Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zimene Mumakhulupirira Zili ndi Maziko Otani?

Kodi Zimene Mumakhulupirira Zili ndi Maziko Otani?

Kodi Zimene Mumakhulupirira Zili ndi Maziko Otani?

Kukhulupirira kumatanthauza ‘kuvomereza kuti n’zoona kapena zenizeni.’ Chikalata cha mfundo za ufulu wachibadwidwe cha United Nations Universal Declaration of Human Rights chimateteza ‘ufulu wa munthu aliyense wa kuganiza, chikumbumtima, ndi chipembedzo.’ Ufulu umenewu ukuphatikizapo ufulu “wosintha chipembedzo kapena chikhulupiriro chake” ngati wafuna kutero.

KODI n’chifukwa chiyani munthu angafune kusintha chipembedzo kapena chikhulupiriro chake? Nthaŵi zambiri anthu amanena kuti: “Ndili ndi zikhulupiriro zanga ndipo ndimakhutira nazo.” Ambiri amaganiza kuti ngakhale zikhulupiriro zolakwika sizivulaza kwenikweni aliyense. Mwachitsanzo, munthu sangadzivulaze kapena kuvulaza wina aliyense ngati akukhulupirira kuti dziko lapansi ndi lathyathyathya. Ena amati: “Tiyenera kuvomereza kuti tili ndi maganizo osiyana ndipo palibe chifukwa chakuti tizitsutsana.” Kodi zimenezo n’zanzeru nthaŵi zonse? Kodi dokotala adzangovomereza ngati dokotala mnzake akupitiriza kukhulupirira kuti angathandize odwala m’chipatala atangochokera ku nyumba yachisoni kumene wagwira mitembo ya anthu?

Pankhani ya chipembedzo, zikhulupiriro zolakwika zadzetsa mavuto akulu m’mbiri yonse. Talingalirani zinthu zoopsa zimene zinachitika pamene atsogoleri a chipembedzo “analimbikitsa Akristu a changu chopambanitsa kuti aphe mopanda chifundo” pa Nkhondo za Mtanda za zaka za m’ma 1000 mpaka m’ma 1500. Kapena talingalirani za zigaŵenga “zachikristu” zamakono m’nkhondo yachiŵeniŵeni yaposachedwapa. “Izinso zinamata zithunzi za Namwali pa mfuti zawo ngati ankhondo a m’zaka za m’ma 1000 mpaka m’ma 1500 amene analemba maina a anthu oyera mtima kogwirira malupanga awo.” Onseŵa anali kukhulupirira kuti zimene anali kuchita zinali zolondola. Komatu, mwachionekere m’nkhondo zachipembedzo zimenezi pamodzi ndi zinanso, chinachake chinalakwika kwambiri.

Kodi n’chifukwa chiyani pali kusokonezeka ndi kukangana kwakukulu motere? Baibulo limayankha kuti Satana Mdyerekezi ‘akunyenga dziko lonse.’ (Chivumbulutso 12:9; 2 Akorinto 4:4; 11:3) Mtumwi Paulo anachenjeza kuti mwachisoni anthu achipembedzo ambiri ‘adzawonongeka’ chifukwa Satana adzawanyenga mwa kuchita “zizindikiro ndi zozizwa zonama.” Paulo anati anthu otero, ‘sadzalandira chikondi cha choonadi kuti akapulumutsidwe iwo’ ndipo motero ‘adzawasocheretsa, kuti akhulupirire bodza.’ (2 Atesalonika 2:9-12) Kodi mungatani kuti mupewe kukhulupirira bodza? N’chifukwa chiyani kwenikweni muli ndi chikhulupiriro chimene muli nacho pakalipano?

Kodi Mumakhulupirira Chifukwa Chakuti Munaleredwa ndi Makolo Okhulupirira?

