Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mtendere wa Kristu Ungachite Motani Ufumu M’mitima Yathu?

Kodi Mtendere wa Kristu Ungachite Motani Ufumu M’mitima Yathu?

Kodi Mtendere wa Kristu Ungachite Motani Ufumu M’mitima Yathu?

“Mtendere wa Kristu uchite ufumu m’mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m’thupi limodzi.”​—AKOLOSE 3:15.

1, 2. Kodi “mtendere wa Kristu” umachita motani ufumu mumtima wa Mkristu?

KUCHITA ufumu pa wina ndi mawu amene anthu ambiri sitifuna kuwamva, chifukwa amatichititsa kuganiza zoponderezana ndiponso zodyerana masuku pamutu. Motero, langizo la Paulo kwa Akristu anzake ku Kolose lakuti “Mtendere wa Kristu uchite ufumu m’mitima yanu,” mwina ena amaliona ngati losayenera. (Akolose 3:15) Kodi tilibe ufulu wosankha zimene tikufuna kuchita? N’kuloleranji chinthu china kapena munthu wina kuchita ufumu m’mitima yathu?

2 Paulo sanali kuwauza Akolose kuti ataye ufulu wawo wosankha zimene akufuna. Liwu lachigriki limene alimasulira kuti “kuchita ufumu” pa Akolose 3:15 likugwirizana ndi liwu loimira munthu wogamula maseŵero amene anali kupereka mphoto pa mipikisano ya nthaŵi imeneyo. Ochita maseŵero anali ndi ufulu ndithu malinga ndi malamulo a maseŵerowo, koma pomaliza, wogamula maseŵeroyo ndiye anali kusankha kuti amene watsatira malamulo ndi kuwina mpikisanowo ndi wakuti. Mofananamo, tili ndi ufulu wosankha zinthu pamoyo wathu, koma pamene tikutero, mtendere wa Kristu ukhale “wogamula” nthaŵi zonse. Kapena ukhale “mphamvu yolamulira” m’mitima yathu, malinga ndi mmene wotembenuza wina Edgar J. Goodspeed analimasulira liwuli.

3. Kodi “mtendere wa Kristu” n’chiyani?

3 Kodi “mtendere wa Kristu” n’chiyani? Ndiwo bata, mtendere wa mumtima, umene timaupeza tikakhala ophunzira a Yesu ndi kudziŵa kuti Yehova Mulungu ndi Mwana wake amatikonda ndipo amatiyanja. Pamene Yesu anali pafupi kuwasiya ophunzira ake, anawauza kuti: “Mtendere wanga ndikupatsani. . . . Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha.” (Yohane 14:27) Odzozedwa okhulupirika oimira ziwalo za thupi la Kristu akhala ndi mtendere umenewu kwa zaka pafupifupi 2,000, ndipo lerolino anzawo, a “nkhosa zina,” alinawonso. (Yohane 10:16) Mtendere umenewo uyenera kukhala mphamvu yolamulira m’mitima yathu. Tikayesedwa modetsa nkhaŵa, mtenderewu ungatithandize kuti mantha asatifoole kapena kuti tisadandaule mopitirira muyeso. Tiyeni tione mmene ungatithandizire ngati anthu atichitira mosalungama, tikakhala ndi nkhaŵa, ndiponso tikamaganiza kuti ndife opanda pake.

Anthu Akatichitira Mosalungama

4. (a) Kodi ndi motani mmene Yesu anadziŵira bwino za kusoŵeka kwa chilungamo? (b) Kodi Akristu achita motani pamene anthu awachitira mosalungama?

