Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Musasiye Kuchita Zabwino

Musasiye Kuchita Zabwino

Musasiye Kuchita Zabwino

“Tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.”​—AGALATIYA 6:9.

1, 2. (a) N’chifukwa chiyani kupirira kuli kofunika kuti titumikire Mulungu? (b) Kodi Abrahamu anasonyeza motani kupirira, ndipo chinam’thandiza n’chiyani?

MONGA Mboni za Yehova, timakondwera kwambiri kuchita chifuniro cha Mulungu. Timapezanso mpumulo posenza “goli” lokhala ophunzira. (Mateyu 11:29) Komabe, kutumikira Yehova ndi Kristu sikwapafupi nthaŵi zonse. Mtumwi Paulo ananena mfundo imeneyi momveka bwino polimbikitsa Akristu anzake kuti: “Chikusoŵani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano.” (Ahebri 10:36) Kupirira n’kofunika kwambiri chifukwa chakuti kutumikira Mulungu n’kovuta.

2 Ndithudi, moyo wa Abrahamu ndi umboni wotsimikiza zimenezi. Nthaŵi zambiri anakumana ndi zinthu zovuta kusankha ndiponso zothetsa nzeru. Kum’lamula kuti asiye moyo wosangalatsa wa mumzinda wa Uri chinali chiyambi chabe. Pasanapite nthaŵi yaitali, anavutika ndi njala, kudana ndi anthu oyandikana nawo, kufuna kum’landa mkazi, kukangana ndi achibale ake ena, ndiponso nkhondo yoopsa. Komabe ziyeso zazikulu zinali m’tsogolo. Abrahamu sanasiye kuchita zabwino. Zimenezi n’zochititsa chidwi kwambiri makamaka tikaganizira kuti iye analibe Mawu a Mulungu athunthu monga ifeyo. Komabe, mosakayika anadziŵa ulosi woyamba umene Mulungu anati: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.” (Genesis 3:15) Popeza kuti Mbewuyo inali kudzachokera mwa Abrahamu, mwachibadwa anali kudzakhala mdani wa Satana. Kuzindikira mfundo imeneyi mosakayika kunam’thandiza kupirira ziyeso zake mokondwera.

3. (a) N’chifukwa chiyani anthu a Yehova lerolino ayenera kuyembekezera masautso? (b) Kodi Agalatiya 6:9 akutilimbikitsa chiyani?

3 Anthunso a Yehova lerolino ayenera kuyembekezera masautso. (1 Petro 1:6, 7) Chivumbulutso 12:17 amatichenjeza kuti Satana ‘akuchita nkhondo ndi otsalira odzozedwa. Satana amakwiyiranso a “nkhosa zina” chifukwa chakuti iwo amagwirizana kwambiri ndi odzozedwa. (Yohane 10:16) Kuwonjezera pa kutsutsidwa pochita utumiki wawo wothandiza anthu, Akristu angakumanenso ndi ziyeso zina zothetsa nzeru pa moyo wawo. Paulo akutilimbikitsa kuti: “Tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.” (Agalatiya 6:9) Inde, ngakhale kuti cholinga cha Satana ndi kuthetsa chikhulupiriro chathu, tiyenera kulimbana naye kwambiri, ndi kukhalabe ndi chikhulupiriro cholimba. (1 Petro 5:8, 9) Kodi zotsatira za chikhulupiriro chathu n’zotani? Yakobo 1:2, 3 akunena kuti: “Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m’mene mukugwa m’mayesero a mitundumitundu; pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro.”

