Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Limbikirani ntchito yotuta!

Limbikirani ntchito yotuta!

Limbikirani ntchito yotuta!

“Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera.”​—SALMO 126:5.

1. N’chifukwa chiyani tifunikira ‘kupempha Mwini zotuta kuti akokose antchito’ lerolino?

YESU KRISTU atamaliza ulendo wake wachitatu wokalalikira ku Galileya, anauza ophunzira ake kuti: “Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka.” (Mateyu 9:37) Zinthu zinali chimodzimodzi ku Yudeya. (Luka 10:2) Popeza kuti zinali choncho zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, nanga lero zili bwanji? Eya, chaka chautumiki chathachi, Mboni za Yehova zopitirira 6,000,000 zinalimbikira ntchito yotuta yophiphiritsa imeneyi pakati pa anthu 6,000,000,000 apadziko lonse. Ambiri mwa anthu ameneŵa ali “okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” Choncho, ‘kupempha Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake’ komwe Yesu analimbikitsa, n’kofunika kwambiri tsopano mofanana ndi zaka mazana ambiri m’mbuyomo.”​—Mateyu 9:36, 38.

2. Kodi n’chiyani chimatidziŵikitsa kwa anthu?

2 Yehova Mulungu pokhala Mwini zotuta wayankha pempho loti atumize antchito ambiri. Ndipotu n’zosangalatsa kwambiri kugwira nawo ntchito yotuta imene iyeyo akuitsogolera! Ngakhale kuti ndife ochepa poyerekeza ndi anthu a dzikoli, khama lathu pa ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira limatidziŵikitsa ku dzikoli. M’mayiko ambiri, amatitchula kaŵirikaŵiri m’zofalitsira nkhani. Akamva kugogoda pachitseko m’seŵero la pawailesi yakanema, ena m’seŵerolo anganene kuti Mboni za Yehova zafika pakhomopo. Inde, ntchito yathu yachikristu monga otuta ophiphiritsa ikudziŵika kwambiri m’zaka za m’ma 2000 zino.

3. (a) Kodi timadziŵa bwanji kuti ntchito yolalikira Ufumu inadziŵika m’zaka za zana loyamba? (b) N’chifukwa chiyani titha kunena kuti angelo amatithandiza utumiki wathu?

3 M’zaka za zana loyamba dziko lapansi linadziŵanso ntchito yolalikira Ufumu ndipo linazunza olengeza uthenga wabwinowo. N’chifukwa chake Paulo analemba kuti: “Ndiyesa, kuti Mulungu anaoneketsa ife atumwi otsiriza, monga titi tife; pakuti takhala ife [atumwi] choonetsedwa ku dziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu.” (1 Akorinto 4:9) Mofananamo, kulimbikira kwathu monga olengeza Ufumu ngakhale pozunzidwa kumatidziŵikitsa ku dzikoli ndipo n’zofunika kwambiri kwa angelo. Pa Chivumbulutso 14:6 pamanena kuti: “[Ine mtumwi Yohane] ndinaona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nawo uthenga wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu.” Inde, angelo amatithandiza utumiki wathu​—ntchito yathu yotuta!​—Ahebri 1:13, 14.

‘Odedwa’

4, 5. (a) Kodi Yesu anawachenjeza zotani ophunzira ake? (b) N’chifukwa chiyani atumiki amakono a Mulungu ‘amadedwa’?

4 Yesu atatumiza atumwi ake kukachita ntchito yotuta, iwo anamvera malangizo ake oti akakhale “ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.” Yesu anawonjezera kuti: “Koma chenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu kwa akulu a mlandu, nadzakukwapulani inu m’masunagoge mwawo; ndiponso adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu chifukwa cha Ine; kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa anthu akunja. . . . Ndipo adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa; koma iye wakupirira kufikira chimaliziro, iyeyu adzapulumutsidwa.”​—Mateyu 10:16-22.

5 Masiku ano anthu ‘amatida’ chifukwa chakuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo,” Satana Mdyerekezi, amene ali mdani wamkulu wa Mulungu ndi anthu Ake. (1 Yohane 5:19) Adani athu amaona ulemerero wathu wauzimu koma amakana kuvomereza kuti akuchititsa zimenezi ndi Yehova. Tikamachita ntchito yotuta mokondwera, adaniwo amaona chimwemwe chathu ndi nkhope zathu zosangalala. Amadabwa kwambiri ndi umodzi wathu! Ndiponso angakakamizike kuzindikira zimenezi akapita m’dziko lina ndi kukapeza kuti Mboni za Yehova kumeneko zikuchitanso ntchito imodzimodziyo yomwe ikuchitika m’dziko lakwawo. Inde, tikudziŵa kuti nthaŵi yake yoikika, Yehova mthandizi wathu ndiponso gwero la umodzi wathu adzadziŵika ngakhale kwa adani athu.​—Ezekieli 38:10-12, 23.