4 Mfumu Solomo inati: “Wina apweteka mnzake pom’lamulira.” (Mlaliki 8:9) Yesu anadziŵa bwino zimenezi. Pamene anali kumwamba, anaona mmene anthu nthaŵi zambiri anachitirana mosalungama wina ndi mnzake. Ali padziko lapansi, anachitidwa mosalungama kwambiri pamene anamuimba mlandu wochitira mwano Mulungu ndi kumupha ngati mpandu, pamene iye anali wosalakwa. (Mateyu 26:63-66; Marko 15:27) Lerolinonso kulibiretu chilungamo ndipo Akristu oona avutika mopitirira muyeso chifukwa ‘anthu a mitundu yonse akudana nawo.’ (Mateyu 24:9) Komabe, ngakhale kuti anavutika koopsa m’misasa yopherako anthu ya Nazi ndi m’misasa yachibalo ku Soviet Union, kuukiridwa ndi magulu a anthu achiwawa, kuwaimba milandu yonama, ndiponso kuwanamizira, mtendere wa Kristu wawathandiza kukhalabe olimba. Atsanzira Yesu, amene timaŵerenga za iye kuti: “Pochitidwa chipongwe sanabwezera chipongwe, pakumva zoŵaŵa, sanaopsa, koma anapereka mlandu kwa Iye woweruza kolungama.”​—1 Petro 2:23.

5. Tikamva nkhani yosonyeza ngati kuti wina mumpingo sanam’chitire chilungamo, kodi tiyenera choyamba kuganiza chiyani?

5 Pa ife tokha mwina tingaganize kuti munthu wina sanam’chitire chilungamo mumpingo wachikristu. Zikatere, mwina tingamve ngati Paulo, amene ananena kuti: “Akhumudwitsidwa ndani, wosatenthanso ine?” (2 Akorinto 11:29) Kodi tingachite bwanji? Tidzifunse kuti, ‘Kodi n’zoonadi kuti sanam’chitire chilungamo?’ Nthaŵi zambiri, zimakhala zoti sitikuidziŵa bwinobwino nkhani yonse. Mwinanso zingakhale zoti nkhaniyo yatikhudza kwambiri chabe chifukwa choti taimva kwa munthu amene akunena kuti akuidziŵa bwino. M’pake kuti Baibulo limati: “Wachibwana akhulupirira mawu onse.” (Miyambo 14:15) Motero tiyenera kusamala.

6. Kodi tingachite bwanji ngati tikuganiza kuti ena sanatichitire chilungamo mumpingo?

6 Tsono tiyerekeze kuti ndi ifeyo amene sanatichitire chilungamo, malinga ndi mmene tikuganizira. Kodi munthu amene ali ndi mtendere wa Kristu mumtima mwake angachite bwanji? Mwina tingaone kuti n’kofunika kulankhula ndi munthu amene tikuganiza kuti watilakwilayo. Ndiyeno, m’malo mouza wina aliyense nkhaniyo, bwanji osaitula m’manja mwa Yehova m’pemphero ndi kum’khulupirira kuti adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika? (Salmo 9:10; Miyambo 3:5) Mwinanso zingatheke kuti titachita zimenezo, tidzafuna kuithetsa nkhaniyo mumtima mwathu ndi ‘kukhala chete.’ (Salmo 4:4) Nthaŵi zambiri, langizo la Paulo ili lingathandize: “Kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso.”​—Akolose 3:13.

7. Kodi nthaŵi zonse tiyenera kukumbukira chiyani pamene tikukhala ndi abale athu?

7 Komabe, chilichonse chimene tingachite, tiyenera kukumbukira kuti ngakhale kuti sitingaletse zimene zachitikazo, tingathe kulamulira mmene tingachitire pankhaniyo. Ngati tichitapo kanthu mosaganiza bwino tikaona ngati kuti ena sanatichitire chilungamo, tingawononge kwambiri mtendere wathu kuposa mmene chosalungamocho chingauwonongere. (Miyambo 18:14) Tingakhumudwe ndi kuleka kusonkhana ndi mpingo kufikira titaona kuti chilungamo chachitika. Wamasalmo analemba kuti amene amakonda chilamulo cha Yehova “alibe chokhumudwitsa.” (Salmo 119:165) Tiyenera kuzindikira kuti munthu aliyense ena sam’chitira chilungamo nthaŵi ndi nthaŵi. Musalole kuti kutumikira kwanu Yehova kusokonezeke chifukwa choti wina sanakuchitireni chilungamo. M’malo mwake, mtendere wa Kristu uchite ufumu mumtima wanu.