Mazunzo Achindunji

4. Kodi Satana wagwiritsira ntchito motani mazunzo poyesa kuthetsa chikhulupiriro cha anthu a Mulungu?

4 Ndithudi moyo wa Abrahamu ukusonyeza “mayesero osiyanasiyana” omwe Mkristu angakumane nawo lerolino. Mwachitsanzo, asilikali a ku Sinara atamenya nkhondo, Abrahamu anayenera kuchitapo kanthu. (Genesis 4:11-16) N’zosadabwitsa kuti Satana akupitirizabe kugwiritsa ntchito mazunzo achindunji. Kuchokera pamene nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse inatha, maboma a mayiko ambiri anatseka ntchito yophunzitsa yachikristu ya Mboni za Yehova. Yearbook ya Mboni za Yehova ya 2001 imasimba za Akristu a ku Angola amene anapirira ziwawa zomwe adani anali kuwachitira. Chifukwa chodalira Yehova, abale athu m’mayiko ngati ameneŵa akana kwamtuwagalu kubwerera m’mbuyo! Iwo achitapo kanthu osati mwa kuchita ziwawa kapena kuukira, koma mwa kupitirizabe kulalikira mwanzeru.​—Mateyu 24:14.

5. Kodi Akristu achinyamata angazunzidwe motani kusukulu?

5 Komabe, mazunzo sakhala achiwawa nthaŵi zonse. Patapita nthaŵi, Abrahamu anakhala ndi ana aamuna aŵiri, Ismayeli ndi Isake. Genesis 21:8-12 amatiuza kuti nthaŵi ina Ismayeli ‘anali kuseka’ Isake. M’kalata yake yopita kwa Agalatiya, Paulo anasonyeza kuti kumeneku sikunali kuseka wamba chifukwa iye anati, Ismayeli anazunza Isake! (Agalatiya 4:29) Choncho, kusekedwa ndi anzathu akusukulu ndiponso kunyozedwa ndi otsutsa n’chizunzo ndithu. Mkristu wina wachinyamata dzina lake Ryan anakumbukira mazunzo amene anzake a m’kalasi ankam’chitira. Iye anati: “Mphindi 15 zomwe ndinkakhala m’basi popita ndi pochokera kusukulu zinkaoneka ngati maola ambiri chifukwa anzanga ankandinyoza. Ankanditentha ndi topanira mapepala tomwe ankatitenthetsa pa moto woyatsira ndudu.” N’chifukwa chiyani ankachita nkhanza zoterezi? “Chifukwa chakuti maphunziro amene ndinaphunzira kudzera m’gulu la Mulungu anandisiyanitsa ndi anzanga ena kusukuluko.” Komabe, makolo a Ryan anam’thandiza kuti apirire. Achinyamatanu, kodi mumabwerera m’mbuyo anzanu akamakusekani? Chonde, musasiye! Mukapirira mokhulupirika mudzaona kukwaniritsidwa kwa mawu a Yesu akuti: “Odala muli inu mmene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha Ine.”​—Mateyu 5:11.

Nkhaŵa za Tsiku ndi Tsiku

6. Kodi ndi zinthu ziti zomwe zingawononge unasi wa Akristu lerolino?

6 Ziyeso zambiri zomwe timakumana nazo masiku ano zimakhudza nkhaŵa za tsiku ndi tsiku. Abrahamu nayenso anapirira mikangano yomwe inabuka pakati pa abusa ake ndi abusa a mphwake Loti. (Genesis 13:5-7) N’chimodzimodzinso lerolino, kusiyana maganizo ndiponso kuchitirana nsanje pa zinthu zing’onozing’ono kungawononge unasi wathu komanso kusokoneza mtendere wampingo. ‘Pomwe pali kaduka ndi mikangano, pamenepo pali chisokonekero ndi chochita choipa chilichonse.’ (Yakobo 3:16) N’kofunikatu kwambiri kuti ifeyo tisalole kudzikuza kusokoneza mtendere wathu! Abrahamunso sanatero, koma anaika zofuna za ena patsogolo.​—1 Akorinto 13:5; Yakobo 3:17.

7. (a) Kodi Mkristu angatani ngati wakhumudwitsana ndi wokhulupirira mnzake? (b) Kodi Abrahamu anapereka motani chitsanzo chabwino posungabe unansi wabwino ndi ena?

