Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Funafunani Mtendere ndi Kuulondola’

‘Funafunani Mtendere ndi Kuulondola’

Funafunani Mtendere ndi Kuulondola’

“Ngati n’kutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.”​—AROMA 12:18.

1, 2. Kodi n’chifukwa chiyani mtendere umene anthu angaukhazikitse sungakhalitse?

TAYEREKEZANI nyumba imene ili ndi maziko osalimba, nsanamira zofumbwa, ndipo denga latsala pang’ono kugwa. Kodi mungakonde kukakhala m’nyumba imeneyo? Ayi ndithu. Ngakhale ataipaka penti yatsopano, siingasinthe. Ikhalabe yosalimba. Nthaŵi ina iliyonse igwa basi.

2 Mtendere uliwonse umene anthu angakhazikitse padziko lapansi lino uli ngati nyumba imeneyo. Amaumanga pamaziko osalimba​—malonjezo ndi nzeru za munthu “amene mulibe chipulumutso mwa iye.” (Salmo 146:3) M’mbiri yonse pakhala nkhondo zotsatizanatsatizana pakati pa mayiko, mitundu, ndi mafuko. N’zoona kuti nthaŵi zina mtendere wakhalapo kwakanthaŵi. Koma kodi ndi mtendere wanji? Ngati mayiko aŵiri amene anali kumenyana agwirizana zoti pakhale mtendere mwina chifukwa chakuti dziko linalo lagonja kapena onse aona kuti kupitiriza kumenyanako sikuwapindulira kanthu, ndi mtendere wanji umenewo? Udani, kukayikirana, ndi nsanje zimene zinayambitsa nkhondoyo zilipobe. Mtendere wapakamwa chabe umenewo, monga ‘penti yobisa’ udani, ndi wosakhalitsa.​—Ezekieli 13:10.

3. N’chifukwa chiyani mtendere wa anthu a Mulungu ndi wosiyana ndi mtendere wokhazikitsa anthu?

3 Komatu, mtendere weniweni ulipo m’dziko losakazika ndi nkhondoli. Kuti? Kwa otsatira mapazi a Yesu Kristu, Akristu enieni amene amamvera mawu a Yesu ndipo amayesetsa kutsanzira moyo wake. (1 Akorinto 11:1; 1 Petro 2:21) Mtendere umene Akristu oona a mafuko, malo, ndi mitundu yosiyanasiyana ali nawo ndi weniweni popeza umatheka ndi ubwenzi wamtendere umene iwo ali nawo ndi Mulungu. Ubwenzi umenewu wazikidwa pa kukhulupirira kwawo nsembe ya dipo ya Yesu Kristu. Mtendere wawowu ndi mphatso yochokera kwa Mulungu, si wochokera kwa anthu. (Aroma 15:33; Aefeso 6:23, 24) Aupeza chifukwa cha kugonjera kwawo “Kalonga wa mtendere,” Yesu Kristu, ndi kulambira Yehova, “Mulungu wa chikondi ndi mtendere.”​—Yesaya 9:6; 2 Akorinto 13:11.

4. Kodi Mkristu ‘amalondola’ bwanji mtendere?

4 Mtendere sumangobwera wokha kwa anthu opanda ungwiro. N’chifukwa chake Petro ananena kuti Mkristu aliyense “afunefune mtendere ndi kuulondola.” (1 Petro 3:11) Tingachite bwanji zimenezo? Ulosi wakale ukuyankha. Yehova ananena kupyolera mwa Yesaya kuti: “Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.” (Yesaya 54:13; Afilipi 4:9) Inde, anthu okhawo amene amamvera zimene Yehova amaphunzitsa ndi amene amakhala ndi mtendere weniweni. Ndiponso, mtendere ndi chipatso cha mzimu woyera wa Mulungu pamodzi ndi “chikondi, chimwemwe, . . . kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.” (Agalatiya 5:22, 23) Munthu wopanda chikondi, wosoŵa chimwemwe, wosaleza mtima, wopanda chifundo, woipa, wosakhulupirika, waukali, kapena wosadziletsa, sangakhale ndi mtendere.

