Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Sangalalani Ndi Ntchito Yotuta!

Sangalalani Ndi Ntchito Yotuta!

Sangalalani Ndi Ntchito Yotuta!

Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka. Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.” ​—MATEYU 9:​37, 38.

1 . Kodi n’chiyani chimatithandiza kupitiriza kuchita chifuniro cha Mulungu?

TIKAKUMBUKIRA tsiku limene tinabatizidwa kukhala mtumiki wa Yehova, limaoneka ngati ndi dzulodzuloli ngakhale kuti ndi zaka zingapo kapena zambiri m’mbuyomo. Kutamanda Yehova kunakhala chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu womwe tinaupatulira kwa iye. Pamene tinapatula nthaŵi kuthandiza ena kumva, mwinanso kulandira kumene uthenga wa Ufumu, chimene tinali kufuna makamaka ndi kum’tumikira Yehova mosangalala. (Aefeso 5:15, 16) Mpaka lero, timaonabe kuti masiku akuthamanga kwambiri chifukwa chotanganidwa, pokhala “akuchuluka mu ntchito ya Ambuye.” (1 Akorinto 15:58) Ngakhale timakumana ndi mavuto, kukhala kwathu achimwemwe pochita chifuniro cha Yehova kumatilimbikitsa.​—Nehemiya 8:10.

2 . Kodi n’chiyani chimatithandiza kukhala achimwemwe pa ntchito yathu yotuta yophiphiritsa?

2 Monga Akristu, tikuchita ntchito yotuta yophiphiritsa. Yesu Kristu anayerekeza ntchito yosonkhanitsa anthu kuti akapeze moyo wosatha ndi kututa. (Yohane 4:​35-38) Popeza kuti ifeyo tikugwira nawo ntchito yotuta yoteroyo, kupenda chimwemwe chomwe Akristu oyambirira komanso otuta anali nacho kudzatilimbikitsa. Tipendanso mfundo zitatu zomwe zimatithandiza kukhala achimwemwe pa ntchito yotuta yamakono. Mfundo zake ndi izi: (1) uthenga wathu wopatsa chiyembekezo, (2) kuyenda bwino kwa ntchito yathu yofunafuna anthu, ndiponso (3) mtima wathu wofuna mtendere monga otuta.

Anawatuma Kuchita Ntchito Yotuta

3 . Kodi ndi mbali iti imene otsatira oyambirira a Yesu anasangalala nayo?

3 Miyoyo ya otuta oyambirira, makamaka ya atumwi 11 okhulupirika a Yesu, inasintha kwambiri mu 33 C.E. tsiku lomwe anapita ku phiri ku Galileya kukakumana ndi Yesu woukitsidwayo. (Mateyu 28:16) “Abale oposa mazana asanu” ayenera kuti analipo nthaŵi imeneyo. (1 Akorinto 15:6) Iwo nthaŵi zonse anakumbukira ntchito yomwe Yesu anawapatsa. Iye anawauza kuti: “Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:​19, 20) Ngakhale anthu anali kuwazunza koopsa, iwo anasangalala kwambiri ndi ntchito yotuta ataona mipingo ya otsatira a Yesu ikukhazikitsidwa m’malo ambiri. M’kupita kwanthaŵi, ‘uthenga wabwino unalalikidwa kwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.’​—Akolose 1:23; Machitidwe 1:8; 16:5.

4 . Kodi zinthu zinali motani pomwe Kristu anatumiza ophunzira ake?

4 Kumayambiriro kwa utumiki wake ku Galileya, Yesu anali ataitana atumwi 12 ndipo anawatumiza makamaka kukalengeza kuti: “Ufumu wa Kumwamba wayandikira.” (Mateyu 10:​1-7) Iyenso “anayendayenda m’mizinda yonse ndi m’midzi [ya ku Galileya], namaphunzitsa m’masunagoge mwawo, nalalikira uthenga wabwino wa Ufumuwo, nachiritsa nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.” Yesu anachita chisoni ndi anthuwo “popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” (Mateyu 9:​35, 36) Atakhudzika mtima kwambiri, anauza ophunzira ake kuti: “Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka. Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta [Yehova Mulungu] kuti akokose antchito kukututa kwake.” (Mateyu 9:​37, 38) Kutangotsala miyezi isanu ndi umodzi kuti Yesu amalize utumiki wake padziko lapansi, iye sanasinthe maganizo ake akuti ku Yudeya kunkafunikabe otuta. (Luka 10:2) Nthaŵi ziŵiri zonsezi, iye anatumiza otsatira ake monga otuta.​—Mateyu 10:5; Luka 10:3.

