Chokhalitsa Kuposa Golide Weniweni
Chokhalitsa Kuposa Golide Weniweni
ANTHU amafunafuna kwambiri golide chifukwa cha kukongola ndi kukhalitsa kwake. Amam’kondanso kwambiri makamaka chifukwa chakuti amaoneka ngati amakhalabe wonyezimira ndipo sachita dzimbiri mpaka kalekale. Zili choncho chifukwa chakuti golide sawonongeka ndi madzi, mpweya, sulfure, pafupifupi ndi china chilichonse. Ziwiya zambiri za golide zimene anazipeza m’mitsuko yofukulidwa pansi ndi m’malo ena, zidakali zonyezimirabe ngakhale kuti zakhala kwa zaka mazana ambiri.
Komabe, mochititsa chidwi, Baibulo limanena kuti pali chinachake chokhalitsa ndiponso ‘chamtengo wake woposa wa golidi amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto.’ (1 Petro 1:7) Golide ‘woyesedwa’ kapena woyengedwa ndi moto ndiponso njira zina, amakhala golide weniweni. Komabe, golide woyengedwa amawonongekanso, kapena kusungunuka akamuika m’mitundu ina ya asidi. Motero, Baibulo n’lolondola pankhani za sayansi ponena kuti ‘golide amawonongeka.’
Mosiyana ndi golide, chikhulupiriro chenicheni chachikristu chili “cha ku chipulumutso cha moyo.” (Ahebri 10:39) Anthu angaphe munthu wa chikhulupiriro cholimba, monganso anapha Yesu Kristu. Komabe anthu achikhulupiriro chenicheni akuwalonjeza izi: “Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.” (Chivumbulutso 2:10) Amene amamwalira ali ndi chikhulupiriro, Mulungu akuwakumbukira ndipo adzawaukitsa. (Yohane 5:28, 29) Golide sangachite zimenezo ngakhale achuluke motani. Motero, kukhulupirira n’kwamtengo wapatalidi kuposa golide. Komabe, kuti kukhulupirira kukhale kwamtengo wapatali motere, kuyeneranso kuyesedwa. Kwenikweni, ali “mayesedwe a chikhulupiriro” amene Petro akunena kuti ndi amtengo wapatali kuposa golide. Mboni za Yehova zikhala zokondwa kukuthandizani kuphunzira Baibulo kuti mukulitse ndi kusunga chikhulupiriro cholimba mwa Mulungu woona, Yehova, ndi Mwana wake, Yesu Kristu. Malinga ndi kunena kwa Yesu, ngati mutatero mudzapeza “moyo wosatha.”—Yohane 17:3.