Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Munthu Akamwalira Amakhala ndi Moyo Kwinakwake?

Kodi Munthu Akamwalira Amakhala ndi Moyo Kwinakwake?

Kodi Munthu Akamwalira Amakhala ndi Moyo Kwinakwake?

“ATAFA munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi?” Yobu, kholo lakale, anafunsa funso limeneli zaka pafupifupi 3,500 zapitazo. (Yobu 14:14) Funso limeneli lazunguza anthu kwa zaka zikwi zambiri. Kwa nthaŵi yaitali, anthu kulikonse aganiza za nkhaniyi ndipo akhala ndi ziphunzitso zosiyanasiyana.

Ambiri amene amati ndi Akristu amakhulupirira kuti munthu akamwalira amapita kumwamba kapena ku helo. Ahindu amakhulupirira kuti munthu akamwalira amakabadwanso kwina. Mfumu Muawiyah yemwe ndi wachiŵiri kwa mtsogoleri pa likulu lina la Asilamu, anafotokoza zimene iwo amakhulupirira pankhaniyi. Anati: “Timakhulupirira kuti munthu akamwalira, kumakhala tsiku lopereka chiŵeruzo pamene iye amakaonekera pamaso pa Mulungu, Allah, mofanana ndi kuonekera pamaso pa oweruza.” Malinga ndi zimene Asilamu amakhulupirira, Allah kenako amapenda moyo wa munthu aliyense ndipo amam’tumiza kuparadaiso kapena kumoto wa helo.

Ku Sri Lanka, Abuda ndi Akatolika amasiya zitseko ndi mawindo zotsegula munthu akamwalira panyumba pawo. Amayatsa nyali, ndipo amaika bokosi la maliro molozetsa miyendo ya womwalirayo kukhomo la kutsogolo. Amakhulupirira kuti zimenezi zimathandiza kuti mzimu wa womwalirayo utuluke.

Malinga n’kunena kwa Ronald M. Berndt wa pa Yunivesite ya Western Australia, Aaborijini a ku Australia amakhulupirira kuti “anthu ali ndi mzimu wosafa.” Mafuko ena a mu Africa amakhulupirira kuti anthu wamba akamwalira amakhala mizukwa, ndipo anthu otchuka amakhala mizimu ya makolo. Amailemekeza mizimu imeneyi ndipo akakhala ndi vuto amaipempha monga atsogoleri awo osaoneka.

M’mayiko ena, zimene amakhulupirira pankhani ya akufa n’zosakanikirana​—miyambo yawo ndi Chikristu mwa dzina lokha. Mwachitsanzo, Akatolika ndi Apolotesitanti ambiri ku West Africa amatsata mwambo wophimba kalirole munthu akamwalira kuti wina asayang’anemo ndi kuona mzimu wa munthu womwalirayo.

Inde, mayankho a anthu pa funso lakuti ‘Kodi n’chiyani chimachitika tikamwalira?’ ndi osiyanasiyana. Komabe ganizo lake ndi limodzi, lakuti: Anthu ali ndi chinachake chosafa ndipo chimapulumuka munthu akamwalira. Anthu ena amakhulupirira kuti “chinachake” chimenecho ndi mzimu. Mwachitsanzo, anthu ambiri m’mayiko ena mu Africa ndi ku Asia ndiponso m’madera onse akunyanja ya Pacific ku Polynesia, Melanesia, ndi Micronesia, amakhulupirira kuti mzimu sufa.

Kodi munthu ali ndi mzimu? Kodi mzimuwo umachokadi munthu akamwalira? Ngati umatero, n’chiyani chimauchitikira? Ndiponso kodi anthu amene anamwalira akuyembekeza chiyani? Tisanyalanyaze mafunso ameneŵa. Anthu a fuko ndi chipembedzo chilichonse amamwalira. Motero nkhani imeneyi ikukukhudzani kwambiri inuyo panokha. Tikukulimbikitsani kuipenda.