Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Madalitso Ali pa Wolungama’

‘Madalitso Ali pa Wolungama’

‘Madalitso Ali pa Wolungama’

NDINALI mwana ndipo ndakalamba: ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya,” anatero wamasalmo Davide atakalamba. (Salmo 37:25) Yehova Mulungu amakonda olungama ndipo amawasamalira kwambiri. M’Mawu ake, Baibulo, amalimbikitsa omulambira kufunafuna chilungamo.​—Zefaniya 2:3.

Kukhala wolungama kumatanthauza kugwirizana ndi miyezo ya Mulungu ya chabwino ndi choipa. Potilimbikitsa kukhala ogwirizana ndi chifuno cha Mulungu, chaputala 10 cha buku la m’Baibulo la Miyambo chimalongosola madalitso auzimu ochuluka amene anthu omwe amachita zimenezi amakhala nawo. Ena a madalitsoŵa ndi kukhala ndi chakudya chauzimu chopatsa thanzi chochuluka, ntchito yokondweretsa ndi yokhutiritsa, ndiponso kukhala ndi unansi wabwino ndi Mulungu ndi anthu. Motero tiyeni tilingalire Miyambo 10:1-14.

Chosonkhezera Chabwino Kwambiri

Mawu oyambirira a chaputalachi akutidziŵitsa bwino lomwe yemwe analemba chigawo cha buku la Miyambo chimenechi. Mawuwo amati: “Miyambo ya Solomo.” Mfumu Solomo ya Israyeli wakale inatchula chimene chingasonkhezere munthu bwino kwambiri kuchita zolungama, inati: “Mwana wanzeru akondweretsa atate; koma mwana wopusa amvetsa amake chisoni.”​Miyambo 10:1.

Makolo amakhalatu achisoni kwambiri pamene mwana wawo wina akana kulambira Mulungu woona ndi wamoyo. Mfumu yanzeruyo inatchula za chisoni cha mayi, mwina inalingalira kuti ndiye amamva chisoni kwambiri. Zinalidi tero kwa Doris. * Iye anati: “Pamene mnyamata wathu wa zaka 21 anasiya choonadi, tinasweka mitima ine ndi mwamuna wanga Frank. Ine zakhala zikundipweteka maganizo kwambiri kuposa Frank. Kupwetekako sikukutha ngakhale kuti papita zaka 12.”

Zochita za ana zingakhudze mmene atate awo amakhalira achimwemwe ndipo zingadwalitse mtima amawo. Tikhaletu anzeru ndi kusangalatsa makolo athu. Ndipo chofunika kwambiri, tiyeni tikondweretse mtima wa Atate wathu wakumwamba, Yehova.

‘Moyo wa Wolungama Umakhutitsidwa’

“Chuma cha uchimo sichithangata,” inatero mfumuyo, “koma chilungamo chipulumutsa ku imfa.” (Miyambo 10:2) Kwa Akristu oona omwe ali ndi moyo m’nthaŵi ya chimaliziro, mawuŵa ndi otsekemera kwabasi. (Danieli 12:4) Dziko lopanda umulunguli latsala nenene kuwonongeka. Palibe chitetezo chilichonse chopangidwa ndi anthu​—kaya ndi cha zinthu zakuthupi, chuma, kapena zida​—chimene chidzatha kuteteza anthu pa “chisautso chachikulu” chimene chikubwera. (Chivumbulutso 7:9, 10, 13, 14) Anthu okha ‘owongoka mtima ndiwo adzakhale m’dziko, angwiro nadzatsalamo.’ (Miyambo 2:21) Motero tipitirizetu kufunafuna choyamba Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo chake.​—Mateyu 6:33.

Atumiki a Yehova safunikira kuchita kudikira dziko latsopano lolonjezedwa kuti akalandire madalitso a Mulungu. “Yehova samvetsa njala moyo wa wolungama; koma amainga chifuniro cha wochimwa.” (Miyambo 10:3) Yehova wapereka chakudya chauzimu chamwana alirenji kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45) Ndithudi wolungama ali n’chifukwa chabwino chakuti ‘aimbe ndi mtima wosangalala.’ (Yesaya 65:14) Moyo wake umasangalala podziŵa zinthu. Amakondwera pofunafuna chuma chauzimu. Woipa sadziŵa kusangalatsa kwa zimenezi.

