Gonjetsani Zinthu Zokulepheretsani Kupita Patsogolo!
Gonjetsani Zinthu Zokulepheretsani Kupita Patsogolo!
TAYEREKEZANI kuti mwakhoma giya la galimoto yanu, injini ikulira, koma galimotoyo ikukana kupita kutsogolo. Kodi ndi vuto la injini? Ayi, kutsogolo kwa wilo lina kuli mwala waukulu kwambiri. Pakungofunika kuuchotsa kuti galimotoyo iyende.
Mofanana ndi zimenezi, anthu ena omwe akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ali ndi zopinga zomwe zingawalepheretse kupita patsogolo mwauzimu. Mwachitsanzo, Yesu anachenjeza kuti zinthu monga ‘nkhaŵa ya kayendetsedwe ka zinthu m’dziko lino ndi mphamvu yonyenga ya chuma’ zingathe ‘kutsamwitsa mawu’ a choonadi ndi kuwalepheretsa kukula.—Mateyu 13:22.
Kwa anthu ena, zizoloŵezi kapena zofooka zobadwa nazo zimawalepheretsa kupita patsogolo. Mwamuna wina wa ku Japan, yemwe dzina lake ndi Yutaka ankakonda uthenga wa m’Baibulo, koma anali ndi vuto lalikulu la kutchova juga. Anayesapo kambirimbiri kuti agonjetse chizoloŵezi choipachi koma ankalephera. Chifukwa chokonda kutchova juga, iye anataya ndalama zambiri, nyumba zitatu, ndiponso iye ndi banja lake sankapatsidwa ulemu. Kodi akanatha kuchotsa chopinga chimenechi ndiyeno n’kukhala Mkristu?
Kapena talingalirani za mayi wina dzina lake Keiko. Mothandizidwa ndi Baibulo, anasiya zinthu zoipa monga
kupembedza mafano, zachiwerewere, ndi kuchita maula. Komabe, Keiko akuti: “Vuto langa lalikulu linali kusuta fodya. Ndinayesa maulendo ambirimbiri kuti ndisiye koma ndinalephera.”Mwina nanunso muli ndi chokulepheretsani kupita patsogolo chomwe chimaoneka ngati chovuta kuchichotsa. Kaya chingakhale chamtundu wanji, koma khalani ndi chikhulupiriro choti mothandizidwa ndi Mulungu, mungathe kuchigonjetsa.
Kumbukirani uphungu womwe Yesu anapatsa ophunzira ake, iwo atalephera kuchotsa chiŵanda m’thupi la munthu wa khunyu. Yesu atachita zomwe iwo anakanika, anauza ophunzira akewo kuti: “Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambewu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakulakani.” (Mateyu 17:14-20; Marko 9:17-29) Inde, vuto lomwe lingaoneke ngati chiphiri chachikulu kwa ife, n’laling’ono kwambiri ndipo si kanthu kwa Mlengi wathu wamphamvu zonse.—Genesis 18:14; Marko 10:27.
Kuzindikira Zopinga
Musanagonjetse zinthu zokupingani, mufunikira kuzindikira zopingazo. Kodi mungachite motani zimenezo? Nthaŵi zina munthu wina mumpingo, kaya mkulu kapena munthu amene mukuphunzira naye Baibulo, angakuuzeni za chinthu chinachake. Muyenera ‘kumva mwambo, ndi kukhala anzeru’ modzichepetsa, m’malo moipidwa ndi uphungu wachikondi woterowo. (Miyambo 8:33) Nthaŵi zina, mungadziŵe za zofooka zanu chifukwa cha phunziro lanu la Baibulo. Inde, mawu a Mulungu “ali amoyo, ndi ochitachita.” (Ahebri 4:12) Kuŵerenga Baibulo ndiponso mabuku ofotokoza Baibulo kungavumbulutse malingaliro a m’katikati mwa mtima wanu. Kumakuthandizani kuti mudzipime mogwirizana ndi miyezo yapamwamba ya Yehova. Kumavumbula ndi kukuzindikiritsani zinthu zomwe zingachedwetse kupita kwanu patsogolo mwauzimu.—Yakobo 1:23-25.
Mwachitsanzo, tayerekezerani kuti wophunzira Baibulo wakhala ndi chizoloŵezi chomayerekezera anthu akuchita zachiwerewere. Chifukwa choganiza kuti sakuchita cholakwa chenicheni chilichonse, sangaone vuto lililonse ndi zimenezo. M’kati mwa phunziro lake, waŵerenga mawu a pa Yakobo 1:14, 15: “Munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, nichimnyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.” Tsopano akuona mmene kupitiriza kuchita zimenezi kungamulepheretsere kupita patsogolo! Kodi angathetse bwanji chododometsa chimenechi?—Marko 7:21-23.
Kugonjetsa Zopinga
Mwinamwake mothandizidwa ndi munthu wokhwima m’chikristu, wophunzirayo angapangenso kafukufuku m’Mawu a Mulungu, pogwiritsa ntchito buku la Chingelezi lakuti Watch Tower Publications Index. * Mwachitsanzo, mutu wakuti “Malingaliro,” umasonyeza woŵerenga nkhani zambirimbiri zomwe zinafalitsidwa zokhudza kuthetsa malingaliro oipa. Nkhani zimenezi zimagogomezera malemba othandiza kwambiri a m’Baibulo, monga Afilipi 4:8, lomwe limati: “Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.” Inde, malingaliro oipa ayenera kuloŵedwa m’malo ndi oyera, malingaliro olimbikitsa!
