Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuwala Monga Zounikira Mumzinda wa Kuunika

Kuwala Monga Zounikira Mumzinda wa Kuunika

Kuwala Monga Zounikira Mumzinda wa Kuunika

Mawu akuti Fluctuat nec mergitur, omwe amatanthauza kuti “Mafunde amam’kantha koma samira,” amanena za mzinda wa Paris.

M’ZAKA 2,000 zapitazo, mzinda wa Paris, mofanana ndi chombo, wavutika ndi mikuntho yosaŵerengeka yachilendo ndiponso kugalukira boma kwa nzika za momwemo. Komabe mzindawu sunamire. Lerolino, Paris ndi umodzi mwa mizinda yokongola kwambiri padziko lonse. Anthu amaukonda kwambiri chifukwa cha nyumba zake zochititsa chidwi, misewu yaikulu yokhala ndi mitengo m’mbali mwake, ndiponso malo otchuka kwambiri padziko lonse osungirako zinthu zochititsa chidwi. Ena amati olemba ndakatulo, amisiri, ndiponso afilosofi ambiri amakonda kupita kumeneko. Ena amakonda kwambiri chakudya cha mumzindawu ndiponso amasirira malo olangizira za kavalidwe ndi khalidwe la akazi.

Kwanthaŵi yaitali, mzinda wa Paris wakhala chimake cha Chikatolika. Zaka mazana aŵiri zapitazo, Paris anayamba kudziŵika ndi dzina lakuti Mzinda wa Kuunika chifukwa unatenga mbali yaikulu m’gulu la ophunzira la ku Ulaya limene amati Gulu Lokana Zachikale. Kaya anthu a ku Paris akudziŵa kapena ayi, lerolino filosofi yanthaŵi imeneyo ndi imene ikuwasonkhezera kwabasi kuposa chipembedzo.

Komabe, nzeru za munthu sizinaunikire mitima ya anthu monga momwe anali kuyembekezera. Ambiri lerolino akufunafuna kuunika kochokera kumagwero ena. Kwa zaka pafupifupi 90 tsopano, Mboni za Yehova zakhala zikuwala ‘monga zounikira’ m’Paris. (Afilipi 2:15) Mofanana ndi oyendetsa sitima aluso, iwo anali kusintha nthaŵi ndi nthaŵi mogwirizana ndi kusintha kwa zochitika panyanja kuti anyamule “zofunika za amitundu onse.”​—Hagai 2:7.

Mzinda Wovuta Kuulalikira

Kale, mu 1850, m’Paris munali anthu 600,000. Lerolino, mumzindawu komanso m’madera ozungulira muli anthu oposa mamiliyoni asanu ndi anayi. Kuchulukana kumeneku kwachititsa kuti Paris ukhale mzinda wokhala ndi anthu osiyanasiyana kuposa wina uliwonse mu France. Paris m’pachimake pa maphunziro apamwamba padziko lonse. Muli yunivesite yakale kwambiri padziko lonse, ndipo muli ophunzira a kuyunivesite pafupifupi 250,000. Malo omwe ali osasangalatsa ku Paris ndi madera ozungulira amene ali ndi nyumba zambiri zazitali komwe kuli umbanda ndi ulova. N’zosadabwitsa kuti pamafunika luso ndiponso kuzoloŵera kuti Mboni za Yehova zilengeze uthenga wabwino mogwira mtima kwa anthu onse.​—1 Timoteo 4:10.

Alendo oposa mamiliyoni 20 amakacheza ku Paris chaka chilichonse. Mwina amakwera Nsanja ya Eiffel mosangalala. Mwinanso amayenda m’mphepete mwa mtsinje wa Seine, kapena kukhala m’malesitilanti ndi m’mabala omwe ali m’mbali mwa msewu. Komabe, anthu a ku Paris amakhala otanganidwa tsiku lililonse. Christian, mtumiki wanthaŵi zonse, akuti: “Anthu amakhala akufulumira nthaŵi zonse. Pobwerera kunyumba kuchokera kuntchito amakhala atatopa.” Kulankhula ndi anthu otanganidwa ameneŵa n’kovuta.

