Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mutha “Kusiyanitsa Chabwino ndi Choipa”?

Kodi Mutha “Kusiyanitsa Chabwino ndi Choipa”?

Kodi Mutha “Kusiyanitsa Chabwino ndi Choipa”?

‘Yeserani [“tsimikizani,” NW] chokondweretsa Ambuye n’chiyani.’​—AEFESO 5:10.

1. Kodi ndi motani mmene moyo masiku ano ungakhalire wovuta, ndipo chifukwa chiyani?

“INU Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Mawu anzeru ameneŵa amene Yeremiya ananena amatikhudza kwambiri ifeyo masiku ano. Chifukwa chiyani? Chifukwa tikukhala ‘m’nthaŵi zoŵaŵitsa’ zimene Baibulo linalosera. (2 Timoteo 3:1) Tsiku ndi tsiku, timakhala ndi nkhani zovuta kwambiri zimene zimafuna kuti tigamulepo chochita. Kaya nkhanizi zikhale zazikulu kapena zazing’ono, zosankha zathuzo zingatikhudze kwambiri kuthupi, mumtima komanso mwauzimu.

2. Ndi zosankha ziti zimene ena anganene kuti ndi zazing’ono, nanga Akristu odzipatulira amaziona motani?

2 Zinthu zambiri zimene timasankha kuchita pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku anthu ena anganene kuti ndi mwambo chabe kapenanso kuti ndi zazing’ono. Mwachitsanzo, tsiku lililonse timasankha zovala, chakudya, anthu amene tikufuna kukawaona, ndi zina zotero. Posankha zimenezi, sitiganizira kwambiri zinthuzo. Koma kodi nkhani ngati zimenezi ndi zazing’onodi? Kwa ifeyo Akristu odzipatulira, nkhani zimenezi ndi zazikulu chifukwa zonse zimene timasankha, kaya ndi zovala, kaonekedwe kathu, zakudya ndi zakumwa, kalankhulidwe ndi khalidwe lathu, zimasonyeza nthaŵi zonse kuti ndife atumiki a Yehova Mulungu Wam’mwambamwamba. Timakumbukira mawu amene mtumwi Paulo ananena kuti: “Mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.”​—1 Akorinto 10:31; Akolose 4:6; 1 Timoteo 2:9, 10.

3. Kodi ndi nkhani ziti zazikulu zimene zifunikadi kusamala posankha?

3 Ndiyeno pali zosankha zina zimene zili zazikulu zedi. Mwachitsanzo, nkhani yokwatira kapena kukhala mbeta imakhudza kwambiri moyo wonse wa munthu. Kunena zoona, kusankha munthu woyenera kuloŵa naye m’banja, amenenso mudzakhala naye moyo wanu wonse, si nkhani yapafupi ayi. * (Miyambo 18:22) Ndiponso, zonse zimene timasankha kaya ndi mabwenzi, maphunziro, ntchito, ndi zosangalatsa zimakhudza kwambiri khalidwe lathu lauzimu, motero zimakhudzanso zabwino zonse zimene tingadzakhale nazo kosatha.​—Aroma 13:13, 14; Aefeso 5:3, 4.

4. (a) Kodi ndi luso liti lofunika kwambiri? (b) Kodi tipenda mafunso ati?

4 Popeza zinthu zili choncho, luso losiyanitsa chabwino ndi choipa kapenanso kusiyanitsa chooneka ngati chabwino ndi chabwinodi n’lofunika kwambiri. Baibulo limachenjeza kuti: “Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka; koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.” (Miyambo 14:12) Ndiye tingafunse kuti: Tingatani kuti tikulitse luso losiyanitsa chabwino ndi choipa? Kodi malangizo ofunika posankha zochita tingawapeze kuti? Kodi kale komanso makono, anthu achitanji pankhaniyi, ndipo chachitika n’chiyani?

“Kukonda Nzeru ndi Chinyengo Chopanda Pake” za Dzikoli

5. Kodi Akristu oyambirira anali kukhala m’dziko lotani?

5 Akristu a m’zaka za zana loyamba anali kukhala m’dziko lokonda chikhalidwe cha Agiriki ndi Aroma ndi zikhulupiriro zawo. Komanso, moyo wa Aroma unali wapamwamba ndi wosasoŵa kanthu ndipo ambiri anali kuusirira. Kwinaku, zimene anthu anzeru anali kuchita nazo chidwi kwambiri si mfundo zokha za Plato ndi Arisitote zolimbikitsa kukonda nzeru za anthu ayi. Ankachitanso chidwi ndi magulu atsopano monga Aepikureya ndi Asitoiki. Mtumwi Paulo atafika ku Atene paulendo wake wachiŵiri monga mmishonale, anakumana ndi Aepikureya ndi Asitoiki okonda nzeru za anthu amene anaganiza kuti anam’posa “wobwetuka uyu,” Paulo.​—Machitidwe 17:18.

