Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kondwerani Pakuti Mwadziŵa Yehova

Kondwerani Pakuti Mwadziŵa Yehova

Kondwerani Pakuti Mwadziŵa Yehova

“Odala iwo akumva mawu a Mulungu, nawasunga.”​—LUKA 11:28.

1. Kodi Yehova anayamba liti kulankhula ndi anthu?

YEHOVA amakonda anthu ndipo amafunitsitsa kuti azikhala osangalala. Chotero n’zosadabwitsa kuti amalankhula nawo. Kulankhula nawo kumeneku kunayambira m’munda wa Edene. Malinga n’kunena kwa Genesis 3:8, tsiku lina “nthaŵi yamadzulo” Adamu ndi Hava “anamva mawu a Yehova Mulungu.” Ena amati zimenezi zikutanthauza kuti Yehova ankakonda kulankhula ndi Adamu nthaŵi yamadzulo pafupifupi tsiku lililonse. Mulimonse mmene zinalili, Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti Mulungu anapatula nthaŵi yopereka malangizo kwa munthu woyambayo komanso kum’phunzitsa zomwe anayenera kudziŵa kuti akwaniritse maudindo ake.​—Genesis 1:28-30.

2. Kodi mwamuna ndi mkazi oyambawo anatsekereza motani malangizo ochokera kwa Yehova, nanga zotsatira zake zinali zotani?

2 Yehova anapatsa Adamu ndi Hava moyo ndiponso ulamuliro pa nyama ndi pa dziko lonse lapansi. Koma anawaletsa chinthu chimodzi chokha​—kudya chipatso cha mtengo wodziŵitsa zabwino ndi zoipa. Koma Satana atawanyenga, Adamu ndi Hava sanamvere lamulo la Mulungu limeneli. (Genesis 2:16, 17; 3:1-6) Anasankha kuchita zofuna zawo, kudzisankhira chomwe chinali chabwino kwa iwo ndi chomwe chinali choipa. Mwa kuchita mopusa chomwechi, anatsekereza malangizo ochokera kwa Mlengi wawo wachikondi. Zotsatira zake zinali zoopsa kwambiri kwa iwo ndi mbadwa zawo zimene zinali zisanabadwe. Adamu ndi Hava anakalamba ndipo kenako n’kumwalira opanda chiyembekezo chilichonse cha chiukiriro. Mbadwa zawo zinalandira choloŵa cha uchimo limodzi ndi imfa.​—Aroma 5:12.

3. N’chifukwa chiyani Yehova analankhula ndi Kaini, ndipo Kaini anachitanji?

3 Mosasamala kanthu za kupanduka kwa mu Edene, Yehova anapitirizabe kulankhula ndi anthu ake. Kaini, mwana woyamba wa Adamu ndi Hava, anali pangozi yochita tchimo. Yehova anam’chenjeza kuti zochita zakezo zimugwetsa m’mavuto ndipo anamulangiza “kuchita zabwino.” Kaini sanamvere malangizo achikondi ameneŵa ndipo anapha mbale wake. (Genesis 4:3-8) Pamenepo, anthu onse atatu oyambirira omwe anali padziko lapansi anakana malangizo abwino operekedwa ndi amene anawapatsa moyo, Mulungu yemwe amapereka malangizo kwa anthu ake kuti apindule nawo. (Yesaya 48:17) Zimenezitu Yehova anakhumudwa nazo kwabasi!

Yehova Adzivumbula kwa Amuna Akale

4. Kodi Yehova anali wotsimikizira chiyani za mbadwa za Adamu, ndipo polingalira zimenezo, kodi anapereka uthenga wotani wopatsa chiyembekezo?

4 Ngakhale kuti anali ndi ufulu wonse woleka kulankhula ndi anthu, Yehova sanatero. Anali wotsimikizira kuti mbadwa zina za Adamu zidzamvera malangizo Ake mwanzeru. Mwachitsanzo, popereka chiweruzo kwa Adamu ndi Hava, Yehova ananeneratu za kudza kwa “mbewu” yomwe idzalimbane ndi Njoka, Satana Mdyerekezi. Patapita nthaŵi, inayenera kuphwanya mutu wa Satana. (Genesis 3:15) Ulosi umenewu unali uthenga wosangalatsa wopatsa chiyembekezo kwa “iwo akumva mawu a Mulungu, nawasunga.”​—Luka 11:28.

