Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Musakhale Akumva Oiŵala

Musakhale Akumva Oiŵala

Musakhale Akumva Oiŵala

“Khalani akuchita mawu, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha.”​—YAKOBO 1:22.

1. Kodi anthu a mu Israyeli wakale anali ndi mwayi woona zozizwitsa zotani?

MPOMVEKA kunena kuti zozizwitsa zimene Yehova anachita mu Igupto wakale, ndi “zosaiŵalika.” Kunena zoona, uliwonse wa Miliri Khumi ija unali wochititsa mantha kwabasi. Miliri yokhaulitsa imeneyo inatsatana ndi kupulumutsidwa mozizwitsa kwa Aisrayeli mwa kudutsa pakati pa madzi ogaŵanika m’Nyanja Yofiira. (Deuteronomo 34:10-12) Mukanaonerera zochitika zimenezo, ndithudi simukanaiŵala Yemwe ankachititsa zimenezo. Ngakhale ndi choncho, wamasalmo anaimba kuti: “[Aisrayeli] anaiŵala Mulungu mpulumutsi wawo, amene Anachita zazikulu m’Aigupto; zodabwitsa m’dziko la Hamu, zoopsa ku Nyanja Yofiira.”​—Salmo 106:21, 22.

2. N’chiyani chikusonyeza kuti kuyamikira ntchito zodabwitsa za Mulungu kwa Aisrayeli kunali kwakanthaŵi kochepa?

2 Ataoloka Nyanja Yofiira, Aisrayeli “anaopa Yehova; nakhulupirira Yehova.” (Eksodo 14:31) Amuna a Israyeli anagwirizana ndi Mose kuimbira Yehova nyimbo yachilakiko, ndipo Miriamu ndi akazi ena analoŵerera akuimba malingaka ndi kuvina. (Eksodo 15:1, 20) Inde, anthu a Mulungu anali okhutira ndi ntchito zazikulu za Yehova. Koma kuyamikira kwawo Yemwe ankachita zozizwitsa zimenezo kunali kwa kanthaŵi kochepa. Posakhalitsa ambiri aiwo anayamba kuchita zinthu ngati agwidwa ndi matenda oiŵala. Anayamba kung’ung’udza ndi kudandaula motsutsana ndi Yehova. Ena anayamba kulambira mafano ndi kuchita chiwerewere.​—Numeri 14:27; 25:1-9.

Chingatiiŵalitse N’chiyani?

3. Chifukwa chakuti ndife opanda ungwiro, kodi tingaiŵale chiyani?

3 Kusayamikira kwa Aisrayeli n’kovuta kukumvetsa kwabasi. Komabe, zimenezo zingatichitikire nafenso. N’zoona kuti sitinaone zozizwitsa za Mulungu zamtunduwu. Komabe, n’zodziŵikiratu kuti mu ubwenzi wathu ndi Mulungu pali nyengo zinazake zosaiŵalika. Ena a ife tingakumbukire pamene tinalandira choonadi chochokera m’Baibulo. Nthaŵi ina yosangalatsa ingathe kukhala ya pemphero lathu lodzipatulira kwa Yehova komanso ya ubatizo wathu wa m’madzi monga Akristu oona. Ambiri a ife tinalandira thandizo nthaŵi inayake m’moyo wathu kuchokera kwa Yehova. (Salmo 118:15) Choposa zonsezi, kudzera mu imfa ya nsembe ya Mwana weniweni wa Mulungu, Yesu Kristu, talandira chiyembekezo cha chipulumutso. (Yohane 3:16) Komabe, chifukwa cha kupanda ungwiro kwathuku, ngati tagwidwa ndi zilakolako zoipa kapena kuda nkhaŵa chifukwa cha mavuto m’moyo, tingathe kuiŵala mosavuta zinthu zabwino zomwe Yehova watichitira.

4, 5. (a) Kodi Yakobo anachenjeza motani za kuopsa kokhala akumva oiŵala? (b) Kodi chitsanzo cha Yakobo cha munthu ndi kalirole tingachigwiritse ntchito motani?

4 M’kalata yomwe analembera Akristu anzake, Yakobo, mbale wake wa Yesu anachenjeza za kuopsa kokhala akumva osachedwa kuiŵala. Iye analemba kuti: “Khalani akuchita mawu, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha. Pakuti ngati munthu ali wakumva mawu osati wakuchita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang’anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m’kalirole; pakuti wadziyang’anira yekha, nachoka, naiŵala pompaja nali wotani.” (Yakobo 1:22-24) Kodi Yakobo anatanthauzanji ndi mawu ameneŵa?