6. (a) Kodi Akristu ena oyambirira anakopeka kuchita chiyani? (b) Kodi Paulo anachenjeza zotani?

6 Choncho m’posavuta kumvetsa chimene ena mwa Akristu oyambirira anakopekera ndi khalidwe lodzionetsera la anthu owazinga. (2 Timoteo 4:10) Amene anali mbali ya dzikolo anali kuoneka ngati ali ndi mapindu ambiri ndipo zimene anasankha zinaoneka ngati zanzeru. Dziko linali kuoneka ngati lili ndi kanthu kabwino kusiyana ndi moyo wopembedza wa Mkristu. Koma mtumwi Paulo anachenjeza kuti: “Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Kristu.” (Akolose 2:8) N’chifukwa chiyani Paulo ananena zimenezi?

7. Kodi nzeru ya dziko ndi yotani kwenikweni?

7 Paulo anachenjeza motero chifukwa anaona ngozi yaikulu imene aja amene anakopeka ndi dziko anali kuloŵamo. Mawu ake akuti ‘kukonda nzeru, ndi chinyengo chopanda pake’ ali ndi tanthauzo kwambiri. “Kukonda nzeru” kungakhale kothandiza. Pajatu, Baibulo, makamaka m’buku la Miyambo, limatilimbikitsa kufunafuna nzeru yoyenera ndi kudziŵa. (Miyambo 1:1-7; 3:13-18) Koma Paulo anaphatikiza “kukonda nzeru” ndi “chinyengo chopanda pake.” Mwa mawu ena, Paulo anaona nzeru ya dziko kukhala yopanda pake ndi yonyenga. Monga chibaluni chokhuta mpweya, inali kuoneka ngati yodalirika, koma inali yachabechabe. Kutsata zinthu zachabechabe ngati ‘kukonda nzeru ndi chinyengo chopanda pake’ za dzikoli posankha chabwino ndi choipa sikupindula, inde ndi tsoka.

Iwo Oyesa “Zoipa Zabwino, ndi Zabwino Zoipa”

8. (a) Kodi anthu amapita kuti akafuna malangizo? (b) Kodi amawapatsa malangizo otani?

8 Zinthu sizinasinthe kwambiri masiku ano. Ntchito iliyonse imene anthu amachita ili ndi akatswiri ake ankhaninkhani. Alangizi a zaukwati ndi za banja, alangizi olemba nkhani m’manyuzipepala, anthu odziyesa adokotala, openda nyenyezi, amizimu, ndi ena ndi okonzeka kupereka malangizo, ndipotu amalipiritsa! Koma kodi amapereka malangizo otani? Nthaŵi zambiri amakankhira pambali miyezo ya Baibulo yonena za khalidwe ndipo amatsata zimene ambiri amati makhalidwe amakono. Mwachitsanzo, pamene boma linakana kulembetsa “maukwati a amuna okhaokha kapena a akazi okhaokha,” ndemanga ina m’nyuzipepala yotchuka ya The Globe and Mail ku Canada inati: “Ndi malodza kuti m’chaka cha 2000 chino, munthu aletse banja lokondana ndi lokhulupirirana kuti lisachite zimene likufuna chabe chifukwa choti anthu omanga banjawo ndi amuna okhaokha kapena akazi okhaokha!” Ambiri masiku ano amakonda kulolera m’malo moweruza zimene ena akuchita. Amati zili kwa munthu aliyense payekha; sitingauze wina motsimikiza kuti chabwino ndi ichi ndipo ichi n’choipa pakuti zonsezi zimadalira mmene munthu mwini akuonera.​—Salmo 10:3, 4.