‘Kukhala ndi Mtendere ndi Anthu Onse’

5, 6. (a) Malinga ndi Baibulo, kodi kuchita mtendere kumatanthauzanji? (b) Kodi Akristu ayenera kuyesetsa kukhala ndi mtendere ndi ndani?

5 Mtendere aumasulira kuti ndiwo khalidwe la bata. Tanthauzo limeneli lingagwire ntchito nthaŵi zambiri pamene kulibe nkhondo. Inde, ngakhale akufa ali pabata! Komabe, kuti munthu akhale ndi mtendere weniweni, ayenera kuulimbikitsa. Pa Ulaliki wake wa Paphiri, Yesu anati: “Odala ali akuchita mtendere; chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.” (Mateyu 5:9) Yesu anali kulankhula ndi anthu amene adzapeza mwayi wokhala ana a Mulungu auzimu ndi kulandira moyo wosafa kumwamba. (Yohane 1:12; Aroma 8:14-17) Ndiyeno m’kupita kwa nthaŵi, anthu onse okhulupirika amene sakuyembekeza kupita kumwamba adzasangalala ndi “ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Anthu ochita mtendere okha ndi amene angayembekeze zimenezo. Choncho, malinga ndi ganizo la Baibulo, kuchita mtendere kumatanthauza kulimbikitsa mtendere mwachangu, nthaŵi zina kukhazikitsa mtendere pamene panali udani.

6 Mukuganiza zimenezi, talingalirani zimene Paulo analangiza Aroma. Anati: “Ngati n’kutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.” (Aroma 12:18) Paulo sanali kuwauza Aroma kuti angokhala abata, ngakhale kuti zimenezo zikanathandiza. Anali kuwalimbikitsa kuti achite mtendere. Ndi yani? Ndi “anthu onse”​—a m’banja mwawo, Akristu anzawo, ngakhalenso amene sanali Akristu. Anawalimbikitsa Aroma kuti achite mtendere ndi anthu ena ‘monga momwe akanakhoza.’ Apatu sikuti anafuna kuti Aromawo alolere ndi kuleka zimene anali kukhulupirira n’cholinga choti pakhale mtendere. M’malo mokwiyitsa anthu mosayenera, anafunika kuwalankhula mwamtendere. Akristu anayenera kuchita zimenezi kwa anzawo mumpingo ndiponso kwa akunja. (Agalatiya 6:10) Mogwirizana ndi zimenezi, Paulo analemba kuti: “Nthaŵi zonse mutsatire chokoma, kwa anzanu, ndi kwa onse.”​—1 Atesalonika 5:15.

7, 8. Kodi ndi motani ndipo n’chifukwa chiyani Akristu amakhala ndi mtendere ndi anthu omwe si Akristu?

7 Kodi tingakhale motani ndi mtendere ndi anthu amene si Mboni ndiponso mwina amene amatitsutsa? Njira imodzi ndiyo kupewa kudzionetsera kuti ndife abwino kuposa iwo. Mwachitsanzo, sikungakhale kuchita mtendere ngati tilankhula ndi munthu ndi mawu osuliza. Yehova wavumbula kuti adzalanga mabungwe ndi magulu a anthu, koma sanatiuze kuti tizikamba za munthu wina aliyense ngati kuti waweruzidwa kale. Inde, sitiweruza anthu, ngakhale adani athu. Paulo anamuuza Tito kuti alangize Akristu a ku Krete mmene angachitire ndi olamulira. Ndiyeno anamuuza kuti awakumbutse kuti “asachitire mwano munthu aliyense, asakhale andewu, akhale aulere, naonetsere chifatso chonse pa anthu onse.”​—Tito 3:1, 2.

8 Kukhala ndi mtendere ndi anthu omwe si Akristu kumathandiza kuti tiwauze choonadi. Inde, sitipanga maubwenzi amene “aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Komabe, tingakhale aulemu, ndipo tiyenera kulemekeza anthu onse ndi kuwachitira chifundo. Petro analemba kuti: “Mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m’mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m’tsiku la kuyang’anira.”​—1 Petro 2:12.

Kukhala ndi Mtendere Muutumiki

9, 10. Kodi Paulo anapereka chitsanzo chotani chochita mwamtendere ndi anthu osakhulupirira?

