Mmene Mungasankhire Mwanzeru
Mmene Mungasankhire Mwanzeru
UFULU wodzisankhira ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Popanda mphatso imeneyi tikanakhala ngati maloboti tikumalephera kulamulira zochita zathu. Komabe mphatsoyi timapeza nayo mavuto. Popeza tili ndi ufulu wodzisankhira, tiyenera kusankha zochita pamoyo wathu.
N’zoona kuti zosankha zambiri n’zosavuta. Komabe zosankha zina monga ntchito, kukwatira kapena kukwatiwa, zimakhudza tsogolo lanu lonse. Komanso zosankha zina zimakhudza anthu ena. Zina zomwe makolo amasankha zimakhudza kwambiri ana awo. Kuwonjezera apo, tidzadziŵerengera mlandu kwa Mulungu pa zinthu zambiri zomwe timasankha.—Aroma 14:12.
M’pofunika Thandizo
Kuyambira kale, mbiri ikusonyeza kuti munthu sangathe kusankha bwino payekha. Chimodzi mwa zosankha zoyambirira zolembedwa m’mabuku chomwe munthu anasankha chinali chowononga kwabasi. Hava anasankha kudya chipatso chomwe Mulungu analetsa mosapita m’mbali. Zomwe iye anasankha chifukwa cha chikhumbo chake chadyera, zinachititsa mwamuna wake kugwirizana naye kusamvera Mulungu, ndipo zotsatira zake zinali mavuto adzaoneni kwa anthu. Nthaŵi zambiri, anthu amasankhabe zinthu potsata zikhumbo zawo zadyera osati mfundo zabwino zachikhalidwe. (Genesis 3:6-19; Yeremiya 17:9) Kaŵirikaŵiri tikamafuna kusankha zochita pankhani zofunika kwambiri m’pamene timazindikira kupereŵera kwa nzeru zathu.
N’chifukwa chake anthu ambiri akamasankha zochita pankhani zofunika kwambiri amafuna thandizo ku magwero apamwamba kuposa anthu. Baibulo limasimba za nthaŵi imene Nebukadinezara anayenera kusankha zochita nkhondo ili m’kati. Ngakhale kuti anali mfumu anaona kuti ndibwino kuti “aombeze maula,” kufunsa mizimu. Choncho nkhaniyo imati: “Agwedeza mivi, afunsira kwa aterafi, apenda ndi chiwindi.” (Ezekieli 21:21) Anthu ambiri lerolinonso amafunsira kwa anthu olosera mwayi, openda nyenyezi, ndiponso amafunsira kwa mizimu m’njira zinanso. Koma zomwe olosera ndiponso mizimu imauza anthu zimakhala zabodza ndiponso zosocheretsa.—Levitiko 19:31.
Pali Mmodzi yekha amene ali wodalirika ndiponso amene wathandizadi anthu kusankha mwanzeru mmbuyo monsemu. Mmodzi yekha ameneyu sangakhalenso wina koma Yehova Mulungu. Mwachitsanzo, m’nthaŵi zakale, Mulungu anapatsa mtundu wake, Israyeli, Urimu ndi Tumimu, zomwe mwachionekere zinali maere opatulika amene mtunduwo unkagwiritsa ntchito posankha zochita pankhani zofunika kwambiri. Mwakugwiritsa ntchito Urimu ndi Tumimu, Yehova ankayankha mwachindunji zomwe anali kum’funsa ndiponso zinathandiza akulu a Israyeli kukhala otsimikiza kuti zosankha zawo zinali zogwirizana ndi chifuniro chake.—Eksodo 28:30; Levitiko 8:8; Numeri 27:21.