5 Tikadzuka m’mamaŵa, nthaŵi zambiri timadziyang’anira pakalirole kuti tione malo omwe tiyenera kukonza kuti tioneke bwino. Tikatanganidwa ndi ntchito zosiyanasiyana, malingaliro athu amakhala pa zinthu zina, ndipo timasiya kuganiza zomwe tinaona pakalirole paja. Zimenezi zingachitikenso m’lingaliro lauzimu. Pamene tikuŵerenga Mawu a Mulungu, tingathe kuyerekezera momwe ifeyo tilili ndi zimene Yehova amafuna kwa ife. Tikatero, timaona zofooka zathu mwachindunji. Chidziŵitso chimenechi chiyenera kutisonkhezera kusintha umunthu wathu. Koma pamene tikugwira ntchito zathu zatsiku ndi tsiku ndi kulimbana ndi mavuto athu, n’chapafupi kuleka kulingalira nkhani za uzimu. (Mateyu 5:3; Luka 21:34) Zili ngati kuiŵala zomwe Mulungu watichitira mwachikondi. Ngati zimenezi zitachitika, tingapatse mpata zilakolako zauchimo mosavuta.

6. Kodi ndi kupenda Lemba liti komwe kungatithandize kusaiŵala mawu a Yehova?

6 M’kalata yake yoyamba youziridwa yopita kwa Akorinto, mtumwi Paulo anatchula za Aisrayeli oiŵala m’chipululu muja. Monga momwe Akristu a m’zaka za zana loyamba anapindulira ndi mawu a Paulowo, kupenda zomwe analembazo kungatithandize kusaiŵala mawu a Yehova. Choncho, tiyeni tipende 1 Akorinto 10:1-12.

Kanani Zilakolako Zadziko

7. Kodi ndi umboni wosatsutsika wotani wa chikondi cha Yehova umene Aisrayeli analandira?

7 Zimene Paulo ananena zokhudza Aisrayeli ndi chenjezo kwa Akristu. Mwa zina, Paulo analemba kuti: “Sindifuna, kuti mukhale osadziŵa, abale, kuti makolo athu onse anali pansi pa mtambo, nawoloka nyanja onse; nabatizidwa onse kwa Mose, mumtambo, ndi m’nyanja.” (1 Akorinto 10:1-4) Aisrayeli a m’nthaŵi ya Mose anadzionera okha mphamvu zazikulu za Mulungu, kuphatikizapo mtambo wozizwitsa womwe unali kuwatsogolera masana, womwenso unawathandiza kuthaŵa ndi kuwoloka Nyanja Yofiira. (Eksodo 13:21; 14:21, 22) Inde, Aisrayeli amenewo analandira umboni wosatsutsika wakuti Yehova anali kuwakonda.

8. Kodi zotsatira za kuiŵala kwauzimu kwa Aisrayeli zinali zotani?

8 Paulo akupitiriza kuti: “Koma ochuluka a iwo Mulungu sanakondwera nawo; pakuti anamwazika m’chipululu.” (1 Akorinto 10:5) Zomvetsa chisoni bwanji! Aisrayeli ambiri omwe anatuluka mu Igupto analephera okha kukaloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Mulungu sanakondwere nawo chifukwa cha kusoŵa kwawo chikhulupiriro, ndipo anafera m’chipululu. (Ahebri 3:16-19) Kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani? Paulo anati: “Koma zinthu izi zinachitika, zikhale zotichenjeza ife, kuti tisalakalake zoipa ife, monganso iwowo analakalaka.”​—1 Akorinto 10:6.

9. Kodi Yehova anathandiza motani anthu ake, nanga Aisrayeli anachitanji?

9 Aisrayeli anali n’zambiri zowathandiza kukhala atcheru mwauzimu m’chipululumo. Anapanga pangano ndi Yehova ndi kukhala mtundu wopatulika kwa iye. Komanso, anawapatsa ansembe, chihema monga malo olambirirako, ndi dongosolo lakuti azipereka nsembe kwa Yehova. Komabe, m’malo mokondwera ndi mphatso zauzimu zimenezi, iwo sanakhutire ndi zinthu zakuthupi zomwe Mulungu anali kuwapatsa.​—Numeri 11:4-6.

