Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Mungapambanire Paunyamata Wanu

Mmene Mungapambanire Paunyamata Wanu

Mmene Mungapambanire Paunyamata Wanu

ANTHU am’dziko lina ku Ulaya, anawafunsa kusankha chimodzi mwa zinthu zitatu izi: kukongola, kulemera, kapena unyamata. Anthu ambiri anasankha unyamata. Inde, anthu amisinkhu yosiyanasiyana amaganiza kuti unyamata ndiyo nthaŵi yapadera kwambiri m’moyo. Ndipo aliyense amafuna kuti achinyamata asinthe mopambana kuchoka paubwana kufika pauchikulire. Koma motani?

Kodi Baibulo lingathandize? Mwachionekere yankho ndi lakuti, Inde! Tiyeni tipende mbali ziŵiri zimene Mawu a Mulungu angakhale othandiza mwapadera kwa achinyamata, mwinanso othandiza kwambiri achinyamatawo kuposa anthu a msinkhu wina uliwonse.

Kukhala Bwino ndi Anthu Ena

Jugend 2000 ndi lipoti la kafukufuku wamkulu wa maganizo, miyezo, ndi makhalidwe a achinyamata oposa 5,000 ku Germany. Kafukufukuyo anavumbula kuti achinyamata akamachita zinthu zosiyanasiyana panthaŵi yopuma​—monga kumvetsera nyimbo, kuchita maseŵero olimbitsa thupi, kapena kungowongola miyendo​—pafupifupi nthaŵi zonse amakhala ndi anthu ena. Achinyamata amafuna kukhala limodzi ndi anzawo mwina kuposa mmene anthu a misinkhu ina amachitira. N’chifukwa chake, chinsinsi china chakuti wachinyamata apambane ndicho kukhala bwino ndi ena.

Koma nthaŵi zambiri n’kovuta kukhala bwino ndi ena. Inde, anyamata ndi atsikana amavomereza kuti nthaŵi zambiri kukhala bwino ndi anthu kumawavuta. Baibulo lingathandize kwambiri pankhani imeneyi. Mawu a Mulungu ali ndi malangizo abwino othandiza kuti achinyamata akhale ndi ubale woyenera. Kodi Baibulo limati bwanji?

Mfundo yofunika kwambiri yothandiza pakukhala bwino ndi anthu imatchedwa Mfundo Yaikulu ya Makhalidwe. Mfundoyi imati: “Zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.” Kulemekeza anthu ena ndi kuwachitira chifundo kumawalimbikitsa kuti nawonso akuchitireni chimodzimodzi. Khalidwe lachifundo lingachepetse mikangano ndi kuvutika maganizo. Ngati anthu adziŵa kuti mumaganizira ena, mosakayika adzakukondani ndi kukulemekezani. Kodi sizikusangalatsani ngati ena akukukondani?​—Mateyu 7:12.

Baibulo likukulangizani kuti ‘mukonde mnzanu monga mudzikonda inu mwini.’ Muyenera kudzikonda mwa kudzisamalira ndi kudzilemekeza moyenera, osati mopambanitsa kapena osadzilemekeza n’komwe. Kodi n’chifukwa chiyani zimenezi n’zothandiza? N’chifukwa chakuti ngati simudzilemekeza nokha, mwina mungasulize ena mopambanitsa, zimene zimawononga ubale wabwino. Koma kudzilemekeza moyenera ndi maziko amene mungamangepo ubwenzi wolimba.​—Mateyu 22:39.

Ubwenzi ukayamba, nonse aŵiri mufunika kuulimbitsa. Muyenera kukhala wosangalala kupatula nthaŵi yolimbitsa ubwenziwo, popeza “kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” Mtundu wina wa kupatsa ndiwo kukhululuka, kumene kumaphatikizapo kunyalanyaza zolakwa zazing’ono ndi kusayembekezera kuti winayo azichita zangwiro zokhazokha. Baibulo limatiuza kuti: “Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse.” Inde, “monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.” Ngati mnzanu akuuzani zofooka zanu zina, kodi mumachita bwanji? Taganizirani malangizo othandiza awa a m’Baibulo: “Usakangaze mumtima mwako kukwiya,” popeza “kulasa kwa bwenzi kuli kokhulupirika.” Kodi si zoona kuti mabwenzi amasonkhezera mmene mukuganizira, kulankhula, ndiponso makhalidwe anu? N’chifukwa chake Baibulo limachenjeza kuti: “Mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” Koma “ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru.”​—Machitidwe 20:35; Afilipi 4:5; Aroma 12:17, 18; Mlaliki 7:9; Miyambo 13:20; 27:6; 1 Akorinto 15:33.

