamafunika chikhulupiriro kuti munthu azindikire kuti Yehova ndi amene akutiphunzitsa kudzera m’gulu lake lapadziko lapansi. (Mateyu 24:45-47) Kuona Mulungu monga Mlangizi wathu Wamkulu kumaphatikizapo zambiri kuposa kungokhala ndi zizoloŵezi zabwino zophunzirira Baibulo ndi kupezeka pa misonkhano yachikristu nthaŵi zonse. Kumatanthauza kugwiritsa ntchito mokwanira zogaŵira zauzimu zimene Mulungu akutipatsa. Mwachitsanzo, m’pofunika kumvera mwatcheru kwambiri malangizo amene Yehova akupereka kudzera mwa Yesu kuti tisasunthike mwauzimu.​—Ahebri 2:1.

14 Nthaŵi zina pamafunika kuyesetsa mwapadera kuti tipindule kwambiri ndi chakudya chauzimu. Mwachitsanzo, tingakhale n’chizoloŵezi chongoŵerenga mosaikira mtima kwenikweni nkhani zina za m’Baibulo zomwe zimativuta kuzimvetsa. Pamene tikuŵerenga magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! mwinamwake timalumpha nkhani zina chifukwa chakuti nkhani yakeyo sikutikhudza kwenikweni. Kapena tingalole malingaliro athu kumaganiza zina pamene tili m’misonkhano yachikristu. Komabe, tingakhale tcheru mwa kulingalira mozama pa mfundo zomwe tikuphunzirazo. Kuyamikira kwathu malangizo auzimu omwe timalandira kumasonyeza kuti tikudziŵa kuti Yehova ndiye Mlangizi wathu Wamkulu.

Tidzadziŵerengera Mlandu

15. Kodi ena achita motani zinthu ngati kuti Yehova sakuwaona?

15 Kukhulupirira Wosaonekayo n’kofunika kwambiri, makamaka chifukwa chakuti kuipa kwafala kwambiri ‘m’nthaŵi ya chimaliziro’ ino. (Danieli 12:4) Kusaona mtima ndi chiwerewere zili ponseponse. Inde, n’chanzeru kukumbukira kuti Yehova amaona zochita zathu ngakhale kuti anthu sakutiona. Ena amaiŵala zimenezi. Pamene ena sakuwaona, amasonyeza khalidwe losemphana ndi Malemba. Mwachitsanzo, ena alephera kukana chiyeso chakuti aonerere zosangulutsa zowononga ndi zithunzi zolaula pa Intaneti, pa wailesi yakanema, ndi m’njira zina zamakono. Popeza kuti ochita zimenezi amachita mtseri, ena amachita ngati kuti Yehova sakuona zochita zawozo.

16. N’chiyani chomwe chingatithandize kuchita mogwirizana ndi miyezo yapamwamba ya Yehova?

16 Ndi bwino kukumbukira mawu a mtumwi Paulo akuti: “Munthu aliyense wa ife adzadziŵerengera mlandu wake kwa Mulungu.” (Aroma 14:12) Tiyenera kudziŵa kuti nthaŵi zonse tikamachita tchimo, timachimwira Yehova. Kudziŵa zimenezi kuyenera kutithandiza kuchita zinthu mogwirizana ndi miyezo yake yapamwamba ndi kupeŵa khalidwe lodetsa. Baibulo limatikumbutsa kuti: “Palibe cholengedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.” (Ahebri 4:13) N’zoona kuti tidzadziŵerengera mlandu kwa Mulungu, komatu chifukwa chachikulu chomwe timachitira chifuno chake ndi kutsatira miyezo yake yolungama n’chakuti timam’konda kwambiri Yehova. Chotero tichite mwanzeru posankha zinthu zosangulutsa komanso mmene timachitira ndi ena omwe si amuna kapena akazi anzathu.

17. Kodi Yehova amaonerera zochita zathu ndi cholinga chotani?

17 Yehova amaonetsetsa zochita zathu, koma zimenezi sizikutanthauza kuti akuyembekezera kuti tilakwe kuti atipatse chilango ayi. Koma kuti amationerera zochita zathu ndi nkhaŵa yachikondi, ngati ya tate wofunitsitsa kupereka mphoto kwa ana ake omvera. N’zolimbikitsatu kwambiri kudziŵa kuti Atate wathu wakumwamba amakondwera ndi chikhulupiriro chathu ndipo “ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.” (Ahebri 11:6) Tisonyezetu chikhulupiriro chonse mwa Yehova ndi ‘kumtumikira ndi mtima wangwiro.’​—1 Mbiri 28:9.

18. Popeza kuti Yehova amationa ndi kuonanso kukhulupirika kwathu, kodi Malemba akutitsimikizira chiyani?

18 Miyambo 15:3 amati: “Maso a Yehova ali ponseponse, nayang’anira oipa ndi abwino.” Inde, Yehova amaona anthu oipa ndi kuwachitira malinga ndi zochita zawo. Komabe, ngati tili m’gulu la anthu “abwino” tingakhale otsimikizira kuti Yehova amaona zomwe timachita mokhulupirika. N’zolimbikitsa chikhulupiriro kwabasi kudziŵa kuti ‘kuyesetsa kwathu sikuli chabe mwa Ambuye’ ndi kuti wosaonekayo ‘sadzaiŵala ntchito yathu, ndi chikondicho tidachionetsera ku dzina lake.’​—1 Akorinto 15:58; Ahebri 6:10.