6. Kodi ndife otsimikiza za chiyani tikamachita ntchito yathu yotuta, ndipo pakubuka funso lotani?

6 Mwini zotuta wapatsa Mwana wake, Yesu Kristu, “mphamvu zonse . . . kumwamba ndi padziko lapansi.” (Mateyu 28:18) Chotero, Yehova akugwiritsa ntchito Yesu kutsogolera ntchito yotuta kudzera mwa angelo akumwamba ndiponso “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wodzozedwa padziko lapansi pano. (Mateyu 24:45-47; Chivumbulutso 14:6, 7) Koma kodi tingapirire motani adani athu akamatitsutsa kwinaku kukhalabe osangalala pamene tikulimbikira ntchito yathu yotuta?

7. Kodi tiyenera kuyesetsa kukhalabe ndi mtima wotani akamatitsutsa ndi kutizunza?

7 Akamatitsutsa kaya kutizunza, tiyeni tipemphe thandizo kwa Mulungu kuti tikhale ndi mtima wofanana ndi wa Paulo. Iye analemba kuti: “Polalatidwa tidalitsa; pozunzidwa, tipirira; ponamizidwa, tipempha.” (1 Akorinto 4:12, 13) Mtima umenewu pamodzi ndi luso pochita utumiki wathu kwa anthu, nthaŵi zina umasintha maganizo a anthu otitsutsa.

8. Kodi mawu a Yesu opezeka pa Mateyu 10:28 akukulimbikitsani motani?

8 Changu chathu monga otuta sichizilala ngakhale atatiopseza kuti atipha. Timalalikira poyera uthenga wa Ufumu mopanda mantha. Ndipo mawu a Yesu amatilimbikitsa. Mawuwo akuti: “Musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuwononga moyo ndi thupi lomwe m’gehena.” (Mateyu 10:28) Timadziŵa kuti Atate wathu wakumwamba ndiye Wopatsa moyo. Amapatsa mphoto iwo okhulupirikabe kwa iye ndi olimbikira ntchito yotuta.

Uthenga Wopulumutsa Moyo

9. Kodi ena anachita motani ndi mawu a Ezekieli ndipo ndi motani mmene zofananazo zikuchitikira lerolino?

9 Pamene mneneri Ezekieli analengeza mauthenga a Yehova molimba mtima kwa “mitundu ya anthu opanduka”​—ufumu wa Israyeli ndi Yuda​—anthu ena anali osangalala kumva zomwe anali kunena. (Ezekieli 2:3) Yehova anati: “Taona, akuyesa iwe ngati nyimbo yachikondi ya woimba bwino, woimba limba bwino.” (Ezekieli 33:32) Ngakhale kuti anawakonda mawu a Ezekieli, iwo analephera kuwatsatira. Nanga zikuchitika lero n’zotani? Pamene otsalira odzozedwa pamodzi ndi anzawo akulengeza mauthenga a Yehova molimba mtima, anthu ena amasangalala kumva za madalitso a Ufumu koma amalephera kuwalandira ndi manja aŵiri, kukhala ophunzira, ndi kuyamba nawo ntchito yotuta.

10, 11. Kodi chinachitika n’chiyani pofuna kulengeza uthenga wathu wopulumutsa moyo zaka 50 zoyambirira za m’ma 1900, ndipo zotsatira zake zinali zotani?

10 Mosiyana ndi zimenezo, ambiri alabadira mwachidwi ntchito yotuta ndipo alengeza nawo mauthenga a Mulungu. Mwachitsanzo, m’nthaŵi ya misonkhano ikuluikulu yachikristu kuyambira mu 1922 mpaka 1928, mauthenga achiweruzo otsutsa dongosolo la zinthu loipali la Satana analengezedwa momveka bwino. Nyumba za wailesi zinaulutsa mauthenga ameneŵa okambidwa pamisonkhano imeneyo. Pambuyo pake, anthu a Mulungu anagaŵira makope a mauthengawo kwa anthu miyandamiyanda.