5, 6. Kodi Yehova ankalankhula ndi anthu ake m’njira ziti zaka za zana loyamba C.E. zisanafike, nanga zimenezi anthuwo anapindula nazo motani?

5 Yehova anaulula chifuno chake kwa makolo akale okhulupirika monga Nowa, Abrahamu, Isake, Yakobo, ndi Yobu. (Genesis 6:13; Eksodo 33:1; Yobu 38:1-3) Pambuyo pake, anapereka malamulo onse ku mtundu wa Israyeli kudzera mwa Mose. Chilamulo cha Mose anapindula nacho m’njira zambiri. Mwa kumvera chilamulocho, Israyeli anali wolekana ndi mitundu ina yonse, anali anthu apadera a Mulungu. Mulungu anatsimikizira Aisrayeli kuti ngati adzamvera Chilamulo, adzawadalitsa mwakuthupi komanso mwauzimu, adzawapanga kukhala ufumu wa ansembe ndi mtundu wopatulika. Chilamulocho chinaperekanso malangizo okhudza zakudya ndi ukhondo powathandiza kukhala ndi moyo wathanzi. Komabe, Yehova anawachenjeza za zotsatira zowawa ngati sadzamvera.​—Eksodo 19:5, 6; Deuteronomo 28:1-68.

6 M’kupita kwanthaŵi, mabuku ena ouziridwa anawonjezedwa pa mabuku ovomerezeka a m’Baibulo. Mbiri zakale zimafotokoza mmene Yehova ankachitira ndi mitundu ya anthu. Mabuku a ndakatulo anafotokoza bwino lomwe mikhalidwe yake. Mabuku aulosi ananeneratu mmene chifuno cha Yehova chidzachitikire m’tsogolo. Amuna okhulupirika akale anaphunzira mosamalitsa ndi kugwiritsa ntchito mawu ouziridwa ameneŵa. Wina analemba kuti: “Mawu anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.” (Salmo 119:105) Omwe anali ofunitsitsa kumvetsera, Yehova anawaphunzitsa ndi kuwazindikiritsa.

Kuunika Kuŵaliraŵalirabe

7. Ngakhale kuti Yesu ankachita zozizwitsa, kodi kwenikweni ankadziŵika ndi chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani?

7 Pofika m’zaka za zana loyamba, magulu achipembedzo achiyuda anali ataphatikiza miyambo ya anthu pa Chilamulo. Chilamulo chinagwiritsidwa ntchito molakwika, ndipo m’malo mokhala magwero a chidziŵitso, tsopano chinali mtolo wolemetsa chifukwa cha miyambo imeneyo. (Mateyu 23:2-4) Komabe, mu 29 C.E., Yesu anaonekera monga Mesiya. Chimene anadzera sichinali kungopereka moyo wake m’malo mwa anthu komanso ‘anadzachitira umboni choonadi.’ Ngakhale kuti ankachita zozizwitsa, kwenikweni ankadziŵika kuti “Mphunzitsi.” Chiphunzitso chake chinali ngati kuunika koŵalira mumdima wauzimu wokuta malingaliro a anthu. Moyenera, Yesu mwiniyo anati: “Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi.”​—Yohane 8:12; 11:28; 18:37.

8. Ndi mabuku ati ouziridwa omwe analembedwa m’zaka za zana loyamba C.E., nanga Akristu oyambirira anapindula nawo motani?

