Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pezani Chimwemwe mwa Kukhala Wopatsa!

Pezani Chimwemwe mwa Kukhala Wopatsa!

Pezani Chimwemwe mwa Kukhala Wopatsa!

“Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”​—MACHITIDWE 20:35.

1. Kodi Yehova amapereka chitsanzo chotani chakuti kupatsa kumadzetsa chimwemwe?

CHIMWEMWE komanso madalitso zomwe zimadza chifukwa chodziŵa choonadi, ndi mphatso zamtengo wapatali zochokera kwa Mulungu. Amene amudziŵa Yehova ali n’zifukwa zambiri zosangalalira. Koma ngakhale kuti kulandira mphatso n’kokondweretsa, kuperekanso kumadzetsa chimwemwe. Yehova ndi Wopatsa “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro,” ndipo iye ndi “Mulungu wachimwemwe.” (Yakobo 1:17; 1 Timoteo 1:11, NW) Iye amapereka ziphunzitso zabwino kwa onse omvetsera ndipo amakondwera ngati ophunzira akewo ali omvera, monga momwe makolo amasangalalira ngati ana awo akumvera malangizo achikondi.​—Miyambo 27:11.

2. (a) Kodi Yesu ananenanji pankhani ya kupatsa? (b) Kodi timapeza chimwemwe chotani pophunzitsa ena choonadi cha Baibulo?

2 Momwemonso, pamene Yesu anali padziko lapansi anali wokondwa kuona anthu akulabadira ziphunzitso zake. Mtumwi Paulo anabwereza mawu a Yesu akuti: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Chimwemwe chimene timapeza pophunzitsa ena choonadi cha Baibulo si kungokhutira kokha kuti winawake akugwirizana ndi zikhulupiriro za chipembedzo chathu. Mosiyana kwambiri ndi zimenezo, ndife achimwemwe podziŵa kuti tikupereka chinachake chamtengo wapatali komanso chosatha. Mwa kupereka mphatso yauzimu, tingathandize anthu kupindula pakali pano komanso ku nthaŵi za nthaŵi.​—1 Timoteo 4:8.

Kupatsa Kumadzetsa Chimwemwe

3. (a) Kodi mtumwi Paulo ndi mtumwi Yohane anasonyeza motani kuti anali achimwemwe pothandiza ena mwauzimu? (b) N’chifukwa chiyani kuphunzitsa ana athu choonadi cha Baibulo kuli njira yosonyezera chikondi?

3 Inde, monga momwe Yehova ndi Yesu amakondwera popereka mphatso zauzimu, Akristu nawonso amakondwera. Mtumwi Paulo anali wachimwemwe podziŵa kuti anathandiza ena kuphunzira choonadi cha Mawu a Mulungu. Polembera mpingo wa ku Tesalonika, iye anati: “Chiyembekezo chathu, kapena chimwemwe, kapena korona wakudzitamandira naye n’chiyani? Si ndinu nanga, pamaso pa Ambuye wathu Yesu m’kufika kwake? Pakuti inu ndinu ulemerero wathu ndi chimwemwe chathu.” (1 Atesalonika 2:19, 20) Momwemonso mtumwi Yohane, ponena za ana ake auzimu, analemba kuti: “Ndilibe chimwemwe choposa ichi, chakuti ndimva za ana anga kuti ali kuyenda m’choonadi.” (3 Yohane 4) Lingaliraninso za chimwemwe chomwe timapeza pothandiza ana obereka tokha kukhala ana athu auzimu! Makolo amasonyeza chikondi mwa kulera ana “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Pamenepo makolo amasonyeza kufunitsitsa kuti ana awo adzasangalale m’tsogolo kosatha. Ana ameneŵa akamvera, makolo amasangalala kwambiri ndi kukhutira.