Uthenga Wathu Wopatsa Chiyembekezo

5 . Kodi timalengeza uthenga wotani?

5 Monga atumiki a Yehova amakono, timakondwera kuyankha pempho lakuti tichite nawo ntchito yotuta imeneyi. Mfundo yoyamba imene imawonjezera chimwemwe chathu ndiyo yakuti timalengeza uthenga wopatsa chiyembekezo anthu otaya mtima ndi ovutika maganizo. Monga ophunzira a Yesu m’zaka za zana loyamba, tili ndi mwayi waukulu kwabasi wolengeza uthenga wabwino, inde, uthenga weniweni wopatsa chiyembekezo kwa anthu “okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa”!

6 . Kodi ndi ntchito yotani imene atumwi anaigwira m’zaka za zana loyamba?

6 Chapakatikati pa zaka za zana loyamba, mtumwi Paulo anali kulalikira uthenga wabwino mwakhama. Ndipotu ntchito yake yotuta inali yogwira mtima kwambiri chifukwa polembera Akristu a ku Korinto cha m’ma 55 C.E., iye anati: “Ndikudziŵitsani, abale, uthenga wabwino umene ndinakulalikirani inu, umenenso munalandira, umenenso muimamo.” (1 Akorinto 15:1) Atumwi ndi Akristu ena oyambirira anagwira ntchito yotuta mwakhama kwabasi. Ngakhale kuti Baibulo silitiuza kuchuluka kwa atumwi amene anapulumuka mavuto osaiŵalika omwe analiko mpaka Yerusalemu atawonongedwa mu 70 C.E., tikudziŵa kuti mtumwi Yohane anali kulalikirabe patapita zaka pafupifupi 25 chiwonongedwereni Yerusalemu.​—Chivumbulutso 1:9.

7, 8. Kodi ndi uthenga wotani wopatsa chiyembekezo womwe atumiki a Yehova akulengeza mwachangu tsopano kuposa ndi kale lonse?

7 Kenako panatsatira nyengo yaitali yomwe “munthu wosayeruzika” wampatuko, kutanthauza atsogoleri a Matchalitchi Achikristu, anali ndi mphamvu kwambiri. (2 Atesalonika 2:3) Komabe, chakumapeto kwa m’ma 1800, amene anayesetsa kutsata ziphunzitso za Chikristu choyambirira ananyamula uthenga wopatsa chiyembekezo ndipo analengeza Ufumuwo. Ndipotu kuyambira kope lake loyamba (mu July 1879), mutu wa magazini ino waphatikizapo mawu akuti: “Yolengeza Kukhalapo kwa Kristu,” “Yolengeza Ufumu wa Kristu,” kapena “Yolengeza Ufumu wa Yehova.”

8 Ufumu wakumwamba wa Mulungu unapatsidwa m’manja mwa Yesu Kristu mu 1914, ndipo tsopano tikulengeza uthenga wopatsa chiyembekezo umenewu mwachangu kwambiri kuposa ndi kale lonse. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti mwa zina zabwino zimene Ufumu wa Mulungu udzachita polamulira, udzathetsanso dongosolo la zinthu loipali posachedwapa. (Danieli 2:44) Kodi pali uthenga winanso wabwino ngati umenewu? Ndipo kodi pali njira inanso yopezera chimwemwe chochuluka kuposa kulengeza nawo Ufumuwo chisautso chachikulu chisanafike?​—Mateyu 24:21; Marko 13:10.

Ntchito Yofunafuna Anthu Iyenda Bwino

9 . Kodi Yesu anapereka malangizo otani kwa ophunzira ake, ndipo anthu analabadira motani uthenga wa Ufumu?

9 Chinanso chomwe chimatipatsa chimwemwe monga otuta ndicho kuyenda bwino kwa ntchito yathu yofunafuna anthu oti akhale ophunzira ndi kugwirizana nafe pa ntchito yotutayi. Kale mu 31-32 C.E., Yesu analangiza ophunzira ake kuti: “M’mzinda uliwonse, kapena m’mudzi mukaloŵamo, mufunsitse amene ali woyenera momwemo.” (Mateyu 10:11) Malinga ndi kulabadira kwawo uthenga wabwino wa Ufumu, titha kuona kuti si onse amene anali oyenera. Komabe, ophunzira a Yesu analalikira uthenga wabwino mwakhama kulikonse komwe kunali anthu.