8 Kenako anawonjezamo Mauthenga Abwino, mabuku anayi osimba za moyo wa Yesu, ndiponso buku la Machitidwe, losimba za momwe Chikristu chinafalira pambuyo pa imfa ya Yesu. Panalinso makalata ouziridwa olembedwa ndi ophunzira a Yesu, komanso buku la ulosi la Chivumbulutso. Mabuku ameneŵa, kuphatikizapo Malemba Achihebri, ndiwo anapanga mabuku ovomerezeka a m’Baibulo. Pogwiritsa ntchito laibulale youziridwa imeneyi, Akristu akanatha “kuzindikira pamodzi ndi oyera mtima onse, kupingasa, ndi utali, ndi kukwera, ndi kuzama” kwa choonadi. (Aefeso 3:14-18) Akanatha kukhala ndi “mtima wa Kristu.” (1 Akorinto 2:16) Komabe, Akristu oyambirira amenewo sanamvetse mbali iliyonse ya zolinga za Yehova. Mtumwi Paulo analembera olambira anzake kuti: “Tsopano tipenya m’kalirole, ngati chimbuuzi.” (1 Akorinto 13:12) Sanathe kuona zonse mwatsatanetsatane pa kalirole ameneyu. Anayembekezera kudzamvetsa Mawu a Mulungu mokwanira m’tsogolo.

9. Kodi n’kuunikiridwa kotani komwe kwachitika ‘m’masiku otsiriza’?

9 Lerolino, tikukhala m’nyengo yotchedwa “masiku otsiriza,” nyengo yodziŵika ndi “nthaŵi zoŵaŵitsa.” (2 Timoteo 3:1) Mneneri Danieli ananeneratu kuti m’nthaŵi imeneyi “chidziŵitso chidzachuluka.” (Danieli 12:4) Chotero, Yehova, Wolankhula Wamkulu, wathandiza anthu oona mtima kumvetsa tanthauzo la Mawu ake. Khamu la anthu tsopano likudziŵa kuti Kristu Yesu anakhala pampando wachifumu kumwamba kosaonekako m’chaka cha 1914. Akudziŵanso kuti posachedwapa adzathetsa kuipa konse ndi kusintha dziko lonseli kukhala paradaiso. Mbali yofunika imeneyi ya uthenga wabwino wa Ufumu tsopano ikulalikidwa padziko lonse lapansi.​—Mateyu 24:14.

10. Kwa zaka zambiri, kodi anthu aulandira motani uphungu wa Yehova?

10 Inde, m’zochitika zonse za m’mbiri, Yehova wakhala akuuza anthu padziko lapansi chifuno ndi cholinga chake. Nkhani za m’Baibulo zimatchula anthu ochuluka amene anamvera, kugwiritsa ntchito nzeru yaumulungu, ndi kulandira madalitso. Zimasimba za ena omwe anakana uphungu wachikondi wa Mulungu; omwe anatsatira njira ya tsoka ya Adamu ndi Hava. Yesu anayerekeza zimenezi pamene ananena za njira ziŵiri zophiphiritsa. Njira yopita ku chiwonongeko. Pokhala yaikulu ndi yotakata, ambiri okana Mawu a Mulungu akuyenda m’njira imeneyi. Njira ina ndi ya kumoyo wosatha. Ngakhale kuti n’njopapatiza, ndi njira yomwe mukuyenda anthu oŵerengeka amene amavomereza kuti Baibulo lilidi Mawu a Mulungu, ndipo amakhala mogwirizana nalo.​—Mateyu 7:13, 14.

Kuyamikira Zomwe Tili Nazo

11. Kodi kudziŵa kwathu Baibulo ndi kulikhulupirira ndi umboni wa chiyani?

11 Kodi muli m’gulu la anthu omwe asankha njira ya kumoyo? Ngati ndi choncho, mosakayika mudzafuna kukhalabe m’njira imeneyo. Kodi mungachite motani zimenezo? Lingalirani nthaŵi zonse ndi kuyamikira madalitso omwe adza m’moyo wanu chifukwa chodziŵa choonadi cha Baibulo. Kulabadira kwanu uthenga wabwino kokhako ndi umboni wa madalitso a Mulungu. Yesu anasonyeza zimenezi popemphera kwa Atate wake m’mawu aŵa: “Ndivomerezana ndi Inu, Atate, Mwini kumwamba ndi dziko lapansi, kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziŵitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda.” (Mateyu 11:25) Asodzi ndi okhometsa misonkho anazindikira chiphunzitso cha Yesu, pamene atsogoleri achipembedzo ophunzira kwambiri sanatero. Yesu anatinso: “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine am’koka iye.” (Yohane 6:44) Ngati Baibulo mukulidziŵa, ndipo mumakhulupirira ndi kutsatira ziphunzitso zake, umenewu ndi umboni wakuti Yehova wakukokani. Chimenechi n’chifukwa chokondwera.