11 Chakumapeto kwa m’ma 1930, mtundu wina wa ulaliki unayamba​—ndawala zofalitsa uthenga. Poyamba, anthu a Yehova anali kuvala zikwangwani zomwe zinkalengeza nkhani za anthu onse. Kenako, anali kunyamula zikwangwani zolembedwa kuti “Chipembedzo ndi msampha komanso malonda” ndiponso kuti “Tumikirani Mulungu ndi Kristu Mfumu.” Pamene anali kuyenda m’misewu, anthu amene anali kudutsa ankachita chidwi kwambiri. ‘Zimenezi zinathandiza kwambiri kuti Mboni za Yehova zidziŵike kwa anthu ndiponso kukhala zopanda mantha,’ anatero mbale amene ankachita nawo ntchitoyi m’misewu yodzala ndi anthu mumzinda wa London, ku England.

12. Kuwonjezera pa mauthenga a Mulungu achiweruzo, kodi tanenanso chiyani mu utumiki wathu, ndipo ndani amene tsopano agwirizana pa ntchito yolalikira uthenga wabwino?

12 Pamene tikulengeza mauthenga achiweruzo a Mulungu, timanenanso zinthu zabwino zimene walonjeza zomwe zilinso mbali ya uthenga wa Ufumu. Kulalikira kwathu molimba mtima pa dziko lonse kumatithandiza kufunafuna anthu oyenerera. (Mateyu 10:11) Ambiri mwa odzozedwa omalizira analabadira pempho lomveka bwino la otuta limeneli m’ma 1920 ndi 1930. Kenako, pamsonkhano wa mu 1935, panatuluka nkhani yosangalatsa yosimba za tsogolo lodalitsika la “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” padziko lapansi la paradaiso. (Chivumbulutso 7:9; Yohane 10:16) Iwowa amvera mauthenga a Mulungu achiweruzo ndipo agwirizana ndi odzozedwa pa ntchito yolalikira uthenga wabwino wopulumutsa moyo.

13, 14. (a) Kodi Salmo 126:5, 6 likutilimbikitsa motani? (b) Ngati tilimbikira kufesa ndi kuthirira, kodi chidzachitike n’chiyani?

13 Mawu opezeka pa Salmo 126:5, 6 ali olimbikitsa kwambiri kwa otuta makamaka amene amazunzidwa. Mawuwo amati: “Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera. Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbewu yakufesa; adzabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera, alikunyamula mitolo yake.” Mawu a wamasalmo onena za kufesa ndi kututa akusonyeza chisamaliro ndi madalitso a Yehova kwa otsala amene anabwerako ku ukapolo ku Babulo wakale. Anakondwa kwambiri atamasulidwa, koma ayenera kuti analira pofesa mbewu m’dziko labwinja lomwe sanalimemo kwa zaka 70 zomwe anali ku ukapolo. Komabe, amene anapitiriza ntchito yawo yofesa ndi kumanga anapeza zokolola zambiri komanso kukhutira ndi ntchito yawo.

14 Tingakhetse misozi poyesedwa kapena pamene ifeyo ndi okhulupirira anzathu tikuzunzidwa chifukwa cha chilungamo. (1 Petro 3:14) Pa ntchito yathu yotutayi, mwina zinthu zingativute poyamba chifukwa chakuti tikuona ngati palibe umboni wosonyeza phindu la khama lathu mu utumiki. Koma ngati tilimbikira kufesa ndi kuthirira, Mulungu adzakulitsa, mwinanso kuposa mmene tingaganizire. (1 Akorinto 3:6) Zimenezi zikusonyezedwa bwino lomwe ndi mabaibulo ndi mabuku ofotokoza Malemba omwe tagaŵira.

15. Perekani chitsanzo chosonyeza phindu la zofalitsa zachikristu m’ntchito yotuta?

15 Talingalirani chitsanzo cha mwamuna wina wotchedwa Jim. Amayi ake atamwalira, iye anapeza buku lakuti Life​—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? * pakatundu yemwe iwo anasiya. Analiŵerenga mwachidwi kwambiri. Pokambirana ndi Mboni ina yomwe anakumana nayo mumsewu, Jim anavomera kuti Mboniyo ikabwerenso ndipo mapeto ake anayamba kuphunzira Baibulo. Jim anapita patsogolo mwauzimu mofulumira kwambiri ndipo anadzipatulira kwa Yehova ndi kubatizidwa. Anauzanso ena a m’banja lake zomwe anaphunzirazo. Mapeto ake, mlongo wake ndi mbale wake anakhala Mboni za Yehova ndipo Jim anakhala ndi mwayi wodzipereka kutumikira pa Beteli ku London nthaŵi zonse.