10. Kodi Paulo anaichita motani ntchito yake yofunafuna anthu oyenerera?

10 Yesu atafa ndipo atauka kwa akufa, ntchito yofunafuna anthu oyenerera inapitiriza mwamphamvu. Paulo anakambirana ndi Ayuda m’masunagoge awo ndiponso anthu amene anali pa msika ku Atene. Atachitira umboni ku Areopagi mumzinda wa Atene ku Girisi, “ena anadziphatika kwa iye, nakhulupira; mwa iwonso munali Dionisiyo Mareopagi, ndi mkazi dzina lake Damarisi, ndi ena pamodzi nawo.” Kulikonse komwe Paulo anapita anali chitsanzo polalikira ‘pabwalo ndi kunyumba ndi nyumba.’​—Machitidwe 17:​17, 34; 20:20.

11. Kodi ndi njira zochitira ulaliki ziti zomwe ankagwiritsa ntchito zaka za m’mbuyomu?

11 Zaka makumi angapo zomalizira za m’ma 1800, Akristu odzozedwa molimba mtima anagwira ntchito yofunafuna anthu oyenerera. M’nkhani ya mutu wakuti “Odzozedwa Azilalikira,” Zion’s Watch Tower ya July/​August 1881 inati: “Uthenga wabwino ukulalikidwabe . . . ‘kwa ofatsa’​—amene akufunitsitsa kumva. Izi zikuchitika n’cholinga chofuna kupeza thupi la Kristu mwa iwo, kapena kuti oloŵa nyumba limodzi naye.” Nthaŵi zambiri anthu a Mulungu ochita ntchito yotuta ankakumana ndi anthu amene anali kutuluka m’mapemphero m’tchalitchi ndipo anali kuwapatsa mathirakiti a uthenga wa m’Malemba wokonzedwa kuti udzutse chidwi mwa anthu oyenerera. Atapenda mosamalitsa kugwira mtima kwa njira ya ulaliki imeneyi, Nsanja ya Olonda ya May 15, 1903 inalimbikitsa otutawo kugaŵira mathirakiti “kunyumba ndi nyumba” Lamlungu m’maŵa.”

12. Kodi tatani kuti ntchito yathu yolalikira ikhale yogwira mtima kwambiri? Perekani chitsanzo.

12 Zaka zaposachedwapa, tafutukula utumiki wathu mwa kulankhula ndi anthu kumalo osiyanasiyana osakhala kunyumba zawo. Izi zathandiza kwambiri m’mayiko amene chuma ndiponso kufunafuna zosangalatsa kumachititsa anthu kusapezeka panyumba zawo tikamawafikira. Mlongo wina pamodzi ndi mnzake ku England ataona kuti nthaŵi ndi nthaŵi alendo amakwera mabasi akatha kusangalala kugombe la nyanja, analimba mtima kukakwera mabasiwo ndi kugaŵira apaulendowo Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mwezi umodzi wokha, anagaŵira makope 229. Iwo anasimba kuti: “Sitichita mantha kukachitira ulaliki kugombe, m’malo a zamalonda, kapena kuopa vuto lililonse lomwe tingakumane nalo chifukwa timadziŵa kuti Yehova ali nafe nthaŵi zonse.” Mapeto ake anakhala ndi anthu owagaŵira magazini, kuyambitsa maphunziro a Baibulo ndipo onse aŵiri achitapo utumiki wa upainiya wothandiza.

13. N’kusintha kotani mu utumiki wathu komwe tsopano kukufunika m’madera ena?

13 Pamene ntchito yofunafuna anthu oyenerera ikupitiriza, mwina tifunikira kupendanso bwino utumiki wathu mbali zina. Ngakhale kuti Mboni zambiri kaŵirikaŵiri zimalalikira kunyumba ndi nyumba Lamlungu m’maŵa, m’madera ena aona kuti kufikira anthu m’nyumba zawo m’maŵa kumakhala kosathandiza chifukwa mwina amapeza eninyumba akugona. Mwa kusintha zochita zawo ambiri tsopano amachita ntchito yofunafuna anthu imeneyi masana, mwinamwake atamaliza misonkhano yachikristu. Zimenezi zathandiza kwambiri. Chaka chatha chiŵerengero cha olengeza Ufumu chinakwera ndi 2.3 peresenti. Zimenezi zimalemekeza Mwini zotuta ndipo zimasangalatsa mtima wathu.