Mwina mwakulira m’zimene makolo ndi achibale anu amakhulupirira. Zimenezo n’zabwino ndithu. Mulungu amafuna kuti makolo aphunzitse ana awo. (Deuteronomo 6:4-9; 11:18-21) Mwachitsanzo, Timoteo wachinyamata, anapindula kwambiri mwa kumvera mayi ake ndi agogo ake. (2 Timoteo 1:5; 3:14, 15) Malemba amalimbikitsa kuti n’kofunika kulemekeza zimene makolo akukhulupirira. (Miyambo 1:8; Aefeso 6:1) Koma kodi Mlengi wanu anafuna kuti muzikhulupirira zinthu chabe chifukwa chakuti makolo anu amakhulupirira zimenezo? Ndithudi, kuumirira mosaganiza bwino pa zimene mbadwo wakale unali kukhulupirira ndi kuchita, n’koopsa.​—Salmo 78:8; Amosi 2:4.

Mkazi wachisamariya amene anakumana ndi Yesu Kristu anakulira m’chipembedzo chake cha chisamariya chimene anali kukhulupirira. (Yohane 4:20) Yesu analemekeza ufulu wake wosankha zimene akufuna kukhulupirira, komabe anamuuza kuti: “Inu mulambira chimene simuchidziŵa.” Ndithudi, zikhulupiriro zake zachipembedzo zambiri zinali zolakwika. Motero, Yesu anamuuza kuti anayenera kusintha zimene anali kukhulupirira ngati anafuna kuti alambire Mulungu movomerezeka​—“mumzimu ndi m’choonadi.” M’malo mongoumirira zikhulupiriro zimene mosakayikira anali kuzikonda, m’kupita kwa nthaŵi iye ndi enanso onga iye anafunika ‘kumvera chikhulupirirocho’ chimene Yesu Kristu anavumbula.​—Yohane 4:21-24, 39-41; Machitidwe 6:7.

Kodi Mumakhulupirira Chifukwa Chakuti Akatswiri Anakuphunzitsani?

Aphunzitsi ndi akatswiri ambiri a maphunziro osiyanasiyana tiyenera kuwalemekeza kwambiri. Komabe, pali zitsanzo za aphunzitsi otchuka ambiri amene analakwitsa kotheratu. Mwachitsanzo, pofotokoza za mabuku aŵiri a nkhani za sayansi omwe Aristotle, wafilosofi wachigiriki analemba, wolemba mbiri wina, Bertrand Russell anati “palibe chiganizo ngakhale chimodzi m’mabukuŵa chimene chikugwirizana ndi sayansi yamakono.” Akatswiri amakono amaphunzitsanso zolakwika nthaŵi zina. Mu 1895, Lord Kelvin wasayansi wa ku Britain ananena mwachikhulupiriro chonse kuti: “N’zosatheka kupanga makina ouluka olemera kuposa mpweya.” Choncho, munthu wanzeru samangokhulupirira mwa chimbulimbuli kuti zinazake n’zoona chabe chifukwa chakuti katswiri wina waphunzitsa zimenezo.​—Salmo 146:3.

Mofananamo, mpofunikanso kusamala pa nkhani ya maphunziro achipembedzo. Aphunzitsi achipembedzo anam’phunzitsa kwambiri mtumwi Paulo ndipo anali “wachangu koposa pa miyambo ya makolo [ake].” Komabe changu chake pa miyambo ya makolo ake chinam’bweretsera mavuto. Chinam’chititsa ‘kulondalonda Mpingo wa Mulungu koposa, ndi kuupasula.’ (Agalatiya 1:13, 14; Yohane 16:2, 3) Choipa kwambiri chinali chakuti, kwanthaŵi yaitali, Paulo anapitiriza “kutsalima pachobayira,” kutsutsa zimene zikanam’thandiza kuti akhulupirire Yesu Kristu. Anasintha zikhulupiriro zake pamene Yesu mwini analoŵererapo mwamphamvu.​—Machitidwe 9:1-6; 26:14, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono.

Kodi Atolankhani Akusonkhezerani?

Mwinamwake atolankhani asonkhezera kwambiri zimene mukukhulupirira. Anthu ambiri ndi okondwa kuti atolankhani ali ndi ufulu wa kulankhula. Zimenezi zimachititsa anthu kudziŵa zina ndi zina zimene zingakhale zothandiza. Komabe, pali zosonkhezera zamphamvu zimene zingalamulire ndipo nthaŵi zambiri zimalamulira atolankhani. Nkhani zina zimene amafotokoza n’zachinyengo ndipo zingawononge maganizo anu pang’ono ndi pang’ono.

