Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Samalirani Ana ndi Akazi Amasiye M’mayesero Awo

Samalirani Ana ndi Akazi Amasiye M’mayesero Awo

Samalirani Ana ndi Akazi Amasiye M’mayesero Awo

N’kosavuta kuzindikira kuti tikukhala m’dziko lopanda chikondi. Ponenapo za anthu ‘m’masiku otsiriza,’ mtumwi Paulo analemba kuti: “Masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, . . . opanda chikondi chachibadwidwe.” (2 Timoteo 3:1-3) Mawu amenewo analidi oona!

MIKHALIDWE ya m’nthaŵi yathu ino mwa zina ndiyo yachititsa kuti anthu ambiri akhale opanda chikondi. Kuganizira ena, nthaŵi zina ngakhale achibale enieniwo, kukucheperachepera.

Vutoli limakhudza anthu ambiri amene pazifukwa zina, amasoŵa thandizo. Akazi ndi ana amasiye akuchulukirachulukira chifukwa cha nkhondo, masoka achilengedwe ndiponso kusamuka kwa anthu ofuna malo a mtendere. (Mlaliki 3:19) Lipoti la bungwe la United Nations Children’s Fund linanena kuti, “[ana] opitirira miliyoni imodzi ndi amasiye kapena alekanitsidwa ndi mabanja awo chifukwa cha nkhondo.” Mukudziŵanso za amayi ambirimbiri amene sali pabanja kapena onyanyalidwa ndi amuna awo kapenanso kusudzulidwa, amene akuvutika kwambiri kuti apeze zofunika pa moyo komanso kusamalira mabanja awo paokha. Vutoli likukulirakulira chifukwa choti mayiko ena ali pamavuto aakulu azachuma. Zimenezi zikuchititsa nzika za m’mayikowo kukhala paumphaŵi wadzaoneni.

Poganizira zimenezi, kodi pali chiyembekezo chilichonse kwa amene akuvutika? Kodi kuvutika kwa akazi ndi ana amasiye kungachepetsedwe motani? Kodi vutoli lidzathetsedwa n’komwe?

Chisamaliro Chachikondi M’nthaŵi za M’Baibulo

Kusamalira zofunika zazikulu za akazi ndi ana amasiye pa moyo wawo wakuthupi ndiponso wauzimu kunali mbali yofunika kwambiri ya kulambira Mulungu m’nthaŵi za Baibulo. Akamakolora mbewu kapena zipatso zawo, Aisrayeli sanali kutenga zotsalira m’mundamo kapena kukunkha okha. Zotsalirazo anali kuzisiya kuti zikhale za ‘mlendo, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye.’ (Deuteronomo 24:19-21) Chilamulo cha Mose chinali ndi lamulo lachindunji lakuti: “Musazunze mkazi wamasiye, kapena mwana wamasiye aliyense.” (Eksodo 22:22, 23) Akazi ndi ana amasiye amene Baibulo limatchula moyenerera analidi anthu osauka chifukwa choti mwamuna amenenso ndi bambo, kapena makolo onse aŵiri akamwalira, banja lotsalalo limasiyidwa lokha popanda thandizo. Kholo lakale Yobu ananena kuti: “Ndinapulumutsa wozunzika wakufuula; mwana wamasiye yemwe wosoŵa mthandizi.”​—Yobu 29:12.

M’masiku oyambirira a mpingo wachikristu, kusamalira ovutika ndiponso ofunadi thandizo chifukwa cha imfa ya makolo kapena mwamuna, kunali chizindikiro cha kulambira koona. Chifukwa cha kuganizira umoyo wa anthu ngati ameneŵa, wophunzira Yakobo analemba kuti: “Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m’chisautso chawo, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.”​—Yakobo 1:27.

Kuwonjezera pa ana ndi akazi amasiye, Yakobo anasonyezanso kuganizira ena amene ali osauka ndi aumphaŵi. (Yakobo 2:5, 6, 15, 16) Mtumwi Paulo nayenso anasonyeza mtima womwewo. Iye ndi Barnaba atapatsidwa ntchito yawo yolalikira, ena mwa malangizo amene analandira anali akuti ‘aziganizira osauka nthaŵi zonse.’ Paulo ananena ndi chikumbumtima chabwino kuti, “ndicho chomwe ndinafulumira kuchichita.” (Agalatiya 2:9, 10) Nkhani yosimba zochita za mpingo wachikristu atangoukhazikitsa kumene imati: “Munalibe wosoŵa . . . anagaŵira yense monga kusoŵa kwake.” (Machitidwe 4:34, 35) Inde, makonzedwe omwe anawakhazikitsa mu Israyeli wakale osamalira ana ndi akazi amasiye ndiponso aumphaŵi anapitiriza kugwira ntchito mumpingo wachikristu.