Sunganibe Mtendere pa Ntchitoyi Yotuta

14. Kodi uthenga wathu timaulengeza ndi mtima wotani, ndipo n’chifukwa chiyani?

14 Chifukwa china chomwe timasangalalira ndicho mtima wofuna mtendere womwe timakhala nawo pochita ntchito yotuta. Yesu ananena kuti: “Poloŵa m’nyumba muwalankhule [“muwapatse moni a m’nyumbayo,” NW]. Ndipo ngati nyumbayo ili yoyenera, mtendere wanu udze pa iyo.” (Mateyu 10:​12, 13) Moni wachihebri komanso mawu ake m’Chigiriki cha m’Baibulo otanthauza moni yemweyo amatanthauza kuti ‘Tikukufunirani zabwino zonse.’ Timakhala ndi mtima umenewu tikamalalikira uthenga wabwino. Timayembekeza kuti anthuwo amvetsera mwachidwi uthenga wa Ufumu. Amene amatero amayembekezeka kuyanjananso ndi Mulungu akalapa machimo awo, kutembenuka, ndi kuchita chifuniro chake. Ndiyeno, kukhala pa mtendere ndi Mulungu kudzabweretsa moyo wosatha.​—Yohane 17:3; Machitidwe 3:19; 13:​38, 48; 2 Akorinto 5:​18-20.

15. Kodi tingausunge motani mzimu wamtendere ngati anthu sakulabadira ntchito yathu yolalikira?

15 Kodi tingausungebe motani mtendere wathu pamene anthu sakulabadira uthenga wathu. Yesu analamula kuti: “Ngati [nyumbayo] siili yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu.” (Mateyu 10:13) Nkhani ya Luka yosimba za kutumiza ophunzira 70 imawonjezera mawu a Yesu aŵa: “Mukakhala mwana wa mtendere mmenemo, mtendere wanu udzapumula pa iye; koma ngati mulibe, udzabwerera kwa inu.” (Luka 10:6) Tikamafikira anthu ndi uthenga wabwino, timachita zimenezo ndi mtima wabwino ndipo mwamtendere. Mwininyumba akakhala wopanda chidwi, akamadandaula, kapena kunyoza amapereka mpata woti uthenga wathu wamtendere ‘ubwerere kwa ife.’ Koma zonsezi sizitilanda chimwemwe chathu, chipatso cha mzimu woyera wa Yehova.​—Agalatiya 5:​22, 23.

Cholinga Chabwino cha Otuta

16, 17. (a) Kodi cholinga chathu n’chiyani paulendo wobwereza? (b) Kodi amene ali ndi mafunso okhudza Baibulo tingawathandize motani?

16 Monga otuta timakondwera kwambiri kuchita nawo ntchito yosonkhanitsa anthu kuti akapeze moyo wosatha. Ndipotu timakhala ndi chimwemwe chodzaza tsaya pamene munthu amene tamulalikira wachita chidwi, akufuna kuphunzira zambiri, ndipo ngati ali “mwana wa mtendere”! Mwina ali ndi mafunso ambiri okhudza Baibulo ndipo taona kuti n’kosatheka kuwayankha onse paulendo umodzi. Popeza kuti kuphunzira nthaŵi yaitali paulendo woyamba n’kosayenera, kodi tingatani? Titha kukhala ndi cholinga ngati chomwe analimbikitsa zaka 60 zapitazi.

17 “Mboni za Yehova zonse ziyenera kukhala zokonzeka kuchititsa phunziro lachitsanzo la Baibulo.” Mawu amenewo akupezeka m’gawo lachitatu la kabuku ka malangizo kotchedwa Model Study (Phunziro Lachitsanzo) kofalitsidwa mu 1937 mpaka 1941. Kabukuka kanapitiriza kunena kuti: “Ofalitsa [Ufumu] onse ayenera kukhala akhama kuthandiza anthu oyanjidwa komanso ochita chidwi ndi uthenga wa Ufumu m’njira iliyonse yomwe angathe. [Maulendo obwereza] ayenera kuchitidwa kwa anthu oterowo, kuyankha mafunso osiyanasiyana . . . , kenako yambitsani phunziro lachitsanzo . . . mwansanga.” Inde, cholinga chathu paulendo wobwereza ndicho kuyambitsa phunziro la Baibulo lapanyumba ndi kumaphunzira mokhazikika. * Mzimu waubwenzi ndiponso wokonda anthu achidwi umatilimbikitsa kukonzekera bwino ndi kuchititsa phunziro logwira mtima.

