Analandira Satifiketi Chifukwa cha Kuchita Bwino
Analandira Satifiketi Chifukwa cha Kuchita Bwino
BUNGWE la Association of Congolese and African Journalists for the Development (AJOCAD) ku Democratic Republic of Congo limapereka satifiketi “yoyamikira anthu kapena mabungwe amene achita bwino pothandiza chitukuko [m’Congo].”
Pa November 17, 2000, bungwelo linapereka satifiketiyi kwa Mboni za Yehova chifukwa cha “kuthandiza kutukula anthu a ku Congo kupyolera m’zimene mabuku ndi magazini awo amaphunzitsa.”
Pochitira ndemanga za satifiketiyo, nyuzipepala ya ku Kinshasa ya Le Phare inati: “Pafupifupi munthu aliyense wa ku Congo waŵerengapo Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kapena mabuku ena amene Mboni za Yehova zikufalitsa. Magazini ameneŵa [amafotokoza] mbali zonse za moyo.” Nyuzipepalayo inanenanso kuti mabukuŵa amafotokoza “mmene tingachitire ndi mavuto amakonoŵa” ndiponso “tanthauzo lenileni la zimene zikuchitika masiku ano.” Magazini iliyonse ya Galamukani! “siloŵerera nkhani za ndale ndipo sikweza fuko lina kuposa linzake.” Ndiponso, mabukuwo amakulitsa “chikhulupiriro m’zimene Mlengi walonjeza za dziko la mtendere ndi lotetezeka limene posachedwapa lidzaloŵa m’malo dziko lamakono loipa ndi losatsatira malamuloli.”
Monga momwe bungwe la AJOCAD linanenera, mabuku a Mboni za Yehova apindulitsa anthu ambiri ku Congo. Mabuku ameneŵa akupezeka m’zinenero 235. Uthenga wopatsa chiyembekezo umene uli m’mabukuŵa ungakupindulitseni inunso.
Taŵerengani mawu ali pansiwa ndi kuona mmene mungapindulire nawo.