Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndalama Tingazione Motani M’njira Yoyenera?

Kodi Ndalama Tingazione Motani M’njira Yoyenera?

Kodi Ndalama Tingazione Motani M’njira Yoyenera?

Kukonda ndalama ndiponso kukhumba chuma sikwachilendo ayi. Ndipo Baibulo sikuti silinenapo chilichonse pankhaniyi ngati kuti ndi zinthu za masiku ano okha. Zimenezi zinayamba kalekale. M’Chilamulo cha Mose, Mulungu analangiza Aisrayeli kuti: “Usasirire nyumba yake ya mnzako . . . kapena kanthu kalikonse ka mnzako.”​—Eksodo 20:17.

KUKONDA ndalama ndi chuma kunalinso kofala m’nthaŵi ya Yesu. Talingalirani za kukambirana kwa Yesu ndi munthu wina wachinyamata wolemera kwambiri. “[Yesu] anati kwa iye: ‘Usoŵa chinthu chimodzi: gulitsa zilizonse uli nazo, nugaŵire osauka; ndipo udzakhala nacho chuma chenicheni m’mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.’ Koma pakumva izi anagwidwa nacho chisoni chambiri; pakuti anali mwini chuma chambiri.”​—Luka 18:18-23.

Kuona Ndalama Moyenera

Komabe, n’kulakwa kunena kuti Baibulo limadana ndi ndalama zenizenizo kapena ntchito yake iliyonse. Baibulo limasonyeza kuti ndalama zingateteze anthu ku umphaŵi ndiponso mavuto amene umphaŵiwo ungabweretse komanso kuwatheketsa kupeza zomwe akufuna. Mfumu Solomo inalemba kuti: “Nzeru itchinjiriza monga ndalama zitchinjiriza.” Ndipo inalembanso kuti: “Amaphikira zakudya kuti asekere, vinyo nakondweretsa moyo; ndipo ndalama zivomera zonse.”​—Mlaliki 7:12; 10:19.

Kugwiritsa ntchito bwino ndalama n’kovomerezeka ndi Mulungu. Mwachitsanzo, Yesu anati: “Mudziyesere nokha abwenzi ndi chuma chosalungama.” (Luka 16:9) Zimenezi zimaphatikizapo kupereka ndalama zothandizira kupititsa patsogolo kulambira koona kwa Mulungu chifukwa mosakayika timafuna Mulungu akhale Bwenzi lathu. Solomo weniweniyo, potsatira chitsanzo cha atate wake Davide, anapereka ndalama zambiri ndi zinthu zina zamtengo wapatali zothandiza pa ntchito yomanga kachisi wa Yehova. Lamulo lina kwa Akristu n’lakuti azithandiza osoŵa. Mtumwi Paulo anati: “Patsani zosoŵa oyera mtima.” Ndipo anawonjezera kuti: “cherezani alendo.” (Aroma 12:13) Zimenezi zimafuna kugwiritsa ntchito ndalama. Koma bwanji nanga za kukonda ndalama?

‘Kukonda Siliva’

Paulo anafotokoza zambiri za chikondi cha pandalama kapena kuti ‘kukonda siliva’ pamene ankalembera Mkristu mnzake wachinyamatayo Timoteo. Uphungu wa Paulo umenewu umapezeka pa 1 Timoteo 6:6-19. Iye anathirira ndemanga pa za “chikondi cha pandalama” monga mfundo yake yaikulu yokhudza zinthu zakuthupi. Polingalira za kukonda ndalama komwe anthu lerolino akukutamanda, tingachite bwino kuphunzira mosamalitsa mawu a Paulo ouziridwaŵa. Kuphunzira kotereku n’kopindulitsa kwambiri chifukwa kumavumbula chinsinsi cha mmene ‘tingagwirire moyo weniweniwo.’

Paulo anachenjeza kuti: “Muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.” (1 Timoteo 6:10) Nkhani ino kapena lemba lililonse silikunena kuti ndalama n’zoipa pa izo zokha ayi. Ngakhale mtumwiyo sananene kuti ndalama ndizo zimachititsa zinthu “zoipa zonse” kapena kuti ndizo muzu wa vuto lililonse. M’malo mwake, chikondi cha pandalama ndicho muzu wa “zoipa zonse” ngakhale kuti pali zinthu zinanso zomwe zimayambitsa mavuto.