18. Kodi tingawathandize motani atsopano kukhala ophunzira a Yesu Kristu?

18 Mothandizidwa ndi buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha ndiponso mabulosha monga lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?, tingachititse maphunziro a Baibulo apanyumba ogwira mtima. Motero, titha kuchita nawo ntchito yothandiza atsopano omwe ali ndi chidwi kukhala ophunzira. Pamene tikuyesetsa kutsanzira Mphunzitsi Wamkulu, Yesu Kristu, mosakayika ophunzira Baibulowo adzaphunziranso kwa ifeyo mtima wofuna mtendere, wachimwemwe, kuona mtima ndiponso kulemekeza miyezo ya Yehova ndi malangizo ake. Pamene tikuthandiza atsopano mwa kuyankha mafunso awo, tiyeni tichite zomwe tingathe kuwaphunzitsanso mmene iwo angayankhire mafunso amenewo kwa amene angawafunse. (2 Timoteo 2:​1, 2; 1 Petro 2:21) Monga otuta ophiphiritsa, mosakayika konse tikusangalala kuti avareji ya maphunziro a Baibulo apanyumba omwe tinachititsa inakwana 4,766,631 chaka cha utumiki chathachi. Tikusangalala kwambiri makamaka ngati ifeyo tili m’gulu la otuta amene akuchititsa phunziro la Baibulo lapanyumba lawolawo.

Sangalalanibe ndi Ntchito Yotuta

19. N’chifukwa chiyani nthaŵi imene Yesu amachita utumiki wake komanso pambuyo pake anali ndi zifukwa zabwino zosangalalira ndi ntchito yotuta?

19 Nthaŵi imene Yesu amachita utumiki wake komanso pambuyo pake, anali ndi zifukwa zabwino zimene anasangalalira ndi ntchito yotuta. Ambiri panthaŵiyo analabadira uthenga wabwino. Iwo anasangalala kwambiri makamaka pa Pentekoste wa mu 33 C.E., chifukwa chakuti anthu pafupifupi 3,000 anamvera malangizo a Petro, kulandira mzimu woyera wa Yehova, ndipo analowa mtundu wa Mulungu wa Israyeli wauzimu. Inde, anapitiriza kuwonjezeka ndipo chimwemwe chawo chinasefukira pamene “Ambuye anawawonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.”​—Machitidwe 2:​37-41, 46, 47; Agalatiya 6:16; 1 Petro 2:9.

20. N’chiyani chimatisangalatsa kwambiri m’ntchito yathu yotuta?

20 Panthaŵiyo, ulosi wa Yesaya unali kukwaniritsidwa. Ulosiwo umati: “Inu [Yehova] mwachulukitsa mtundu, inu mwawonjezera kukondwa kwawo; iwo akondwa pamaso panu monga akondwera m’masika, monga anthu akondwa pogaŵana zofunkha.” (Yesaya 9:3) Ngakhale kuti tsopano tikuona kuti ‘mtundu wochulukawo’ wa odzozedwa ukutha, timasangalala kwambiri tikamaona otuta akuwonjezeka chaka ndi chaka.​—Salmo 4:7; Zekariya 8:23; Yohane 10:16.

21. Kodi m’nkhani yotsatira tikambirana chiyani?

21 Ndithudi, tili ndi zifukwa zokwanira zokhalirabe osangalala ndi ntchito yotuta. Uthenga wathu wopatsa chiyembekezo, kufunafuna kwathu anthu oyenerera, ndiponso mtima wathu wofuna mtendere, zonsezi zimatisangalatsa monga otuta. Ngakhale zili choncho, zimenezi zimachititsa ambiri kutichitira zoipa. Mtumwi Yohane zinam’chitikira zimenezi. Anamuika m’ndende pa chisumbu cha Patmo “chifukwa cha mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu.” (Chivumbulutso 1:9) Ndiyeno, kodi tingasungebe motani chimwemwe chathu pokumana ndi chizunzo ndiponso chitsutso? Kodi n’chiyani chidzatithandiza kupirira maganizo oipa a anthu ambiri amene tsopano timawalalikira? Nkhani yotsatira ikupereka thandizo la m’Malemba poyankha mafunso ameneŵa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Poyamba maphunziro anali kuchitidwa kumalo amene anthu achidwi anali kusonkhana. Koma posapita nthaŵi, maphunzirowo anayamba kuchitidwanso kwa munthu payekha ndiponso mabanja.​—Onani buku la Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom, tsamba 574, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi ntchito yotuta yophiphiritsa n’chiyani?

• Kodi timalengeza uthenga wotani?

• N’chifukwa chiyani ntchito yathu yofunafuna ophunzira ikuyenda bwino?

• Kodi tingausunge motani mtendere pa ntchito yathu yotuta?

• N’chifukwa chiyani timasangalalabe ndi ntchito yotuta?

[Mafunso]

[Zithunzi pamasamba 12, 13]

Kulalikira m’zaka za zana loyamba ndiponso m’ma 1900

[Zithunzi patsamba 13]

Monga anachitira Paulo, otuta amakono amayesetsa kulalikira kwa anthu kwina kulikonse

[Chithunzi patsamba 13]

Lengezani uthenga wabwino ndi mtima wokondwa