Tikamavutika ndi Nkhaŵa

8. Kodi zinthu zina zimene zimayambitsa nkhaŵa n’ziti, ndipo nkhaŵayo zotsatira zake n’zotani?

8 Aliyense amavutika ndi nkhaŵa “masiku otsiriza” ano. (2 Timoteo 3:1) N’zoona kuti Yesu ananena kuti: “Musade nkhaŵa ndi moyo wanu, chimene mudzadya; kapena ndi thupi lanu, chimene mudzavala.” (Luka 12:22) Koma sikuti nkhaŵa zonse zimayamba chifukwa choganizira zinthu zakuthupi. Loti ‘analema mtima’ chifukwa cha makhalidwe oipa a anthu a ku Sodomu. (2 Petro 2:7) Paulo anavutika ndi “nkhaŵa chifukwa cha mipingo yonse.” (2 Akorinto 11:28, NW) Yesu anavutika maganizo kwambiri usiku wotsatizana ndi tsiku la imfa yake kotero kuti “thukuta lake linakhala ngati madontho aakulu a mwazi alinkugwa pansi.” (Luka 22:44) Inde, nkhaŵa zina zimakhalapo osati chifukwa chakuti chikhulupiriro cha munthuyo chafooka ayi. Komabe, zilibe kanthu kuti nkhaŵayo yayamba bwanji, ngati ikula ndi kupitirizabe kukhalapo, ingatilande mtendere wathu. Nkhaŵa yafooketsa anthu ena ndi kuwachititsa kuganiza kuti sangapitirize kusamalira maudindo a kutumikira Yehova. Baibulo limati: “Nkhawa iŵeramitsa mtima wa munthu.” (Miyambo 12:25) Kodi tingachitenji ngati tikuvutika kwambiri ndi nkhaŵa?

9. Kodi ndi njira zina zothandiza ziti zimene tingatsatire kuti tichepetse nkhaŵa, koma kodi ndi zoyambitsa nkhaŵa ziti zomwe sitingathe kuzichotsa?

9 Nthaŵi zina, tingachite zinthu zothandiza. Ngati nkhaŵayo yayambika chifukwa cha matenda, ndi bwino kuchitapo kanthu mwamsanga, ngakhale kuti nkhani zimenezi n’zoti munthu amasankha payekha. * (Mateyu 9:12) Ngati talema chifukwa cha kuchuluka kwa maudindo, titha kugaŵirako anthu ena. (Eksodo 18:13-23) Koma bwanji za ena​—monga makolo​—amene ali ndi maudindo aakulu osatheka kugaŵira ena? Bwanji za Mkristu amene mwamuna kapena mkazi wake ndi wosakhulupirira ndipo amam’tsutsa kwambiri? Nanga za banja limene likuvutika kwambiri chifukwa chosoŵa ndalama kapena kukhala m’dera limene muli nkhondo? Inde, sitingathe kuchotsa zinthu zonse zimene zimayambitsa nkhaŵa m’dziko lino. Komabe, tingasunge mtendere wa Kristu m’mitima yathu. Motani?

10. Kodi ndi njira ziŵiri ziti zimene Mkristu angatsatire kuti achepetse nkhaŵa?

10 Njira imodzi ndiyo kufuna kuti Mawu a Mulungu atitonthoze mtima. Mfumu Davide inalemba kuti: “Pondichulukira zolingalira zanga m’kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.” (Salmo 94:19) “Zotonthoza” za Yehova zimapezeka m’Baibulo. Kuŵerenga Buku limene analiuzirali nthaŵi zonse kudzatithandiza kusunga mtendere wa Kristu m’mitima yathu. Baibulo limati: “Umsenze Yehova nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza: nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” (Salmo 55:22) Paulo analembanso chimodzimodzi kuti: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Kupemphera nthaŵi zonse kochokera pansi pa mtima kudzatithandiza kusunga mtendere wathu.

11. (a) Kodi Yesu anali motani chitsanzo chabwino pankhani yopemphera? (b) Kodi pemphero tiyenera kuliona motani?

