Kondwerani ndi Chiyembekezo cha Ufumu!
Kondwerani ndi Chiyembekezo cha Ufumu!
PA MARCH 10, 2001 panali mwambo wosangalatsa kwambiri. Pamwambowo panali anthu omvetsera okwana 5,784 omwe anasonkhana m’malo atatu ku New York State omwe banja lalikulu la Beteli limagwiritsa ntchito. Mwambowo unali wokondwerera kuti ophunzira a m’kalasi ya nambala 110 amaliza maphunziro awo pa sukulu ya amishonale ya Gileadi.
Carey Barber, wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova anatsegulira mwambowo mwa kuuza onse kuti alandiridwa ndi manja aŵiri. Ananenanso kuti: “N’zokondweretsa kudziŵa kuti ophunzira m’kalasi ya nambala 110 pa sukulu ya Gileadi tsopano aphunzitsidwa kukhala amishonale ndipo apatsidwa ntchito m’madera osiyanasiyana apadziko lonse.”
Mmene Mungakhalirebe Wachimwemwe
Mbale Barber atatsegulira mwambowo, Don Adams anakamba nkhani kwa osonkhanawo kuphatikizapo ophunzira 48 omwe anamaliza maphunzirowo. Nkhaniyo inali ya mutu wakuti “Madalitso a Yehova Amatilemeretsa.” Pogwiritsa ntchito Miyambo 10:22, anakumbutsa omvetserawo kuti, Yehova amathandiza ndi kudalitsa atumiki ake ngati aika zinthu za Ufumu patsogolo m’miyoyo yawo. Analimbikitsa ophunzirawo kulandira ntchito yawo yatsopanoyo ndi mtima wofanana ndi womwe mtumwi Paulo anasonyeza atam’pempha ‘kuwolokera ku Makedoniya kukathandiza.’ (Machitidwe 16:9) Ngakhale panali mavuto ambiri, kufunitsitsa kwa Paulo kukalalikira kudera lomwe anauzidwa kunadzetsa mapindu ochuluka opatsa chimwemwe.
Ophunzira a m’kalasiyo anali atatsiriza maphunziro awo a miyezi isanu ophunzira Baibulo ndiponso okonzekera ntchito yaumishonale. Komabe, Daniel Sydlik, wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova analimbikitsa ophunzirawo kupitirizabe kuphunzira. M’nkhani yake yakuti, “Khalani Ophunzira Enieni,” iye anati: “Kukhala ophunzira kumatanthauza kumvera mawu a Yesu nthaŵi zonse. Kumaphatikizapo kukhalabe ofunitsitsa kumvera mawu ake, uthenga wake, ndiponso ziphunzitso zake.” Ananenanso kuti, ophunzira a Kristu sasankha zochita popanda kumvera mawu a Ambuye. Nzeru ya Mulungu ili m’moyo wa Kristu. (Akolose 2:3) Palibe angamve mawu a Yesu kamodzi kokha, n’kunena kuti akudziŵa zonse zokhudza iye. Choncho, Mbale Sydlik analimbikitsa omaliza maphunzirowo kupitirizabe kuphunzira, kuchita zomwe aphunzirazo, ndiponso kuphunzitsa choonadi chachikristu. Zimenezi zimabweretsa ufulu.—Yohane 8:31, 32.
Kuti munthu akhalebe wachimwemwe mu utumiki wa Mulungu, ayenera kukhala wofunitsitsa kulandira chilango ndi uphungu. “Kodi Impso Zanu Zidzakulangizani?” anafunsa motero mlangizi wa sukulu ya Gileadi, Lawrence Bowen. Iye anafotokoza kuti m’Baibulo impso zimaimira maganizo a munthu ochokera pansi pa mtima. Maganizo oterowo angawongolere munthu ngati malangizo ouziridwa a m’Mawu a Salmo 16:7; Yeremiya 17:10) Kukhulupirika kwa munthu kumam’khudza kwambiri Yehova. Ataŵerenga Miyambo 23:15, 16, wokamba nkhaniyo anafunsa kuti: “Kodi impso zanu zidzakulangizani?” Powonjezera anati: “Tikupempherera kuti zidzatero ndipo mwakutero mudzakondweretsa kwambiri mtima wa Yehova. Mudzam’chititsa kukondwera kuchokera pansi pa mtima. Inde, pamene mukugwirabe ntchito yanu mokhulupirika mudzachititsa impso za Mulungu kukondwera kwabasi.”