Talingalirani chitsanzo china ichi. Pamene Gideoni anamuitana kuti atsogolere magulu ankhondo a Israyeli kukamenyana ndi a Midyani, iye anayenera kusankha kuvomera udindo wapamwambawo kapena ayi. Gideoni anapempha Oweruza 6:33-40; 7:21, 22.
chizindikiro chozizwitsa kuti atsimikize kuti Yehova adzamuthandiza. Anapemphera kuti chikopa chaubweya chomwe anachisiya panja usiku chichite mame koma dothi lozungulira chikopacho likhale louma. Usiku wotsatira anapempha kuti chikopacho chikhale chouma koma dothi lozungulira chikopacho linyowe ndi mame. Yehova mokoma mtima anamuchitira Gideoni chizindikiro chomwe anapempha. Zotsatira zake zinali zakuti Gideoni anasankha molondola ndipo mothandizidwa ndi Mulungu, anagonjetseratu adani a Israyeli.—Nanga Bwanji Lerolino?
Lerolino, Yehova amathandizanso atumiki ake akamasankha zochita pankhani zofunika kwambiri. Motani? Kodi ifenso tiyenera kupempha Yehova ‘chizindikiro cha mame pachikopa chaubweya,’ monga anachitira Gideoni, kuti chitithandize kusankha bwino? Mwamuna wina ndi mkazi wake ankadzifunsa ngati kunali koyenera kuti asamukire kudera lomwe kunkafunika olalikira Ufumu ambiri. Pofuna kupeza yankho, iwo anakonza mayeso. Anapangana zogulitsa nyumba yawo pamtengo winawake. Iwo anagwirizana kuti anthu akagula nyumbayo pamasiku omwe anaika ndiponso pamtengo womwe anaika kapena kuposerapo ndiye kuti Mulungu walola kuti iwo asamuke. Koma ngati anthu sagula nyumbayo ndiye kuti Mulungu sakufuna kuti iwo asamuke.
Anthu sanagule nyumbayo. Kodi zimenezi zinasonyeza kuti Yehova sanafune kuti banjalo likatumikire komwe kunkafunika olalikira ambiri? Kunena zoona, sitingathe kutchula zinthu zomwe Yehova amachitira atumiki ake ndi zomwe samawachitira. Sitinganene kuti Yehova masiku ano saloŵerera kuti atisonyeze chifuno chake. (Yesaya 59:1) Komabe, sitiyenera kuyembekezera kuti Mulungu aziloŵerera pa zosankha zathu zofunika kwambiri, tikumamusiyira udindo wotisankhira zochita. Ndithudi, ngakhale Gideoni nthaŵi zambiri ankasankha yekha zochita popanda zizindikiro zozizwitsa zochokera kwa Yehova.
Komabe, Baibulo limanena kuti Mulungu amatitsogolera. Linalosera za nthaŵi yathu ino kuti: “Makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.” (Yesaya 30:21) Tikamasankha zochita pankhani zofunika kwambiri, ndibwino kuonetsetsa kuti zomwe tasankhazo n’zogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndi kuti tikutsatira nzeru zake zapamwamba. Tingachite motani zimenezi? Mwakuŵerenga Mawu ake ndi kuwalola kukhala ‘nyali ya ku mapazi athu, ndi kuunika kwa panjira pathu.’ (Salmo 119:105; Miyambo 2:1-6) Kuti tichite zimenezi, tiyenera kukulitsa chizoloŵezi chofuna kudziŵa zolondola kuchokera m’Baibulo. (Akolose 1:9, 10) Ngati tikufuna kusankha zochita, tifufuze mosamalitsa mfundo zachikhalidwe zonse za m’Baibulo zokhudzana ndi nkhaniyo. Kufufuza koteroko kudzatithandiza “kutsimikizira zinthu zofunika kwambiri.”—Afilipi 1:9, 10, NW.