‘Khama Lilemeretsa’

Wolungama amapindulanso m’njira ina. “Wochita ndi dzanja laulesi amasauka; koma dzanja la akhama lilemeretsa. Wokolola m’malimwe ndi mwana wanzeru; koma wogona pakututa ndi mwana wochititsa manyazi.”​Miyambo 10:4, 5.

Mawu a mfumuŵa akutanthauza zambiri makamaka kwa ogwira ntchito yotuta. Nthaŵi yotuta si nthaŵi yogona. Ndi nthaŵi yogwira ntchito mwakhama kwa maola ochuluka. Ndithudi imeneyi imakhala nthaŵi yofunika kuchita changu.

Pamene Yesu anali kulingalira za kututa anthu osati zokolola zakumunda, anauza ophunzira ake kuti: “Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka. Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta [Yehova Mulungu] kuti akokose antchito kukututa kwake.” (Mateyu 9:35-38) M’chaka cha 2000, anthu oposa 14 miliyoni anafika pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu; kuŵirikiza kaŵiri chiŵerengero cha Mboni za Yehova. Motero ndani angatsutse kuti ‘m’minda mwayera kufikira kumweta’? (Yohane 4:35) Olambira oona amapempha Mwini ntchito kuti atumize antchito ena. Akamatero amakhalanso akudzipereka zolimba m’ntchito yopanga ophunzira mogwirizana ndi mapemphero awowo. (Mateyu 28:19, 20) Ndipotu Yehova wadalitsa khama lawo mosaneneka! M’chaka chautumiki cha 2000, munabatizidwa anthu atsopano oposa 280,000. Ameneŵanso amayesetsa kukhala aphunzitsi a Mawu a Mulungu. Tikhaletu achimwemwe ndi okhutira panthaŵi yotuta ino mwa kugwira nawo mokwanira ntchito yopanga ophunzira.

‘Madalitso Ali Pamutu Pake’

“Madalitso ali pamutu pa wolungama,” anapitiriza motero Solomo, “koma m’kamwa mwa oipa mubisa chiwawa.”​Miyambo 10:6.

Munthu amene mtima wake ndi woyera ndi wolungama amasonyeza umboni wochuluka wakuti ndi munthu wolungama. Amalankhula mokoma mtima ndiponso zolimbikitsa; amachita zinthu zothandiza ndiponso amakhala wowoloŵa manja. Anthu ena amasangalala kucheza naye. Munthu wotero ena amamulemekeza, amamudalitsa, m’njira yakuti amakamba zabwino za iyeyo.

Komano munthu woipa amakhala n’chidani kapena kuti njiru ndipo kwakukulu amalingalira zovulaza ena. Mawu ake akhoza kukhala okoma ndipo akhoza ‘kubisa chiwawa’ chimene chili mu mtima mwake, koma m’kupita kwanthaŵi amayamba kumenya kapena kunyoza ena. (Mateyu 12:34, 35) Kapena m’mawu ena, “chiwawa chidzabisa [kapena kuti chidzatseka] pakamwa penipenipo pa anthu oipa.” (Miyambo 10:6, NW, mawu am’munsi) Izi zikusonyeza kuti munthu woipa nthaŵi zambiri amalandira chidani chomwecho chimene iye amaonetsa kwa ena. Tingatero kuti zimenezi zimabisa, kapena kutseka, pakamwa pake iye nakhala chete. Nanga munthu wotereyu angayembekeze madalitso otani kwa anthu ena?

