Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kale Tinali Mimbulu—Tsopano Ndife Nkhosa!

Kale Tinali Mimbulu—Tsopano Ndife Nkhosa!

Kale Tinali Mimbulu​—Tsopano Ndife Nkhosa!

Ine ndi Sakina tinali kukhala moyandikana tili aang’ono. Sakina anali wamkulu thupi ndiponso wamphamvu pamene ine ndinali wamng’ono ndi woonda. Tinali kukangana nthaŵi zambiri, moti tsiku lina tinatidzimulana modetsa nkhaŵa. Kuyambira tsiku limenelo, tinaleka kulankhulana ngakhale kupatsana moni. M’kupita kwa nthaŵi, tonse tinachoka pamalowo ndipo aliyense sankadziŵa kumene mnzake anali kukhala.

Mu 1994, ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndipo khalidwe langa linasintha pang’ono ndi pang’ono. Patapita zaka zinayi, ndinali pa msonkhano wapadera watsiku limodzi ku Bunjumbura, Burundi, ndipo ndinadabwa kukumana mwadzidzidzi ndi Sakina. Ndinasangalala kuti anafika pamsonkhanowu, komabe tinalonjerana momangika. Ndinadabwa kwambiri tsiku limenelo kumuona ali pagulu la anthu oti abatizidwe. Iyenso anali atasinthiratu. Sanalinso munthu wamphulupulu amene ndinali kukangana naye nthaŵi zambiri. Zinalitu zosangalatsa kumuona akusonyeza poyera kudzipatulira kwake kwa Mulungu mwa kubatizidwa m’madzi!

Atatuluka m’madzi, ndinathamanga kukam’kumbatira. Ndiyeno ndinam’nong’oneza kuti: “Kodi ukukumbukira mmene tinkamenyerana?” Anayankha kuti: “Inde, ndikukumbukira, koma n’zakale zimenezo. Panopa ndine munthu watsopano.”

Tonsefe ndife okondwa kuti tapeza choonadi cha Baibulo chimene chimagwirizanitsa. Ndiponso tili ndi chimwemwe kuti tasintha miyoyo yathu yonga mimbulu n’kukhala monga nkhosa za Mbusa Wamkulu, Yehova Mulungu. Ndithudi, choonadi cha Baibulo chimasintha miyoyo.