12. Kodi Baibulo limatithandiza kuzindikira m’njira zotani?

12 Mawu a Mulungu ali ndi choonadi chomasula ndipo amazindikiritsa. Omwe amakhala mogwirizana ndi chidziŵitso cha m’Baibulo ndi omasuka ku miyambo, ziphunzitso zonyenga, ndi kusazindikira zomwe zakuta miyoyo ya anthu mamiliyoni ambiri. Mwachitsanzo, kudziŵa zoona zake pankhani ya akufa kumatimasula ku mantha alionse akuti akufa angativulaze kapena kuti okondedwa athu omwe anamwalira akuvutika. (Ezekieli 18:4) Kudziŵa zoona zake pankhani ya angelo oipa kumatithandiza kupeŵa kugwa m’mavuto chifukwa chokhulupirira mizimu. Chiphunzitso cha chiukiriro n’cholimbikitsa kwa omwe okondedwa awo anamwalira. (Yohane 11:25) Maulosi a m’Baibulo amatithandiza kuzindikira nthaŵi yomwe tikukhalamo ino ndi kutipatsa chidaliro m’malonjezo a Mulungu a m’tsogolo. Amalimbitsanso chiyembekezo chathu chodzakhala ndi moyo kosatha.

13. Kodi kumvera Mawu a Mulungu kumatipindulitsa motani mwakuthupi?

13 Mfundo zachikhalidwe zaumulungu zopezeka m’Baibulo zimatiphunzitsa kukhala ndi moyo umene umatipindulitsa mwakuthupi. Mwachitsanzo, timaphunzira kupeŵa makhalidwe owononga matupi, monga kusuta fodya ndi kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo. Timapeŵa uchidakwa. (2 Akorinto 7:1) Kumvera malamulo a Mulungu pankhani ya khalidwe kumatiteteza ku matenda opatsirana pochita chiwerewere. (1 Akorinto 6:18) Mwa kumvera uphungu wa Mulungu wakuti tipeŵe kukonda ndalama, sitisoŵa mtendere m’maganizo, monga momwe amachitira ena, pofunafuna kulemera. (1 Timoteo 6:10) Kodi mwapindula mwakuthupi m’njira ziti chifukwa chogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu m’moyo wanu?

14. Kodi mzimu woyera umakhudza motani moyo wathu?

14 Tikamakhala mogwirizana ndi Mawu a Mulungu, timalandira mzimu woyera wa Yehova. Timakulitsa umunthu wonga wa Kristu, wodziŵika ndi mikhalidwe yochititsa chidwi monga chifundo ndi kukoma mtima. (Aefeso 4:24, 32) Mzimu wa Mulungu umabalanso zipatso zake mwa ife monga chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chikhulupiriro, chifatso, ndi chiletso. (Agalatiya 5:22, 23) Mikhalidwe imeneyi imalimbikitsa ubwenzi wosangalatsa ndi watanthauzo ndi ena kuphatikizapo apabanja lathu. Timapeza nyonga zomwe zimatithandiza kuthana ndi mavuto molimba mtima. Kodi mukutha kuona mmene mzimu woyera wasinthira moyo wanu?

15. Kodi timapindula motani pamene tikugwirizanitsa miyoyo yathu ndi chifuno cha Mulungu?

15 Tikagwirizanitsa miyoyo yathu ndi chifuno cha Mulungu, timalimbitsa unansi wathu ndi Yehova. Timatsimikizira mowonjezeka kuti amatimvetsa ndi kutikonda. Timaphunzira kuchokera m’zotichitikira kuti amatithandiza m’nthaŵi zovuta. (Salmo 18:18) Timadziŵa kuti amamvetseradi mapemphero athu. (Salmo 65:2) Timadalira malangizo ake, ndi chitsimikizo chakuti tidzapindula nawo. Ndipo tili n’chiyembekezo chamtengo wapatali chakuti m’nthaŵi yake Mulungu adzaika ungwiro mwa okhulupirika ndi kuwapatsa mphatso ya moyo wosatha. (Aroma 6:23) “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu,” analemba motero wophunzira Yakobo. (Yakobo 4:8) Kodi munaona kuti unansi wanu ndi Yehova walimba mutayandikira kwa iye?