Komabe, limodzi mwa mavuto aakulu kwambiri amene Mboni za Yehova zikukumana nawo ku Paris ndilo kulankhula ndi anthu m’nyumba zawo. Nyumba zina zili ndi makina olankhulira ndi munthu wapanja. Chifukwa cha kuchuluka kwa umbanda, nyumba zambiri anaika ziwiya zamagetsi zotetezera, ndipo n’kosatheka kuti munthu aloŵe. N’chifukwa chake m’madera ena muli Mboni imodzi yokha mwa anthu 1,400 alionse. Motero, nthaŵi zambiri abale akuchitira umboni patelefoni ndi kuchita umboni wamwamwayi. Kodi Mboni za Yehova ‘zawalitsanso kuunika kwawo’ mwanjira zina?​—Mateyu 5:16.

Kuli mipata yambiri ndiponso malo ambiri ochitira umboni wamwamwayi. Martine anaona mayi wina ataima pokwerera basi koma akuoneka wachisoni. Mwana wake wamkazi mmodzi yekha anali atangomwalira kumene. Martine anampatsa mayiyu bulosha lofotokoza chiyembekezo chotonthoza cha m’Baibulo cha kuuka kwa akufa. Ndiyeno sanakumane nayenso kwa miyezi ingapo. Martine atakumananso ndi mayi uja, anayamba kuphunzira naye Baibulo. Ngakhale kuti mwamuna wake anam’tsutsa, iye anakhala Mboni.

Umboni Wamwamwayi Wopindulitsa

Zoyendera za anthu onse za ku Paris ndi zina mwa zoyendera zotsogola kwambiri padziko lonse. Sitima zapansi panthaka zomwe n’zotchuka kumeneko, zimanyamula anthu 5,000,000 tsiku lililonse. Akuti Châtelet-Les-Halles ya m’Paris ndi siteshoni yapansi panthaka yaikulu kwambiri ndiponso pamafika anthu ambiri kuposa ina iliyonse padziko lapansi. Mipata yokumana ndi anthu kumeneko ndi yambiri. Alexandra amakwera sitima zapansizi tsiku lililonse popita kuntchito. Tsiku lina anacheza ndi mwamuna wina amene anali kudwala leukemia, nthenda yosachiritsika ya m’magazi. Anampatsa thirakiti lofotokoza chiyembekezo cha Paradaiso. Anayamba kuphunzira naye Baibulo pamalo amodzimodziwo ndiponso panthaŵi yofananayo tsiku lililonse kwa milungu isanu ndi umodzi. Ndiyeno tsiku lina mwamunayo sanafike pamalowo. Patangopita nthaŵi yochepa, mkazi wake anam’chitira foni Alexandra n’kumuuza kuti abwere kuchipatala chifukwa mwamuna wake anali kudwala mwakayakaya. Mwatsoka, Alexandra anafika mochedwa. Mwamunayu atamwalira, mkazi wake anasamukira ku Bordeaux, kumwera cha kumadzulo kwa France, kumene Mboni za kumeneko zinamuchezera. Alexandra anasangalalatu kwambiri kumva pambuyo pa chaka chimodzi kuti mkazi wamasiyeyo anakhala Mkristu wobatizidwa wa Mboni za Yehova, yemwe tsopano akuyembekeza kudzaona mwamuna wake akuuka kwa akufa!​—Yohane 5:28, 29.