7 Mtendere ungakhale wovuta kwambiri pamene tikuona kuti wokhulupirira mnzathu ndiye watichitira mopanda chilungamo. Miyambo 12:18 imati: “Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga; koma lilime la anzeru lilamitsa.” Mawu opanda pake, ngakhale atalankhulidwa popanda chifukwa angakhale opweteka kwambiri. Ndipo kupwetekako kumawonjezeka ngati tikudziŵa kuti anatinamizira kapena ndi miseche chabe. (Salmo 6:6, 7) Komabe Mkristu sangabwerere m’mbuyo chifukwa chokhumudwa. Ngati zimenezi ndizo zinakuchitikirani, yesetsani kuthetsa nkhaniyo pokambirana ndi wolakwayo moleza mtima. (Mateyu 5:23, 24; Aefeso 4:26) Khalani wokonzeka kukhululukira munthuyo. (Akolose 3:13) Kungoiŵala osasunga chakukhosi, kumatonthoza mtima komanso kubwezeretsa unansi wathu ndi mbale wathuyo. Abrahamu ayenera kuti anakhumudwitsana ndi Loti koma sanam’sungire chidani chilichonse. Inde, Abrahamu anathamanga kukateteza Loti ndi banja lake.​—Genesis 14:12-16.

Ziyeso Zodzibweretsera Tokha

8. (a) Kodi Akristu ‘angadzipyoze motani ndi zoŵaŵa zambiri’? (b) N’chifukwa chiyani Abrahamu anali kuona zinthu zakuthupi moyenera?

8 Ndithudi ziyeso zina timadzibweretsera tokha. Mwachitsanzo, Yesu analamula otsatira ake kuti: “Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziwononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba.” (Mateyu 6:19) Komabe, abale ena ‘adzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri’ mwa kuika zinthu zakuthupi patsogolo pa zinthu za Ufumu. (1 Timoteo 6:9, 10) Abrahamu anali wofunitsitsa kudzimana zinthu zabwino zakuthupi n’cholinga chofuna kukondweretsa Mulungu. “Ndi chikhulupiriro anakhala mlendo ku dziko la lonjezano, losati lake, nakhalira m’mahema pamodzi ndi Isake ndi Yakobo, oloŵa nyumba pamodzi ndi iye a lonjezano lomwe; pakuti analindirira mudzi wokhala nawo maziko, mmisiri wake ndi womanga wake ndiye Mulungu.” (Ahebri 11:9, 10) Chikhulupiriro cha “mudzi” wam’tsogolo kapena kuti boma la Mulungu chomwe Abrahamu anali nacho chinam’thandiza kusadalira chuma. Kodi sikwanzeru kuti ifenso tichite zomwezo?

9, 10. (a) Kodi mtima wofuna kutchuka ungabweretse chiyeso motani? (b) Kodi mbale lerolino angadzichepetse motani?

9 Talingalirani mbali inanso. Baibulo limalangiza motsindika kuti: “Ngati wina ayesa ali kanthu pokhala ali chabe, adzinyenga yekha.” (Agalatiya 6:3) Komanso timalimbikitsidwa kupeŵa mikangano, kapena kuchita zinthu monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima. (Afilipi 2:3) Ena amadzibweretsera ziyeso chifukwa cholephera kugwiritsa ntchito uphungu umenewu. Ena mosonkhezeredwa ndi mtima wofuna kutchuka m’malo mokhala ndi mtima wofuna kuchita “ntchito yabwino,” amagwa ulesi ndi kukhumudwa ngati sakuwapatsa maudindo mumpingo.​—1 Timoteo 3:1.

10 Abrahamu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pankhani ya kusadziganizira mopambanitsa. (Aroma 12:3) Atakumana ndi Melikizedeke, Abrahamu sanachite zinthu ngati kuti anali wapamwamba kuposa ena chifukwa chakuti Mulungu anamuyanja. M’malo mwake, anapereka chachikhumi kwa Melikizedeke pozindikira udindo wake wapamwamba monga wansembe. (Ahebri 7:4-7) Akristunso lerolino ayenera kufunitsitsa kukhala odzichepetsa osati kufuna malo apamwamba. (Luka 9:48) Ngati otsogolera mumpingo sakukupatsani maudindo ena ake, dzipendeni moona mtima kuti muone mbali zomwe mungawongolere pakhalidwe lanu kapenanso mmene mumachitira zinthu. M’malo mokhumudwa chifukwa cha maudindo amene mulibe, gwiritsani ntchito mokwanira udindo womwe muli nawo wothandiza ena kudziŵa Yehova. Inde, “dzichepetseni pansi pa dzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni.”​—1 Petro 5:6.