11 Yesu anali chitsanzo chabwino kwambiri pankhani imeneyi. Nthaŵi zina, anali kulankhula ndi Atate wake wakumwamba m’pemphero kwa maola ambiri. (Mateyu 14:23; Luka 6:12) Pemphero linamuthandiza kupirira chiyeso choipa kwambiri. Usiku uja asanaphedwe, anavutika maganizo kwambiri. Ndiyeno anachita bwanji? Anapemphera “kolimba.” (Luka 22:44) Inde, Mwana wangwiro wa Mulungu anali munthu wokonda kupemphera. Kuli bwanji nanga otsatira ake opanda ungwiro! Kodi safunika kukhala ndi chizoloŵezi chopemphera? Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti “ayenera iwo kupemphera nthaŵi zonse, osafooka mtima.” (Luka 18:1) Pemphero ndi njira yeniyeni ndiponso yofunika kwambiri yolankhulana ndi Iye amene amatidziŵa bwino kwambiri kuposa mmene timadzidziŵira ife eni. (Salmo 103:14) Kuti tisunge mtendere wa Kristu m’mitima yathu, tiyenera ‘kupemphera kosaleka.’​—1 Atesalonika 5:17.

Kugonjetsa Zofooka Zathu

12. Kodi zifukwa zimene zingachititse ena kuganiza kuti utumiki wawo ndi wosakwanira n’ziti?

12 Yehova amaona mtumiki wake aliyense kukhala wofunika. (Hagai 2:7) Komabe, ambiri zimawavuta kuti avomereze zimenezi. Ena angataye mtima chifukwa cha kukalamba, kuchuluka kwa maudindo a banja, kapena kudwala. Ena angaganize kuti alibe mwayi uliwonse chifukwa cha zinthu zokhumudwitsa zimene akumana nazo paubwana wawo. Ndiponso ena angavutike maganizo chifukwa cha zolakwa zimene anachita kale, ndipo amakayika ngati Yehova angawakhululukire. (Salmo 51:3) Kodi tingatani ngati tili ndi nkhaŵa zimenezo?

13. Kodi Malemba amawalimbikitsa motani anthu amene akuganiza kuti ali opereŵera?

13 Mtendere wa Kristu udzatithandiza kutsimikiza kuti Yehova amatikonda. Tingasunge mtendere umenewo mumtima mwathu mwa kusinkhasinkha mawu a Yesu. Iye sananene kuti kufunika kwathu kumadziŵika poyerekeza zimene ife tikuchita ndi zimene ena akuchita. (Mateyu 25:14, 15; Marko 12:41-44) Anatsindika kuti chofunika kwambiri ndi kukhulupirika. Anawauza ophunzira ake kuti: “Iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.” (Mateyu 24:13) Yesu mwini “ananyozedwa” ndi anthu, komabe sanakayike kuti Atate wake anali kum’konda. (Yesaya 53:3; Yohane 10:17) Ndipo anawauza ophunzira ake kuti nawonso anali kuwakonda. (Yohane 14:21) Potsindika zimenezi, Yesu anati: “Kodi mpheta ziŵiri sizigulidwa kakobiri? ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu [kudziŵa, NW]: komatu inu, matsitsi onse a m’mutu mwanu aŵerengedwa. Chifukwa chake musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri.” (Mateyu 10:29-31) Umenewu ndi umboni wosangalatsa wotsimikiza kuti Yehova amatikonda!

14. Kodi tikutsimikiza bwanji kuti Yehova amationa tonsefe kukhala ofunika kwambiri?

14 Yesu ananenanso kuti: “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine am’koka iye.” (Yohane 6:44) Popeza kuti Yehova watikoka kuti titsatire Yesu, ndiye kuti akufuna kuti tikapulumuke. Yesu anawauza ophunzira ake kuti: “Sichili chifuniro cha Atate wanu wa Kumwamba kuti mmodzi wa ang’ono awa atayike.” (Mateyu 18:14) Choncho, ngati mukutumikira ndi mtima wonse, kondwerani ndi ntchito zanu zabwino. (Agalatiya 6:4) Ngati mukumva chisoni chifukwa cha zolakwa zimene munachita kale, khulupirirani kuti Yehova adzakhululukira “koposa” anthu amene alapadi. (Yesaya 43:25; 55:7) Ngati mwataya mtima pazifukwa zina, kumbukirani kuti “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.”​—Salmo 34:18.