Mkazi wina wachikulire wachikristu analankhula ndi Renata m’sitima pochokera ku Paris kupita ku Limoges, m’kati mwa France. Ali kwawo ku Poland, Renata anachita maphunziro apamwamba a zaumulungu, ndi kuphunzira Chihebri, ndi Chigiriki kwa zaka zisanu koma analeka kukhulupirira Mulungu. Miyezi itatu m’mbuyomo asanakumane ndi mayiyu, Renata anapemphera kwa Mulungu. Ngakhale kuti analibe chidwi ndi zimene mlongo wachikulireyo anali kunena ndiponso akuganiza kuti sadzakumananso, Renata anam’patsa mlongoyo nambala yake ya foni. Komabe, mlongoyo anachita khama ndipo anaonetsetsa kuti abale amuchezera Renata mwamsanga. Mbale wina ndi mkazi wake atafika kudzam’chezera, iye anaganiza kuti, ‘Kodi akufuna kundiphunzitsa chiyani?’ Ngakhale kuti anachita maphunziro apamwamba a zaumulungu, anachita chidwi ndi choonadi cha Baibulo. Akufotokoza kuti: “Nthaŵi yomweyo ndinazindikira kuti ichi n’choonadi.” Tsopano akusangalala kuuza ena uthenga wa m’Baibulo.

Michèle anali kuphunzira kuyendetsa galimoto. Ophunzira ena m’kalasi lakelo anayamba kulankhula za kugonana ukwati usanachitike. Michèle anatsutsa zimenezo. Patapita mlungu umodzi, mphunzitsi wawo dzina lake Sylvie anam’funsa kuti: “Kodi ndiwe wa Mboni za Yehova?” Sylvie anachita chidwi ndi maganizo ozikidwa m’Baibulo a Michèle pankhaniyi. Phunziro la Baibulo linayambika ndipo patapita chaka chimodzi Sylvie anabatizidwa.

Mapaki ambirimbiri a ku Paris ndi malo abwino oti n’kulankhulana ndi anthu. Panthaŵi yopuma, Jesette anatengerapo mwayi wopita ku paki kumene mayi wina wachikulire dzina lake Aline anali kuwongola miyendo. Josette anafokoza malonjezo osangalatsa amene ali m’Baibulo. Anakonza zoti aziphunzira Baibulo, ndipo posachedwa Aline anapita patsogolo mpaka kubatizidwa. Tsopano, pausinkhu wa zaka 74, iye ndi mpainiya wokhazikika wochita bwino zedi ndipo amasangalala kuuza ena choonadi chachikristu.

Muuni wa Anthu Onse

Mboni za ku Paris sizidalira kupita ku mayiko ena akutali kuti akaone zikhalidwe zosiyanasiyana. Pafupifupi anthu 20 mwa anthu 100 alionse kumeneko ndi ochokera kumayiko ena. Kuli mipingo ndi magulu achikristu m’zinenero 25.

Luso limathandiza kukhala n’zotsatira zabwino m’ntchito yapadera yolalikirayi. Mboni ina ya ku Philippine inapanga dera lakelake lapadera. Pogula zinthu m’masitolo, iye anayambitsa maphunziro a Baibulo ambiri mwa kuyamba kulankhulana ndi anzake a ku Philippine.

Kukhala patsogolo pantchito yolalikira kumapindulitsa. Mu December 1996, Mboni za mpingo wina wa chinenero chakunja zitamva kuti asangalatsi otchuka padziko lonse akubwera m’tauniyo, zinaganiza zoti ziyese kulankhula ndi asangalatsiwo. Madzulo ena atamaliza kuonetsa maseŵero awo, Mboni zinalankhula ndi akatswiriwo pamene anali kubwerera ku hotela yawo. Zimenezi zinachititsa kuti agaŵire mabaibulo 28, mabuku achikristu 59, mabulosha 131, ndi magazini 290. Itatha milungu itatu imene anakhala kumeneko, katswiri wina anafunsa kuti: “Nditani kuti ndikhale mmodzi wa Mboni za Yehova?” Wina ananena kuti: “Ndikalalikira ku dziko lakwathu!”