“Amayesa wolungama wodala pomukumbukira,” inalemba motero mfumu ya Israyeli, “koma dzina la oipa lidzavunda.” (Miyambo 10:7) Anthu, komanso kuposa onse Yehova Mulungu, amakonda kukumbukira munthu wolungama. Chifukwa choti Yesu anakhala wokhulupirika mpaka pa imfa yake, “adaloŵa dzina lakuposa” la angelo. (Ahebri 1:3, 4) Lerolino Akristu oona amakumbukira amuna ndi akazi okhulupirika omwe anakhalapo nthaŵi ya Chikristu isanafike monga zitsanzo zoti azitengere. (Ahebri 12:1, 2) Zimenezi zikusiyanatu kwambiri ndi dzina la oipa, lomwe anthu amanyansidwa nalo ndiponso safuna kulimva. Inde, “mbiri yabwino ifunika kopambana chuma chambiri; kukukomera mtima anzako kuposa siliva ndi golidi.” (Miyambo 22:1) Tipangetu mbiri yabwino kwa Yehova ndi kwa anthu anzathu.

‘Munthu Wowongoka Amayenda Wosatekeseka’

Posiyanitsa munthu wanzeru ndi chitsiru, Solomo anati: “Mwini mtima wanzeru amalandira malamulo; koma chitsiru cholongolola chidzagwa.” (Miyambo 10:8) Munthu wanzeru amadziŵa bwino kuti “sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Amazindikira kuti amafunika kufunafuna Yehova kuti amutsogolere ndipo amavomereza mosavuta malamulo a Mulungu. Komano chitsiru cholongolola chimalephera kuzindikira mfundo yofunika imeneyi. Kulongolola kwake kopanda nzeruko kumamubweretsera mavuto.

Munthu wolungama amakhalanso mosatekeseka m’njira inayake kusiyana ndi woipa. “Woyenda mowongoka amayenda osatekeseka; koma wokhotetsa njira zake adzadziŵika. Wotsinzinira achititsa chisoni; koma wodzudzula momveka achita mtendere.”​Miyambo 10:9, 10.

Munthu wowongoka amachita zinthu moona mtima. Ena amamulemekeza ndi kumukhulupirira. Munthu woona mtima mabwana ake amamudalira kuntchito ndipo kaŵirikaŵiri amamupatsa maudindo akuluakulu. Chifukwa chokhala ndi mbiri yoti ndi woona mtima, ntchito simuthera wambawamba kapenanso savutika kuipeza ngakhale pamene ntchito zikusoŵa. Ndiponso, anthu panyumba pake amakhala osangalala ndi amtendere chifukwa cha kuona mtima kwake. (Salmo 34:13, 14) Amakhala wosatekeseka pochita zinthu ndi a pabanja lake. Ndithudi kukhala mosatekeseka kumabwera chifukwa chokhala wokhulupirika.

Zimakhala zosiyana kwa munthu yemwe amakhala wosaona mtima kuti apeze phindu mwadyera. Tambwali amayesa kubisa bodza lake polankhula mokhotakhota kapenanso polankhula ndi thupi lake. (Miyambo 6:12-14) Anthu amene amawanyengawo angavutike maganizo kwambiri pamene iye akutsinzinira maso ake ndi zolinga zanjiru kapena zachinyengo. Koma m’kupita kwa nthaŵi, zimadziŵika kuti munthuyo ndi kamberembere. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Zochimwa za anthu ena zili zooneka kale, zitsogola kumka kumlandu; koma enanso ziwatsata. Momwemonso pali ntchito zokoma zinaonekera kale; ndipo zina zosati zotere sizikhoza kubisika.” (1 Timoteo 5:24, 25) Mosasamala kanthu kuti zikukhudza ndani​—kaya ndi kholo lako, bwenzi lako, mkazi wako kapena mwamuna wako, kapena munthu wodziŵana naye​—kusaona mtima kumaululika ndithu. Kodi alipo amene angakhulupirire munthu wambiri yakuti ndi wosaona mtima?

‘M’kamwa Mwake Ndi Kasupe wa Moyo’

“M’kamwa mwa wolungama ndi kasupe wa moyo,” anatero Solomo, “koma m’kamwa mwa oipa mubisa chiwawa.” (Miyambo 10:11) Mawu otuluka m’kamwa mwa munthu akhoza kuchiritsa kapena kuvulaza. Akhoza kutsitsimula munthu ndi kumusangalatsa, kapena akhoza kumukhumudwitsa.