Kukhulupirira Zinthu Zosaoneka

11, 12. (a) N’chifukwa chiyani ena mumpingo angalephere kuona kufunika kokhala achangu? (b) Kodi Abrahamu anapereka motani chitsanzo chabwino pankhani ya kukhulupirira malonjezo a Mulungu?

11 Kuona ngati mapeto a dongosolo loipali la zinthu akuchedwa chingakhale chiyeso china. Monga momwe 2 Petro 3:12 amanenera, Akristu ‘akuyembekezera kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu.’ Komabe, ambiri ayembekezera “tsiku” limeneli kwa zaka makumi ambiri. Mapeto ake, ena angabwerere m’mbuyo ndi kulephera kuona kufunika kokhala achangu.

12 Pamenepanso, lingalirani chitsanzo cha Abrahamu. Anakhulupirira malonjezo a Mulungu pa moyo wake wonse ngakhale kuti zinali zosatheka kuti onsewo akwaniritsidwe iye ali moyo. N’zoona kuti anakhala ndi moyo nthaŵi yaitali kwakuti anatha kuona mwana wake Isake atakula. Koma panali kudzatenga zaka mazana ambiri kuti mbewu ya Abrahamu idzachuluke ngati “nyenyezi za kumwamba” kapena ngati “mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.” (Genesis 22:17) Komabe, Abrahamu sanakhumudwe kapena kubwerera mmbuyo. N’chifukwa chake mtumwi Paulo anasimba za Abrahamu ndi makolo ena akale kuti: “Iwo onse adamwalira m’chikhulupiriro, osalandira malonjezano, komatu adawaona ndi kuwalankhula kutali, navomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko.”​—Ahebri 11:13.

13. (a) Kodi Akristu lerolino ali ngati “alendo” motani? (b) N’chifukwa chiyani Yehova adzathetsa dongosolo la zinthu lilipoli?

13 Ngati Abrahamu anaika mtima kwambiri pamalonjezo amene anali kudzakwaniritsidwa nyengo yaitali m’tsogolo, nanga bwanji ifeyo amene malonjezowo adzakwaniritsidwa posachedwapa! Monga Abrahamu, tiyenera kudziona monga alendo m’dziko la Satanali, tikumakana kuloŵerera moyo wosadziletsa wadzikoli. Mwachibadwa, timalakalaka “chitsiriziro cha zinthu zonse” chitafika osati kukhala pafupi chabe. (1 Petro 4:7) N’kutheka kuti mwina tikudwala matenda aakulu kapena kuvutika kwambiri kupeza ndalama. Komabe, tikumbukire kuti Yehova abweretsa mapeto osati kokha chifukwa choti atiwombole ku mavuto athu, komanso kuti ayeretse dzina lake. (Ezekieli 36:23; Mateyu 6:9, 10) Mapeto adzafika osati panthaŵi yomwe tikufuna koma panthaŵi yogwirizana ndi zifuno za Yehova.

14. Kodi kuleza mtima kwa Mulungu kumapindulitsa Akristu motani lerolino?

14 Kumbukiraninso kuti, “Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.” (2 Petro 3:9) Zindikirani kuti Mulungu ‘akuleza mtima ndi inu,’ a mumpingo wachikristu. Mwachionekere, ena a ife tifunikira nthaŵi kuti tisinthe ndi kuwongolera zina ndi zina kuti ‘tikapezedwe ndi Iye mumtendere, opanda banga ndi opanga chirema.’ (2 Petro 3:14) Choncho kodi sitiyenera kuyamikira kuti Mulungu waleza mtima motere?

Mmene Tingapezere Chimwemwe Ngakhale Patakhala Zopinga

15. Kodi Yesu anatha bwanji kukhalabe wachimwemwe nthaŵi zonse, nanga kutsanzira chitsanzo chake kumapindulitsa motani Akristu lerolino?