Marco akuimira anyamata ndi atsikana ambiri ponena kuti: “Mfundo za m’Baibulo n’zothandiza kwambiri kuti munthu ukhale bwino ndi ena. Anthu ena amene ndikuwadziŵa ndi odzikonda ndipo amangochita zimene zingapindulitse iwo okha basi. Baibulo limatiphunzitsa kuti tisamangodziganizira tokha, koma tiziganiziranso anthu ena. Malinga ndi mmene ndikuonera, imeneyi ndi njira yabwino kwambiri yothandiza kuti tikhale bwino ndi anthu.”

Zimene achinyamata onga Marco aphunzira m’Baibulo zimawathandiza muunyamata wawo ndiponso zaka zawo zam’tsogolo. Ndipo pankhani ya m’tsogolo, tikupezanso mmene Baibulo limathandizira achinyamata mwapadera.

Kudera Nkhaŵa za M’tsogolo

Achinyamata ambiri amafunitsitsa kudziŵa zambiri. Amafuna kudziŵa zomwe zikuchitika ndi zifukwa zake, mwina kuposa mmene anthu a misinkhu ina amachitira. Ndipo Baibulo, kuposa buku lina lililonse, limafotokoza chifukwa chake dziko lili motere ndiponso limatiuza zimene tikuyembekezera m’tsogolo. Izi n’zimenetu achinyamata amafuna kudziŵa. Tikutsimikiza bwanji?

Ngakhale kuti ambiri amakhulupirira kuti achinyamata sasamala kwenikweni za m’tsogolo, ofufuza ena apeza kuti sizili choncho kwenikweni. Anapeza kuti achinyamata nthaŵi zambiri amayang’anitsitsa zimene zikuchitika, ndiyeno amayesa kutanthauzira mwa okha mmene zinthu zidzakhalira m’tsogolo. Umboni wa zimenezi ndi wakuti “nthaŵi zambiri” kapena “nthaŵi zonse,” anyamata ndi atsikana atatu mwa anayi alionse amaganiza za m’tsogolo. Ngakhale kuti achinyamata nthaŵi zambiri amaganiza kuti m’tsogolo zinthu zidzakhala bwino, ambiri amada nkhaŵa akamaganiza za m’tsogolo.

N’chifukwa chiyani amada nkhaŵa? Pakalipano, achinyamata ambiri ali kale ndi vuto la upandu, chiwawa, ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Akuda nkhaŵa ngati angapeze ntchito yokhazikika m’dziko lampikisano lino. Amaona kuti ali pampanipani wakuti akhoze ndi magiredi abwino kusukulu kapena kukhala wochita bwino kwambiri pantchito. Mtsikana wina wa zaka 17 anadandaula kuti: “Tikukhala m’moyo wa dziŵa zako. Aliyense angochita zimene akufuna. Munthu ufunika kutsimikizira zimene ungathedi kuchita, ndipo zimenezi zimandivutitsa maganizo.” Mnyamata wina wa zaka 22 anati: “Anthu ochita bwino moyo umawayendera bwino ndipo amakhala mosangalala. Anthu atsoka, amene pazifukwa zosiyanasiyana sangathe kuchita bwino mofanana ndi anzawo, amangotsalira m’mbuyo.” Kodi n’chifukwa chiyani pali kupikisana kotereku? Kodi ndi mmene tizikhalira mpaka kalekale?

Kufotokoza Molondola

Achinyamata akamavutika maganizo ndi kuda nkhaŵa poona mmene anthu akukhalira, akugwirizana ndi Baibulo, kaya akudziŵa kapena sakudziŵa. Mawu a Mulungu amanena kuti “moyo wa dziŵa zako” wamakonowu ndi chizindikiro cha nthaŵi ino yamapeto. Polembera mnyamata wina dzina lake Timoteo, Mtumwi Paulo anafotokoza za nthaŵi yathu ino kuti: “Zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa.” N’chifukwa chiyani zili nthaŵi zoŵaŵitsa? Monga momwe Paulo analembera, chifukwa chake n’chakuti “anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, . . . osayamika, osayera mtima, . . . aukali.” Kodi sikufotokoza kolondola kumeneko malinga ndi mmene ambiri akuchitira masiku ano?​—2 Timoteo 3:1-3.

Baibulo linanena kuti nthaŵi zoŵaŵitsazi zidzafika ‘m’masiku otsiriza,’ kusintha kwakukulu kusanafike pa anthu onse. Kusintha kumeneku kudzakhudza aliyense, mwana kapena mkulu. Kodi n’kusintha kotani? Boma lakumwamba posachedwapa liyamba kulamulira anthu onse, ndipo nzika zake kulikonse zidzakondwera ndi “mtendere wochuluka.” “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” Nkhaŵa ndi mantha zidzakhala za makedzana.​—Salmo 37:11, 29.