Mulungu aloŵa m’kati mwenimweni mwa mbali iliyonse ya umunthu wake. (Nkhani yomaliza m’chigawo chimenechi anakamba ndi Mark Noumair yemwe anatumikirapo ku Kenya monga mmishonale asanakhale mlangizi wa sukulu ya Gileadi. Nkhani yake inali yakuti, “Kupenya ndi Maso N’kwabwino Koposa.” Nkhaniyi inagogomeza kufunika kokhala wokhutira. Mogwirizana ndi Mlaliki 6:9, Mbale Noumair anati: “Kakumaneni ndi zochitika zenizeni m’moyo. M’kunena kwina, ‘kupenya ndi maso.’ Mmalo moganizira zomwe mukufuna kuchita koma zomwe sizikutheka, ikirani mtima kwambiri pa kugwiritsa ntchito mokwanira mpata uliwonse malinga ndi mmene zinthu zilili panthaŵiyo. Kuganizira zinthu zosatheka, kuyembekezera zinthu mopambanitsa, kapena kuganizira kuvuta kwa ntchito yanu kudzangokuchititsani kukhala opanda chimwemwe ndi osakhutira.” Inde, kaya tikukhala kumalo otani kapena m’mikhalidwe yotani, mfundo n’njakuti, kukhala okhutira chifukwa cha unansi wathu ndi Mulungu m’mikhalidwe yathu kumatipatsa chimwemwe potumikira Mlengi wathu Wamkulu.
Zochitika Zosangalatsa Pogwira Ntchito ya Ufumu Ndiponso pa Gileadi
Atatha kulandira malangizo othandiza kuchokera m’nkhani zimenezo, ophunzirawo anasimba zochitika zomwe asangalala nazo mu utumiki wakumunda m’miyezi isanu ya maphunzirowo. Motsogozedwa ndi Wallace Liverance yemwe ndi mkulu wosunga kaundula wa Sukulu ya Gileadi, ophunzirawo anasimba mmene adzisonyezera monga atumiki a Mulungu. (2 Akorinto 4:2) Iwo akhala akukopa chikumbumtima chopatsidwa ndi Mulungu cha anthu ena. Zokumana nazo za ophunzirawo zinasonyeza mmene ankayambira maphunziro a Baibulo ndi anthu oona mitima amene anali kukumana nawo m’misewu, mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba, ndi m’malo ena. M’zochitika zosiyanasiyana, anthu achidwi ananena kuti zofalitsa zofotokoza Baibulo za gulu la Yehova zilidi ndi choonadi. Mwininyumba wina anachita chidwi kwambiri ndi vesi linalake m’Baibulo. Iyeyu tsopano akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova.
Kenako, Joel Adams anafunsa ophunzira omwe anamaliza maphunziro awo zaka zam’mbuyomu. Nkhani yakeyo inali yakuti, “Osaleka Kuphunzira Ndiponso Kutumikira Yehova.” Omwe anawafunsawo anali ndi malangizo apanthaŵi yake kwa amishonale atsopanowo. Pokumbukira nthaŵi zomwe anali wophunzira m’kalasi ya nambala 26 ya Gileadi, Harry Johnson anati: “Tinaphunzitsidwa kuti Yehova amatsogolera anthu ake nthaŵi zonse ndipo adzapitiriza kutero. Kutsimikiza koteroko kwakhala kolimbikitsa m’zaka zonsezi.” William Nonkes yemwe anali wophunzira m’kalasi ya nambala 53 ya Gileadi analangiza ophunzirawo kuti: “Koposa zonse, musaiwale mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo, ndipo zigwiritsireni ntchito m’zochita zanu zonse tsopano ndiponso mpaka kalekale. Mukatero, mudzapitiriza ntchito yanu ndipo Yehova adzakudalitsani kwambiri.”
Papulogalamuyo, Richard Rian anasankha kukakamba nkhani ya mutu wakuti: “Olimbikitsidwa Kuchita Chifuniro cha Yehova.” Mwa anthu omwe anawafunsa, panali John Kurtz yemwe anali wophunzira m’kalasi ya nambala 30 ya Gileadi. Iyeyu anakhala ku Spain zaka 41 monga mmishonale. Atam’funsa za dongosolo la maphunziro a sukulu ya Gileadi, Mbale Kurtz anati: “Baibulo ndilo buku lomwe kwenikweni limaphunziridwa. Ndiponso timakhala ndi mabuku ena otithandiza kumvetsa Baibulo. Mabukuwo amapatsidwa kwa onse. Palibe zachinsinsi zomwe amaphunzitsa ku Gileadi. Sindilephera kunena motsindika zimenezi chifukwa chakuti Mboni zonse zili ndi ufulu wopeza chidziŵitso chomwe amaphunzitsa ku Gileadi.”