4. N’chochitika chiti chomwe chikusonyeza chimwemwe chimene chimadza mwa kupereka mphatso zauzimu?

4 Dell ndi mpainiya wokhazikika komanso mayi wa ana asanu. Iye anati: “Ndikutha kumvetsa momwe mtumwi Yohane ankamvera ponena mawu akewo chifukwa chakuti nanenso ndikunyadira kwambiri kuti ana anga anayi ‘akuyenda m’choonadi.’ Ndikudziŵa kuti ngati mabanja ndi ogwirizana pa kulambira koona, zimadzetsa ulemu ndi ulemerero kwa Yehova, choncho ndine wokhutira kwambiri kuona mmene wadalitsira khama langa pophunzitsa ana anga choonadi. Chiyembekezo chamtengo wapatali cha moyo wosatha m’Paradaiso limodzi ndi banja langa chimandikhutiritsa ndi kundisonkhezera kuti ndithe kupirira mavuto ndi zopsinja.” N’zomvetsa chisoni kuti mwana wamkazi mmodzi wa Dell anachotsedwa mumpingo chifukwa chotsata njira yomwe si yachikristu. Komabe, Dell akuyesetsa kukhalabe ndi malingaliro abwino. Iye anati: “Ndili n’chiyembekezo chakuti tsiku lina mwana wangayo adzabwerera kwa Yehova modzichepetsa ndi moona mtima. Komabe ndikuthokoza Mulungu kuti ana anga ena onse akupitiriza kum’tumikira mokhulupirika. Chimwemwe chomwe ndili nacho chakhala gwero lenileni la chilimbikitso kwa ine.”​—Nehemiya 8:10.

Kupanga Mabwenzi Osatha

5. Tikadzipereka m’ntchito yopanga ophunzira, kodi timakhala okhutira podziŵa chiyani?

5 Yesu analangiza otsatira ake kupanga ophunzira achikristu ndi kuwaphunzitsa za Yehova ndi zifuno zake. (Mateyu 28:19, 20) Modzipereka, Yehova ndi Yesu athandiza anthu kuphunzira njira ya choonadi. Chotero pamene tadzipereka m’ntchito yopanga ophunzira, timakhutira podziŵa kuti tikutsanzira chitsanzo cha Yehova ndi Yesu, monga momwe Akristu oyambirira anachitira. (1 Akorinto 11:1) Tikagwirizana ndi Mulungu Wamphamvuyonse ndi Mwana wake wokondedwa m’njira imeneyi, miyoyo yathu imakhala ndi tanthauzo lenileni. Ndi dalitsotu lalikulu kukhala m’gulu la “antchito anzake” a Mulungu! (1 Akorinto 3:9) Ndipo kodi si zochititsa chidwi kuti ngakhale angelo akugwira nawo ntchito imeneyi yolalikira uthenga wabwino?​—Chivumbulutso 14:6, 7.

6. Pamene tikupereka mphatso zauzimu, kodi mabwenzi athu amakhala yani?

6 Kwenikweni, mwa kugwira ntchito imeneyi yopereka mphatso zauzimu kwa ena, sikuti zimangothera pa kukhala antchito anzake a Mulungu basi, komanso timapanga naye ubwenzi wosatha. Chifukwa cha chikhulupiriro chake, Abrahamu anatchedwa bwenzi la Yehova. (Yakobo 2:23) Titayesetsa kuchita chifuno cha Mulungu, nafenso tidzakhala mabwenzi a Mulungu. Tikatero, tidzakhalanso mabwenzi a Yesu. Iye anauza ophunzira ake kuti: “Ndatcha inu abwenzi; chifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziŵitsani.” (Yohane 15:15) Ambiri amanyadira kukhala mabwenzi a anthu otchuka kapena akuluakulu aboma, koma ife ndife mabwenzi a anthu aŵiri akuluakulu kuposa wina aliyense m’chilengedwe chonse!

7. (a) Kodi mayi wina anapanga motani bwenzi lenileni? (b) Kodi inuyo zoterezi zinakuchitikiranipo?

7 Kuwonjezera pamenepo, tikathandiza anthu kum’dziŵa Mulungu, amakhalanso mabwenzi athu, ndipo zimatipatsa chimwemwe chapadera. Joan, amene akukhala ku United States, anayamba kuphunzira Baibulo ndi mayi wina wodziŵika ndi dzina lakuti Thelma. Ngakhale am’banja la Thelma ankatsutsa phunziroli, iye anapirira ndipo patangotha chaka chimodzi anabatizidwa. Joan analemba kuti: “Unansi wathu sunathere pomwepo; m’malo mwake, unakhala ubwenzi womwe tsopano watha pafupifupi zaka 35. Nthaŵi zambiri tinkapitira limodzi muutumiki ndi m’misonkhano ikuluikulu. Patapita nthaŵi, ndinasamukira ku nyumba yatsopano pa mtunda wa makilomita 800. Koma Thelma akupitiriza kunditumizira makalata osangalatsa ndi olimbikitsa kwambiri, kundiuza kuti amandiganizira nthaŵi zonse ndi kundithokoza pokhala bwenzi ndi chitsanzo chake komanso chifukwa chomuphunzitsa choonadi kuchokera m’Baibulo. Kukhala ndi bwenzi lenileni ndi lokondedwa ngati limeneli ndi mphoto yamtengo wapatali ya zomwe ndinachita pom’thandiza kuphunzira za Yehova.”