10. N’chifukwa chiyani tiyenera kulingalira za Mulungu nthaŵi zonse?

10 Mosiyana ndi Aisrayeli m’chipululumo, anthu a Yehova lerolino akunyadira chifukwa Mulungu akukondwera nawo. Komabe, m’pofunika kuti aliyense payekha azilingalira za Mulungu nthaŵi zonse. Kuchita zimenezi kudzatithandiza kukana zilakolako zadyera zomwe zingaphimbe malingaliro athu auzimu. Titsimikize mtima ‘kukana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m’dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza.’ (Tito 2:12) Ife amene tagwirizana ndi mpingo wachikristu kuyambira ukhanda wathu, tisaganize kuti tikumanidwa chinachake chabwino ayi. Ngati malingaliro amenewo angayerekeze kubwera m’maganizo athu, tidzachita bwino kukumbukira Yehova ndi madalitso amtengo wapatali omwe watikonzera.​—Ahebri 12:2, 3.

Kumvera Yehova ndi Mtima Wonse

11, 12. Kodi munthu angapembedze motani mafano ngakhale sakulambira zifanizo zosema?

11 Paulo akutipatsa chenjezo lina pamene akulemba kuti: “Kapena musakhale opembedza mafano, monga ena a iwo, monga kwalembedwa, anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nanyamuka kusewera.” (1 Akorinto 10:7) Paulo akunena za nthaŵi ija pamene Aisrayeli anaumiriza Aroni kuti awapangire mwana wang’ombe wagolidi. (Eksodo 32:1-4) Ngakhale kuti n’zokayikitsa kuti tingayambe kulambira mafano osema, tingakhale olambira mafano mwa kulola zilakolako zathu zadyera kutilepheretsa kulambira Yehova ndi mtima wathu wonse.​—Akolose 3:5.

12 Nthaŵi inayake, Paulo analemba za ena omwe anali kudera nkhaŵa kwambiri zinthu zakuthupi kusiyana ndi zinthu zauzimu. Ponenapo za amene ‘amayenda ngati adani a mtengo wozunzirapo wa Kristu,’ iye analemba kuti: “Chitsiriziro chawo ndicho kuwonongeka, mulungu wawo ndiyo mimba yawo.” (Afilipi 3:18, 19) Mafano omwe anali kupembedza sanali chosema chenicheni. Anali chilakolako chawo cha zinthu zakuthupi. Inde, sikuti zilakolako zonse n’zoipa. Yehova anatilenga n’chilakolako cha zinthu zofunika kwa munthu ndi kuti tizitha kusangalala ndi zinthu zosiyanasiyana zokondweretsa. Koma amene amaika zosangalatsa patsogolo pa unansi wawo ndi Mulungu, ndithudi, amapembedza mafano.​—2 Timoteo 3:1-5.

13. Kodi tingaphunzirepo chiyani pankhani ya mwana wang’ombe wagolidi?

13 Atatuluka mu Igupto, Aisrayeli anapanga mwana wa ng’ombe wagolidi ndi kumulambira. Kuwonjezera pa chenjezo lakuti sitiyenera kulambira mafano, nkhani imeneyi ilinso ndi phunziro lina lofunika kwambiri. Aisrayeli sanamvere malangizo omveka bwino ochokera kwa Yehova. (Eksodo 20:4-6) Komatu iwo analibe cholinga chokana Yehova monga Mulungu wawo. Iwo anapereka nsembe kwa mwana wa ng’ombe woumbayo ndi kunena kuti amenewo anali “madyerero a Yehova.” Mwa njira imeneyi anadzinyenga okha mwa kulingalira kuti Mulungu adzanyalanyaza kusamvera kwawoko. Kumeneku kunali kum’puta dala Yehova, ndipo zinam’kwiyitsa kwambiri.​—Eksodo 32:5, 7-10; Salmo 106:19, 20.

14, 15. (a) N’chifukwa chiyani Aisrayeli analibe chifukwa chokhalira akumva oiŵala? (b) Ngati tatsimikiza mtima kusakhala akumva oiŵala, kodi malamulo a Yehova tidzatani nawo?

14 Zingakhale zachilendo kwabasi Mboni ya Yehova italoŵa chipembedzo chonyenga. Komabe, ena angakane kutsatira malangizo a Yehova m’njira zina ali mumpingo momwemo. Aisrayeli analibe chifukwa chokhalira akumva oiŵala. Anamva Malamulo Khumi ndipo pamene Mose amapereka lamulo la Mulungu iwo anali pomwepo. Lamulolo linali lakuti: “Musapange milungu yasiliva ikhale pamodzi ndi ine; musadzipangire milungu yagolidi.” (Eksodo 20:18, 19, 22, 23) Komabe, Aisrayeli analambira mwana wang’ombe wagolidi.

