Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

N’chifukwa chiyani Baibulo la New World Translation pa 2 Petro 3:13 limati “miyamba yatsopano [mochulukitsa] ndi dziko latsopano,” pamene pa Chivumbulutso 21:1 limanena za “kumwamba kwatsopano [kusonyeza chimodzi] ndi dziko latsopano”?

Izi zili choncho makamaka chifukwa cha malamulo a zinenero zoyambirirazo. Koma tanthauzo lake n’limodzimodzi.

Choyamba, tiyeni tione m’Malemba achihebri. M’zolemba zoyambirira zachihebri, mawu akuti sha·maʹyim, otanthauza “miyamba kapena kumwamba,” nthaŵi zonse amasonyeza zochuluka. Posonyeza kuchuluka, mawuŵa sakunena za kuchuluka kolemekeza, koma kuchuluka kwa chinthu chimodzi chachikulu kwambiri chokhala ndi mbali zosiyanasiyana zosaŵerengeka. Ndi mmene zilili ndi miyamba yeniyeniyi yomwe n’njaikulu kumbali zonse kuchokera padziko lapansi yokhala ndi nyenyezi mabiliyoni ambirimbiri. Pamene mawu akuti sha·maʹyim atchulidwa pambuyo pa mawu otsimikiza, kaŵirikaŵiri Baibulo la New World Translation limawatanthauzira kuti “miyamba,” monga pa Yesaya 66:22. Koma pamene mawu akuti sha·maʹyim sanatchulidwe limodzi ndi mawu osonyeza kutsimikiza, Baibulo la New World Translation lingawamasulire monga chinthu chimodzi (“kumwamba,” monga pa Genesis 1:8; 14:19, 22; Salmo 69:34) kapena mochulukitsa (“miyamba,” monga pa Genesis 49:25; Oweruza 5:4; Yobu 9:8; Yesaya 65:17).

Pa Yesaya 65:17 ndiponso 66:22, mawu achihebri otanthauzidwa kuti miyamba n’ngosonyeza zambiri, ndipo mawu akuti “miyamba yatsopano ndi [kapena] dziko latsopano,” ndiwo anasankhidwa powamasulira mosasintha.

Mawu achigiriki, akuti ou·ra·nosʹ amatanthauza “kumwamba” ndipo ochulukitsa ake ou·ra·noi ʹamatanthauza “miyamba.” N’zochititsa chidwi kuti otembenuza a Baibulo lachigiriki la Septuagint anagwiritsa ntchito mawu osonyeza chinthu chimodziwo pa Yesaya 65:17 ndi 66:22.

Nanga bwanji za mawu akuti “kumwamba [kapena miyamba] kwatsopano ndi dziko latsopano” opezeka kaŵiri m’Malemba Achigiriki Achikristu?

Pa 2 Petro 3:13, mtumwiyo anagwiritsa ntchito mawu achigiriki ochulukitsa. Asanatchule zimenezi (m’mavesi 7, 1012), iye ananena za “miyamba” yoipa yomwe ilipoyi, mochulukitsa. Choncho, iye anagwiritsa ntchito mawuwo mosasintha poitchula mochulukitsa pa vesi 13. Komanso zikuoneka kuti anatenga mawu oyambirira a pa Yesaya 65:17, pomwe mawu achihebriwo ali ochulukitsa, monganso pa 2 Petro 2:22, pamene anatenga mawu a m’zolemba zachihebri pa Miyambo 26:11. Choncho Petro ananena za “miyamba yatsopano [mochulukitsa] ndi dziko latsopano zimene tikuyembekeza monga mwa lonjezo lake.”

Mosiyana pang’ono, pa Chivumbulutso 21:1, mtumwi Yohane ayenera kuti anagwiritsa ntchito mmene Baibulo la Septuagint linamasulira Yesaya 65:17. Monga taona kale, ilo linamasulira mawu achigiriki otanthauza “kumwamba” monga chinthu chimodzi. N’chifukwa chake Yohane analemba kuti: “Ndinaona kumwamba kwatsopano [kusonyeza chimodzi] ndi dziko latsopano; pakuti kumwamba koyamba ndi dziko loyamba zidachoka.”

Izi n’zokhudza malamulo a chinenero potembenuza. Tibwerezenso kuti palibe kusiyana kwa tanthauzo kulikonse ngati munthu aŵerenga kapena kunena za “miyamba yatsopano” kapena “kumwamba kwatsopano.” Tanthauzo lake n’limodzi.

[Mawu a Chithunzi patsamba 31]

Nyenyezi: Frank Zullo