8. Ndi malingaliro abwino ati amene angatithandize mu utumiki?

8 Chiyembekezo chakuti tipeza winawake amene akufunitsitsa kuphunzira choonadi chingatithandize kupirira ngakhale tikumane ndi anthu ambiri opanda chidwi ndi Mawu a Yehova. Kupanda chidwi koteroko kungayese chikhulupiriro ndi kupirira kwathu. Komabe, malingaliro oyenera adzatithandiza. Fausto, wa ku Guatemala, anati: “Ndikamalalikira kwa ena, ndimalingalira za chisangalalo chimene ndingakhale nacho ngati munthu amene ndikulankhula nayeyo atasintha n’kukhala mbale kapena mlongo wauzimu. Ndimaganiza kuti m’kupita kwanthaŵi, munthu mmodzi yekha mwa omwe ndidzakumana nawo adzalandira choonadi cha Mawu a Mulungu. Malingaliro amenewo amandithandiza kupitirizabe kulalikira ndipo ndimakhala wachimwemwe.”

Kusunga Chuma Kumwamba

9. Kodi Yesu ananenanji pankhani ya chuma kumwamba, nanga kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani?

9 Si kophweka nthaŵi zonse kupanga ana athu kapena anthu ena kukhala ophunzira. Kumafuna nthaŵi yokwanira, kuleza mtima, ndi khama. Komabe, kumbukirani kuti ambiri ali ofunitsitsa kugwira ntchito zolimba kuti asunge chuma chakuthupi chochuluka, zinthu zomwe kaŵirikaŵiri sizidzetsa chimwemwe ndipo n’zosakhalitsa. Yesu anauza omvetsera ake kuti n’kwabwino kuyesetsa kupeza chuma chauzimu. Iye anati: “Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziwononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba: koma mudzikundikire nokha chuma m’Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba.” (Mateyu 6:19, 20) Mwa kutsata zolinga zauzimu​—zomwe zikuphatikizapo kugwira ntchito yofunika kwambiri yopanga ophunzira​—tingakhale okhutira podziŵa kuti tikuchita chifuno cha Mulungu ndikuti adzatipatsa mphoto. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.”​—Ahebri 6:10.

10. (a) N’chifukwa chiyani Yesu anali ndi chuma chauzimu? (b) Kodi Yesu anadzipereka yekha motani, nanga ndi phindu lalikulu lotani lomwe ena amapezapo?

10 Tikachita khama popanga ophunzira, timadzisungira “chuma m’Mwamba,” mogwirizana ndi zomwe Yesu ananena. Zimenezi zimatipatsa chimwemwe cha kulandira. Pamene tipereka mooloŵa manja, pamapeto pake timalandira zochuluka. Yesu mwiniyo anali atatumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zosaŵerengeka. Talingalirani za chuma chomwe anali atasunga kumwamba! Komabe, Yesu sanatsate zofuna zake. Mtumwi Paulo analemba kuti: ‘[Yesu] anadzipereka yekha chifukwa cha machimo athu, kuti akatilanditse ife m’nyengo ya pansi pano ino yoipa, monga mwa chifuniro cha Mulungu ndi Atate wathu.’ (Agalatiya 1:4) Si kuti Yesu anangodzipereka mu utumiki mokha, komanso anapereka moyo wake weniweniwo monga dipo kuti ena akapeze mwayi wosunga chuma kumwamba.

11. N’chifukwa chiyani mphatso zauzimu zili zabwino kuposa mphatso zakuthupi?

11 Mwa kuphunzitsa anthu za Mulungu, timawathandiza kuona mmene nawonso angasungire chuma chosawonongeka chauzimu. Kodi ndi mphatso yaikulu yotani imene mungapereke? Ngati mnzanu mutam’patsa watchi yamtengo wapatali, galimoto, kapena nyumba, n’zodziŵikiratu kuti mnzanuyo adzayamikira ndi kunyadira, ndipo inuyo mudzakhala wachimwemwe chifukwa mwapereka. Koma kodi mphatso imeneyo idzaoneka motani m’zaka 20? M’zaka 200? M’zaka 2,000? Komano, ngati mutadzipereka kuthandiza munthu kutumikira Yehova, iye angapindule ndi mphatso imeneyo kosatha.