Kupeza Chuma Chobisika

Pomwazamwaza maso, alendo ofika ku Paris amaona kamangidwe ka mtengo wapatali ka nthaŵi za makedzana. Komabe, akuyembekeza kupeza zinthu za mtengo wapatali kuposa zimenezo. Aniza anafika ku France limodzi ndi amalume ake omwe ndi kazembe. Aniza anali kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse kunyumba kwawo. Tsiku lina akuchoka panyumba mofulumira, mpainiya wina anampatsa thirakiti lakuti Chifukwa Chimene Mungakhulupirire Baibulo. Anapangana kuti akumane mlungu wotsatira ndipo Aniza anayamba kuphunzira Baibulo. Achibale ake anam’tsutsa kwambiri. Anapita patsogolo kuphunzira mpaka anabatizidwa. Kodi amaganiza bwanji za mwayi umene ali nawo wouza ena choonadi? Akuti: “Poyamba ntchito yolalikira inali kundivuta chifukwa ndine wamanyazi. Komabe, Baibulo limandilimbikitsa ndikaliŵerenga. Sindimva bwino ngati ndikhala osalalikira.” Mboni zambiri ku Paris zili ndi maganizo onga ameneŵa. Iwo ali “akuchuluka mu ntchito ya Ambuye.”​—1 Akorinto 15:58.

Choonadi cha Baibulo chikuŵalanso m’nyumba zambiri zoyandikana za m’madera ozungulira Paris, kuonetsa zinthu zinanso “zamtengo wapatali.” Bruce anafuna kuti akabwereke makaseti kwa mnzake wina amene anangokhala kumene Mboni ya Yehova. Atafika anapeza kuti mnzakeyo akukambirana za Baibulo ndi anthu ena amene Bruce anali kuwadziŵa, motero nayenso anamvetsera. Anavomera kuphunzira Baibulo koma anali ndi mavuto ena. Iye akuti: “Ndinali kudziŵika kwambiri m’derali. Mkulu wanga anali kukonda ndewu nthaŵi zonse, ndipo ine ndinali kuchititsa madansi a phokoso. Anthu akanavomereza bwanji kuti ndinafuna kukhala Mboni?” Bruce anasiya kuchititsa maphwando ngakhale kuti anthu anampempha moumirira kuti atero. Patapita mwezi umodzi anayamba kulalikira. Akuti: “Aliyense m’deralo amafuna kudziŵa chifukwa chake ndinakhala Mboni.” Patapita nthaŵi yochepa, anabatizidwa. M’kupita kwa nthaŵi, anapeza mwayi wokaphunzira m’Sukulu Yophunzitsa Utumiki.

Kufunafuna chuma kumafuna kulimbikira. Komatu zimasangalatsa kwambiri ntchitoyo ikakhala yopindulitsa! Jacky, Bruno, ndi Damien anali kuphika buledi m’Paris. Jacky akuti: “Zinali zosatheka kuti alankhule nafe chifukwa tinali kugwira ntchito nthaŵi zonse ndipo sitinali kupezeka panyumba.” Patrick, mpainiya wokhazikika, anaona kuti panali zipinda zina zazing’ono pamwamba panyumba imene anali kukhala, ndipo anaganiza kuti m’chipinda china munali kukhala anthu. Kuyesetsa kwake mwakhama kuti alankhule ndi anthu amene anali kukhala m’chipindacho kunapindula pamene tsiku lina madzulo analankhula ndi Jacky, amene anali kukhalamo mongoyembekezera. Zotsatirapo zake? Onse atatuwo anakhala Mboni ndipo anapeza ntchito ina imene inawalola kuchita zinthu zauzimu mokwanira.

Kuletsa Namondwe

Posachedwapa, atolankhani ena ku France anafalitsa kuti Mboni za Yehova n’chipembedzo champatuko, choopsa. Mu 1996, Mboni zinagaŵira ndi mtima wonse mathirakiti a chidziŵitso chapadera oposa mamiliyoni asanu ndi anayi a mutu wakuti Zimene Muyenera Kudziŵa za Mboni za Yehova. Zotsatirapo zake zinali zosangalatsa.