Mosakayikira, m’kati mwa kafukufuku wakeyo, wophunzirayo adzapezanso mfundo zina zachikhalidwe za m’Baibulo zomwe zidzam’thandiza kupeŵa kukulitsa vuto lake. Mwachitsanzo, Miyambo 6:27 ndi Mateyu 5:28 amachenjeza za kudzaza malingaliro a munthu ndi nkhani zoyambitsa chilakolako cha kugonana. Wamasalmo anapemphera kuti: “Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe.” (Salmo 119:37) Inde, kungoŵerenga malemba a m’Baibulo ameneŵa sikokwanira. Munthu wanzeru anati: “Mtima wa wolungama uganizira.” (Miyambo 15:28) Mwa kusinkhasinkha osati pa zinthu zokhazo zomwe Mulungu amalamula komanso chifukwa chake amalamula zimenezo, wophunzirayo angazindikire mwakuya kwambiri nzeru ndi ubwino wa njira za Yehova.
Komanso, munthu yemwe akuyesetsa kugonjetsa Salmo 103:14) Mapemphero osaleka a kwa Mulungu opempha chithandizo, pamodzi ndi kuyesetsa mwakhama kufuna kupeŵa kupitiriza kukhala ndi malingaliro oyerekezera anthu akuchita zachiwerewere, m’kupita kwanthaŵi adzapindula zabwino—chikumbumtima choyera ndi chabwino.—Ahebri 9:14.
chopinga chamtunduwu ayeneranso kupempha chithandizo cha Yehova. M’poyenera kupempha chithandizo kwa Mulungu chifukwa chakuti iye amadziŵa bwino mmene tinapangidwira, kuti ndife opanda ungwiro, opangidwa kuchokera ku fumbi. (Musasiye
Kaya mukulimbana ndi vuto lamtundu wanji, dziŵani kuti nthaŵi zina mungafooke. N’zachibadwa kuti munthu akhumudwe kapena agwe mphwayi, zinthu zoterozo zikachitika. Koma kumbukirani mawu a pa Agalatiya 6:9: “Tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.” Nawonso atumiki odzipereka a Mulungu monga Davide ndi Petro nthaŵi zina analepherapo mochititsa manyazi. Koma sanabwerere m’mbuyo. Analandira uphungu modzichepetsa, n’kusintha momwe munkafunika kusintha ndi kupitirizabe kudzionetsa kukhala atumiki abwino kwambiri a Mulungu. (Miyambo 24:16) Ngakhale kuti Davide anali ndi zophophonya, Yehova anamutcha kuti “munthu wa pamtima panga, amene adzachita chifuniro changa chonse.” (Machitidwe 13:22) Petro nayenso anagonjetsa zophophonya zake ndiyeno anakhala mzati wa mpingo wachikristu.
Mofanana ndi anthu ameneŵa, ambiri lerolino apambananso polimbana ndi zopinga. Yutaka, amene tam’tchula poyamba uja, anavomera kuphunzira Baibulo. Iye anafotokoza kuti: “Chithandizo cha Yehova ndiponso madalitso pa chilichonse chomwe ndinkachita kuti ndipite patsogolo zinandithandiza kuthetsa vuto langa lotchova juga. Ndikusangalala kwambiri kuona zoona zake za mawu a Yesu akuti, ndi chikhulupiriro, ngakhale ‘mapiri’ angasunthidwe.” M’kupita kwanthaŵi, Yutaka anakhala mtumiki wotumikira mu mpingo.
Bwanji za Keiko, amene anali ndi chizoloŵezi chosuta fodya? Mlongo yemwe ankaphunzira naye anakonza zoti Keiko aŵerenge nkhani zosiyanasiyana zokhudza chizoloŵezi chosuta, zolembedwa mu Galamukani! Keiko anafika mpaka poika mawu a pa 2 Akorinto 7:1 m’galimoto yake monga chikumbutso cha tsiku n’tsiku choti akhale woyera kwa Yehova. Komabe sanasiye kusuta. “Ndinakhumudwa kwambiri,” akutero Keiko. “Chotero ndinayamba kudzifunsa za chinthu chomwe ndinkafuna kwenikweni—kodi ndinkafuna kutumikira Yehova kapena Satana?” Atasankha Yehova kuti ndi amene ankafuna kum’tumikira, anapemphera ndi mtima wonse kuti apeze chithandizo. Iye anati, “Ndinadabwa kuti ndinatha kusiya kusuta, mosavutikira kwenikweni. Ndimangodandaula kuti sindinachite zimenezi mofulumira.”
Nanunso mungapambane pothetsa zinthu zokulepheretsani kupita patsogolo. Mukatsimikiza mtima, zofuna zanu, mawu anu, ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi miyezo ya Baibulo, m’pamenenso mumadzilemekeza kwambiri ndiponso mumakhala ndi chidaliro. Abale ndi alongo anu auzimu, komanso a m’banja mwanu, adzasangalala ndipo adzalimbikitsidwa akamacheza nanu. Chofunika kwambiri kuposa zonsezi n’chakuti mudzakhala pa unansi waukulu ndi Yehova Mulungu. Iye analonjeza kuti ‘adzachotsa chokhumudwitsa chilichonse m’njira ya anthu ake’ pamene akuthaŵa m’manja mwa Satana. (Yesaya 57:14) Ndipo mungakhale otsimikiza kuti ngati muchita khama pofuna kuchotsa ndi kugonjetsa zokupingani pa kukula kwanu mwauzimu, Yehova adzakudalitsani kwambiri.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 12 Lofalitsidwa m’zinenero zingapo ndi Mboni za Yehova.
[Chithunzi patsamba 28]
Yesu analonjeza kuti ndi chikhulupiriro, zopinga zofanana ndi mapiri zingagonjetsedwe
[Chithunzi patsamba 30]
Kuŵerenga Baibulo kumakulitsa khama lathu lofuna kugonjetsa zofooka zauzimu