Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi Danieli anali kuti pamene Ahebri atatu aja anawayesa kuti alambire fano lalikulu limene Nebukadinezara anaimika m’chigwa cha Dura?

Baibulo silimanena, motero palibe munthu lerolino amene angadziŵe kumene Danieli anali panthaŵi ya kuyesedwako.

Ena anena kuti udindo wa Danieli m’boma kapena mphamvu zapadera zimene Nebukadinezara anam’patsa zinali zapamwamba kuposa za Sadrake, Mesake, ndi Abedinego ndipo motero sanafunike kupita ku chigwa cha Dura. Danieli 2:49 amanenadi kuti nthaŵi ina iye anali ndi udindo wapamwamba kuposa anzake atatuwo. Koma palibe umboni wakuti zimenezi zinam’chititsa kuti asapezeke nawo pa kulambira fanoli.

Poyesa kufotokoza chifukwa chake Danieli sanapezekepo, ena anena kuti mwina anapita kwina kukagwira ntchito za boma kapena anadwala motero analephera kupezekapo. Komabe, Baibulo silinena zimenezo. Mulimonse mmene zinalili, zimene Danieli anachita ziyenera kuti sizinali zoti angampeze nazo chifukwa. Zikanakhala zotero, mosakayika nduna za boma za nsanje zikanagwiritsa ntchito kusapezekapo kwakeko kukhala chifukwa chomuimbira mlandu. (Danieli 3:8) Zimenezi zisanachitike ndiponso pambuyo pake, Danieli anasunga umphumphu ndipo anakhulupirika kwa Mulungu ngakhale kuti anakumana ndi mayesero ambiri. (Danieli 1:8; 5:17; 6:4, 10, 11) Choncho, ngakhale kuti Baibulo silinena chifukwa chake Danieli sanapezeke ku chigwa cha Dura, tingakhulupirire kuti anakhulupirikabe kwa Yehova Mulungu mosagonja.​—Ezekieli 14:14; Ahebri 11:33.