Peŵani Kusakhutira

Popeza kuti Malemba sadana ndi ndalama, sindiye kuti chenjezo la Paulo n’lopanda pake ayi. Akristu amene ayamba kukonda ndalama ali pangozi yopeza mavuto ambiri, ndipo choipitsitsa kwambiri ndicho kusiya kukhulupirira. Paulo anatsindika zimenezi pomwe anauza Akristu a ku Kolose kuti: “Chifukwa chake fetsani ziŵalozo zili padziko . . . chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano.” (Akolose 3:5) Kodi kusirira, kusakhutira ndi zomwe ulinazo, kapena ‘kukonda ndalama’ kungakhale motani kupembedza mafano? Kodi zimenezi zikutanthauza kuti n’kulakwa kufuna nyumba yaikulu, galimoto latsopano, kapena ntchito yopindulitsa kwambiri? Iyayi, palibe n’chimodzi chomwe mwa zinthu zimenezi chimene chili choipa pachokha. Nkhani yagona pakuti: Kodi chimakufunitsani zinthu zimenezi n’chiyani? Ndipo kodi n’zofunikadi?

Kusiyana kofuna zinthu moyenera ndi mosonyeza kusakhutira kungafanizidwe ndi kusiyana kwa moto wophikira ndi moto umene umatentha nkhalango. Kufuna zinthu moyenera ndi mwadongosolo n’kopindulitsa. Kumatisonkhezera kugwira ntchito ndi kupeza phindu. Miyambo 16:26 imati: “Wantchito adzigwirira yekha ntchito; pakuti m’kamwa mwake mum’fulumiza.” Koma kusakhutira ndi zomwe ulinazo ndi koopsa ndiponso kowononga. Ndiko kukhumba zinthu mwadyera.

Kulamulira chikhumbo chathu cha ndalama ndilo vuto lalikulu. Kodi ndalama zomwe tidzapeza kapena chuma chomwe tikufuna zidzatitumikira? Kapena kodi ife ndiye tidzatumikire ndalamazo? N’chifukwa chake Paulo ananena kuti kukhala ‘munthu wosirira n’kupembedza mafano.’ (Aefeso 5:5) Kufuna chinthu china mwadyera kumatanthauza kudzipereka ku chinthucho, mwakutero timapanga chinthu chomwe timatumikiracho kukhala mbuye wathu ndi mulungu wathu. Mosiyana kwambiri ndi zimenezo, Mulungu amalamula kuti: “Usakhale nayo milungu ina koma Ine ndekha.”​—Eksodo 20:3.

Kukhumba chuma mwadyera kumasonyezanso kuti sitikhulupirira Mulungu kuti atha kukwaniritsa lonjezo lake la kutipatsa zofuna zathu. (Mateyu 6:33) Choncho, chilakolako chodzikundikira chuma chimachititsa munthu kupatuka kwa Mulungu. Zikafika pamenepa nakonso kumakhala, “kupembedza mafano.” N’chifukwa chake Paulo anachenjeza momveka bwino za kusirira kapena kuti kulakalaka chuma mopambanitsa.

Yesunso anachenjeza mwachindunji kuipa kwa kusirira. Iye anatilamula kupeŵa kulakalaka chinthu chomwe tilibe pamene anati: “Yang’anirani, mudzisungire kupeŵa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.” (Luka 12:15) Malinga ndi mawu ameneŵa ndiponso fanizo la Yesu limeneli, maziko a zikhumbo zadyera ndiwo chikhulupiriro chopusa chakuti chinthu chofunika kwambiri pa moyo wa munthu ndicho kuchuluka kwa zinthu zomwe ali nazo. Zimenezi zitha kukhala ndalama, udindo, ulamuliro, ndi zina zotero. N’zotheka kulakalaka mwadyera china chilichonse chomwe tikufuna. Mwina titha kuganiza kuti tikapeza chinthucho chidzatikhutiritsa. Koma malinga ndi zomwe Baibulo limanena ndiponso mbiri ya anthu, Mulungu yekha ndiye angatikhutiritse​—ndipo adzakhutiritsa zofuna zathu zenizeni monga momwe Yesu anauzira otsatira ake.​—Luka 12:22-31.