N’zoona kuti thandizolo linali lochepa mogwirizana ndi njira zomwe mpingo uliwonse unkalipezera. Sanali kuwononga ndalama mwachisawawa ndipo okhawo ofunikiradi thandizo ndiwo anali kuthandizidwa. Panalibe Mkristu amene amapezerapo mwayi mwachinyengo pa makonzedwe ameneŵa ndiponso mpingo sunali kusenza mtolo wosayenera. Zimenezi zikusonyezedwa ndi malangizo a Paulo olembedwa pa 1 Timoteo 5:3-16. Pamenepa timaŵerenga kuti, ngati achibale a osoŵayo ali okhoza kuthandiza, ayenera kutenga udindo umenewo. Akazi amasiye osoŵa anayenera kukwaniritsa zowayenereza kuti alandire thandizo. Zonsezi zikusonyeza zomwe Yehova amakonza mwanzeru kuti asamalire osoŵa. Komanso zikusonyeza kuti m’pofunika kulingalira bwino kuti munthu wina asapezerepo mwayi mwachinyengo pa makonzedwe achikondi ameneŵa.​—2 Atesalonika 3:10-12.

Kusamalira Ana ndi Akazi Amasiye Lerolino

Njira zomwe zinali kutsatidwa ndi atumiki a Mulungu m’nthaŵi yakale zimagwiranso ntchito m’mipingo ya Mboni za Yehova pankhani ya kusonyeza kuganizira ena ndi kuthandiza ovutika. Chikondi chaubale ndicho chizindikiro monga momwe Yesu ananenera kuti: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Ngati ena akusoŵa thandizo kapena akuvutika ndi tsoka linalake, kapena nkhondo, abale padziko lonse amayesetsa kupeza njira zowathandizira mwauzimu ndiponso mwakuthupi. Tiyeni tione zitsanzo zina zamakono zomwe zikusonyeza zimene zikuchitika pankhani imeneyi.

Pedro sakukumbukira zambiri zokhudza amayi ake omwe anamwalira iye ali ndi chaka chimodzi chokha ndi theka. Pamene Pedro anali ndi zaka zisanu, bambo ake nawonso anamwalira. Choncho Pedro anatsala yekha ndi abale ake. Mboni za Yehova zinali zitayamba kale kucheza ndi bambo ake, chotero Pedro ndi abale akewo anayamba kuphunzira Baibulo panyumba.

Pedro akusimba kuti: “Mlungu wotsatira tinayamba kupita ku misonkhano. Pamene tinali kusonkhana ndi abale, tinali kuona chikondi chomwe ankatisonyeza. Mpingo unalidi malo anga obisalako chifukwa abale ndi alongo anandisonyeza chikondi ngati kuti anali makolo anga.” Pedro anakumbukira kuti mkulu wina wachikristu ankatha kumuitana ku nyumba kwake. Kumeneko Pedro anali kucheza ndiponso kusangalala ndi banjalo. “Ndimayamikira kwambiri ndikamakumbukira zimenezi” anatero Pedro, yemwe anayamba kulalikira za chikhulupiriro chake ali ndi zaka 11 ndipo anabatizidwa ali ndi zaka 15. Mothandizidwa ndi ena mumpingo wawo, akulu ake nawonso anapita patsogolo kwambiri mwauzimu.

Palinso nkhani ina yokhudza David. Iye pamodzi ndi mlongo wake amene anabadwa naye monga mapasa ananyanyalidwa pamene makolo awo anapatukana. Agogo awo akuchikazi ndi mchemwali wa amayi awo ndi amene anawalera. “Titakula ndi kuzindikira mmene zinthu zinalili, tinayamba kuona kuti sitinali otetezeka ndipo timakhala okhumudwa. Tinafunikira kudalira chinachake. Mwa mwayi, azakhali athu anakhala a Mboni za Yehova ndipo chifukwa cha zimenezi, anatiphunzitsa choonadi cha m’Baibulo. Abale anatikondanso ndipo tinali mabwenzi awo. Anali kutikonda kwambiri ndipo anatilimbikitsa kukwaniritsa zolinga zinazake ndi kupitiriza kutumikira Yehova. Ndili pafupi kufikitsa zaka khumi, mtumiki wotumikira wina anali kunditenga kupita nane muutumiki wakumunda. Mbale wina anandilipirira zonse zofunika nditapita kumsonkhano. Mbale winanso mpaka anandithandiza kuti ndipereke chopereka ku Nyumba ya Ufumu.”