Chuma Chosayerekezeka

16. Kodi Akristu ena a m’zaka za zana loyamba anasintha m’zinthu ziti?

16 Paulo anakumbutsa Akristu odzozedwa ndi mzimu a m’zaka za zana loyamba kuti ena a iwo nthaŵi inayake anali adama, achigololo, ogonana amuna kapena akazi okhaokha, akuba, osirira, zidakwa, olalata, ndi olanda. (1 Akorinto 6:9-11) Choonadi cha Baibulo chinawathandiza kusintha m’zambiri; mwakuti ‘anasambitsidwa ndi kuyeretsedwa.’ Yesani kulingalira mmene moyo wanu ukanakhalira mukanapanda kuphunzira choonadi chomasulachi kuchokera m’Baibulo. Ndithudi choonadi ndi chuma chosayerekezeka. Ndife okondwa zedi kuti Yehova amalankhula nafe.

17. Kodi Mboni za Yehova zalandira motani chakudya chauzimu m’misonkhano yachikristu?

17 Komanso, lingalirani za madalitso omwe tili nawo mu ubale wathu wa anthu amitundu yosiyanasiyana! “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amapereka chakudya panthaŵi yake, kuphatikizapo mabaibulo, magazini, ndi zofalitsa zina m’zinenero zambiri. (Mateyu 24:45-47) M’misonkhano ya mpingo m’chaka cha 2000, Mboni za Yehova m’mayiko ambiri zinapenda mfundo zazikulu kuchokera m’mabuku akuluakulu asanu ndi atatu a Malemba a Chihebri. Zinakambirana nkhani 38 za m’Baibulo kuchokera m’buku la Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Zinaphunzira mitu 23 yotsirizira m’buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako komanso pafupifupi buku lonse la Samalani Ulosi wa Danieli! Zinaphunzira nkhani zina zapadera 36 kuchokera m’magazini a Nsanja ya Olonda kuwonjezera pa mitu yophunzira 52. Kuwonjezera pamenepo, anthu a Yehova analandira makope 12 a Utumiki Wathu wa Ufumu ndi kumvetsera nkhani za anthu onse za mlungu ndi mlungu m’mitu yosiyanasiyana ya nkhani za m’Baibulo. Ndithudi chidziŵitso chochuluka chauzimu chaperekedwa.

18. Kodi timathandizidwa m’njira ziti mumpingo wachikristu?

18 Padziko lonse lapansi, mipingo yoposa 91,000 imapereka thandizo ndi chilimbikitso kudzera m’misonkhano ndi mayanjano. Komanso timathandizidwa ndi Akristu anzathu okhwima omwe ngofunitsitsa kutithandiza mwauzimu. (Aefeso 4:11-13) Inde, tapindula kwambiri kulandira chidziŵitso cha choonadi. N’kokoma kudziŵa ndi kutumikira Yehova. Mawu a wamasalmo ndi oonadi. Iye analemba kuti: “Odala anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.”​—Salmo 144:15.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi Yehova analankhula ndi yani Chikristu chisanayambe?

• Kodi kuunika kwauzimu kunaŵaliraŵalirabe motani m’zaka za zana loyamba? Nanga m’nthaŵi yathu ino?

• Kodi kukhala ndi moyo mogwirizana ndi kudziŵa Yehova kumapindulitsa motani?

• N’chifukwa chiyani tikukondwera kuti tadziŵa Mulungu?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 8, 9]

Yehova anauza Mose, Nowa, ndi Abrahamu za chifuno chake

[Chithunzi patsamba 9]

M’masiku athu ano, Yehova waunikira Mawu ake

[Zithunzi patsamba 10]

Talingalirani za madalitso omwe tili nawo mu ubale wathu wa anthu amitundu yosiyanasiyana!