Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Kulasa kwa Bwenzi”

“Kulasa kwa Bwenzi”

“Kulasa kwa Bwenzi”

MTUMWI Paulo anaona kuti kunali kofunika kudzudzula zolakwika pakati pa Akristu a m’zaka za zana loyamba a ku Galatiya. Koma pofuna kupewa kuwakwiyitsa, iye anafunsa kuti: “Kotero kodi ndasanduka mdani wanu, pakukunenerani zoona?”​—Agalatiya 4:16.

‘Ponena zoona,’ Paulo sanakhale mdani wawo. Iye anatero mogwirizana ndi mfundo yachikhalidwe ya m’Baibulo yakuti: “Kulasa kwa bwenzi kuli kokhulupirika.” (Miyambo 27:6) Anadziŵa kuti anthu olakwawo akhumudwa. Anadziŵanso kuti kupewa kulangiza wolakwa ndiko kukana kum’sonyeza chikondi cha Yehova Mulungu. (Ahebri 12:5-7) Choncho, pokhala bwenzi lokhulupirika la mpingowo ndi poufunira zabwino nthaŵi zonse, Paulo sanapeŵe kudzudzula kuti akonze zinthu.

Masiku ano, Mboni za Yehova zikugwira ntchito yawo ‘yophunzitsa anthu a mitundu yonse, . . . kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene [Yesu Kristu] walamula.’ Pochita zimenezo, Akristu okhulupirika ameneŵa, sapeŵa kufotokoza choonadi cha m’Baibulo chomwe chimavumbula ndi kutsutsa ziphunzitso zolakwika ndi makhalidwe osayenera Akristu. (Mateyu 15:9; 23:9; 28:19, 20; 1 Akorinto 6:9, 10) Sachita zimenezi kuti anthu ena aziwada. Iwo akusonyeza chidwi chimene mabwenzi enieni amasonyeza.

Mouziridwa ndi Mulungu, wamasalmo analemba kuti: “Akandipanda munthu wolungama ndidzati n’chifundo: akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu; mutu wanga usakane: pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera.”​—Salmo 141:5.