9. Kodi anthu amene ena amawaona ngati olemekezeka amachita chiyani nthaŵi zambiri?

9 Ena amayang’ana kwa anthu okhala pabwino ndi ochita bwino m’zachuma​—olemera ndi otchuka​—monga zitsanzo zawo posankha zimene akufuna kuchita. Ngakhale kuti anthu masiku ano amaona ngati olemera ndi otchuka ali olemekezeka, anthu olemerawo ndi otchukawo nthaŵi zambiri amangolankhula za khalidwe labwino monga kuona mtima ndi kukhulupirika basi osatsata zimenezo ayi. Polakalaka kukhala amphamvu komanso pofuna phindu, ambiri saopa kuswa malamulo ndi kunyalanyaza mfundo za makhalidwe abwino. Ena, pofuna kutchuka amaiŵaliratu za makhalidwe abwino ndipo amachita zinthu zachilendo zochititsa kakasi mtima uli zi. Zimenezi zachititsa kuti anthu azingofuna phindu basi ndiponso kuti azilekerera zoipa, ndipo amati, “Zonse n’zabwino.” Kodi tikudabwa kuti anthu ndi osokonezeka maganizo ndipo sakudziŵa chabwino ndi choipa?​—Luka 6:39.

10. Kodi mawu a Yesaya okhudza chabwino ndi choipa akhala oona m’njira yanji?

10 Mavuto amene akhalapo chifukwa chosankha zinthu mopanda nzeru potsata malangizo osocheretsa ali ponseponse. Kutha kwa maukwati ndi kusokonezeka kwa mabanja, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndi uchidakwa, magulu achiwawa a anyamata, chiwerewere, matenda opatsirana mwa kugonana, kungotchula zochepa chabe. Kunena zoona, kodi tingayembekeze zinthu kukhala bwino pamene anthu anyalanyaziratu miyezo yonse akafika pankhani yokhudza chabwino ndi choipa? (Aroma 1:28-32) Zili mongadi zimene mneneri Yesaya ananena kuti: “Tsoka kwa iwo amene ayesa zoipa zabwino, ndi zabwino zoipa; amene aika mdima m’malo mwa kuyera, ndi kuyera m’malo mwa mdima; amene aika zoŵaŵa m’malo mwa zotsekemera, ndi zotsekemera m’malo mwa zoŵaŵa! Tsoka kwa iwo amene adziyesera anzeru ndi ochenjera!”​—Yesaya 5:20, 21.

11. N’chifukwa chiyani kuli kupanda nzeru kudzidalira tikafuna kudziŵa chabwino ndi choipa?

11 Popeza Mulungu anali nawo mlandu Ayuda akale aja amene ‘anadziyesa anzeru,’ ifeyo tifunikadi kupeŵa kudzidalira pamene tikufuna kudziŵa chabwino ndi choipa. Anthu ambiri masiku ano ali ndi maganizo oti “tangotsatani zimene mtima wanu ukufuna,” kapena oti “chitani zimene mukuganiza kuti n’zabwino.” Kodi njira imeneyi ndi yanzeru? Ayi, chifukwa zimenezi zikusemphana ndi Baibulo, lomwe mosapita m’mbali limati: “Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziŵa?” (Yeremiya 17:9) Kodi mungadalire munthu wonyenga amenenso zinthu zimam’sokoneza msanga kuti akuthandizeni kusankha zochita? Kutalitali. M’malo mwake, mudzachita zosiyana ndi zimene munthu ameneyo wakuuzani. Ndiye chifukwa chake Baibulo limatikumbutsa kuti: “Wokhulupirira mtima wakewake ali wopusa; koma woyenda mwanzeru adzapulumuka.”​—Miyambo 3:5-7; 28:26.

Kudziŵa Zokondweretsa Mulungu

12. N’chifukwa chiyani tifunikira kuzindikira “chifuno cha Mulungu”?

12 Popeza sitifunika kudalira nzeru ya dzikoli kapena kudzidalira tikafika pankhani ya kusiyanitsa chabwino ndi choipa, kodi tiyenera kuchitanji? Tamverani uphungu womveka uwu umene mtumwi Paulo anapereka, wakuti: “Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.” (Aroma 12:2) N’chifukwa chiyani tifunikira kuzindikira chifuno cha Mulungu? M’Baibulo Yehova amatipatsa chifukwa chomveka komanso chachikulu, ponena kuti: “Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga zili zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.” (Yesaya 55:9) Choncho, m’malo modalira nzeru zathu kapena maganizo athu, akutichenjeza kuti: “[Tsimikizani] chokondweretsa Ambuye n’chiyani.”​—Aefeso 5:10.