Mbale Gerrit Lösch wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova anamaliza pulogalamu yauzimu imeneyi ndi nkhani yakuti, “Pamwamba ndi Kunsi kwa Mapiko a Yehova.” Analongosola mmene m’Baibulo chitetezo ndi chithandizo cha Mulungu pa atumiki ake chimaimiridwira ndi mapiko a mphungu. (Deuteronomo 32:11, 12; Salmo 91:4) Nthaŵi zina mphungu yaikulu imatambasula mapiko ake kwa maola angapo n’cholinga choteteza ana ake. Nthaŵi zinanso, mphungu yaikazi imafungatira ana ake kuwateteza ku chisanu. M’njira yofananayo ndiponso mogwirizana ndi chifuniro chake, Yehova angathandize atumiki ake okhulupirika makamaka ngati akuyesedwa mwauzimu. Yehova salola kuti atumiki ake ayesedwe mopitirira muyezo moti sangathe kupirira. Mmalo mwake, amaika njira yopulumukira kuti apirire. (1 Akorinto 10:13) Mbale Lösch anamaliza ndi mawu akuti: “Kuti tipitirizebe kutetezedwa mwauzimu tiyenera kukhalabe kunsi kwa mapiko a Yehova. Zimenezi zikutanthauza kusakhala ndi mtima wodziimira. Nthaŵi zonse tikhale pafupi ndi Yehova ndiponso gulu lake longa mayi. Tisadzilekanitse ku malangizo ndiponso uphungu wawo wachikondi.”
Tcheyamani anaŵerenga makalata amafuno abwino ochokera kwa anthu akufuna kwabwino apadziko lonse. Kenako inakwana nthaŵi yopereka madipoloma. Pamene Sukulu ya Gileadi inkakhazikitsidwa, inali n’cholinga chophunzitsa makalasi oŵerengeka chabe m’zaka zopitirira zisanu. Komabe, kwa zaka 58 Yehova Mulungu walola sukuluyi kugwirabe ntchito zake. Monga momwe Mbale Barber ananenera m’mawu ake otsegulira mwambowo: “Ophunzira a sukulu ya Gileadi apanga mbiri yosangalatsa zedi chiyambireni mu 1943 pomwe sukuluyi inatsegulidwa. Kuyesetsa kwawo kwachititsa kuti anthu ofatsa zikwi mazana ambiri padziko lonse aloŵe m’gulu la Yehova laulemerero.” Inde, sukulu yaumishonale imeneyi yathandiza kwambiri anthu miyandamiyanda kukondwera ndi chiyembekezo cha Ufumu.
[Bokosi patsamba 24]
ZIŴERENGERO ZA KALASI
Mayiko omwe kunachokera ophunzira: 8
Mayiko omwe ophunzira anatumizidwa: 18
Ophunzira onse m’kalasiyi: 48
Avareji ya zaka zawo: 34
Avareji ya zaka zomwe akhala m’choonadi: 18
Avareji ya zaka za utumiki wa nthaŵi zonse: 13
[Chithunzi patsamba 25]
Kalasi la 110 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo
Mu mndandanda uli m’munsiwu, mizera ikuŵerengedwa kuchokera kutsogolo kupita kumbuyo, ndipo mayina andandalikidwa kuyambira kumanzere kupita kumanja mu mzera uliwonse.
(1) Vacek, E.; Madelin, L.; Evans, G.; Watanabe, K. (2) Trafford, P.; Turfa, J.; Wilson, P; Williams, R.; Weber, A. (3) Johnson, T.; Hanau, K.; Mourlhou, F.; Charpentier, F.; Peckham, R.; Androsoff, P. (4) Seegers, T.; Seegers, D.; Bailey, P.; Bailey, M.; Madelin, K.; Lippold, E.; Lippold, T. (5) Evans, N.; Gold, R.; Bollmann, I.; Vacek, R.; Oundjian, J.; Wilson, N. (6) Turfa, J.; Zuidema, L.; Zuidema, R.; Bengtsson, C.; Bengtsson, J.; Galano, M.; Galano, L. (7) Peckham, T.; Mourlhou, J.; Charpentier, C.; Gold, M.; Bollmann, R.; Oundjian, F. (8) Weber, R.; Johnson, B.; Hanau, D.; Watanabe, Y.; Williams, R.; Trafford, G.; Androsoff, T.