Tiyeneranso kulankhula ndi Yehova m’pemphero tikumakhulupirira kuti adzatimva. N’zolimbikitsatu kwambiri kufotokozera Mulungu wathu wachikondi zomwe tikufuna kusankha ndiponso zomwe tikufunika kuzilingalira. Tikatero, tim’pemphe mosakayikira kuti atitsogolere kusankha molondola. Nthaŵi zambiri mzimu woyera udzatikumbutsa mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo zomwe zikugwirizana ndi nkhaniyo, kapena ungatithandize kumvetsa bwino lemba Yakobo 1:5, 6.
linalake lomwe likugwirizana ndi nkhaniyo.—Yehova waperekanso anthu okhwima maganizo mumpingo amene tingakambirane nawo zosankha zathu. (Aefeso 4:11, 12) Komabe, pofunsira kwa anthu ena tisatsatire zomwe ena amachita zofunsa anthu ambiri mpaka atapeza yemwe akunena zofuna zawo, ndiyeno n’kutsatira uphungu wake. Tikumbukirenso chitsanzo chotichenjeza cha Rehabiamu. Pamene ankafuna kupanga chosankha chachikulu kwambiri, analandira uphungu wabwino kwabasi kuchokera kwa anthu achikulire amene ankagwira ntchito ndi abambo ake. Koma m’malo motsatira uphungu wawo, iye anakafunsira kwa anyamata anzake. Atatsatira uphungu wa anyamatawo, sanasankhe mwanzeru ndipo zotsatira zake zinali zakuti anthu m’chigawo chachikulu cha ufumu wake anam’pandukira.—1 Mafumu 12:1-17.
Tikafuna kufunsira uphungu, tifunsire kwa anthu amene aona zambiri m’moyo ndiponso omwe amadziŵa bwino Malemba komanso amene amaona mfundo zabwino zachikhalidwe kukhala zofunika. (Miyambo 1:5; 11:14; 13:20) Ngati n’kotheka, sinkhasinkhani pa mfundo zachikhalidwe zomwe zikugwirizana ndi nkhaniyo ndiponso zomwe mwapeza pakufufuza kwanu. Mukayamba kuona zinthu m’kuunika kwa Mawu a Mulungu, chosankha cholondola chidzaonekeratu.—Afilipi 4:6, 7.
Zomwe Timasankha
Zochita zina n’zosavuta kusankha. Atawalamula kuti aleke kulalikira, atumwi anadziŵa kuti ayenera kupitiriza kulalikira za Yesu. Mwamsanga anauza bwalo lamilandu la Sanihedirini kuti asankha kumvera Mulungu koposa anthu. (Machitidwe 5:28, 29) Zosankha zina zingafunikire kuzilingalira mofatsa chifukwa chakuti palibe mawu a m’Baibulo achindunji ogwirizana ndi nkhanizo. Komabe, mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo zidzatiunikira kusankha molondola kwambiri. Mwachitsanzo, ngakhale kuti zosangalatsa zambiri zomwe ziliko masiku ano kunalibe m’nthaŵi ya Yesu, pali mawu omveka bwino a m’Baibulo okhudza zomwe zimakondweretsa Yehova ndi zomwe sizimukondweretsa. Choncho, Mkristu aliyense amene amachita nawo kapena kuonerera zosangalatsa zimene zimalimbikitsa chiwawa, chiwerewere, kapena kupanduka ndiye kuti sanasankhe bwino.—Salmo 97:10; Yohane 3:19-21; Agalatiya 5:19-23; Aefeso 5:3-5.
Nthaŵi zina, n’kutheka kuti zosankha zonse ziŵiri n’zolondola. Kusankha kukatumikira kumene kukufunika olalikira ambiri ndi mwayi wapadera kwambiri ndipo tingapeze nako madalitso ochuluka. Koma ngati munthu pazifukwa zina wasankha kusachita zimenezo, angachitebe ntchito yabwino mumpingo wakwawo. Nthaŵi zina pamakhala zosankha zina zomwe zimatipatsa mwayi wosonyeza kudzipereka kwathu konse kwa Yehova kapena kusonyeza zomwe timakonda kwambiri pamoyo wathu. Choncho, Yehova amatilola kugwiritsa ntchito ufulu wathu wodzisankhira kuti tisonyeze zomwe zili m’mitima yathu.