Kufufuza Ofuna Choonadi

12. Kodi ambiri adzipereka motani kuti athandize ena mwauzimu?

12 Kuti akhale achimwemwe mwa kupereka mphatso zauzimu, anthu a Yehova afika kumalekezero adziko. Masauzande asiya nyumba zawo ndi mabanja awo ndi kukayamba utumiki waumishonale m’mayiko ena, komwe anafunikira kukaphunzira chinenero ndi chikhalidwe chatsopano. Ena asamukira m’madera ena m’dziko lawo lomwelo kukathandiza komwe olengeza Ufumu akufunika kwambiri. Ndipo ena aphunzira chinenero chatsopano, kuti akhale ndi mwayi wokalalikira kwa anthu ochokera kumayiko ena amene akukhala m’dera lakwawoko. Mwachitsanzo, atalera ana aŵiri omwe tsopano akutumikira pa likulu la dziko lonse la Mboni za Yehova, banja lina ku New Jersey, U.S.A., linayamba kuchita upainiya ndipo linaphunzira Chitchaina. M’zaka zitatu zokha, anachita maphunziro a Baibulo ndi anthu 74 olankhula Chitchaina omwe anali kuphunzira pa koleji ina ya komweko. Kodi mukufutukula utumiki wanu m’njira iliyonse kuti mupeze chimwemwe chochuluka m’ntchito yopanga ophunzira?

13. Kodi mungachitenji ngati mukufuna kukhala ndi utumiki wopindulitsa kwambiri?

13 Mwinamwake mukulakalaka mutakhala ndi phunziro la Baibulo koma simukulipeza. M’mayiko ena n’kovuta kupeza osonyeza chidwi. Mwinamwake anthu amene mumakumana nawo sasonyeza chidwi ndi Baibulo. Ngati ndi choncho, mwina mungatchule chikhumbo chanucho mobwerezabwereza m’pemphero, podziŵa kuti Yehova ndi Yesu Kristu ali ndi chidwi kwambiri ndi ntchito imeneyi ndipo angakutsogolereni kwa munthu wonga nkhosa. Funsirani nzeru kwa ena mu mpingo wanu omwe agwira ntchitoyo kwa nthaŵi yaitali kapena amene akupindula kwambiri ndi utumiki wawo. Gwiritsani ntchito maphunziro ndi malingaliro operekedwa m’misonkhano yachikristu. Gwiritsani ntchito malangizo a oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo. Koma choposa zonse, musagwe mphwayi n’kusiya. Mwamuna wanzeru analemba kuti: “Mamawa fesa mbewu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziŵa ziti zidzalola bwino.” (Mlaliki 11:6) Padakali pano, kumbukirani amuna okhulupirika monga Nowa ndi Yeremiya. Ngakhale kuti si onse amene analabadira ulaliki wawo, komabe utumiki wawo unali wopambana. Choposa zonse, unakondweretsa Yehova.

Kuchita Zomwe Mungathe

14. Kodi Yehova amawaona bwanji anthu amene akalamba akumutumikira?

14 N’kutheka kuti pa zifukwa zina, simutha kuchita monga momwe m’mafunira muutumiki. Mwachitsanzo, ukalamba ungakulepheretseni kuchita zambiri potumikira Yehova. Komabe, kumbukirani zimene mwamuna wanzeru analemba. Iye anati: “Imvi ndiyo korona wa ulemu, [ikapezedwa] m’njira ya chilungamo.” (Miyambo 16:31) Yehova amakondwera ndi amene wathera nthaŵi ya moyo wake pomutumikira. Komanso, Malemba amati: “Ngakhale mpaka mudzakalamba Ine [Yehova] ndine, ndipo ngakhale mpaka tsitsi laimvi, Ine ndidzakusenzani inu; ndalenga, ndipo ndidzanyamula; inde, ndidzasenza, ndipo ndidzapulumutsa.” (Yesaya 46:4) Atate wathu wachikondi wakumwamba akulonjeza kulimbikitsa ndi kuthandiza okhulupirika ake.