15. (a) Kodi Satana amayesa kuchita zotani kuti atilande mtendere wathu? (b) Kodi tingakhale ndi chidaliro chotani mwa Yehova?

15 Satana amafuna kuti akulandeni mtendere wanu. Ndi amene anayambitsa tchimo lobadwa nalo limene tonsefe tikulimbana naloli. (Aroma 7:21-24) Amafuna kuti muziganiza kuti Mulungu sayanja utumiki wanu chifukwa chakuti ndinu wopanda ungwiro. Musalole kuti Mdyerekezi akufooketseni! Dziŵani kuchenjera kwake, ndipo kudziŵa zimenezo kukuthandizeni kupirirabe. (2 Akorinto 2:11; Aefeso 6:11-13) Kumbukirani kuti “Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse.” (1 Yohane 3:20) Yehova samangoyang’ana zofooka zathu zokha ayi. Amaonanso maganizo athu ndi zolinga zathu. Ndiyetu mawu a wamasalmo akutonthozeni mtima. Iye anati: “Yehova sadzasiya anthu ake, ndipo sadzataya cholandira chake.”​—Salmo 94:14.

Ogwirizana pa Mtendere wa Kristu

16. Kodi ndi motani mmene sitili tokha pamene tikuyesetsa kupirira?

16 Paulo analemba kuti mtendere wa Kristu uchite ufumu m’mitima yathu chifukwa ‘tinaitanidwa m’thupi limodzi.’ Akristu odzozedwa amene Paulo anali kuwalembera, anaitanidwa kuti akhale ziwalo za thupi la Kristu, monga momwe alili otsalira odzozedwa lerolino. Anzawo a “nkhosa zina” akugwirizana nawo monga “gulu limodzi” limene Yesu Kristu “mbusa mmodzi” akuliyang’anira. (Yohane 10:16) Onse pamodzi, “gulu” la anthu miyandamiyanda, alola mtendere wa Kristu kuchita ufumu m’mitima yawo. Kudziŵa kuti sitili tokha kumatithandiza kwambiri kuti tipirire. Petro analemba kuti: “Mum’kanize [Satana] okhazikika m’chikhulupiriro, podziŵa kuti zoŵaŵa zomwezo zilimkukwaniridwa pa abale anu ali m’dziko.”​—1 Petro 5:9.

17. Kodi tili ndi zifukwa zotani zochititsa kuti mtendere wa Kristu uchite ufumu m’mitima yathu?

17 Ndiyetu tiyeni tonsefe tikulitse mtendere, chipatso chofunika kwambiri chimenechi cha mzimu woyera wa Mulungu. (Agalatiya 5:22, 23) M’kupita kwa nthaŵi, anthu amene Yehova adzawapeza opanda banga, opanda chilema, ndiponso amtendere adzawadalitsa ndi moyo wosatha m’dziko lapansi la paradaiso, mmene mudzakhalitsa chilungamo. (2 Petro 3:13, 14) Tili ndi zifukwa zokwanira zochititsa kuti mtendere wa Kristu uchite ufumu m’mitima yathu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Nthaŵi zina, nkhaŵa ingayambe kapena kukula chifukwa cha matenda, monga matenda a maganizo.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi mtendere wa Kristu n’chiyani?

• Kodi mtendere wa Kristu ungachite ufumu m’mitima yathu motani ngati ena atichitira mosalungama?

• Kodi mtendere wa Kristu umatithandiza motani kulimbana ndi nkhaŵa?

• Kodi mtendere wa Kristu umatitonthoza mtima motani tikamaganiza kuti ndife opanda pake?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 15]

Yesu ali pamaso pa om’neneza mlandu, anatula nkhani m’manja mwa Yehova

[Chithunzi patsamba 16]

Monga kukumbatira kwa tate wachikondi, zotonthoza za Yehova zingachepetse nkhaŵa yathu

[Chithunzi patsamba 18]

Kupirira n’kwamtengo wapatali pamaso pa Yehova