Kodi Mukukumbukira?
Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwapindula poŵerenga makope a Nsanja ya Olonda aposachedwapa? Tayesani kuyankha mafunso otsatiraŵa:
• Kodi n’chifukwa chiyani kupenda mafunso amene ali pa Yobu chaputala 38 n’kofunika ngakhale lerolino?
Ntchito zodabwitsa zimene Yehova wachita, n’zovuta kuzimvetsa bwinobwino ngakhale kwa asayansi amakono. Zina mwa zimenezi ndizo mmene mphamvu yokoka imachititsira dziko lapansi kukhalabe mumpita wake, kuwala n’chiyani kwenikweni, chifukwa chake pali mitundu yosiyanasiyana ya zidutswa za chipale chofeŵa, mmene madontho a mvula amapangidwira, ndi mphamvu za mabingu.—4/15, masamba 4-11.
• Kodi n’zitsanzo za m’Baibulo ziti zimene zingatithandize tikavutika maganizo?
Asafu, Baruki, ndi Naomi analefuka kapena kuvutika maganizo nthaŵi zina. Nkhani za m’Malemba zofotokoza mmene anapiririra n’kupambana atakumana ndi zimenezi, zingatithandize.—4/15, masamba 22-4.
• Kodi tingathandize bwanji akazi amasiye achikristu?
Mabwenzi angadzipereke kuthandiza mwachifundo ndiponso moyenera. Achibale ndi ena angathandize ndi ndalama kapena zinthu zina, ngati zimenezo zikufunikadi kwambiri. Akristu anzawo angathandize mwakukhala mabwenzi awo, kuwalimbikitsa mwauzimu ndi kuwasangalatsa.—5/1, masamba 5-7.
• N’chifukwa chiyani n’kofunika kukwatira kapena kukwatiwa kokha “mwa ambuye,” monga momwe 1 Akorinto 7:39 amalangizira?
Banja lomanga ndi munthu wosakhulupirira limalephera momvetsa chisoni. Ndiponso, mwa kutsatira langizo limeneli timakhala okhulupirika kwa Yehova Mulungu. Tikachita mogwirizana ndi Mawu a Mulungu, mitima yathu simatitsutsa. (1 Yohane 3:21, 22)—5/15, masamba 20-1.
• Popeza Yehova ndiye angatikhululukire machimo athu, n’chifukwa chiyani Akristu amaulula machimo aakulu kwa akulu mumpingo?
Inde, Mkristu ayenera kupempha Yehova kuti am’khululukire machimo aakulu. (2 Samueli 12:13) Koma monga momwe mneneri Natani anathandizira Davide, akulu okhwima mumpingo angathandize ochimwa omwe alapa. Kupita kwa akulu n’kogwirizana ndi malangizo amene ali pa Yakobo 5:14, 15.—6/1, tsamba 31.
• Kodi pali umboni wotani wakuti tiyenera kusamala ana ndi akazi amasiye amene akufuna thandizo?
Mbiri ikusonyeza kuti kusamala ana ndi akazi amasiye kunali chizindikiro cha kulambira koona pakati pa Ahebri akale ndiponso kwa Akristu oyambirira. (Eksodo 22:22, 23; Agalatiya 2:9, 10; Yakobo 1:27) Mtumwi Paulo anafotokoza m’Malemba malangizo omveka akuti Akristu asamalire akazi amasiye amene akufuna thandizo. (1 Timoteo 5:3-16)—6/15, masamba 9-11.
• Kodi chinsinsi cha moyo wachimwemwe ndiponso watanthauzo n’chiyani?
Tikulitse ndi kusunga unansi woyenera ndi Yehova, Atate wathu wakumwamba. Tiyenera kuphunzira Baibulo kuti tithe kuchita zimenezo.—7/1, masamba 4-5.
• Kodi munthu aliyense ali ndi mzimu wosafa umene umapulumuka munthuyo akamwalira?
Ngakhale kuti anthu ena amakhulupirira kuti mzimu sufa, Baibulo limatsutsa zimenezo. Limanena kuti munthu akamwalira, amabwerera kufumbi ndipo sakhalanso ndi moyo. Koma Mulungu angathe kubwezeretsa moyo mwa iye. Motero, ngati munthuyo ati adzakhale ndi moyo m’tsogolo, mwa kuuka kwa akufa, zimadalira Mulungu basi. (Mlaliki 12:7)—7/15, masamba 3-6.
• Kodi Danieli anali kuti pamene Ahebri atatu aja anawayesa m’chigwa cha Dura?
Baibulo silinena. Mwina Danieli sanafunike kupitako chifukwa cha udindo wake, kapena anapita kwina kukagwira ntchito zaboma. Koma tingakhulupirire kuti anakhulupirikabe kwa Yehova mosagonja.—8/1, tsamba 31.