Chikhalidwe cha anthu masiku ano chokhalira kugula ndi kugulitsa malonda chalimbikitsa mtima wofuna kudzikundikira chuma. Mosonkhezeredwa ndi njira zovuta kuzizindikira koma zamphamvu, anthu ambiri amakhulupirira kuti zinthu zilizonse zomwe ali nazo n’zosakwanira. Iwo amafuna zina zambiri, zokulirapo, ndiponso zabwinopo. Ngakhale kuti sitingayembekezere kusintha zinthu m’dzikoli, kodi ifeyo patokha tingapeŵe motani chizoloŵezi chimenechi?

Kukhutira Osati Kulakalaka Chuma Mwadyera

Paulo anatchula mawu osiyana ndi kukhumba chuma mwadyera omwe ndi kukhutira. Iye anati: “Koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.” (1 Timoteo 6:8, 9) Kunena kuti “zakudya ndi zofunda” ndizo timafunikira kwenikweni kungaoneke ngati kusadziŵa zinthu. Anthu ambiri amasangalala ndi mapulogalamu a pa wailesi yakanema amene amaonetsa anthu amene amakhala m’nyumba zapamwamba. Komabe zimenezi sizingakukhutiritseni.

N’zoona kuti atumiki a Mulungu safunika kudzipatsa dala umphaŵi. (Miyambo 30:8, 9) Komabe, Paulo amatikumbutsa kuti umphaŵi umatanthauza: kusoŵa chakudya, zovala, ndi malo okhala okwanira. Ndipo ngati zimenezi tili nazo, ndiye kuti titha kukhala okhutira.

Kodi Paulo anali kunena moona mtima za kukhutira koteroko? Kodi n’zothekadi kuti munthu akhutire ndi zakudya, zovala ndi nyumba basi? Paulo ankadziŵa chomwe ankanena. Iye anakhalapo wolemera komanso ndi maudindo apamwamba pakati pa Ayuda ndiponso monga nzika ya Roma. (Machitidwe 22:28; 23:6; Afilipi 3:5) Paulo anavutikanso kwadzaoneni pa ntchito yake yaumishonale. (2 Akorinto 11:23-28) Podutsa monsemo, iye anadziŵa chinsinsi chomwe chinam’thandiza kukhalabe wokhutira. Kodi chinsinsi chimenechi chinali chiyani?

“Ndaphunzira Chinsinsi”

Paulo analongosola m’kalata yake ina kuti: “Ndadziŵa ngakhale kupeputsidwa, ndadziŵanso kusefukira; konseko ndi m’zinthu zonse ndaloŵa mwambo wakukhuta [“ndaphunzira chinsinsi cha kukhuta,” NW] ndiponso kumva njala; kusefukira, ndiponso kusoŵa.” (Afilipi 4:12) Paulo analitu wotsimikiza ndiponso wachidaliro. N’kwapafupi kuganiza kuti moyo wake unali wabwino kwabasi panthaŵiyo, komatu sizinali choncho ayi. Iye anali m’ndende ku Roma.​—Afilipi 1:12-14.

N’zochititsa chidwi kuti mawu ameneŵa akunena motsindika za kukhutira osati ndi chuma chokha komanso ndi mikhalidwe. Chuma chamwana alirenji kapena mavuto adzaoneni zingaike pachiyeso zinthu zomwe mu maziika patsogolo. Paulo anatchula zinthu zauzimu zomwe zinam’theketsa kukhala wokhutira mosalingalira za chuma. Iye anati: “Ndikhoza zonse mwa Iye [Mulungu] wondipatsa mphamvuyo.” (Afilipi 4:13) M’malo modalira chuma chake, kaya chinali chochuluka kapena chochepa, Paulo nthaŵi zonse anadalira Mulungu kukwaniritsa zofuna zake pamtendere ndi pamavuto pomwe. Mwakutero iye anali wokhutira.