Zinayesetsa kugaŵira wina aliyense. Akuluakulu ena a boma anayamikira kwambiri Mboni. Khansala wa tauni ina analemba kuti: “Mboni za Yehova zachita bwino kugaŵa thirakiti limeneli. Lathetsa bodza.” Dokotala wina anati: “Ndakhala ndikuyembekeza kumva zimenezi kwa nthaŵi yaitali!” Mwamuna wina wa m’Paris analemba kuti: “Ndinapeza mwamwayi thirakiti lakuti Zimene Muyenera Kudziŵa za Mboni za Yehova ndipo ndinaliŵerenga. Ndikufuna kudziŵa zambiri ndiponso kukhala ndi phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.” Mkazi wina analemba kuti: “Zikomo kwambiri chifukwa cha kuona mtima kwanu.” Mkazi wina wachikatolika anauza Mboni kuti: “Ha! Mwayankhadi mabodza ameneŵa!”

Mboni zachinyamata m’Paris zinapeza chimwemwe chapadera pa ndawala yolalikira imene anaikonza nthaŵi ya Masiku a Achinyamata Achikatolika Padziko Lonse mu 1997. Ngakhale kuti nyengo inali yotentha kwambiri, Mboni pafupifupi 2,500 zinalalikira nawo. Kwamasiku ochepa chabe, anagaŵira mabulosha 18,000 a Buku la Anthu Onse kwa achinyamata ochokera mbali zonse za dziko lapansi. Ndawalayi inachitira umboni dzina la Yehova ndi kufesa mbewu zachoonadi. Ndiponso, inalimbikitsa Mboni zachinyamata. Mlongo wina wachitsikana, amene anadukiza tchuti chake kuti alalikire mokwanira pandawala yapaderayi, analemba kuti: “Yehova ali ndi anthu achimwemwe padziko lapansi amene amagwiritsa ntchito mphamvu zawo kutamanda dzina lake. Masiku opindulitsa aŵiri ameneŵa, anali amtengo wapatali kuposa masiku atchuti a moyo wonse! (Salmo 84:10)”

February 28, 1998, linali tsiku la 65 lokumbukira lamulo la Hitler loletsa Mboni za Yehova ku Germany. Mboni za ku France zinagwiritsa ntchito tsikulo kuonetsa kwa anthu onse vidiyo yakuti Jehovah’s Witnesses Stand Firm Against Nazi Assault, imene imafotokoza mwatsatanetsatane mmene anthu a Yehova anavutikira. Anaonetsa vidiyoyi m’maholo amene anachita lendi. Anagaŵa mapepala oitanira oposa mamiliyoni asanu ndi aŵiri. Olemba mbiri ndiponso anthu amene anavutika m’misasa yachibalo anapereka umboni wokhudza mtima. Anthu pafupifupi 5,000 anamvetsera m’Paris, kuphatikizapo anthu ambiri omwe sanali Mboni.

Ambiri ku Paris akuyamikira kuwala kwauzimu, ndipo ali okondwa kuti ofalitsa Ufumu akuwala kwambiri monga zounikira. Zili monga mmene Yesu ananenera kuti: “Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka.” (Mateyu 9:37) Mzimu wa Mboni za Yehova wofunitsitsa kugonjetsa zinthu zolepheretsa kulalikira mumzindawu wachititsa kuti Paris ukhale Mzinda wa Kuunika kwamtundu wina​—kolemekeza Yehova.

[Chithunzi patsamba 9]

Holo ya Mzinda

[Chithunzi patsamba 9]

Opera Garnier

[Chithunzi patsamba 9]

Nyumba yosungiramo zinthu zochititsa chidwi ya Louvre

[Zithunzi patsamba 10]

Kuuza anthu otanganidwa uthenga wa Baibulo kulikonse kumene angapezeke