15. Kodi mukukhulupirira kuti Yehova amamvetsa mavuto anu? Chifukwa chiyani?

15 Mwinamwake mukupirira matenda, kutsutsa kwa mwamuna kapena mkazi wanu wosakhulupirira, maudindo aakulu a m’banja, kapena mavuto ena aakulu. Yehova amadziŵa zomwe sitingathe kuchita ndiponso zovuta zathu, ndipo amatikonda chifukwa cha kuyesetsa kwathu kumutumikira. Zimenezi zili choncho ngakhale timachita zochepa kusiyana ndi zomwe ena amachita. (Agalatiya 6:4) Yehova akudziŵa kuti ndife opanda ungwiro, ndipo amayembekezera kuti tim’chitire zomwe tingathe. (Salmo 147:11) Ngati tichita zomwe tingathe, tingakhale otsimikiza kuti ndife amtengo wapatali kwa Mulungu ndikuti sadzaiŵala zomwe tachita mokhulupirika.​—Luka 21:1-4.

16. Kodi mpingo wonse umaphatikizidwa motani popanga wophunzira?

16 Kumbukiraninso kuti ntchito yopanga ophunzira ikugwiridwa ndi gulu. Munthu mmodzi sapanga wophunzira payekha, monganso momwe dontho limodzi la madzi silingakulitse mbewu. N’zoona kuti Mboni imodzi ingapeze munthu wachidwi ndi kuphunzira naye Baibulo. Koma wachatsopano ameneyo akangobwera ku Nyumba ya Ufumu, mpingo wonse umam’thandiza kuzindikira choonadi. Chikondi chaubale chimasonyeza ntchito ya mzimu wa Mulungu. (1 Akorinto 14:24, 25) Ana ndi achinyamata amapereka mayankho ogwira mtima, kusonyeza wachatsopanoyo kuti ana athu ndi osiyana ndi ana akudziko. Odwala, ofooka, ndi okalamba mu mpingo amaphunzitsa wachatsopanoyo tanthauzo la kupirira. Mosalingalira za msinkhu kapena mavuto amene tikukumana nawo, tonsefe timachita mbali yofunika kuthandiza atsopano pamene chikondi chawo pa choonadi cha Baibulo chikuzama ndipo amapita patsogolo kufikira pa kubatizidwa. Ola lililonse limene timathera mu utumiki, ulendo uliwonse wobwereza, nthaŵi iliyonse pamene tikukambirana ndi munthu wachidwi pa Nyumba ya Ufumu, zingaoneke ngati zosapindulitsa mwa izo zokha, koma ndi mbali ya ntchito yaikulu imene Yehova akukwaniritsa.

17, 18. (a) Kuwonjezera pa kugwira ntchito yopanga ophunzira, kodi tingapeze motani chimwemwe mwa kukhala wopatsa? (b) Mwa kupeza chimwemwe pokhala opatsa, kodi timatsanzira yani?

17 Inde, kuwonjezera pa kugwira ntchito yofunika yopanga ophunzira, ife monga Akristu timapezanso chimwemwe popereka m’njira zinanso. Tingaike padera ndalama zopereka mwaufulu kuchirikiza kulambira koyera ndi kuthandiza osoŵa. (Luka 16:9; 1 Akorinto 16:1, 2) Tingayesetse kupeza mpata wochereza ena. (Aroma 12:13) Tingayesetse ‘kuchitira onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.’ (Agalatiya 6:10) Ndiponso, m’njira yaing’ono koma yofunika, tingakhale opatsa, mwa kulembera ena makalata, kuwaimbira telefoni, kuwapatsa mphatso, kuwathandiza ntchito zina, ndi kuwauza mawu olimbikitsa.

18 Mwa kupatsa, timasonyeza kuti timatsanzira Atate wathu wakumwamba. Timasonyezanso chikondi chathu chaubale, chizindikiro cha Akristu enieni. (Yohane 13:35) Kukumbukira zinthu zimenezi kungatithandize kupeza chimwemwe mwa kukhala wopatsa.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi Yehova ndi Yesu apereka motani chitsanzo cha kupereka mphatso zauzimu?

• Kodi tingapange motani mabwenzi osatha?

• Kodi tingatsate njira ziti kuti utumiki wathu ukhale wopindulitsa kwambiri?

• Kodi onse mumpingo angapeze bwanji chimwemwe mwa kukhala opatsa?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 13]

Ana akamalabadira zomwe akuphunzira, makolo amanyadira kwambiri ndipo amakhutira

[Chithunzi patsamba 15]

Popanga ophunzira, tingapange mabwenzi enieni

[Chithunzi patsamba 16]

Yehova amatiyangata muukalamba wathu

[Zithunzi patsamba 17]

Timapeza chimwemwe mwa kupatsa m’njira zing’onozing’ono koma zofunika kwambiri