Ozunzidwa Koma Osangalala

16. (a) N’chifukwa chiyani ntchito yotuta yayenda bwino? (b) Kodi Yesu anapereka chenjezo lotani lokhudza mphamvu ya uthenga wabwino, koma kodi ifeyo timafikira anthu motani?

16 N’chifukwa chiyani ntchito yotuta yayenda motere? N’chifukwa chakuti Akristu odzozedwa ndi anzawo amvera malangizo a Yesu akuti: “Chimene ndikuuzani inu mumdima, tachinenani poyera; ndi chimene muchimva m’khutu, muchilalikire pa matchindwi a nyumba.” (Mateyu 10:27) Komabe, timayembekezera mavuto popeza Yesu anachenjeza kuti: “Mbale adzapereka mbale wake kuimfa, ndi atate mwana wake: ndipo ana adzatsutsa akuwabala, nadzawafetsa iwo.” Yesu anawonjezera kuti: “Musalingalire kuti ndidadzera kuponya mtendere padziko lapansi; sindinadzera kuponya mtendere, koma lupanga.” (Mateyu 10:21, 34) Cholinga cha Yesu sichinali kudzagaŵanitsa mabanja ayi. Koma kuti nthaŵi zina uthenga wabwino ndiwo unachititsa zimenezo. Ndi mmenenso zilili ndi atumiki a Mulungu lerolino. Tikamachezera mabanja, cholinga chathu sindicho kugaŵanitsa mabanjawo ayi. Timafunitsitsa kuti aliyense alandire uthenga wabwino. Choncho, timayesetsa kufikira onse m’banja mokoma mtima. Zimenezi zimachititsa uthenga wathu kukopa “onse ofuna moyo wosatha.”​—Machitidwe 13:48, NW.

17. Kodi amene amavomereza uchifumu wa Mulungu amasiyana motani ndi ena, ndipo kodi chitsanzo chimodzi cha zimenezi n’chiti?

17 Uthenga wa Ufumu walekanitsa anthu amene amavomereza uchifumu wa Mulungu. Mwachitsanzo, talingalirani mmene okhulupirira anzathu anakhalira osiyana chifukwa ‘chopereka kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu,’ m’nthaŵi ya ulamuliro wa National Socialism ku Germany. (Luka 20:25) Mosiyana ndi atsogoleri a zipembedzo ndiponso Akristu mwa dzina lokha a m’Matchalitchi Achikristu, atumiki a Yehova anakanitsitsa kwamtuwagalu kuswa mfundo za m’Baibulo. (Yesaya 2:4; Mateyu 4:10; Yohane 17:16) Pulofesa Christine King, yemwe analemba buku lakuti The Nazi State and the New Religions anati: “Boma [la Nazi] linalephera polimbana ndi Mboni pokha basi, chifukwa chakuti ngakhale iwo anapha anthu ambirimbiri, ntchito ya Mboni inapitirizabe ndipo m’May 1945 gulu la Mboni za Yehova linali kugwirabe ntchito zake, pamene ulamuliro wa National Socialism unali utatha.”

18. Kodi anthu a Yehova amasonyeza mzimu wotani ngakhale amazunzidwa?

18 Chochititsa chidwi kwambiri ndi mzimu umene anthu a Yehova amasonyeza pamene akuzunzidwa. Ngakhale kuti akuluakulu a boma angachite chidwi ndi chikhulupiriro chathu, amadabwa kwabasi kuti sitisunga chidani. Mwachitsanzo, Mboni zimene zinapulumuka nkhanza za boma la Nazi zimakhala zosangalala ndiponso zokhutira zikamakumbukira zomwe zinawachitikira m’mbuyomo. Amadziŵa kuti Yehova anawapatsa “ukulu woposa wamphamvu.” (2 Akorinto 4:7) Odzozedwa amene tili nawo ndi otsimikiza kuti ‘mayina awo alembedwa m’Mwamba.” (Luka 10:20) Kupirira kwawo kumawapatsa chiyembekezo chosakhumudwitsa, ndipo otuta okhulupirika omwe akuyembekeza kukhala padziko lapansi nawonso ndi otsimikiza mofananamo.​—Aroma 5:4, 5.

