Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Pa 1 Petro 4:3, timaŵerenga kuti Akristu ena panthaŵi ina anali “kupembedza mafano kosaloleka.” Kodi kupembedza mafano kulikonseko si kosaloleka, komanso kuti Mulungu amakutsutsa ndiponso amaletsa?

Inde, kupembedza mafano kulikonseko n’kosaloleka kwa Mulungu. Omwe amafuna kuyanjidwa ndi Mulungu salambira mafano.​—1 Akorinto 5:11; Chivumbulutso 21:8.

Komano zikuoneka kuti mtumwi Paulo anali kutchula za kupembedza mafano m’lingaliro lina. Zili choncho chifukwa chakuti, m’mitundu yambiri kalelo kupembedza mafano kunali kofala zedi ndiponso akuluakulu a mitunduyo sanali kuika malamulo oletsa zimenezi. M’kunena kwina, malamulo a dziko lawo anali kuloleza kupembedza mafano. Nthaŵi zina dziko kaya boma limakhala ndi mfundo zolambira mafano ena. M’lingaliro limenelo, ena ‘analambira [nawo] mafano osaletsedwa ndi lamulo’ asanakhale Akristu. (New World Translation, lofalitsidwa mu 1950) Mwachitsanzo, tingakumbukire kuti Mfumu Nebukadinezara ya Babulo inaimika fano la golide kuti lilambiridwe, koma atumiki a Yehova, Sadrake, Mesake, ndi Abedinego anakana kulilambira.​—Danieli 3:1-12.

Komanso, miyambo yambiri yopembedza mafano inaphatikizapo zochitika zosemphana kotheratu ndi lamulo lachibadwa lililonse kapena malingaliro alionse a khalidwe labwino amene timakhala nawo mwa chikumbumtima chobadwa nacho. (Aroma 2:14, 15) Mtumwi Paulo analemba za makhalidwe onyansa amene anali “osalingana ndi chibadwidwe” ndi ‘amanyazi,’ ndipo kaŵirikaŵiri zimenezi zinali kuzika mizu m’miyambo yachipembedzo. (Aroma 1:26, 27) Amuna ndi akazi amene anali kupembedza mafano kosaloleka sanali kulabadira malingaliro awo achibadwa amene anali kuwaletsa kuchita zimenezo. Motero kunalidi koyenera kuti amene anakhala Akristu asiye makhalidwe oipa oterowo.

Kuwonjezera pa zimene tanenazi, Yehova Mulungu anatsutsa kupembedza mafano koteroko komwe kunali kofala pakati pa anthu osakhala Ayuda. Motero kunali kosaloleka. *​—Akolose 3:5-7.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Mawu achigiriki omwe ali pa 1 Petro 4:3, kwenikweni amatanthauza “kupembedza mafano kosaloleka mwalamulo.” Mawuŵa atembenuzidwa mosiyanasiyana m’mabaibulo a Chicheŵa monga “kupembedza koipa kwa mafano,” ndi “kupembedza mafano konyansa.”