15 Nafenso sitingakhale n’chifukwa chomveka chokhalira akumva oiŵala. M’Malemba, tili ndi malangizo ochokera kwa Mulungu okhudza mbali zosiyanasiyana m’moyo. Mwachitsanzo, Mawu a Yehova amatsutsa chizoloŵezi chotenga ngongole koma osabweza. (Salmo 37:21) Ana akulamulidwa kumvera makolo awo, ndipo atate ayenera kulera ana awo “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:1-4) Akristu omwe ndi mbeta akulangizidwa kukwatira kapena kukwatiŵa “mwa Ambuye,” ndipo atumiki a Mulungu omwe ali pabanja, akuuzidwa kuti: “Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse; ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.” (1 Akorinto 7:39; Ahebri 13:4) Ngati tatsimikiza mtima kusakhala akumva oiŵala, tidzalabadira malangizo ameneŵa ndi enanso ochokera kwa Mulungu mosamala kwambiri ndipo tidzayesetsa kuwatsatira.

16. Kodi zotsatira za kulambira mwana wa ng’ombe wa golidi zinali zotani?

16 Yehova sanavomereze kuti Aisrayeli amulambire m’njira zodziŵa okha. M’malo mwake anthu 3,000 anawonongedwa, kwenikweni chifukwa cha zomwe anachita polimbikitsa kupanduka kumeneko mwa kulambira mwana wa ng’ombe wagolidi. Ochimwa ena anakanthidwa ndi mliri wochokera kwa Yehova. (Eksodo 32:28, 35) Phunziro labwino kwabasi kwa onse amene amaŵerenga Mawu a Mulungu koma n’kudzisankhira kumvera zofuna zawo.

“Thaŵani Dama”

17. Kodi 1 Akorinto 10:8 akunena za chochitika chiti?

17 Paulo anatchula mbali ina yomwe zilakolako zathupi zingachititse kuiŵala kwauzimu pamene anati: “Kapena tisachite dama monga ena a iwo anachita dama, nagwa tsiku limodzi zikwi makumi aŵiri ndi zitatu.” (1 Akorinto 10:8) Pano Paulo akunena zomwe zinachitika m’Chigwa cha Moabu chakumapeto kwa ulendo wa zaka 40 wa Aisrayeli m’chipululu. Aisrayeli anali atangolandira kumene thandizo kuchokera kwa Yehova pogonjetsa mayiko a kum’maŵa kwa Yordano, koma ambiri anaiŵala ndi kusonyeza kusayamikira. M’malire mwenimweni mwa Dziko Lolonjezedwa, anakopeka ndi khalidwe loipa lachiwerewere ndi kulambira kodetsa kwa Baala wa ku Peori. Anthu pafupifupi 24,000 anawonongedwa, mwa ameneŵa 1,000 anali otsogolera anzawo kuchita zoipazo.​—Numeri 25:9.

18. Ndi khalidwe lotani limene lingam’pangitse munthu kuchita chiwerewere?

18 Anthu a Yehova lerolino n’ngodziŵika bwino chifukwa cha miyezo yawo yapamwamba ya makhalidwe abwino. Koma akagwa m’chiyeso choti achite chiwerewere, Akristu ena amasiya kulingalira za Mulungu ndi mfundo zake zamakhalidwe. Amakhala akumva oiŵala. Poyamba, chiyesocho sichingakhale chokhudza dama. Chingakhale chilakolako chongofuna kuonerera zolaula, nthabwala kapena kuseleula konyanyira, kapena kupanga ubwenzi weniweni ndi anthu a makhalidwe oipa. Zinthu zonsezi zachititsa Akristu kugwa m’tchimo.​—1 Akorinto 15:33; Yakobo 4:4.

