Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi Yobu anavutika kwa nthaŵi yaitali motani?

Anthu ena amaganiza kuti Yobu anamuyesa kwa zaka zambiri. Koma buku lake silinena kuti anavutika kwa nthaŵi yaitali motero.

Mayeso oyamba a Yobu, kumwalira kwa ana ndi antchito ake ndi kuwonongeka kwa katundu, akuoneka kuti anachitika m’nthaŵi yochepa. Timaŵerenga kuti: ‘Tsono panali tsiku loti ana [a Yobu] aamuna ndi aakazi analinkudya ndi kumwa vinyo m’nyumba ya mkulu wawo.’ Yobu analandira mauthenga otsatizana akuti chuma chake​—ng’ombe, abulu, nkhosa, ngamila​—zawonongeka ndipo antchito ake amene anali kusamalira nyamazo, amwalira. Mwachionekere, zitangochitika zimenezi, Yobu anamva kuti ana ake aamuna ndi aakazi, amene “analinkudya ndi kumwa vinyo m’nyumba ya mkulu wawo,” amwalira. Zikuoneka kuti zonsezi zinachitika tsiku limodzi.​—Yobu 1:13-19.

Mayeso achiŵiri a Yobu ayenera kuti anatenga nthaŵi yaitali. Satana anaonekera pamaso pa Yehova ndi kunena kuti Yobu akanagonja ngati akanakhala kuti akuvutika​—thupi lake lenilenilo. Ndiyeno anam’kantha ndi “zilonda zowawa, kuyambira ku phazi lake kufikira pakati pamutu pake.” Mwina panapita kanthaŵi kuti matendaŵa afalikire thupi lonse. Ndipo mwachionekere, mwina panapita nthaŵi kuti anthu amene anaoneka ngati om’sangalatsa amve za “choipa ichi chonse” ndi kudza kwa iye.​—Yobu 2:3-11.

Elifazi anachokera ku Temani m’dziko la Edomu, ndipo Zofari anachokera kudera la kumpoto chakumadzulo kwa Arabiya. Motero, kwawoko kunali kufupi ndi kwawo kwa Yobu ku Uzi, kumene kunali kumpoto kwa Arabiya. Koma Bilidadi anali Msuki, ndipo zikudziŵika kuti anthu a mtundu wake anali kukhala m’mbali mwa mtsinje wa Firate. Ngati iye anali kwawo panthaŵi imeneyi, mwina panapita milungu kapena miyezi kuti amve za vuto la Yobu ndi kupita ku Uzi. Komabe, n’zotheka kuti onse atatuŵa anali kufupi ndi kwawo kwa Yobu pamene iye anayamba kuvutika. Mulimonse mmene zinalili, anzake atatuŵa atafika, “[a]nakhala pansi pamodzi naye panthaka masiku asanu ndi aŵiri usana ndi usiku” osalankhula.​—Yobu 2:12, 13.

Ndiyeno panafika mayeso a Yobu omaliza, amene anawafotokoza m’machaputala ambiri a bukuli. Panali kutsutsana kapena kulankhula kotsatizanatsatizana kwa amene anaoneka ngati om’sangalatsawo, ndipo nthaŵi zambiri Yobu anali kuwayankha. Zimenezo zitatha, Elihu wachinyamata anam’dzudzula, ndipo Yehova anamuwongolera Yobu kuchokera kumwamba.​—Yobu 32:1-6; 38:1; 40:1-6; 42:1.

Choncho, kuvutika kwa Yobu ndi mapeto ake ziyenera kuti zinachitika kwa miyezi ingapo, mwina chaka sichinathe. Mwina mukudziŵa kuchokera pa zimene munakumana nazo kuti mayesero ovuta amaoneka ngati sadzatha. Koma tiyenera kukumbukira kuti amatha, monga anachitira a Yobu. Ngakhale atatiyesa kwa nthaŵi yaitali motani, tiyenera kukumbukira kuti Mulungu adzatithandiza, monga momwe mawu amene anawauzira amanenera kuti: “Chisautso chathu chopepuka cha kanthaŵi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero.” (2 Akorinto 4:17) Mtumwi Petro analemba kuti: “Mulungu wa chisomo chonse, amene anakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Kristu, mutamva zowawa kanthaŵi, adzafikitsa inu opanda chirema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.”​—1 Petro 5:10.