Kupempha Yehova Kuti Atipende

19. Kodi ena mwa mapindu omwe amadza ndi chikhulupiriro cholimba mwa Yehova ndi ati?

19 Monga atumiki okhulupirika a Yehova, ndife amtengo wapatali kwa iye. (Mateyu 10:29-31) Ngakhale kuti sititha kumuona, angakhale weniweni kwa ife, ndipo tingaone kufunika kokhala naye paubwenzi wamtengo wapatali. Kuona Atate wathu wakumwamba mwanjira imeneyi kumatidzetsera mapindu ochuluka. Chikhulupiriro chathu cholimba chimatithandiza kukhala ndi mtima woyera ndi chikumbumtima chabwino kwa Yehova. Chikhulupiriro chopanda chinyengo chimatithandizanso kupeŵa moyo wa chiphamaso. (1 Timoteo 1:5, 18, 19) Chikhulupiriro chosagwedera mwa Mulungu chimapereka chitsanzo chabwino ndipo chingalimbikitse ena. (1 Timoteo 4:12) Komanso, chikhulupiriro choterocho chimasonkhezera makhalidwe aumulungu, ndi kukondweretsa mtima wa Yehova.​—Miyambo 27:11.

20, 21. (a) N’chifukwa chiyani m’pofunika kuti Yehova aziyang’anira zochita zathu? (b) Kodi Salmo 139:23, 24 tingaligwiritse ntchito motani pamoyo wathu?

20 Ngati ndifedi anzeru, ndiye kuti tikukondwera kuti Yehova akuonerera zochita zathu. Sitikufuna kuti angotiona chabe komanso tikufunitsitsa kuti apende bwino lomwe malingaliro athu ndi zochita zathu. M’pemphero lathu, tidzachita bwino kupempha Yehova kuti afufuze mtima wathu ndi kuona ngati tili ndi zizoloŵezi zosayenera. Ndithudi angatithandize kuthana ndi mavuto athu ndi kuwongolera mbali zofunikirazo. Moyenerera, wamasalmo Davide anaimba kuti: “Mundisanthule, Mulungu, nimudziŵe mtima wanga; mundiyese nimudziŵe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndili nawo mayendedwe oipa, nimunditsogolere pa njira yosatha.”​—Salmo 139:23, 24.

21 Davide anachonderera kuti Yehova amusanthule ndi kuona ngati ‘ali nawo mayendedwe oipa.’ Monga wamasalmoyo, kodi nafenso sitilakalaka kuti Mulungu asanthule mitima yathu ndi kuona ngati tili ndi malingaliro oipa? Chotero mwa chikhulupiriro timpemphe Yehova kuti atipende. Koma bwanji ngati tikuvutika maganizo chifukwa cha tchimo linalake kapena tili ndi chinachake chopweteka m’kati mwathu? Ngati ndi choncho, tipitirizebe kupemphera moona mtima kwa Mulungu wathu wachikondi, Yehova, ndi kumvera modzichepetsa malangizo a mzimu wake woyera ndi uphungu wopezeka m’Mawu ake. Tili n’chikhulupiriro chonse kuti adzatithandiza komanso kutitsogolera njira yopita ku moyo wosatha.​—Salmo 40:11-13.

22. Kodi tiyenera kutsimikiza mtima kutani ponena za Wosaonekayo?

22 Inde, Yehova adzatidalitsa mwa kutipatsa moyo wosatha ngati tikuchita zofuna zake. Kunena zoona, tingavomereze mphamvu zake ndi ulamuliro wake, monga momwe mtumwi Paulo anachitira pamene analemba kuti: “Kwa Mfumu yosatha, yosavunda, yosaoneka, Mulungu wa yekha, ukhale ulemu ndi ulemerero, kufikira nthaŵi za nthaŵi. Amen.” (1 Timoteo 1:17) Tisonyezetu ulemu woterewu kwa Yehova nthaŵi zonse kuchokera pansi pa mtima. Ndipo zivute zitani, tipitirizebe motsimikiza mtima kukhalabe osasunthika ngati oona Wosaonekayo.

Kodi Mungayankhe Motani?

• Kodi n’zotheka motani kuti anthu aone Mulungu?

• Ngati Yehova ali weniweni kwa ife, kodi tidzachita motani m’kati mwa chizunzo?

• Kodi kuona Yehova monga Mlangizi wathu Wamkulu kumatanthauzanji?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kulakalaka kuti Yehova atipende?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 18]

Mose, mosaopa Farao, anachita ngati anali kuona Yehova, Mulungu wosaonekayo

[Chithunzi patsamba 21]

Tisachite zinthu ngati kuti Yehova sangaone zimene tikuchita

[Chithunzi patsamba 23]

Ife timafunitsitsa kum’dziŵa Mulungu chifukwa chakuti timamuona monga Mlangizi wathu Wamkulu