15 Moyo wa Abrahamu umaphunzitsa Akristu zinthu zambiri lerolino. Anasonyeza osati chikhulupiriro chokha komanso kuleza mtima, kuchenjera, kulimba mtima, ndi chikondi chenicheni. Anaika kulambira Yehova patsogolo m’moyo wake. Komabe, kumbukirani kuti chitsanzo chachikulu koposa chofunika kutsanzira n’cha Yesu Kristu. Iyenso anakumana ndi ziyeso zambiri, koma anakhalabe wachimwemwe nthaŵi zonse. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti anaika maganizo ake pa chiyembekezo cha zinthu za m’tsogolo. (Ahebri 12:2, 3) N’chifukwa chake Paulo anapemphera kuti: ‘Ndipo Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake, monga wa Kristu Yesu.’ (Aroma 15:5) Titakhala ndi mtima wabwino titha kupeza chimwemwe ngakhale Satana atatiikira zopinga kutsogolo.

16. Kodi tingatani ngati mavuto athu akuoneka aakulu kwambiri?

16 Ngati mavuto akuoneka aakulu kwambiri, kumbukirani kuti monga Yehova anakonda Abrahamu, amakondanso inu. Amafuna kuti mupambane. (Afilipi 1:6) Khulupirirani kwambiri kuti Yehova “sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.” (1 Akorinto 10:13) Kulitsani chizoloŵezi choŵerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku. (Salmo 1:2) Limbikirani kupemphera kuti Yehova akuthandizeni kupirira. (Afilipi 4:6) Iye ‘adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akum’pempha Iye’ (Luka 11:13) Gwiritsani ntchito mokwanira zofalitsa zofotokoza Baibulo zomwe Yehova wapereka kuti zikuthandizeni kukhalabe amoyo mwauzimu. Komanso, pemphani abale kuti akuthandizeni. (1 Petro 2:17) Pitani kumisonkhano yachikristu mokhulupirika chifukwa kumeneko mukalimbikitsidwa kuti muthe kupirira. (Ahebri 10:24, 25) Kondwerani podziŵa kuti kupirira kwanu kumachititsa Mulungu kukuyanjani ndiponso kumakondweretsa mtima wake!​—Miyambo 27:11; Aroma 5:3-5.

17. N’chifukwa chiyani Akristu sataya mtima?

17 Mulungu anakonda Abrahamu monga bwenzi lake. (Yakobo 2:23) Ngakhale zinali choncho, moyo wa Abrahamu unali ndi ziyeso komanso mavuto osautsa kwambiri. Choncho, Akristu amayembekezera zomwezo m’masiku oipa “otsiriza” ano. Ndiponsotu Baibulo limatichenjeza kuti “anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire.” (2 Timoteo 3:1, 13) M’malo motaya mtima, zindikirani kuti mavuto omwe tikukumana nawo ndi umboni wakuti dongosolo loipali la Satana lili pafupi kutha. Yesu akutikumbutsa kuti, “iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.” (Mateyu 24:13) Choncho ‘musaleme pakuchita zabwino!’ Tsanzirani Abrahamu ndi kukhala pakati pa anthu amene ‘akuloŵa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima.’​—Ahebri 6:12.

Kodi Mwazindikira?

• N’chifukwa chiyani anthu a Yehova lerolino ayenera kuyembekezera ziyeso ndi masautso?

• Kodi Satana angagwiritse ntchito mazunzo m’njira zotani?

• Kodi kusiyana maganizo pakati pa Akristu kungathetsedwe bwanji?

• Kodi kunyada ndi kudzikuza zingabweretse ziyeso motani?

• Kodi Abrahamu anapereka chitsanzo chabwino motani poyembekezera kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 26]

Achinyamata ambiri achikristu amazunzidwa ndi kunyozedwa ndi anzawo

[Chithunzi patsamba 29]

M’nthaŵi ya Abrahamu malonjezo a Mulungu anali kudzakwaniritsidwa ‘nthaŵi yaitali m’tsogolo,’ komabe Abrahamu analola malonjezowo kulamulira moyo wake