Chitsanzo cha Paulo chinali chofunika kwambiri makamaka kwa Timoteo. Mtumwiyo analangiza mwamuna wachinyamatayo kukhala ndi moyo umene umaika kudzipereka kwaumulungu ndiponso unansi wabwino ndi Mulungu patsogolo pa chuma. Paulo anati: “Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, thaŵa izi; nutsate chilungamo, chipembedzo, [“kudzipereka kwaumulungu,” NW] chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso.” (1 Timoteo 6:11) N’kutheka kuti mawu ameneŵa anauza Timoteo, koma amagwira ntchito kwa aliyense amene akufuna kulemekeza Mulungu ndiponso kukhala ndi moyo wachimwemwe weniweni.

Monga Mkristu aliyense, Timoteo nayenso anafunika kupeŵa kukhumba chuma mopambanitsa. Zikuoneka kuti panali okhulupirira ena olemera kwambiri mumpingo wa ku Efeso komwe Paulo anali pamene ankalemba kalatayi. (1 Timoteo 1:3) Paulo anali atabweretsa uthenga wabwino wa Yesu mumzinda wolemerawo zomwe zinachititsa ambiri kutembenuka. Mosakayika konse, ambiri mwa iwo anali anthu olemera monga mmenenso alili ena mumpingo wachikristu lerolino.

Ndiyeno, funso makamaka mogwirizana ndi mawu opezeka pa 1 Timoteo 6:6-10, n’lakuti: Kodi anthu olemera ayenera kuchitanji ngati akufuna kulemekeza Mulungu? Paulo anati, ayenera kupenda kaye mitima yawo. Ndalama zimakonda kuyambitsa mtima wodzikuza. Paulo anati: “Lamulira iwo achuma m’nthaŵi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziŵika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo.” (1 Timoteo 6:17) Anthu olemera ayenera kuphunzira kuona zoposa chuma chawocho. Afunikira kuyang’ana kwa Mulungu amene ali gwero la chuma chonse.

Komabe, kupenda mtima ili mbali imodzi chabe ya zofunika kuti tipambane. M’kupita kwanthaŵi, Akristu olemera ayenera kugwiritsa ntchito bwino chuma chawo. Paulo analangiza kuti: ‘Chitani zabwino, khalani ochuluka mu ntchito zabwino, khalani owoloŵa manja, okonzeka kugaŵira ena.’​—1 Timoteo 6:18, NW.

‘Moyo Weniweni’

Mfundo yaikulu ya uphungu wa Paulo n’njakuti, tiyenera kukumbukira kufunika koyenera kwa chuma. Mawu a Mulungu amati: “Chuma cha wolemera ndicho mudzi wake wolimba; alingalira kuti ndicho khoma lalitali.” (Miyambo 18:11) Inde, chitetezo chimene chuma chingabweretse mapeto ake chimakhala chongoganizira ndiponso chonyenga. Choncho si bwino kuika maganizo athu onse pa chuma m’malo mowaika pa kupeza chiyanjo cha Mulungu.

Kuyembekezera chuma chosadalirikachi kumakhala kwangozi. Chiyembekezo chenicheni chiyenera kukhala pa chinthu cholimba chatanthauzo ndiponso chokhalitsa. Chiyembekezo cha Akristu chili mwa Mlengi, Yehova Mulungu, ndi lonjezo lake la moyo wosatha. Popeza kuti ndalama sizingagule chimwemwe, momwemonso ndalama sizingagule n’komwe chipulumutso. Chikhulupiriro chathu chokha mwa Mulungu ndicho chingatipatse chiyembekezo chimenechi.

Choncho, kaya ndife olemera kapena osauka, tiyeni titsatire moyo umene udzatichititsa kukhala “nacho chuma cha kwa Mulungu.” (Luka 12:21) Palibe chinthu chamtengo wapatali kuposa kukhala woyanjidwa ndi Mlengi. Kuyesetsa kwathu konse kufuna kukhalabe oyanjidwa kumatithandiza ‘kudzikundikira tokha maziko okoma a nyengo ikudzayi, kuti tikagwire moyo weniweniwo.’​—1 Timoteo 6:19.

[Chithunzi patsamba 7]

Paulo anaphunzira chinsinsi chokhala wokhutira

[Zithunzi patsamba 8]

Titha kukhala wachimwemwe ndi wokhutira ndi zimene tili nazo