Kodi Mulungu Amalangadi Anthu M’moto wa Helo?”
Kodi Mulungu Amalangadi Anthu M’moto wa Helo?”
“Kodi mukuchita maphunziro apamwamba a zaumulungu?”
Funso limeneli linadzidzimutsa Joel ndi Carl. Anyamata aŵiri ameneŵa omwe amagwira ntchito yodzifunira palikulu la Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York, anali kuona mabuku m’sitolo lina lapafupi. Pamene Joel anali kupenda mabuku amene amandandalika mawu a m’Baibulo, Carl anayamba kum’simbira zimene anakambirana ndi munthu wina muutumiki. Mwamuna wina amene anali pafupi anamva zina zimene anali kukambirana, ndipo anafika pafupi.
Komabe, mwamunayu anali ndi nkhani ina osati kuti angodziŵa ngati anyamataŵa anali kuchita maphunziro apamwamba a zaumulungu. Anafotokoza kuti: “Ndine Myuda, ndipo anzanga ena achikristu andiuza kuti ndidzapsa m’helo chifukwa Ayuda anakana Yesu. Zimenezi zikundivutitsa maganizo kwambiri. Chilangochi chikuoneka kuti si chachilungamo poganizanso kuti chikuchokera kwa Mulungu wachikondi. Kodi Mulungu amalangadi anthu m’moto wa helo?”
Joel ndi Carl anamuuza mwamuna woona mtimayu kuti iwo anali kuphunzira Baibulo mwakhama. Anamusonyeza m’Malemba kuti anthu omwalira sadziŵa kanthu ndipo ali m’tulo ta imfa kuyembekeza kuti adzauke kwa akufa. Choncho, sakumana ndi mavuto kapena kuzunzika ndi moto wa helo. (Salmo 146:3, 4; Mlaliki 9:5, 10; Danieli 12:13; Yohane 11:11-14, 23-26) Atatha kukambirana kwa mphindi 45, mwamunayu anapereka adiresi yake kwa Joel ndi Carl ndipo anapempha kuti adzam’fotokozere zambiri pankhaniyi.
Ngati helo akanakhala malo a moto kumene anthu amakazunzika, ndani akanapempha kuti am’tumize kumeneko? Komatu, Yobu, kholo lakale, pofuna kuti alekane ndi mavuto, anapempha kuti: “Ndani adzandipatsa zimenezi, kuti munganditeteze m’helo, ndi kundibisa mpaka mkwiyo wanu utapita?” (Yobu 14:13, Douay Version) Inde, Yobu sanali kukhulupirira kuti helo ndi malo amene anthu amakazunzika. M’malo mwake, iye anafuna chitetezo kumeneko. Imfa ndiyo kusakhalako, ndipo helo wa m’Baibulo ndi manda a anthu onse.
Kodi mukufuna kudziŵa zambiri za zimene zimachitika tikamwalira ndi zimene timayembekezera? Ngati ndi tero, yankhani pempho lotsatirali.