Anapirira ‘Kufikira Chimaliziro’
Anapirira ‘Kufikira Chimaliziro’
MU VIDIYO ya 1993 imene amaionetsa kwa anthu obwera kumene kudzatumikira palikulu la Mboni za Yehova, Lyman Alexander Swingle ananena maganizo ake pankhani yotumikira Yehova kuti: “Ifani nsapato zili kuphazi!” *
Mbale Swingle wazaka 90, anachita zimene analimbikitsa ena kuti achite. Iye anapirira ‘kufikira chimaliziro.’ (Mateyu 24:13) Ngakhale amadwala, Lachitatu pa March 7, anapezeka pamsonkhano wa Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova lomwenso iye anali membala. Lachiŵiri mlungu wotsatira, matenda ake anakula ndipo nthaŵi ya 4:26. a.m, dokotala wake anati mbaleyu wamwalira.
Lyman Swingle anayamba kutumikira pamalikulu a Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York pa April 5, 1930. Anatumikira kumeneko zaka pafupifupi 71. Poyamba Mbale Swingle ankagwira ntchito kumene amaikira zikuto kumabuku, kenako kosindikizira mabuku, komanso anathandiza kupanga inki. Mwachidule, Mbale Swingle anagwira ntchito zaka 25 ku dipatimenti yopanga inki. Anagwiranso ntchito zaka 20 ku dipatimenti yolemba mabuku kumalikuluko. Zaka 17 zakumapeto kwa moyo wake, ankagwira ntchito mu Ofesi ya Msungachuma.
Mbale Swingle anali wolimba mtima polalikira Ufumu wa Mulungu. Zaka zake zoyambirira ku Brooklyn, iye pamodzi ndi Arthur Worsley, amene amagona naye m’chipinda chimodzi, ankakonda kuyendetsa boti lina la Mboni mpaka kukafika kumtsinje wa Hudson. Anali kukhala kumeneko mapeto a masabata ambiri ndipo anali kuulutsa uthenga wa Ufumu kwa anthu okhala m’madera a m’mphepete mwa mtsinjewo. Anali kugwiritsa ntchito zokuzira mawu.
Mbale Swingle anabadwa pa November 6, 1910, ku Lincoln, Nebraska. Posakhalitsa, makolo ake anasamukira ku Salt Lake City, Utah. Mu 1913 ali komweko, makolo ake anakhala Ophunzira Baibulo, ndipo limeneli linali dzina la Mboni za Yehova nthaŵi imeneyo. Kwa zaka zambiri, makolo ake ankasunga anthu ambiri okamba nkhani ochokera ku malikulu a Mboni ku Brooklyn, ndipo anthu ameneŵa anam’limbikitsa kwambiri Mbale Swingle. Mu 1923, ali ndi zaka 12, anabatizidwa posonyeza kudzipatulira kwake kwa Mulungu.
Atatumikira zaka zoposa 26 ali mbeta ku Brooklyn, Mbale Swingle anadala kwambiri atakwatira Crystal Zircher pa June 8, 1956. Iwo sanali kusiyana, kulikonse amakhala ali limodzi ngakhale mu utumiki mpaka pamene Crystal anamwalira mu 1998. Zaka zitatu zimenezi zisanachitike, Crystal anadwala sitiroko imene inam’pundula kwabasi. Mmene Mbale Swingle ankasamalira mkazi wake tsiku n’tsiku chinali chitsanzo cha kudzipereka cholimbikitsa kwa onse amene ankawadziŵa, makamaka amene ankaona Mbale Swingle akuonetsa chikondi kwa mkazi wake mwa kum’yendetsa panjinga ya opuwala m’tinjira takumaloko, mkaziyo n’kumagaŵira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kwa anthu odutsa.
Mbale Swingle anali munthu wachilungamo, wokoma mtima ndipo anthu omudziŵa ankamukonda. Monga makolo ake, iye analinso ndi chiyembekezo cha m’Baibulo chokakhala ndi Yesu Kristu mu Ufumu wakumwamba, ndipo tikukhulupirira kuti zimenezi zachitika.—1 Atesalonika 4:15-18, Chivumbulutso 14:13.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 2 Kutanthauza kuti munthu azifa akugwirabe ntchito yake mwachangu.
[Chithunzi patsamba 31]
Mbale Swingle anagwira ntchito zaka 25 kopangira inki
[Chithunzi patsamba 31]
Mbale Swingle sankasiyana ndi Crystal mkazi wake