9 Akristu a zaka za zana loyamba anali olimba mtima. Sanaluluze uthenga wawo, ndipo anthu akawatsutsa, anali kutsimikiza mtima kumvera Mulungu monga wolamulira koposa kumvera anthu. (Machitidwe 4:29; 5:29) Komabe, anatha kusiyanitsa kulimba mtima ndi chipongwe. Taganizani mmene Paulo analankhulira pamene anali kufotokoza zimene anali kukhulupirira pamaso pa Mfumu Herode Agripa II. Mfumuyi inakwatira mlongo wake dzina lake Bernike. Komabe, Paulo sanafune kutengerapo mwayi wophunzitsa Agripa za makhalidwe abwino. M’malo mwake, anatsindika mfundo zimene onse anali kuzidziŵa. Anavomereza kuti Agripa anali katswiri wa miyambo ya Ayuda ndi kuti anakhulupirira aneneri.​—Machitidwe 26:2, 3, 27.

10 Kodi Paulo anali kungokometsa pakamwa ndi cholinga choti am’patse ufulu? Ayi. Paulo anatsatira malangizo amene iye yemwe ananena ndipo analankhula choonadi. Zonse zimene analankhula kwa Herode Agripa zinali zoona. (Aefeso 4:15) Koma Paulo anali wochita mtendere ndipo anali kudziŵa mmene angakhalire “zonse kwa anthu onse.” (1 Akorinto 9:22) Cholinga chake chinali chakuti ateteze ufulu wake wolalikira za Yesu. Monga mphunzitsi wogwira mtima, anayamba mwa kutchula zinthu zimene iye ndi Agripa anali kuzidziŵa. Motero Paulo anathandiza mfumu ya khalidwe loipayi kuti isamadane ndi Chikristu.​—Machitidwe 26:28-31.

11. Kodi tingauchite motani mtendere muutumiki wathu?

11 Kodi tingauchite motani mtendere muutumiki wathu? Monga Paulo, tizipeŵa kukangana. Inde, nthaŵi zina tiyenera ‘kulankhula mawu a Mulungu mopanda mantha,’ kuteteza chikhulupiriro chathu molimba mtima. (Afilipi 1:14) Koma nthaŵi zambiri cholinga chathu chachikulu ndicho kulalikira uthenga wabwino. (Mateyu 24:14) Munthu akadziŵa choonadi cha zolinga za Mulungu, amayamba kusiya zikhulupiriro za chipembedzo chonyenga ndipo amaleka kuchita zinthu zodetsa. Choncho, malinga ndi mmene tingathere, ndi bwino kutsindika zinthu zimene zingakhudze mtima anthu amene akutimvetsera, kuyamba ndi zinthu zimene tonse tikuzidziŵa. Tingakhale tikubwezera m’mbuyo ntchito ngati tikwiyitsa munthu amene tikanakhala kuti tam’lankhula mwaluso, mwina akanamvera uthenga wathu.​—2 Akorinto 6:3.

Kuchita Mtendere m’Banja

12. Kodi tingauchite motani mtendere m’banja?

12 Paulo ananena kuti anthu amene akuloŵa m’banja “adzakhala nacho chisautso m’thupi.” (1 Akorinto 7:28) Amakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Vuto lina n’lakuti okwatirana ena amasiyana maganizo nthaŵi ndi nthaŵi. Kodi ayenera kuchita motani akasiyana maganizo? Mwamtendere. Munthu wochita mtendere adzayesetsa kuti mkangano usakule. Motani? Choyamba, mwa kulamulira lilime lake. Tikagwiritsa ntchito kulankhula mawu achipongwe kapena otukwana, kachiŵalo kakang’ono kameneka kangakhaledi ‘choipa chotakataka, chodzala ndi ululu wakupha.’ (Yakobo 3:8) Munthu wochita mtendere amagwiritsa ntchito lilime lake kumangirira osati kupasula.​—Miyambo 12:18.

13, 14. Kodi tingasunge motani mtendere ngati talankhula molakwika kapena ngati tapsa mtima?