David anabatizidwa ali ndi zaka 17, ndipo kenako anayamba kutumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Mexico. Ngakhale panopo akuvomereza kuti: “Pali akulu ambiri amene anandithandiza kuti ndiphunzire ndiponso kundipatsa malangizo othandiza. Mwanjira imeneyi, ndikuthana ndi maganizo odziona kukhala osatetezeka ndiponso wosukidwa.”

Abel, yemwe ndi mkulu mumpingo wa ku Mexico kumene kuli akazi amasiye ambiri ofuna thandizo, anasimba kuti: “Ndikuona kuti chinthu chofunika kwambiri chomwe akazi amasiye amafuna ndicho kuwalimbikitsa. Nthaŵi zina amavutika maganizo kwambiri mwakuti amasukidwa. Choncho, n’kofunika kwambiri kuwathandiza ndiponso kuwamvetsera. Ifeyo [akulu mumpingo] timawayendera pafupipafupi. N’kofunika kwambiri kumva mavuto awo modekha. Zimenezi zimawalimbikitsa mwauzimu.” Koma nthaŵi zina chithandizo cha ndalama chimafunikanso. Nthaŵi inayake, Abel anati, “Tsopano tikumanga nyumba ya mlongo wamasiye. Timagwira ntchitoyi m’kati mwa mlungu madzulo ndi Loŵeruka.”

Ponenapo zomwe mkulu wa mpingo wina anachita pothandiza ana ndi akazi amasiye, mkuluyo anati: “Ndimaona kuti ana amasiye amafunikira chikondi chachikristu kwambiri kuposa akazi amasiye. Sachedwa kuona kuti sakondedwa kusiyana ndi ana amene makolo awo onse ali moyo. Amafuna kuwasonyeza chikondi chachikristu m’njira zambiri. N’koyenera kucheza nawo pambuyo pa misonkhano kuti mudziŵe za moyo wawo. Pali mbale wina wokwatira amene makolo ake anamwalira akadali wamng’ono. Nthaŵi zonse ndimam’patsa moni mosangalala ndipo amandikumbatira akandiona. Zimenezi zimalimbikitsa kwambiri chikondi chaubale.”

Yehova “Adzapulumutsa Waumphaŵi”

Kukhulupirira Yehova n’kofunika kwambiri pothana ndi mavuto a akazi ndi ana amasiye. Ponena za iye, Baibulo limati: “Yehova asunga alendo; agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye.” (Salmo 146:9) Ufumu wa Mulungu wolamulidwa ndi Yesu Kristu, ndiwo udzathetseretu mavuto ameneŵa. Polosera ulamuliro wa Mesiya, wamasalmo analemba kuti: “Adzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi.”​—Salmo 72:12, 13.

Pamene mapeto a dongosolo la zinthu lilipoli akuyandikira, mavuto amene Akristu amakumana nawo adzachulukabe. (Mateyu 24:9-13) N’kofunika kuti tsiku lililonse Akristu aziganizira za ena ndi ‘kukhala nacho chikondano chenicheni mwa iwo okha.’ (1 Petro 4:7-10) Amuna achikristu makamaka akulu, afunikira kusonyeza chikondi ndi kuganizira ana amasiye. Nawonso amayi okhwima maganizo a mumpingo angathandize ndi kulimbikitsa akazi amasiye. (Tito 2:3-5) Ndipotu aliyense angathandize mwa kusonyeza kuganizira ena amene akuvutika.

Akristu oona ‘satsekereza chifundo chawo’ akaona ‘mbale wawo ali wosoŵa.’ Amaona kufunika komvera langizo la mtumwi Yohane lakuti: “Tiana, tisakonde ndi mawu, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m’choonadi.” (1 Yohane 3:17, 18) Chotero tiyeni tisamalire “ana amasiye ndi akazi amasiye m’chisautso chawo.”​—Yakobo 1:27.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

“Tisakonde ndi mawu, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m’choonadi.” 1 Yohane 3:18

[Zithunzi patsamba 10]

Akristu oona amasamalira ana ndi akazi amasiye mwakuthupi,mwauzimu ndiponso kuwalimbitsa mtima