Nthaŵi zambiri, zomwe timasankha zimakhudza anthu ena. Mwachitsanzo, Akristu a m’zaka za zana loyamba anasangalala kwambiri kukhala omasuka kuchita zambiri zomwe Chilamulo chinkaletsa. Mwachitsanzo, zimenezi zinatanthauza kuti iwo anali ndi ufulu wosankha kudya kapena kusadya chakudya chomwe m’Chilamulo chinali 1 Akorinto 10:32) Kufuna kusakhumudwitsa ena kungatithandize kwambiri pa zosankha zathu zambiri. Ndiponsotu kukonda anansi athu ndilo lamulo lachiŵiri lalikulu.—Mateyu 22:36, 39.
chodetsedwa. Komabe, analimbikitsidwa kuganizira anthu ena potsatira ufulu wawo umenewu. Mawu a Paulo pankhaniyi angagwire ntchito pa zosankha zathu zambiri. Iye anati: “Khalani osakhumudwitsa.” (Zotsatira za Zosankha Zathu
Kusankha zochita titalingalira bwino ndi moona mtima komanso mogwiritsa ntchito mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo, m’kupita kwa nthaŵi kumakhala ndi zotsatira zabwino nthaŵi zonse. N’zoona kuti zosankha zimenezo mwina zingabweretse mavuto poyambirira. Atumwi atauza bwalo la Sanihedirini kuti asankha kupitirizabe kulalikira za Yesu, anawakwapula asanawamasule. (Machitidwe 5:40) Ahebri atatu aja—Sadrake, Mesake, ndi Abedinego—atasankha kusagwadira fano lagolide la Nebukadinezara, anaika miyoyo yawo pangozi. Anali okonzeka kufa chifukwa cha chosankha chawo. Anadziŵa kuti Mulungu adzawakonda ndiponso kuwadalitsa.—Danieli 3:16-19.
Ngati tavutika pambuyo posankha zochita mwachikumbumtima, palibe chifukwa choganizira kuti tinasankha molakwika. “Nthaŵi ndi zochitika zosadziŵika” zingawononge kwambiri zotsatira za zimene tasankha ngakhale zitakhala zabwino kwambiri. (Mlaliki 9:11) Ndiponso, Yehova amalola mavuto kuti aone ngati tilidi otsimikiza pa zomwe tasankhazo. Yakobo analimbana kwambiri ndi mngelo usiku wonse asanalandire madalitso. (Genesis 32:24-26) Nafenso tingalimbane kwambiri ndi mavuto ngakhale zomwe tikuchitazo zili zolondola. Komabe, ngati zomwe tasankha zili zogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu, titha kukhulupirira kuti adzatithandiza kupirira ndipo potsirizira pake tidzapeza madalitso.—2 Akorinto 4:7.
Choncho, posankha zochita pankhani zofunika kwambiri, musadalire nzeru zanu zokha. Fufuzani mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo zomwe zikugwirizana ndi nkhaniyo. Lankhulani ndi Yehova za nkhaniyo. Ngati kuli koyenera, funsirani kwa Akristu anzanu okhwima maganizo. Ndiyeno limbani mtima. Gwiritsani ntchito mwanzeru ufulu wanu wodzisankhira womwe Mulungu anakupatsani. Sankhani mwanzeru ndipo sonyezani kwa Yehova kuti mtima wanu uli wowongoka kwa iye.
[Chithunzi patsamba 28]
Fufuzani kaye m’Mawu a Mulungu musanasankhe zochita pankhani zofunika kwambiri
[Zithunzi patsamba 28, 29]
Lankhulani ndi Yehova pa zomwe muyenera kusankha
[Chithunzi patsamba 30]
Mungakambirane zosankha zanu zazikulu ndi Akristu okhwima maganizo