Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Buku Limene Achinyamata Ambiri Amalinyalanyaza

Buku Limene Achinyamata Ambiri Amalinyalanyaza

Buku Limene Achinyamata Ambiri Amalinyalanyaza

“KODI ndingadziŵe bwanji kuti Baibulo lilidi Mawu a Mulungu? Bukuli silimandisangalatsa,” anatero mtsikana wina dzina lake Beate.

Ku Germany, kumene Beate akukhala, achinyamata ambiri ali ndi maganizo ngati ameneŵa. Amaganiza kuti kuŵerenga Baibulo n’kopanda phindu. Kufufuza kumene anachita posachedwapa kumeneko, anapeza kuti mwa achinyamata 100, mmodzi yekha amaŵerenga kwambiri Baibulo, aŵiri amaliŵerenga mochepera, 19 amangoŵerenga mwakamodzikamodzi, ndipo pafupifupi 80 samaliŵerenga m’pang’ono pomwe. Mosakayika, ziŵerengero zimenezi zilinso chimodzimodzi m’mayiko ena, mwinanso ngakhale kwanuko. Inde, achinyamata ambiri amanyalanyaza Baibulo.

Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti achinyamata ambiri salidziŵa bwino Baibulo. Kuchiyambi kwa chaka cha 2000, nyuzipepala ya Lausitzer Rundschau inapereka lipoti la kafukufuku amene anavumbula chiŵerengero cha anthu amene amadziŵa bwino kwambiri Malamulo Khumi ndi kuwatsatira m’moyo wawo. Mwa anthu a zaka zoposa 60, amene anali kudziŵa malamuloŵa ndi kuwatsatira anali 67 peresenti. Koma mwa anthu a zaka zosakwana 30, 28 peresenti okha ndi amene anali kudziŵa ndi kutsatira malamuloŵa. Inde, achinyamata ambiri sadziŵa Mawu a Mulungu.

Ena Akulidziŵa Bwino Baibulo

Mosiyana ndi ameneŵa, pali achinyamata mamiliyoni ambiri padziko lonse amene apeza kuti Mawu a Mulungu ngopindulitsa kwambiri. Mwachitsanzo, Alexander ali ndi zaka 19 ndipo amaŵerenga Baibulo mmaŵa uliwonse asanapite kuntchito. Iye akuti: “Kwa ine, imeneyi ndi njira yabwino yoyambira tsiku.” Sandra ali ndi chizoloŵezi choŵerenga Baibulo madzulo aliwonse. Akulongosola kuti: “Kuŵerenga Baibulo ndi chimodzi mwa zinthu zomwe ndazoloŵera kuchita tsiku ndi tsiku.” Ndipo Julia, yemwe ali ndi zaka 13, wazoloŵera kuŵerenga pafupifupi chaputala chimodzi cha Baibulo usiku asanakagone. “Ndimasangalala nazo kwambiri ndipo ndikufuna kupitiriza kuchita zimenezi.”

Kodi amene akuŵerenga Baibulo ndi amene sakuŵerenga ndi ati akuchita molondola ndiponso mwanzeru? Kodi Baibulo n’lofunikadi kuliŵerenga? Kodi n’lopindulitsa ndiponso lofunika kwa achinyamata? Mukuganiza bwanji?