Kuphatikizanso apa, pofuna kusangalatsa kapena kukopa anthu ambiri, atolankhani amafalitsa nkhani zimene zimadzutsa zikhumbo zoipa ndiponso nkhani zodabwitsa. Nkhani zimene sakanazilola kuti anthu onse amve kapena kuŵerenga zaka zingapo zapitazo, tsopano zikupezeka paliponse lerolino. Ngakhale kuti zikuchitika pang’onopang’ono, miyezo yabwino ya makhalidwe ikuwonongeka ndi kutha. Maganizo a anthu akusintha pang’ono ndi pang’ono. Ayamba kukhulupirira kuti ‘zoipa n’zabwino, ndipo zabwino n’zoipa.’​—Yesaya 5:20; 1 Akorinto 6:9, 10.

Kupeza Maziko Abwino a Chikhulupiriro

Kumanga pa malingaliro ndi mafilosofi a anthu kuli ngati kumanga pamchenga. (Mateyu 7:26; 1 Akorinto 1:19, 20) Ndiyeno, kodi n’chiyani chomwe chiyenera kukhala maziko odalirika a chikhulupiriro chanu? Popeza Mulungu wakupatsani nzeru zoti muthe kufufuza zinthu m’dzikoli ndi kufunsa mafunso okhudza nkhani zauzimu, kodi sizoona kuti angaperekenso njira yopezera mayankho olondola a mafunso anu? (1 Yohane 5:20) Inde, angaterodi! Komano, kodi mungapeze bwanji zoona kapena zenizeni pa nkhani ya kulambira? Sitikayika kunena kuti Mawu a Mulungu, Baibulo ndi amene amapereka maziko okha ochitira zimenezi.​—Yohane 17:17; 2 Timoteo 3:16, 17.

Wina anganene kuti: “Taimani kaye. Kodi si anthu okhala ndi Baibulo omwewo amene ayambitsa mikangano yambiri ndi chisokonezo padziko lapansi?” Inde, n’zoona kuti atsogoleri a chipembedzo amene amati amatsatira Baibulo ayambitsa chisokonezo ndi mikangano. Kwenikweni, iwo achita zimenezi chifukwa sanazike zikhulupiriro zawo m’Baibulo. Mtumwi Petro anawanena kuti ndi “aneneri onama” ndi “aphunzitsi onama” amene adzayambitsa “mipatuko yotayikitsa.” Chifukwa cha zochita zawo, Petro anati, “njira ya choonadi idzanenedwa zamwano.” (2 Petro 2:1, 2) Komabe, Petro analemba kuti, “tili nawo mawu a chinenero okhazikika koposa; amene muchita bwino powasamalira, monga nyali younikira m’malo a mdima.”​—2 Petro 1:19; Salmo 119:105.

Baibulo limatilimbikitsa kupenda zimene timakhulupirira kuti tione ngati zikugwirizana ndi zimene ilo limaphunzitsa. (1 Yohane 4:1) Anthu miyandamiyanda amene amaŵerenga magazini ano, angachitire umboni kuti kuchita zimenezo kwachititsa moyo wawo kukhala watanthauzo ndiponso wokhazikika. Motero khalani monga mfulu za ku Bereya. ‘Santhulani m’malembo masiku onse’ musanasankhe zoti mukhulupirire. (Machitidwe 17:11) Mboni za Yehova zidzakhala zokondwa kukuthandizani kuti muchite zimenezo. Inde, ndi chosankha chanu kukhulupirira zimene mukufuna. Komabe, n’kwanzeru kuonetsetsa kuti Mawu a Choonadi a Mulungu ndi amene akuumba zimene mukukhulupirira osati nzeru ndi zikhumbo za anthu.​—1 Atesalonika 2:13; 5:21.

[Zithunzi patsamba 6]

Mungazike zikhulupiriro zanu m’Baibulo mwachidaliro