Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Amagwiritsa Ntchito Dzina la Mulungu ku Central Africa

Amagwiritsa Ntchito Dzina la Mulungu ku Central Africa

Amagwiritsa Ntchito Dzina la Mulungu ku Central Africa

ANTHU ambiri ku Central Africa amakhulupirira Mulungu. Amakhulupirira kuti iye ndiye Analenga zinthu zonse. (Chivumbulutso 4:11) Komabe, monga amachitira anthu ambiri kwina kulikonse, nthaŵi zambiri iwo amanyalanyaza dzina lake lenileni lakuti Yehova.

Anthu a ku Central Africa, ndiponso a m’madera ena a dziko lapansi, amanena za dzina la Mulungu akamatchula mawu a m’pemphero la Ambuye akuti, “Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Koma kwanthaŵi yaitali, anthu ochepa okha ndiwo ankalidziŵa dzina limeneli. Komabe kwa zaka zambiri, ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova yasintha maganizo a anthu pankhani yogwiritsa ntchito dzina la Mulungu. Masiku ano, dzina la Mulungu n’lodziŵika kwambiri ndiponso ndi lovomerezeka m’zinenero zambiri za mu Africa monga Chizulu (uJehova), Chiyoruba (Jehofah), Xhoza (uYehova), ndiponso Chiswahili (Yehova). Ngakhale zili choncho, mabaibulo ambiri a m’zinenero zimenezi akupeŵabe kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu.

Baibulo labwino lomwe limagwiritsa ntchito dzina la Mulungu ndi la m’chinenero cha Chizande chomwe amalankhula m’madera ena a dziko la Central African Republic, Sudan, ndi Democratic Republic of Congo. M’madera amenewo, anthu amagwiritsa ntchito dzina la Mulungu lomwe m’chinenero chawocho amalilemba kuti Yekova. Kaya dzina la Mulungu limeneli amalilemba motani m’chinenero cha kwanuko, n’kofunika kwambiri kuligwiritsira ntchito. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti, ‘aliyense amene adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.’​—Aroma 10:13.

[Mapu/​Chithunzi patsamba 32]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

SUDAN

CENTRAL AFRICAN REPUBLIC

DEMOCRATIC REPUBLIC OF CONGO

[Mawu a Chithunzi]

The Complete Encyclopedia of Illustration/​J. G. Heck