Limbikirani Ntchito Yotuta

19. Kodi ndi njira zogwira mtima zotani zomwe zagwiritsidwa ntchito mu utumiki wachikristu?

19 Sitikudziŵa kuti Yehova adzatilola kugwirabe ntchito yotuta yophiphiritsa imeneyi kwanthaŵi yaitali motani. Pakali pano, tiyenera kukumbukira kuti otuta ali ndi njira zawo zogwirira ntchito yawo. Mofananamo, tikutsimikiza kuti kukhulupirika kwathu pogwiritsa ntchito njira zolalikirira zomwe zinayesedwa kudzathandiza. Paulo anauza Akristu anzake kuti: “Ndikupemphani, khalani akutsanza ine.” (1 Akorinto 4:16) Paulo atakumana ndi akulu a ku Efeso ku Mileto, anawakumbutsa kuti sanawabisire kuwaphunzitsa ‘pabwalo ndi kunyumba ndi nyumba.’ (Machitidwe 20:20, 21) Mnzake wa Paulo, Timoteo, anali ataphunzira njira za mtumwiyo ndipo anaziphunzitsa kwa Akorinto. (1 Akorinto 4:17) Mulungu anadalitsa kaphunzitsidwe ka Paulo monganso mmene adzadalitsire khama lathu pa ntchito yolalikira uthenga wabwino poyera, kunyumba ndi nyumba, kumaulendo obwereza, pamaphunziro a Baibulo apanyumba, ndiponso kulikonse komwe anthu angapezeke.​—Machitidwe 17:17.

20. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti kututa zinthu zauzimu zochuluka kunali pafupi, nanga zimenezi zachitikadi motani zaka zaposachedwapa?

20 Yesu atalalikira kwa mkazi wachisamariya pafupi ndi mudzi wa Sukari mu 33 C.E., analankhula za kututa kwauzimu. Anauza ophunzira ake kuti: “Kwezani maso anu, nimuyang’ane m’minda, kuti mwayera kale kufikira kumweta. Wakumweta alandira kulipira, nasonkhanitsira chobala ku moyo wosatha; kuti wofesayo akakondwere pamodzi ndi womwetayo.” (Yohane 4:34-36) Mwina Yesu anali ataona kale phindu la kulankhulana kwake ndi mkazi wachisamariya, popeza ambiri anali kukhulupirira iye chifukwa cha umboni wa mkaziyo. (Yohane 4:39) Zaka zaposachedwapa, mayiko ambiri achotsa ziletso kwa Mboni za Yehova kapenanso awalola kulembetsa kuboma mwalamulo. Zimenezi zatsegula minda yatsopano yofunika kututa. Zotsatira zake n’zakuti kututa zinthu zauzimu zochuluka kuli m’kati. Ndipotu padziko lonse, tikupeza madalitso ochuluka pamene tikupitiriza mokondwera kugwira ntchito yotuta yauzimu.

21. N’chifukwa chiyani tifunikira kulimbikirabe monga osangalala ndi ntchito yathu yotuta?

21 Mbewu zikacha ndipo zikufunika kukolola, antchito amachita changu. Sazengereza pogwira ntchitoyo. Lerolino, tifunikira kugwira ntchito mwakhama ndiponso mwachangu chifukwa chakuti tikukhala ‘m’nthaŵi ya chimaliziro.’ (Danieli 12:4) Inde, timakumana ndi ziyeso, koma pali ntchito yaikulu yotuta olambira a Yehova kuposa ndi kale lonse. Choncho ino ndiyo nthaŵi yokondwera. (Yesaya 9:3) Pokhala osangalala monga otuta, tiyeni tilimbikire ntchito yotuta imeneyi!

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mwini zotuta wayankha motani pempho lofuna antchito ochuluka?

Ngakhale kuti anthu ‘amatida,’ kodi timakhalabe ndi mzimu wotani?

N’chifukwa chiyani timasangalala ngakhale kuti amatizunza?

N’chifukwa chiyani tiyenera kulimbikira ntchito yotuta ndiponso kuichita mwachangu?

[Mafunso]

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Angelo amathandiza amene akugwira ntchito yotuta yauzimu

[Chithunzi patsamba 18]

Ndawala zofalitsa uthenga zinachititsa kuti anthu ambiri amve uthenga wa Ufumu

[Chithunzi patsamba 18]

Timabzala ndi kuthirira, koma Mulungu ndiye amakulitsa