Mfumu ya Israyeli inatchula chimene chimachititsa munthu kulankhula mawu ena ake pamene inati: “Udani upikisanitsa; koma chikondi chikwirira zolakwa zonse.” (Miyambo 10:12) Chidani chimayambitsa anthu kupikisana, chimadzetsa mikangano. Amene amakonda Yehova ayenera kuthetsa chidani chilichonse pamoyo wawo. Motani? Mwa kukhala ndi chikondi. “Chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo.” (1 Petro 4:8) Chikondi “chikwirira zinthu zonse.” (1 Akorinto 13:7) Chikondi chaumulungu sichiyembekezera kuti anthu opanda ungwiro azichita zinthu mwangwiro. M’malo mowanditsa zolakwa za ena, chikondi chotero chimatithandiza kunyalanyaza zolakwa zawozo kusiyapo ngati lili tchimo lalikulu. Chikondi chimapiriranso pamene anthu sakutilandira bwino mu utumiki wakumunda, kuntchito, kapenanso kusukulu.

Mfumu yanzeruyo inapitiriza kuti: “Nzeru ipezedwa m’milomo ya wozindikira; koma wopusa pamsana pake nthyole.” (Miyambo 10:13) Nzeru za munthu wozindikira zimatsogolera kayendedwe kake. Mawu olimbikitsa amene iye amalankhula amathandiza ena kuyenda m’njira yachilungamo. Iyeyo ngakhalenso amene amamumvetsera safunika kuwakakamiza kuti ayende m’njira yolungama pogwiritsa ntchito nthyole yolangira.

‘Kundikani Zomwe Mudziŵa’

Kodi n’chiyani chimachititsa mawu athu kukhala ‘mtsinje wodzala wa nzeru’ m’malo mokhala mfuleni wosokosera ndi nkhani zopanda pake? (Miyambo 18:4) Solomo anayankha kuti: “Anzeru akundika zomwe adziŵa; koma m’kamwa mwa chitsiru muwononga tsopano lino.”​Miyambo 10:14.

Chofunika choyambirira n’chakuti m’maganizo mwathu mudzale chidziŵitso cholimbikitsa cha Mulungu. Tingadziŵe zimenezo kuchokera ku gwero limodzi lokha. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.” (2 Timoteo 3:16, 17) Kudziŵa za Mulungu tiyenera kukuona kukhala kwa mtengo wapatali ndipo tizikumba m’Mawu a Mulungu ngati kuti tikufunafuna chuma chobisika. Kufufuza koteroko kumasangalatsatu zedi ndiponso n’kopindulitsa!

Kuti pamilomo pathu pakhale nzeru, mtima wathu uyeneranso kudziŵa Malemba. Yesu anauza anthu amene ankamumvetsera kuti: “Munthu wabwino atulutsa zabwino m’chuma chokoma cha mtima wake; ndi munthu woipa atulutsa zoipa m’choipa chake: pakuti m’kamwa mwake mungolankhula mwa kuchuluka kwa mtima wake.” (Luka 6:45) Motero, tikhale ndi chizoloŵezi chosinkhasinkha zimene tikuphunzira. N’zoona kuti pamafunika khama kuti tiziphunzira ndi kusinkhasinkha, komatu kuphunzira kotereku n’kopindulitsa kwambiri mwauzimu. Palibe chifukwa chilichonse choti wina aliyense atsatire njira yangozi ya munthu wolankhula mosalingalira.

Inde, munthu wanzeru amachita zinthu zolungama m’maso mwa Mulungu ndipo amalimbikitsa ena kuchita zabwino. Amasangalala ndi chakudya chauzimu chochuluka ndipo amakhala ndi zochita zambiri m’ntchito yopindulitsa ya Ambuye. (1 Akorinto 15:58) Pokhala munthu wokhulupirika, amachita zinthu mosatekeseka ndipo Mulungu amamuvomereza. Ndithudi, madalitso a munthu wolungama ndi ochulukadi. Tiyeni tifunefune chilungamo mwa kutsatira miyezo ya Mulungu ya chabwino ndi choipa m’miyoyo yathu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Tagwiritsa ntchito dzina lina.

[Chithunzi patsamba 25]

Kukhala woona mtima kumatithandiza kukhala ndi moyo wabanja wachimwemwe

[Chithunzi patsamba 26]

‘Anzeru amakundika zomwe adziŵa’