13 Monga anthu opanda ungwiro, tonsefe nthaŵi zina timalankhula mawu amene timamva nawo chisoni pambuyo pake. Zimenezi zikachitika, pepesani mofulumira​—kuti muchite mtendere. (Miyambo 19:11; Akolose 3:13) Musataye nthaŵi ndi “makani a mawu” ndiponso “makani opanda pake.” (1 Timoteo 6:4, 5) Musangoganiza za kupsa mtima kwa mnzanuyo, m’malo mwake yesani kumvetsa maganizo ake. Ngati wakulankhulani mwaukali, musabwezere. Kumbukirani kuti “mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo.”​—Miyambo 15:1.

14 Nthaŵi zina, mungafunike kuganizira malangizo a pa Miyambo 17:14 akuti: “Kupikisana kusanayambe tasiya makani.” Yesani kuganiza za nkhaniyo ngati kuti sinakukhudzeni. Pambuyo pake, mkwiyo ukatha, mwina mudzatha kuthetsa vutolo mwamtendere. Nthaŵi zina, mungafunike kupempha woyang’anira wachikristu wokhwima kuti akuthandizeni. Amuna achidziŵitso ndiponso achifundo ameneŵa angakulimbikitseni ngati mtendere m’banja wasokonezeka.​—Yesaya 32:1, 2.

Kuchita Mtendere Mumpingo

15. Malinga ndi kunena kwa Yakobo, kodi ndi mzimu wotani umene Akristu ena anali nawo, ndipo n’chifukwa chiyani mzimu umenewo uli wa “padziko,” wa “chifuniro chachibadwidwe,” ndiponso wa “ziwanda”?

15 N’zachisoni kuti Akristu ena a zaka za zana loyamba anali ndi mzimu wakaduka ndi kutetana​—zinthu zosagwirizana ndi mtendere. Yakobo anati: “Nzeru iyi, sindiyo yotsika kumwamba, komatu ili ya padziko, ya chifuniro chachibadwidwe, ya ziwanda. Pakuti pomwe pali kaduka ndi zotetana, pamenepo pali chisokonekero ndi chochita choipa chilichonse.” (Yakobo 3:14-16) Ena akuti liwu lachigiriki lomwe analimasulira kuti “zotetana” limatanthauza zolinga zadyera, kulimbirana udindo. N’koyeneradi kuti Yakobo anati nzeru imeneyi ndi “ya padziko, ya chifuniro chachibadwidwe, ya ziwanda.” M’mbiri yonse, olamulira a dziko achita zinthu motetana, kumenyana wina ndi mnzake ngati nyama zakuthengo. Ndithudi, kutetana ndi kwa “padziko” ndiponso “chifuniro chachibadwidwe.” Ndi kwa “ziwanda.” Amene anayamba kuonetsa khalidwe loipa limeneli ndi mngelo wokhumba kulamulira amene anadzipanga mdani wa Yehova Mulungu ndipo anakhala Satana, mtsogoleri wa ziwanda.

16. Kodi Akristu ena azaka za zana loyamba anaonetsa motani mzimu wonga wa Satana?

16 Yakobo analimbikitsa Akristu kuti asakhale ndi mzimu wotetana, chifukwa subweretsa mtendere. Analemba kuti: “Zichokera kuti nkhondo, zichokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizichokera ku zikhumbitso zanu zochita nkhondo m’ziwalo zanu?” (Yakobo 4:1) Pano, “zikhumbitso” zingakhale zikutanthauza kukhumba mwadyera zinthu zakuthupi kapena kukhumba kutchuka, ulamuliro, kapena mphamvu. Monga Satana, ena m’mipingo ayenera kuti anafuna kukhala apamwamba m’malo mokhala ‘aang’onong’ono’ monga momwe Yesu ananenera za ofuna kukhala otsatira ake. (Luka 9:48) Mzimu umenewo ungasoŵetse mtendere mumpingo.

17. Kodi Akristu lerolino angauchite motani mtendere mumpingo?

17 Lerolino, tiyeneranso kukana maganizo okonda chuma, kaduka, kapena kufunitsitsa udindo. Ngati ndifedi ochita mtendere, sitidzaipidwa ngati ena mumpingo ali ndi luso pazochita zina kuposa ife. Ndiponso, sitiwapeputsa pamaso pa ena mwa kukayikira zolinga zawo. Ngati tili ndi luso linalake losiririka, sitiligwiritsa ntchito kudzionetsera kuti ndife ofunika kuposa ena, kudziona ngati kuti mpingo ukuyenda bwino kokha chifukwa cha maluso ndi chidziŵitso chathu. Mzimu umenewo ungagaŵanitse anthu ndipo sungabweretse mtendere. Anthu ochita mtendere sadzitamandira ndi maluso awo koma amawagwiritsa ntchito modzichepetsa kutumikira abale awo ndi kulemekeza Yehova. Amazindikira kuti chimene chimadziŵikitsa Akristu oona ndi chikondi osati luso.​—Yohane 13:35; 1 Akorinto 13:1-3.