13. Kodi mawu a Yesu olembedwa pa Yohane 17:3 akusonyeza motani kuti kudziŵa zokondweretsa Mulungu n’kofunika?

13 Yesu Kristu anasonyeza kuti zimenezi n’zofunika mmene anati: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.” (Yohane 17:3) Mawu oyambirira a Chigiriki otembenuzidwa kuti “akadziŵe” ali ndi tanthauzo lalikulu kwambiri. Malinga ndi buku la Vine’s Expository Dictionary, mawuwo “amasonyeza ubale umene ulipo pakati pa munthu wodziŵayo ndi uja amene akum’dziŵa; choncho, chodziŵikacho n’chofunika kwa amene akuchidziŵayo ndipo amachiŵerengera, n’chifukwa chake ubalewo umakhalapo.” Kukhala paubale ndi munthu kumatanthauza kudziŵa zambiri osati chabe kudziŵa munthuyo kapena dzina lake. Kumafunanso kudziŵa zimene iye amafuna ndi zimene safuna, kudziŵa khalidwe lake ndi miyezo yake komanso kuilemekeza.​—1 Yohane 2:3; 4:8.

Tizoloŵeretse Mphamvu Zathu za Kuzindikira

14. Kodi ndi mbali iti imene Paulo anati makanda auzimu ndi anthu aakulu msinkhu amasiyana kwambiri?

14 Nangano tingalipeze bwanji luso losiyanitsa chabwino ndi choipa? Yankho tikulipeza m’mawu amene Paulo anauza Akristu achihebri m’zaka za zana loyamba. Analemba kuti: “Yense wakudya mkaka alibe chizoloŵezi cha mawu a chilungamo; pakuti ali khanda. Koma chakudya chotafuna chili cha anthu akulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo [“kuzigwiritsa ntchito,” NW] anazoloŵeretsa zizindikiritso zawo [“mphamvu zawo za kuzindikira,” NW] kusiyanitsa chabwino ndi choipa.” Pano Paulo anasiyanitsa “mkaka” umene m’vesi inayo anati ndiwo “zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu,” ndi “chakudya chotafuna” cha “anthu akulu misinkhu,” amene “anazoloŵeretsa zizindikiritso zawo kusiyanitsa chabwino ndi choipa.”​—Ahebri 5:12-14.

15. N’chifukwa chiyani tifunika kulimbikira kuti tipeze chidziŵitso cholondola cha Mulungu?

15 Zimenezi zikutanthauza kuti choyamba tifunikira kulimbikira kuti timvetse molondola miyezo ya Mulungu imene ili m’Baibulo, Mawu ake. Sitifunikira mndandanda wa malamulo otiuza zimene tingachite ndi zimene sitingachite. Baibulo si buku lotero ayi. M’malo mwake, Paulo anafotokoza kuti: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.” (2 Timoteo 3:16, 17) Kuti tipindule ndi chiphunzitsocho, chitsutsano ndi chilangizo, tiyenera kugwiritsa ntchito maganizo athu ndi nzeru zathu. Zimenezi zimafuna khama, koma zotsatira zake​—kukhala “wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino”​—n’zabwino kwambiri.​—Miyambo 2:3-6.

16. Kodi kuzoloŵeretsa mphamvu zathu za kuzindikira kumatanthauzanji?

16 Ndiye monga Paulo anasonyezera, anthu akulu msinkhu ‘anazoloŵeretsa mphamvu zawo za kuzindikira kusiyanitsa chabwino ndi choipa.’ Apa ndiye tafika pachimake pa mfundo yake. Mawu akuti ‘anazoloŵeretsa mphamvu zawo za kuzindikira” ganizo lake lenileni n’lakuti “maganizo awo anawaphunzitsa (ngati katswiri wa maseŵero olimbitsa thupi).” (Kingdom Interlinear Translation) Katswiri wa maseŵero ngati apidigoli, amatha kulumpha ndi kumatembenuka mofulumira ali m’mwamba kuchita ngati kuti sangagwe. Mphindi iliyonse amalamulira thupi lake lonse ndipo, ngati kuti n’chibadwa chake, amadziŵa zimene ayenera kuchita kuti amalize kutembenukako ndi kutera bwinobwino. Kuti achite zonsezi amayamba wavutikapo kuphunzira ndi kuchita pulakatisi nthaŵi zonse.