Baibulo lokha ndilo limathandiza kudziŵa za m’tsogolo. Wachinyamata akadziŵa zimene zidzachitika zaka zingapo m’tsogolo, amakonzekera pasadakhale ndipo amakhala wotetezeka ndi kusamala kwambiri moyo wake. Kudziŵa zimenezi kumachepetsa kuvutika maganizo ndi nkhaŵa. Motero, Baibulo limafotokoza zinthu zapadera zimene achinyamata akufuna​—kumvetsa mmene anthu akukhalira ndi kudziŵa za m’tsogolo.

Kupambana Paunyamata

Kodi m’madziŵa bwanji kuti uku n’kupambana paunyamata? Kodi ndi mwakukhala ndi maphunziro apamwamba, kulemera, ndi kukhala ndi mabwenzi ambiri? Ambiri angaganize choncho. Zaka zaunyamata ziyenera kuthandiza munthu kukhala ndi chiyambi chabwino cha moyo wam’tsogolo. M’mawu ena, kupambana paunyamata kungasonyeze zimene zidzatsatirapo m’tsogolo.

Monga taonera, Baibulo lingathandize wachinyamata kuchititsa zaka zake zaunyamatazo kukhala zopambana. Achinyamata ambiri apeza kale kuti zimenezi n’zoonadi. Amaŵerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse ndipo amagwiritsa ntchito zimene akuphunzira. (Onani kamutu kakuti “Langizo Lothandiza Lochokera kwa Mtumiki Wachinyamata wa Yehova,” patsamba 6.) Ndithudi, Baibulo ndi buku la achinyamata lerolino chifukwa lingawathandize kuti ‘akhale oyenera, okonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.’​—2 Timoteo 3:16, 17.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

Chinsinsi chimodzi chakuti wachinyamata apambane ndicho kukhala bwino ndi ena

[Mawu Otsindika patsamba 6]

Achinyamata amafuna kudziŵa zomwe zikuchitika ndi zifukwa zake, mwina kuposa mmene anthu amisinkhu ina amachitira

[Bokosi pamasamba 6, 7]

Langizo Lothandiza Lochokera kwa Mtumiki Wachinyamata wa Yehova

Alexander ali ndi zaka 19. Anabadwira m’banja la Mboni za Yehova, ndipo amatsatira ndi mtima wonse zimene akukhulupirira. Koma nthaŵi zina sizinali choncho. Alexander akufotokoza kuti:

“Mwina mukhoza kudabwa kuti ndinali kusonkhana ndi Mboni za Yehova monga mnyamata wosabatizidwa kwa zaka zoposa zisanu ndi ziŵiri. Komatu panthaŵi yonseyi, sindinali kulambira ndi mtima wonse. Ndinali kungochita mwamwambo chabe. Ndikuganiza kuti sindinathe kudzipenda ndekha moona mtima.”

Ndiyeno maganizo a Alexander anasintha. Akupitiriza kuti:

“Makolo anga ndi mabwenzi a mumpingo anali kundilimbikitsa kuti ndiziŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, kuti ndim’dziŵe bwino Yehova. Kenaka, ndinaganiza kuti ndiyese kuchita zimenezo. Ndinachepetsa kuonera wailesi yakanema ndipo ndinakonza ndandanda yoŵerenga Baibulo m’maŵa uliwonse. Ndiyeno ndinayamba kulidziŵa bwino Baibulo. Ndinaona mmene lingandithandizire ineyo pandekha. Ndipo chofunika kwambiri kuposa zonsezi chinali chakuti ndinadziŵa kuti Yehova akufuna kuti ndim’dziŵe. Nditatsatira zimenezo, ubale wanga ndi iye unayamba kukula, ndipo ndinapeza mabwenzi abwino mumpingo. Baibulo lasinthadi moyo wanga! Ndikulimbikitsa mtumiki wa Yehova wachinyamata aliyense kuti aziŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku.”

Pali achinyamata mamiliyoni ambiri padziko lonse amene akusonkhana ndi Mboni za Yehova. Kodi inunso mumasonkhana nawo? Kodi mukufuna kupindula mwa kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse? Bwanji osatsatira chitsanzo cha Alexander? Chepetsani kuchita zinthu zosafunika kwenikweni. Khalani ndi chizoloŵezi cha kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku. Ndithudi, mudzapindula kwambiri.