“Akapitawo a Mtendere”

18. Kodi akulu amaulimbikitsa motani mtendere pakati pawo?

18 Akulu mumpingo amatsogolera kuchita mtendere. Yehova ananeneratu za anthu ake kuti: “Ndidzakuikira akapitawo a mtendere, ndi oyang’anira ntchito a chilungamo.” (Yesaya 60:17) Mogwirizana ndi mawu aulosi ameneŵa, abusa achikristu amayesetsa kulimbikitsa mtendere pakati pawo ndiponso pakati pa nkhosa. Akulu angasunge mtendere pakati pawo mwa kuonetsa “nzeru yochokera kumwamba” yamtendere ndi yololera. (Yakobo 3:17) Popeza akulu mumpingo amasiyana chikhalidwe kumene anakulira ndiponso zimene akumana nazo pamoyo n’zosiyana, nthaŵi zina angasiyane maganizo pankhani zina. Kodi zikatere ndiye kuti alibe mtendere? Sizingakhale choncho ngati asamalira nkhaniyo moyenera. Anthu ochita mtendere amafotokoza maganizo awo modzichepetsa ndiyeno amamvetsera mwaulemu maganizo a ena. M’malo mongoumirira maganizo ake, munthu wochita mtendere amapenda maganizo a mbale wake mwapemphero. Ngati maganizo a winayo sakuswa mfundo yachikhalidwe ya m’Baibulo, bwanji osavomereza? Ngati ena sanagwirizane ndi maganizo ake, wochita mtendereyo amalolera ndi kuthandiza pazimene anthu ambiri asankha. Motero amasonyeza kuti ndi wofatsa. (1 Timoteo 3:2, 3) Woyang’anira wanzeru amadziŵa kuti kusungitsa mtendere n’kofunika kwambiri kuposa kuti zinthu zizichitika mogwirizana ndi mmene iye akufunira basi.

19. Kodi akulu amauchita motani mtendere mumpingo?

19 Akulu amalimbikitsa mtendere pakati pa nkhosa mwa kuzithandiza ndiponso mwa kupeŵa kuzisuliza mosayenera pa zoyesayesa zawo. Inde, nthaŵi zina ena angafunike kuwabweza. (Agalatiya 6:1) Komabe ntchito yaikulu ya oyang’anira achikristu sindiyo kupereka chilango. Amaziyamikira nkhosazo. Akulu achikondi amayesetsa kuona zabwino zimene ena akuchita. Oyang’anira amayamikira ntchito yaikulu imene Akristu anzawo akuchita, ndipo amadalira okhulupirira anzawowo kuti akuchita zonse zimene angathe.​—2 Akorinto 2:3, 4.

20. Kodi mpingo umapindula motani ngati anthu onse achita mtendere?

20 Motero, timayesetsa kukhala ndi mtendere, kapena kuti kuulimbikitsa m’banja lathu, mumpingo, ndiponso ndi anthu amene sali Akristu. Ngati tiyesetsa mwakhama kulimbikitsa mtendere, tidzathandiza kuti mpingo ukhale wachimwemwe. Ndiponso, tidzatetezedwa ndi kulimbikitsidwa m’njira zambiri, monga momwe tionere m’nkhani yotsatira.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi kuchita mtendere kumatanthauzanji?

• Kodi tingakhale bwanji akuchita mtendere kwa anthu omwe si Mboni?

• Kodi njira zina zolimbikitsira mtendere m’banja ndi ziti?

• Kodi akulu angalimbikitse motani mtendere mumpingo?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 9]

Ochita mtendere amapeŵa mzimu wodzionetsera

[Zithunzi patsamba 10]

Akristu amachita mtendere muutumiki, panyumba, ndi mumpingo