Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Akolose 1:16 amanena za Mwana wa Mulungu kuti “zinthu zonse zinalengedwa mwa Iye ndi kwa Iye.” Kodi zinthu zonse zinalengedwa “kwa” Mwana wa Mulungu, Yesu, motani?

Yehova anagwiritsa ntchito Mwana wake wobadwa yekha ngati mmisiri polenga zinthu zina zonse, ndiko kuti, zinthu zonse kupatulapo Yesu mwiniyo. (Miyambo 8:27-30; Yohane 1:3) Moyenerera, Mwanayo amakondwera ndi zinthu zimene analengazi, ndipo m’ganizo limeneli zinalengedwa “kwa” iye.

Tikudziŵa kuti makolo amayembekeza kukondwera, ndipo nthaŵi zambiri amakondweradi ndi ana awo. N’chifukwa chake mwambi wa Baibulo umanena za “mwana amene [atate ake] akondwera naye.” (Miyambo 3:12; 29:17) N’chimodzimodzinso kuti Yehova Mulungu anakondwera ndi Aisrayeli pamene anthu akewo anali okhulupirika. (Salmo 44:3; 119:108; 147:11) Amakondweranso ndi kukhulupirika kwa anthu ake lerolino.​—Miyambo 12:22; Ahebri 10:38.

Motero, zinali zoyenera kuti Mulungu anafuna kuti wantchito mnzake, Yesu, akondwere ndi ntchito imene anagwira. Ndipotu, Miyambo 8:31 imanena kuti Mwanayo ‘anakondwera ndi dziko lake lokhalamo anthu, ndi kusekerera ndi ana a anthu.’ Akolose 1:16 amatanthauza zimenezi pamene akuti: ‘zinthu zonse zinalengedwa mwa Iye ndi kwa Iye.’