19. Ndi uphungu wa m’Malemba uti umene umatithandiza ‘kuthaŵa dama’?

19 Ngati takumana ndi chiyeso chakuti tichite khalidwe loipa, sitiyenera kuleka kuganiza za Yehova. M’malo mwake tiyenera kutsatira zikumbutso zopezeka m’Mawu ake. (Salmo 119:1, 2) Monga Akristu, pafupifupi tonsefe tikuyesetsa kuti tikhale amakhalidwe oyera, koma kuchita choyenera pamaso pa Mulungu kumafuna khama nthaŵi zonse. (1 Akorinto 9:27) Paulo analembera Akristu a ku Roma kuti: “Kumvera kwanu kunabuka kwa anthu onse. Chifukwa chake ndikondwera ndi inu; koma ndifuna kuti mukakhale anzeru pa zabwino, koma ozungulidwa pa zoipa.” (Aroma 16:19) Monga momwe Aisrayeli 24,000 anafera chifukwa cha machimo awo, adama ndi ena ochimwa, posachedwapa aweruzidwa ndi Yehova. (Aefeso 5:3-6) Chotero, m’malo mokhala akumva oiŵala, tipitirizebe ‘kuthaŵa dama.’​—1 Akorinto 6:18.

Nthaŵi Zonse Yamikirani Zomwe Yehova Akutipatsa

20. Kodi Aisrayeli anam’yesa motani Yehova, nanga zotsatira zake zinali zotani?

20 Akristu ochuluka sagonjera chilakolako chakuti achite chiwerewere. Komabe, m’pofunika kusamala kwambiri kuti tisatsate chizoloŵezi chochita zinthu mong’ung’udza zimene zingadzetse mkwiyo wa Mulungu pa ife. Paulo anachenjeza kuti: “Kapena tisayese Ambuye, monga [Aisrayeli] ena a iwo anayesa, nawonongeka ndi njoka zija. Kapena musadandaula, monga ena a iwo anadandaula, nawonongeka ndi wowonongayo.” (1 Akorinto 10:9, 10) Aisrayeli anang’ung’udza kutsutsana ndi Mose ndi Aroni​—inde, ngakhalenso kutsutsana ndi Mulungu weniweniyo​—kudandaula ndi mana operekedwa mozizwitsa. (Numeri 16:41; 21:5) Kodi Yehova anamulakwira pang’ono ndi kung’ung’udzako kusiyana ndi dama lawo lija? Nkhani ya m’Baibulo ikusonyeza kuti njoka zinapha ong’ung’udza ambiri. (Numeri 21:6) Nthaŵi yoyamba ija, anthu opanduka ndi ong’ung’udza oposa 14,700 anawonongedwa. (Numeri 16:49) Chotero tisayese kuleza mtima kwa Yehova mwa kusalemekeza zopereka zake.

21. (a) Kodi Paulo anauziridwa kulemba chenjezo lotani? (b) Malinga ndi Yakobo 1:25, kodi chimwemwe chenicheni tingachipeze motani?

21 Polembera Akristu anzake, Paulo anatsiriza machenjezo ake ndi chenjezo lakuti: “Koma izi zinachitika kwa iwowa monga zotichenjeza, ndipo zinalembedwa kutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthaŵi ya pansi pano anafika pa ife. Chifukwa chake iye wakuyesa kuti ali chilili, ayang’anire kuti angagwe.” (1 Akorinto 10:11, 12) Mofanana ndi Aisrayeliwo, nafenso talandira madalitso ochuluka kuchokera kwa Yehova. Koma mosiyana ndi iwowo, tisaiŵale ndi kulephera kuyamikira zabwino zonse zimene Mulungu akutichitira. Mavuto a m’moyo akatilefula, tilingalire malonjezo osangalatsa opezeka m’Mawu ake. Tikumbukire unansi wathu wamtengo wapatali ndi Yehova ndi kupitiriza kugwira ntchito yomwe tapatsidwa yolalikira Ufumu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Mosakayika konse kuchita zimenezi kudzatidzetsera chimwemwe chenicheni, chifukwa chakuti Malemba akulonjeza kuti: “Iye wakupenyerera m’lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiŵala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m’kuchita kwake.”​—Yakobo 1:25.

Kodi Mungayankhe Motani?

• N’chiyani chomwe chingatipangitse kukhala akumva oiŵala?

• N’chifukwa chiyani kumvera Mulungu ndi mtima wonse kuli kofunika?

• Kodi ‘tingathaŵe motani dama’?

• Kodi zinthu zomwe Yehova akutipatsa tiyenera kuziona motani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 15]

Aisrayeli anaiŵala ntchito zodabwitsa za Yehova zomwe anawachitira

[Chithunzi patsamba 16]

Anthu a Yehova ndi otsimikiza mtima kusungabe miyezo yapamwamba ya makhalidwe