17. Kodi ndi motani mmene tingakhalire ngati akatswiri a maseŵero olimbitsa thupi?

17 Ifenso, m’lingaliro lauzimu, tiyenera kudziphunzitsa monga katswiri wa maseŵero olimbitsa thupi ameneyo, ngati nthaŵi zonse tikufuna kutsimikiza kuti zosankha zathu zili zanzeru. Nthaŵi zonse tifunikira kulamulira maganizo athu ndi thupi lathu lonse. (Mateyu 5:29, 30; Akolose 3:5-10) Mwachitsanzo, kodi mumaphunzitsa maso anu kuti asaone zolaula kapena makutu anu kuti asamve nyimbo kapena mawu oipa? Inde, zinthu zoipa ngati zimenezi zili ponseponse. Koma zimadalirabe ifeyo kuti zinthuzo zikhazikike mumtima ndi m’maganizo mwathu kapena kuti zisatero. Titsanzire wamasalmo amene anati: “Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga; chochita iwo akupatuka padera chindiipira; sichidzandimamatira. . . . Wakunena mabodza sadzakhazikika pamaso panga.”​—Salmo 101:3, 7.

Zoloŵeretsani Mphamvu Zanu za Kuzindikira mwa Kuzigwiritsa Ntchito

18. Kodi ndi mfundo yotani yomwe ili m’mawu akuti “kuzigwiritsa ntchito” amene Paulo anatchula pofotokoza zozoloŵeretsa mphamvu zathu za kuzindikira?

18 Kumbukirani kuti tingazoloŵeretse mphamvu zathu za kuzindikira kuti tisiyanitse chabwino ndi choipa mwa “kuzigwiritsa ntchito.” M’mawu ena, tikakumana ndi nkhani yofuna kuti tigamulepo, nthaŵi iliyonse tizigwiritsa ntchito nzeru zathu kuzindikira mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo zokhudza nkhaniyo ndi mmene tingagwiritsire ntchito mfundozo. Khalani ndi chizoloŵezi chofufuza m’mabuku ofotokozera Baibulo amene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amapereka. (Mateyu 24:45) Tithanso kupempha thandizo kwa Akristu okhwima. Koma khama lathu limene timachita pofufuza m’Mawu a Mulungu, limodzi ndi pemphero kwa Yehova, kum’pempha chitsogozo ndi mzimu wake, zidzatipindulitsa m’kupita kwa nthaŵi.​—Aefeso 3:14-19.

19. Kodi tingakhale ndi madalitso otani ngati pang’ono ndi pang’ono tizoloŵeretsa mphamvu zathu za kuzindikira?

19 Tikamazoloŵeretsa mphamvu zathu za kuzindikira pang’onopang’ono, cholinga chake n’chakuti “tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusokeretsa.” (Aefeso 4:14) Koma malinga ndi chidziŵitso chathu ndi kuzindikira kwathu zimene Mulungu amakondwera nazo, titha kusankha mwanzeru pankhani zazikulu ndi zazing’ono, ndipo zingatipindulitse ifeyo, kulimbikitsa olambira anzathu, ndipo makamaka kukondweretsa Atate wathu wakumwamba. (Miyambo 27:11) Limenelo ndi dalitso komanso chitetezo chachikulu m’nthaŵi zino zovuta.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Pamndandanda wa zinthu zoposa 40 zosautsa mtima kwambiri pamoyo wa munthu zimene Dr. Thomas Holmes ndi Dr. Richard Rahe anasanja, pamalo atatu oyambirira anaikapo imfa ya mnzako wa m’banja, kusudzulana, ndi kupatukana. Kukwatira kuli panambala seveni.

Kodi Mutha Kufotokoza?

• Kuti munthu asankhe mwanzeru afunika luso lotani?

• N’chifukwa chiyani kuli kupanda nzeru kuyang’ana kwa anthu otchuka kapena kudalira maganizo athu pofuna kusiyanitsa chabwino ndi choipa?

• N’chifukwa chiyani tifunika kutsimikiza chokondweretsa Mulungu pa zosankha zathu, ndipo tingachite zimenezo motani?

• Kodi ‘kuzoloŵeretsa mphamvu zathu za kuzindikira’ kumatanthauzanji?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 9]

Kuyembekeza kuti olemera ndi otchuka azititsogolera sikuthandiza

[Chithunzi patsamba 10]

Monga katswiri wa maseŵero, tifunikira kulamulira maganizo athu onse ndi thupi lonse